Mutu 72
Yesu Atuma Okwanira 70
MPHAKASA ya 32 C.E. yafika, zaka zitatu zathunthu chiyambire paubatizo wa Yesu. Posachedwapa iye ndi ophunzira ake anali ku Phwando la Misasa ku Yerusalemu, ndipo mwachiwonekere adakali chapafupipo. Kwenikweni, Yesu akuthera yochuluka ya mbali ya miyezi isanu ndi umodzi yotsala ya uminisitala wakewo mu Yudeya kapena patsidya pa Mtsinje wa Yordano m’dera la Pereya. Gawo limeneli lifunikiranso kumalizidwa.
Zowona, pambuyo pa Paskha wa 30 C.E., Yesu anathera pafupifupi miyezi isanu ndi itatu akulalikira mu Yudeya. Koma Ayudawo atayesayesa kumupha kumeneko pa Paskha wa 31 C.E., iye akuthera chaka chotsatira ndi theka kuphunzitsa pafupifupi ku Galileya kokha. Mkati mwa nthaŵiyo, iye anasonkhanitsa gulu lalikulu, lophunzitsidwa bwino, la alaliki, chinthu chimene sadakhale nacho poyambirirapo. Chotero iye tsopano akuyambitsa mkupiti waukulu womaliza wa kuchitira umboni mu Yudeya.
Yesu akuyambitsa mkupiti umenewu mwa kusankha ophunzira 70 ndi kuwatumiza aŵiriaŵiri. Motero, onse pamodzi pali magulu 35 a olalikira Ufumu ogwira ntchito m’gawolo. Ameneŵa akutsogolera kuloŵa mumzinda uliwonse ndi kumalo kumene Yesu, mwachiwonekere limodzi ndi atumwi ake, akukonzekera kupita.
Mmalo mwa kulangiza 70 amenewo kupita kumasunagoge, Yesu akuwauza kuloŵa m’nyumba za anthu, akumafotokoza kuti: “Ndipo m’nyumba iriyonse mukaloŵamo muthange mwanena, Mtendere ukhale panyumba iyi. Ndipo mukakhala mwana wa mtendere mmenemo, mtendere wanu udzapumula pa iye.” Kodi uthenga wawo uyenera kukhala wotani? “Nimunene nawo,” Yesu akutero, “ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.” Ponena za ntchito ya 70 amenewo, Matthew Henry’s Commentary imasimba kuti: “Mofanana ndi Mbuye wawo, kulikonse kumene anachezako, analalikira kunyumba ndi nyumba.”
Malangizo a Yesu kwa 70 amenewo ngofanana ndi opatsidwa kwa okwanira 12 aja pamene anatuma ameneŵa pa mkupiti wa kulalikira mu Galileya pafupifupi chaka chimodzi chapitacho. Iye sakungochenjeza 70 ameneŵa za chitsutso chomwe adzayang’anizana nacho, kuwakonzekeretsa kupereka uthengawo kwa eni nyumba, koma akuwapatsanso mphamvu ya kuchiritsa odwala. Motero, pamene Yesu akufika mwamsanga pambuyo pake, ambiri adzakhala ofunitsitsa kukumana ndi Mbuyeyo amene ophunzira ake ali okhoza kuchita zinthu zozizwitsa zotero.
Kulalikira kochitidwa ndi 70 amenewo ndi ntchito ya Yesu yotsatira zikutenga nthaŵi yaifupi. Mwamsanga magulu 35 a olalikira Ufumuwo akuyamba kubwerera kwa Yesu. “Ambuye,” iwo akutero mwachisangalalo, “zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” Lipoti lautumiki labwino loterolo likusangalatsadi Yesu, popeza akuyankha kuti: “Ndinawona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Tawonani, ndakupatsani ulamuliro wa kuponda panjoka ndi zinkhanira.”
Yesu akudziŵa kuti pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu panthaŵi ya mapeto, Satana ndi ziwanda zake adzachotsedwa kumwamba. Koma tsopano kuchotsedwa kwa ziwanda zosawoneka kumeneku kochitidwa ndi anthu wamba kukutumikira monga chitsimikizo chowonjezereka cha chochitika cham’tsogolo chimenecho. Chifukwa chake, Yesu akulankhula za kugwa kwam’tsogolo kwa Satana kuchokera kumwamba kukhala kotsimikizirika kotheratu. Chifukwa cha chimenecho, kuli m’lingaliro lophiphiritsira kuti 70 amenewo akupatsidwa mphamvu za kuponda panjoka ndi zinkhanira. Komabe, Yesu akuti: “Musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m’mwamba.”
Yesu ali ndi chisangalalo chochuluka ndipo akutamanda Atate wake mwapoyera kaamba ka kugwiritsira ntchito atumiki ake odzichepetsa ameneŵa mwanjira yamphamvu yoteroyo. Mwakutembenukira kwa ophunzira ake, iye akuti: “Odala masowo akuwona zimene muwona. Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuwona zimene inu muziwona, koma sanaziwona; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimva.” Luka 10:1-24; Mateyu 10:1-42; Chivumbulutso 12:7-12.
▪ Kodi nkuti kumene Yesu analalikirako mkati mwa zaka zitatu zoyambirira za uminisitala wake, ndipo kodi akumaliza gawo liti m’miyezi yake yomalizira isanu ndi umodzi?
▪ Kodi nkuti kumene Yesu akutsogozako 70 amenewo kukafunafuna anthu?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akunena kuti anawona Satana atagwa kale kuchokera kumwamba?
▪ Kodi ndim’lingaliro lotani limene 70 amenewo angapondere njoka ndi zinkhanira?