Mutu 54
“Mkate Wowona Wakumwamba”
TSIKU ladzulo linalidi la zochitika zambiri. Yesu anadyetsa mozizwitsa zikwi zambiri ndiyeno anazemba kuyesayesa kwa anthu kwa kumpanga mfumu. Usiku umenewo iye anayenda pa Nyanja ya Galileya yoŵindukayo; anapulumutsa Petro, amene anayamba kumira pamene anayenda pamwamba pamadzi oŵinduka ndi mkutho; ndipo anatontholetsa mafunde kupulumutsa ophunzira ake kuti chombo chisasweke.
Tsopano anthu amene Yesu anadyetsa mozizwitsa chakumpoto kummaŵa kwa Nyanja ya Galileya akumpeza pafupi ndi Kapernao nafunsa kuti: “Munadza kuno liti?” Powadzudzula, Yesu akunena kuti iwo amfunafuna kokha chifukwa chakuti akuyembekezera kuti apeza chakudya china chaulere. Iye akuwafulumiza kugwirira ntchito osati chakudya chimene chimawonongeka, koma chakudya chimene chimakhala kumoyo wosatha. Chotero anthuwo akufunsa kuti: “Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?”
Yesu akutchula imodzi yokha ya ntchito zamtengo wapamwamba koposa. “Ntchito ya Mulungu ndi iyi,” iye akufokoza motero, “kuti mukhulupilire iye amene Iyeyo anamtuma.”
Komabe, anthuwo, sakukhulupilira Yesu, mosasamala kanthu za zozizwitsa zonse zimene wachita. Modabwitsa, ngakhale pambuyo pa zinthu zonse zozizwitsa zimene iye wachita, iwo akufunsa kuti: “Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tiwone ndi kukhulupilira inu? muchita chiyani? Atate athu anadya mana m’chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m’mwamba anawapatsa iwo kudya.”
Poyankha pempho lawo la chizindikiro, Yesu akumveketsa Magwero a makonzedwe ozizwitsawo, akumati: “Si Mose amene anakupatsani inu mkate wakumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate wowona wakumwamba. Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.”
“Ambuye,” anthuwo akutero, “tipatseni ife mkate umenewu nthaŵi zonse.”
“Ine ndine mkate wa moyowo,” akufotokoza motero Yesu. “Iye amene akhulupirira ine sadzamva njala konse, ndi iye amene akhulupilira ine sadzamva ludzu nthaŵi zonse. Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiwona, simukhulupilira. Chinthu chonse chimene anandipatsa ine Atate chidzadza kwa ine; ndipo wakudza kwa ine sindidzamtaya iye kunja. Pakuti ndinatsika kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma ine. Koma chifuniro cha iye amene anandituma ine ndi ichi, kuti za ichi chonse iye anandipatsa ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza. Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupilira iye, akhale nawo moyo wosatha.”
Pa izi Ayuda akuyamba kung’ung’udza kwa Yesu chifukwa chakuti adati, “Ine ndine mkate wotsika kumwamba.” Iwo sakuwona mwa iye chirichonse koposa kuti ndiye mwana wa makolo aumunthu ndipo chotero mofanana ndi mmene anachitira anthu a ku Nazarete, iwo atsutsa, kuti: “Si Yesu uyu mwana wa Yosefe, atate wake ndi amake timawadziŵa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika kumwamba?”
“Musang’ung’udze wina ndi mnzake,” Yesu akuyankha motero. “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Chalembedwa kwa aneneri, Ndipo iwo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa ine. Sikuti munthu wina wawona Atate, koma iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo wawona Atate. Indetu, indetu ndinena ndi inu, Iye wokhulupilira ali nawo moyo wosatha.”
Popitirizabe, Yesu akubwereza kuti: “Ine ndine mkate wa moyo. Makolo anu adadya m’chipululu, ndipo adamwalira. Mkate wotsika kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wamoyo wotsika kumwamba ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha.” Inde, mwa kusonyeza chikhulupiliro mwa Yesu, wotumidwa ndi Mulungu, anthu angathe kukhala ndi moyo wosatha. Palibe mana, kapena mkate wina uliwonse, umene ungapereke zimenezo!
Mwachiwonekere kukambitsirana konena za mkate wochokera kumwamba kunayamba mwamsanga anthu atapeza Yesu pafupi ndi Kapernao. Koma kukupitirizabe, kukumafika pachimake pambuyo pake pamene Yesu akuphunzitsa m’sunagoge m’Kapernao. Yohane 6:25-51, 59; Salmo 78:24; Yesaya 54:13; Mateyu 13:55-57.
▪ Kodi ndizochitika zotani zimene zinayambitsa kukambitsirana kwa Yesu konena za mkate wochokera kumwamba?
▪ Polingalira za zimene Yesu wangochita kumene, kodi nchifukwa ninji pempho la chizindikiro liri losayenerera kwambiri?
▪ Kodi nchifukwa ninji Ayuda akung’ung’udza ponena za kudzinenera kwa Yesu kuti iye ndiye mkate wowona wochokera kumwamba?
▪ Kodi nkuti kumene kukambitsirana konena za mkate wochokera kumwamba kunachitikira?