Mutu 88
Munthu Wachuma ndi Lazaro
YESU anali kulankhula ndi ophunzira ake za kugwiritsidwa ntchito koyenera kwa chuma chakuthupi, akumafotokoza kuti sitingathe kukhala akapolo a chimenechi panthaŵi imodzimodziyo kukhala akapolo a Mulungu. Afarisi nawonso akumvetsera, ndipo iwo akuyamba kunyodola Yesu chifukwa chakuti iwo ali okonda ndalama. Chotero iye akuti kwa iwo: “Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chiri chonyansa pamaso pa Mulungu.”
Nthaŵi yafika yakuti zinthu zisinthidwe kwa anthu amene ali olemera ndi chuma cha m’dziko, m’mphamvu za ndale za dziko, ndi muulamuliro wachipembedzo ndi chisonkhezero. Iwo adzatsitsidwa. Komabe, anthu amene amazindikira chosoŵa chawo chauzimu adzatukulidwa. Yesu akusonyeza masinthidwe otero pamene iye akupitirizabe kunena ndi Afarisi kuti:
“Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane [Mbatizi]; kuyambira pamenepo ulalikidwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akukangamira kulowamo. Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang’ono ka Chilamulo kagwe nkwapatali.”
Alembi ndi Afarisi ngonyada ndi kudzinenera kwawo kukhala omamatira ku Chilamulo cha Mose. Kumbukirani kuti pamene Yesu anachiritsa mwamuna wina mozizwitsa kuti awone mu Yerusalemu, iwo anadzitamandira kuti: “Ife ndife akuphunzira a Mose. Tidziŵa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose.” Koma tsopano Chilamulo cha Mose chakwaniritsa chifuno chake chimene chinalinganizidwira cha kutsogolera anthu odzichepetsa kwa Mfumu yosankhidwa ya Mulungu, Yesu Kristu. Chotero ndi kuyambika kwa uminisitala wa Yohane, anthu amitundu yonse, makamaka odzichepetsa ndi osauka, akuyesetsa kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu.
Popeza kuti Chilamulo cha Mose tsopano chikukwaniritsidwa, thayo la kuchisunga liyenera kuchotsedwa. Chilamulo chimaloleza chisudzulo pazifukwa zosiyanasiyana, koma tsopano Yesu akuti: “Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina achita chigololo; ndipo iye amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, achita chigololo.” Mawuwo ayenera kukhala ovutitsa maganizo Afarisiwo chotani nanga, makamaka popeza kuti iwo amalola chisudzulo pamaziko alionse!
Popitirizabe ndi mawu ake kwa Afarisi, Yesu akusimba za fanizo limene liri ndi anthu aŵiri omwe kaimidwe kawo, kapena mkhalidwe wawo, potsirizira pake ukusintha mwadzidzidzi. Kodi mungazindikire amene amunawo akuimirira ndi chimene kusintha kwa mikhalidwe yawo kumatanthauza?
“Ndipo panali munthu mwini chuma,” Yesu akufotokoza motero, “amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zironda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pagome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake.”
Panopa Yesu akugwiritsira ntchito munthu wachuma kuimira atsogoleri achipembedzo Achiyuda, kuphatikizapo osati kokha Afarisi ndi alembi komanso Asaduki ndi akulu ansembe. Iwo ngolemera m’mwaŵi ndi m’mipata yauzimu, ndipo akudzisungira monga momwe anachitira munthu wachuma. Zovala zawo za chibakuwa chachifumu zimaimira mkhalidwe wawo woyanjidwa, ndipo bafuta wawo amaimira kudzilungamitsa kwawo.
Kagulu ka munthu wachuma konyada kameneka kamawona osauka, anthu wamba mowaluluza kotheratu akumawatcha kuti ‛am ha·’aʹrets, kapena anthu wamba a m’fumbi. Motero Lazaro wopemphapemphayo amaimira anthu ameneŵa amene atsogoleri achipembedzo amamana chakudya choyenerera chauzimu ndi mwaŵi. Chifukwa chake, mofanana ndi Lazaro wodzala ndi zilonda, anthu wambawo amanyozedwa monga odwala mwauzimu ndi oyenerera kokha kuyanjana ndi agalu. Komabe, akagulu ka Lazarowo nganjala ndi aludzu kaamba ka chakudya chauzimu ndipo chotero ali pachipata, akumafunafuna kulandira muyeso waung’onong’ono wachakudya chauzimu chimene chingagwe kuchokera pagome la munthu wachuma.
Tsopano Yesu akupitirizabe kufotokoza za masinthidwe m’mikhalidwe ya wachuma ndi Lazaro. Kodi masinthidwewo ngotani, ndipo kodi iwo amaimiranji?
Munthu Wachuma ndi Lazaro Akumana ndi Masinthidwe
Munthu wachuma amaimira atsogoleri achipembedzo amene ali oyanjidwa ndi mwaŵi ndi mipata yauzimu, ndipo Lazaro amaimira anthu wamba amene amamva njala yauzimu. Yesu akupitiriza kunena nkhaniyo, akumafotokoza kusintha kwadzidzidzi m’mikhalidwe ya amunawo.
“Ndipo kunali kuti,” Yesu akutero, “wopemphayo anafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kumka ku chifuŵa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m’manda. Ndipo m’Hade anakweza maso ake, pokhala nawo mazunzo, nawona Abrahamu patali ndi Lazaro m’chifuwa mwake.”
Popeza kuti wachuma ndi Lazaro sali anthu enieni koma ophiphiritsira timagulu taanthu, mwachiwonekere imfa zawo nazonso nzophiphiritsira. Kodi imfa zawo zimaphiphiritsiranji kapena kuimira?
Yesu wangotha kumene kusonyeza masinthidwe m’mikhalidwe mwa kunena kuti ‘Chilamulo ndi Aneneri zinaliko kufikira Yohane Mbatizi, koma kuyambira pamenepo kumkabe mtsogolo Ufumu wa Mulungu ukulengezedwa.’ Chifukwa chake, kuli mwa kulalikira kwa Yohane ndi Yesu Kristu kumene onse aŵiriwo munthu wachuma ndi Lazaro akufa kumikhalidwe yawo yoyambirira, kapena mkhalidwe.
Akagulu kodzichepetsa ka Lazarowo, amafa kumkhalidwe wawo woyambirira womanidwa mwauzimu ndi kuloŵa m’malo achiyanjo a Mulungu. Pamene kuli kwakuti poyambirirapo anayang’ana kwa atsogoleri achipembedzo kaamba ka nyenyeswa zirizonse zakugwa kuchokera pagome lauzimu, tsopano chowonadi Chamalemba choperekedwa ndi Yesu chikukhutiritsa zosoŵa zawo. Chotero iwo abweretsedwa pachifuŵa, kapena malo achiyanjo, a Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu.
Kumbali ina, awo amene akupanga kagulu ka munthu wachuma akukhala osayanjidwa chifukwa cha kukana kwawo kosalekeza kuvomereza uthenga Waufumu wophunzitsidwa ndi Yesu. Mwa kutero iwo akufa kumkhalidwe wawo woyambirira wowonekera monga kuyanjidwa. Kwenikweni, iwo akulankhulidwa kukhala ali m’chizunzo chophiphiritsira. Tamvetserani tsopano, pamene munthu wachumayo akulankhula:
“Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lirime langa; pakuti ndizunzidwa m’laŵi ili la moto.” Mauthenga achiŵeruzo onga moto a Mulungu olengezedwa ndi ophunzira a Yesu ndiwo amene ukuzunza anthu alionse pa okha akagulu kamunthu wachumayo. Iwo akufuna kuti ophunzirawo aleke kulengeza mauthenga ameneŵa, motero kuwapatsa mlingo wochepekera wa mpumulo pakuzunzika kwawo.
“Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuwoloka kuchokera kuno kumka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.”
Nkolungama ndi koyenerera chotani nanga kuti masinthidwe amwadzidzidzi ameneŵo achitika pakati pakagulu ka Lazaro ndi kagulu ka munthu wachuma! Kusintha m’mikhalidweko kukumalizidwa miyezi yochepekera pambuyo pake pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene pangano Lachilamulo lakale likuloŵedwa m’malo ndi pangano latsopano. Pamenepo kukufikira kukhala kowonekera motsimikizirika kuti ophunzirawo, osati Afarisi ndi atsogoleri ena achipembedzo, ndiwo amene akuyanjidwa ndi Mulungu. Chifukwa chake “phompho lalikulu” limene limalekanitsa wachuma wophiphiritsira ndi ophunzira a Yesu limaimira chiweruzo cholungama chosasintha cha Mulungu.
Kenako munthu wachumayo akupempha “atate Abrahamu” kuti: “Mumtume [Lazaro] kunyumba ya atate wanga; pakuti ndiri nawo abale asanu.” Chotero munthu wachumayo akuvomereza kuti ali ndi unansi wapafupi kwambiri ndi atate wina, amene kwenikweni ali Satana Mdyerekezi. Wachumayo akupempha kuti Lazaro asukulutse mauthenga achiweruzo a Mulungu kotero kuti asaike ‘abale ake asanu,’ anzake ogwirizana nawo achipembedzo, ‘m’malo achizunzo ano.’
“Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi Aneneri; amvere iwo.” Inde, ngati “abale asanu” ati akapulumuke chizunzo, zokha zimene anayenera kuchita ndizo kulabadira zolembedwa za Mose ndi Aneneri zimene zimadziŵikitsa Yesu monga Mesiya ndiyeno kukhala ophunzira ake. Koma wachumayo akutsutsa kuti: “Iyayi, atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa akufa adzasandulika mtima.”
Komabe, iye akuuzidwa kuti: “Ngati samvera Mose ndi Aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.” Mulungu sadzapereka zizindikiro zapadera kapena zozizwitsa kuti akhutiritse anthu. Iwo ayenera kuŵerenga ndi kugwiritsira ntchito Malemba ngati iwo ati apeze chiyanjo chake. Luka 16:14-31; Yohane 9:28, 29; Mateyu 19:3-9; Agalatiya 3:24; Akolose 2:14; Yohane 8:44.
▪ Kodi nchifukwa ninji imfa za munthu wachuma ndi Lazaro ziyenera kukhala zophiphiritsira, ndipo kodi imfa zawo zimaphiphiritsira chiyani?
▪ Kuyamba ndi uminisitala wa Yohane, kodi ndimasinthidwe otani amene Yesu akusonyeza kuti akuchitika?
▪ Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchotsedwa pambuyo pa imfa ya Yesu, ndipo kodi chimenechi chidzayambukira motani nkhani ya chisudzulo?
▪ M’fanizo la Yesu, kodi ndani amene akuimiriridwa ndi wachuma ndi Lazaro?
▪ Kodi ndimazunzo otani amene wachuma anavutika nawo, ndipo kodi iye akupempha kuti aziziritsidwe ndi chiyani?
▪ Kodi “phompho lalikulu” limaimira chiyani?
▪ Kodi atate weniweni wa munthu wachuma ndani, ndipo kodi abale ake asanu ndani?