Mutu 60
Kuwoneratu Ulemelero wa Ufumu wa Kristu
YESU wadza kumadera a Kaisareya wa Filipi, ndipo akuphunzitsa khamu la anthu lophatikizapo atumwi ake. Iye akuwadabwitsa ndi chilengezo ichi: “Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu atadza muufumu wake.”
‘Kodi Yesu akutanthauzanji?’ ophunzirawo ayenera kuzizwa motero. Pafupifupi mlungu umodzi pambuyo pake, Yesu akutenga Petro, Yakobo, Yohane, nakwera nawo m’phiri. Mwinamwake ndiusiku, popeza kuti ophunzirawo akuwodzera. Pamene Yesu akupemphera, iye akusandulika pamaso pawo. Nkhope yake ikuyamba kuŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake kunyezimira ngati kuŵala.
Ndiyeno, pakuwoneka anthu aŵiri, ozindikiridwa kukhala “Mose ndi Eliya,” nayamba kulankhula ndi Yesu ponena za ‘kuchoka kwake kumene kudzachitikira mu Yerusalemu.’ Kuchokako mwachiwonekere kukusonya ku imfa ya Yesu ndi chiukiriro chake chotsatirapo. Motero, kukambitsiranaku kukutsimikizira kuti imfa yake yochititsa manyaziyo sikhoza kupeŵedwa, monga mmene Petro adakhumbira.
Ali ogalamuka kotheratu, ophunzirawo akupenya ndi kumvetsera mozizwa. Ngakhale kuti amenewa ali masomphenya, akuwonedwa kukhala chochitika chenicheni kotero kuti Petro akuyamba kutengamo mbali m’chochitikacho, akumati: “Ambuye, kuli kwabwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.”
Pamene Petro ali chilankhulire, mtambo woŵala ukuwaphimba, ndipo liwu lochokera mumtambowo likuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” Pomva liwulo, ophunzirawo akugwetsa nkhope zawo pansi. Koma Yesu akuti: “Ukani musawopa.” Pamene akutero, sakuwona wina aliyense kusiyapo Yesu yekha.
Paulendo wawo wotsika m’phirimo tsiku lotsatira, Yesu akulamula kuti: “Musakauze munthu chowonekeracho, kufikira Mwana wa munthu adzauka kwa akufa.” Kuwonekera kwa Eliya m’masomphenyawo kukudzutsa funso m’maganizo mwa ophunzirawo. “Bwanji,” iwo akufunsa motero, “alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?”
“Eliya anadza kale,” Yesu akutero, “ndipo iwo sanamdziŵa iye.” Komabe, Yesu, akulankhula za Yohane Mbatizi, yemwe anakwaniritsa ntchito yofanana ndi ya Eliya. Yohane anakonzekeretsa njira kaamba ka Kristu, monga Eliya anachitira kaamba ka Elisa.
Masomphenya ameneŵa akukhala olimbikitsa chotani nanga, ponse paŵiri kwa Yesu ndi kwa ophunzirawo! Masomphenyawa ali, kuwoneratu ulemerero wa Ufumu wa Kristu, kunena kwake titero. M’chenicheni, ophunzirawo anawona, “Mwana wa munthu atadza muufumu wake,” monga momwe Yesu analonjezera mlungu umodzi pasadakhale. Pambuyo pa imfa ya Yesu, Petro analemba za kukhala kwawo ‘mboni zowona ndi maso za ulemelero wa Kristu pamene anali naye m’phiri loyeralo.’
Afarisiwo afuna chizindikiro kwa Yesu chotsimikizira kuti analidi wolonjezedwayo m’Malemba kukhala Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Iwo sanapatsidwe chizindikiro chotero. Kumbali ina, ophunzira a Yesu a ponda apa npondepo akuloledwa kuwona kusandulika kwa Yesu monga chitsimikizo cha maulosi Aufumu. Motero, Petro pambuyo pake analemba kuti: “Ndipo tiri nawo mawu a chinenero [ulosi] okhazikika koposa.” Mateyu 16:13, 28–17:13; Marko 9:1-13; Luka 9:27-37; 2 Petro 1:16-19.
▪ Kristu asanalaŵe imfa, kodi ena akumuwona motani alinkudza mu Ufumu wake?
▪ M’masomphenyawo, kodi Mose ndi Eliya akukambitsirana za chiyani ndi Yesu?
▪ Kodi nchifukwa ninji masomphenyawa ali chilimbikitso chachikulu motero kwa ophunzirawo?