Mutu 104
Liwu la Mulungu Limveka Kachitatu
ADAKALI m’kachisi, Yesu wakhala akuvutika maganizo kaamba ka imfa imene ayenera kuyang’anizana nayo msanga. Nkhaŵa yake yaikulu nja mmene dzina la Atate wake lidzayambukiridwira, chotero iye akupemphera kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.”
Atatero, liwu lalikulu likudza kuchokera kumwamba, likumalengeza kuti: “Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.”
Khamu loimilira mozungulira likudabwa. “Mngelo walankhula ndi iye,” ena akuyamba kunena motero. Ena akunena kuti kwagunda. Koma, ndithudi, ali Yehova Mulungu amene analankhula! Komabe, imeneyi, sinthaŵi yoyamba kuti liwu la Mulungu linamvedwa mogwirizana ndi Yesu.
Paubatizo wa Yesu, zaka zitatu ndi theka zapitazo, Yohane Mbatizi anamva Mulungu akumati kwa Yesu: “Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Pamenepo, nthaŵi ina pambuyo pa Paskha yapitayo, pamene Yesu anasandulika pamaso pawo, Yakobo, Yohane, ndi Petro anamva Mulungu akulengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” Ndipo tsopano, kwanthaŵi yachitatu, pa Nisani 10, masiku anayi imfa ya Yesu isanakhale, kachiŵirinso liwu la Mulungu likumvedwa ndi anthu. Koma panthaŵi ino Yehova akulankhula kotero kuti makamuwo athe kumva!
Yesu akufotokoza kuti: “Mawu awa sanafika chifukwa cha ine, koma cha inu.” Amapereka umboni wakuti Yesu alidi Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwayo. “Tsopano pali kuweruzidwa kwa dziko ili lapansi,” Yesu akupitiriza, “mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.” M’chenicheni, njira ya moyo ya Yesu yokhulupirika imatsimikiziritsa kuti Satana Mdyerekezi, wolamulira wa dziko, ayenerera ‘kutayidwa kunja,’ kuphedwa.
Posonyeza za zotulukapo za imfa yake yoyandikirayo, Yesu akuti: “Ndipo ine, mmene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa ine ndekha.” Imfa yake siri chigonjetso mwanjira iriyonse, chifukwa mwa imfayo, iye adzazisonkhanitsira ena kotero kuti nawonso alandire moyo wosatha.
Koma khamulo likutsutsa kuti: “Tinamva ife m’Chilamulo kuti Kristu akhala kunthaŵi yonse; ndipo inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?”
Mosasamala kanthu za umboni wonse, kuphatikizapo kumva liwu la Mulungu mwiniyo, ambiri sakukhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wowona wa munthu, Mesiya wolonjezedwayo. Komabe, monga mmene anachitira miyezi isanu ndi umodzi yapitayo pa Phwando la Misasa, kachiŵirinso Yesu akunena za iye mwini kukhala “kuunika” ndi kulimbikitsa omvetsera ake kuti: “Pokhala muli nako kuunika, khulupilirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.” Atalankhula zinthu zimenezi, Yesu akuchoka ndi kukabisala, mwachiwonekere chifukwa chakuti moyo wake uli paupandu.
Kusakhulupirira Yesu kwa Ayudawo kukukwaniritsa mawu a Yesaya onena za ‘maso a anthu ochititsidwa khungu ndi mitima yawo youmitsidwa kotero kuti sakutembenuka kuti achiritsidwe.’ Yesaya anawona m’masomphenya mabwalo akumwamba a Yehova, kuphatikizapo Yesu muulemelero wake asanakhale munthu limodzi ndi Yehova. Komabe, Ayuda, mokwaniritsa chimene chinalembedwa ndi Yesaya, akana mouma khosi umboni wakuti Ameneyu ndiye Momboli wawo wolonjezedwayo.
Kumbali ina, ambiri ngakhale olamulira (mwachiwonekere ziŵalo za bwalo lalikulu Lachiyuda la Sanhedrin) kwenikweni akukhulupilira Yesu. Nikodemo ndi Yosefe wa ku Arimateya ali aŵiri a olamulira ameneŵa. Koma olamulirawo, kwapafupifupi pakali pano, akulephera kulengeza chikhulupiliro chawo, chifukwa cha kuwopera kuti angathamangitsidwe m’malo awo antchito m’sunagoge. Anthu oterowo akuphonya mwaŵiwo chotani nanga!
Yesu akupitirizabe kunena kuti: “Iye wokhulupilira ine, sakhulupilira ine, koma iye wondituma ine. Ndipo wondiwona ine awona amene anandituma ine. . . . Ndipo ngati wina akumva mawu anga, ndi kusawasunga, ine sindimweruza; pakuti sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi. . . . Mawu amene ndalankhula, iwowa adzamuweruza tsiku lomaliza.”
Chikondi cha Yehova kaamba ka dziko la mtundu wa anthu chinamsonkhezera kutumiza Yesu kotero kuti awo amene akumkhulupilira akapulumuke. Kuti anthu apulumuke kapena ayi zidzadalira pakumvera kwawo zinthu zimene Mulungu analangiza Yesu kulankhula. Chiweruzo chidzachitika “tsiku lomaliza,” mkati mwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu.
Yesu akumaliza mwa kunena kuti: “Pakuti sindinalankhula mwa ine ndekha; koma Atate wondituma ine, yemweyu anandipatsa ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. Ndipo ndidziŵa kuti lamulo lake liri moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi ine, momwemo ndilankhula.” Yohane 12:28-50; 19:38, 39; Mateyu 3:17; 17:5; Yesaya 6:1, 8-10.
▪ Kodi ndipazochitika zitatu ziti pamene liwu la Mulungu linamvedwa ponena za Yesu?
▪ Kodi mneneri Yesaya anawona motani ulemelero wa Yesu?
▪ Kodi ndi oweruza ati amene akukhulupilira Yesu, koma kodi nchifukwa ninji iwo sakumvomereza mwapoyera?
▪ Kodi “tsiku lomaliza,” nchiyani ndipo ndipamaziko otani pamene anthu adzaweruzidwirapo panthaŵiyo?