MUTU 14
Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”
1, 2. Kodi Baibulo limafotokoza kuti anthu akukumana ndi mavuto ati, nanga njira yokhayo yothetsera mavutowa ndi iti?
“CHILENGEDWE chonse chikubuula pamodzi komanso kumva kuwawa pamodzi.” (Aroma 8:22) Ndi mawu amenewa, mtumwi Paulo anafotokoza mavuto amene anthufe tikukumana nawo. Anthufe timangoona kuti palibe njira iliyonse yothetsera kuvutika, uchimo ndi imfa. Koma mosiyana ndi anthu, palibe zinthu zimene Yehova angalephere kuchita. (Numeri 23:19) Iye ndi Mulungu wachilungamo ndipo anakonza njira yodzathetsera mavuto athu. Njirayi imatchedwa kuti dipo.
2 Dipo ndi mphatso yoposa zonse imene Yehova anapatsa anthu. Limachititsa kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Chifukwa cha dipoli, tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Yohane 3:16; 1 Petulo 1:4) Koma kodi dipo n’chiyani? Nanga limatiphunzitsa chiyani zokhudza chilungamo chapadera cha Yehova?
N’chifukwa Chiyani Panafunika Dipo?
3. (a) N’chifukwa chiyani panafunika dipo? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sanangosintha chilango cha imfa chomwe ana a Adamu ankayenera kulandira?
3 Panafunika kuperekedwa dipo chifukwa cha tchimo la Adamu. Chifukwa choti sanamvere Mulungu, Adamu anachititsa kuti ana ake azidwala, azikhala ndi chisoni, azimva kupweteka ndiponso azimwalira. (Genesis 2:17; Aroma 8:20) Sizikanatheka kuti Mulungu angowamvera chisoni n’kusintha chilango cha imfa chomwe ankayenera kulandira. Ngati akanachita zimenezi, akanakhala kuti sakutsatira lamulo lake lakuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Ndiponso ngati Yehova akanathetsa mfundo zake za chilungamo, m’chilengedwe chonse mukanakhala chipwirikiti chokhachokha komanso kusamvera malamulo.
4, 5. (a) Kodi Satana ananena mabodza ati okhudza Mulungu, nanga n’chifukwa chiyani Yehova anaona kuti n’zofunika kuti ayankhe mabodzawa? (b) Kodi Satana ananena zotani zokhudza atumiki okhulupirika a Yehova?
4 Monga tinaonera m’Mutu 12, zimene Satana, Adamu ndi Hava anachita poukira ulamuliro wa Mulungu, zinayambitsa nkhani zofunika kwambiri. Satana anadetsa dzina la Mulungu lomwe ndi loyera. Iye ananena kuti Yehova ndi wabodza, ndi wolamulira wopondereza komanso sapereka ufulu kwa amene amawalamulira. (Genesis 3:1-5) Zimene Satana anachitazi zinaoneka ngati walepheretsa cholinga cha Mulungu chodzaza dziko lapansi ndi anthu olungama. Choncho anachititsa kuti Mulungu aoneke ngati wolephera. (Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11) Yehova akanapanda kuchitapo kanthu, anthu ndi angelo ambiri akanayamba kukayikira ngati iye amalamuliradi bwino.
5 Satana ananamiziranso atumiki okhulupirika a Yehova kuti amatumikira Yehovayo chifukwa chofuna kupezapo kenakake ndipo ngati atakumana ndi mavuto aakulu sangakhalebe okhulupirika. (Yobu 1:9-11) Nkhani zimenezi zinali zofunika kwambiri kuposa kupulumutsa anthu ku mavuto awo. Choncho Yehova anaona kuti ankafunika kupeza njira yoyankhira zimene Satana ananena. Koma kodi Mulungu akanathetsa bwanji nkhani zimenezi n’kupulumutsanso anthu?
Dipo Ndi Malipiro Ofanana Ndi Zimene Zinatayika
6. Tchulani mawu ena omwe anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza njira ya Mulungu yopulumutsira anthu.
6 Yehova anasankha kuthetsa nkhanizi m’njira yachilungamo komanso yosonyeza chifundo kwambiri yomwe palibe munthu aliyense amene akanaiganizira. Njirayi inali yosavuta koma inasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri. Njirayi imatchulidwa ndi mawu osiyanasiyana monga kugula, kugwirizanitsanso, kuwombola ndiponso kuphimba machimo. (Salimo 49:8; Danieli 9:24; Agalatiya 3:13; Akolose 1:20; Aheberi 2:17) Koma mwina mawu abwino kwambiri ndi amene Yesu mwiniwakeyo anagwiritsa ntchito. Iye anati: “Mwana wa munthu . . . sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo [m’Chigiriki, lyʹtron] kuti awombole anthu ambiri.”—Mateyu 20:28.
7, 8. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “dipo” amatanthauza chiyani? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti mawu akuti “dipo” amanena za chinthu chofanana ndendende ndi chinthu china?
7 Kodi dipo n’chiyani? Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito palembali akuchokera ku mawu otanthauza “kumasula.” Mawuwa ankawagwiritsa ntchito ponena za ndalama zomwe ankapereka kuti amasule akaidi ogwidwa pankhondo. Choncho tingati dipo ndi ndalama kapena chinthu chimene munthu amapereka powombola zinazake. M’Malemba a Chiheberi, mawu amene anawamasulira kuti “dipo” (koʹpher) amachokera ku mawu otanthauza “kuphimba.” Mwachitsanzo, Mulungu anauza Nowa kuti ‘amate’ (Chiheberi, ‘aphimbe’) chingalawa ndi phula. (Genesis 6:14) Zimenezi zikutithandiza kumvetsa mfundo yakuti kupereka dipo kumatanthauzanso kuphimba machimo.
8 N’zochititsanso chidwi kuti buku lina linanena kuti mawuwa (koʹpher) “nthawi zonse amanena za kufanana ndendende.” (Theological Dictionary of the New Testament) Choncho kuti apereke dipo, kapena kuti kuphimba machimo, panafunika kupereka mtengo wofanana ndendende ndi zimene zinawonongeka chifukwa cha uchimo. N’chifukwa chake Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli chinkanena kuti: “Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.”—Deuteronomo 19:21.
9. N’chifukwa chiyani anthu okhulupirika ankapereka nsembe za nyama, nanga Yehova ankaziona bwanji nsembezo?
9 Kungoyambira pa Abele, anthu okhulupirika ankapereka nsembe za nyama kwa Mulungu. Pochita zimenezi ankasonyeza kuti ankazindikira kuti anali ochimwa ndipo ankafunika kuwomboledwa. Anasonyezanso kuti ankakhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzawombola anthu pogwiritsa ntchito “mbadwa” yake. (Genesis 3:15; 4:1-4; Levitiko 17:11; Aheberi 11:4) Yehova ankasangalala ndi nsembezo ndipo ankaona kuti anthuwa anali atumiki ake okhulupirika. Komabe, nsembe za nyama zinali chizindikiro chabe. Nyama sizikanaphimbiratu machimo a anthu, chifukwa anthu ndi amtengo wapatali kuposa nyama. (Salimo 8:4-8) N’chifukwa chake Baibulo limati: “N’zosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.” (Aheberi 10:1-4) Nsembe zimenezi zinkangoimira nsembe yeniyeni ya dipo imene inadzaperekedwa.
‘Dipo Lokwanira Ndendende’
10. (a) Kodi wopereka dipo ankafunika kukhala wofanana ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani pankangofunika munthu mmodzi yekha woti apereke nsembe?
10 Mtumwi Paulo ananena kuti: “Anthu onse amafa chifukwa cha Adamu.” (1 Akorinto 15:22) Choncho pankafunika munthu wangwiro ngati mmene Adamu analili kuti apereke moyo wake dipo. (Aroma 5:14) Palibe cholengedwa chilichonse chimene chikanaperekedwa n’kukwaniritsa mfundo za chilungamo pa nkhaniyi. Ndi munthu wangwiro yekha, yemwe si woyenera kufa chifukwa cha tchimo la Adamu, amene akanapereka “dipo la anthu onse lokwanira ndendende.” (1 Timoteyo 2:6) Sikuti pankafunika kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri aperekedwe nsembe kuti munthu aliyense yemwe ndi mbadwa ya Adamu awomboledwe. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu] ndipo uchimowo unabweretsa imfa.” (Aroma 5:12) “Popeza imfa inabwera kudzera mwa munthu mmodzi,” Mulungu anakonza zoti anthu awomboledwenso “kudzera “mwa munthu mmodzi.” (1 Akorinto 15:21) Kodi anachita bwanji zimenezi?
“Dipo la anthu onse lokwanira ndendende”
11. (a) Kodi wopereka dipo anali woti adzalawa bwanji imfa m’malo mwa munthu aliyense? (b) N’chifukwa chiyani dipo silingathandize Adamu ndi Hava? (Onani mawu a m’munsi.)
11 Yehova anakonza zoti munthu wangwiro apereke nsembe moyo wake mosachita kumukakamiza. Mogwirizana ndi Aroma 6:23, “malipiro a uchimo ndi imfa.” Popereka moyo wake nsembe, wopereka dipoyo anali woti ‘adzalawa imfa m’malo mwa munthu aliyense.’ M’mawu ena tinganene kuti anapereka malipiro a uchimo wa Adamu. (Aheberi 2:9; 2 Akorinto 5:21; 1 Petulo 2:24) Zotsatira zake ndi zothandiza kwambiri kwa anthu. Dipo lidzachititsa kuti ana omvera a Adamu asadzalandire chilango cha imfa. Choncho uchimo ndi imfa sizidzakhalanso ndi mphamvu pa anthu amenewa.a—Aroma 5:16.
12. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kubweza ngongole imodzi kukhoza kuthandiza anthu ambiri.
12 Tiyerekeze kuti mukukhala m’tauni inayake imene anthu ambiri amagwira ntchito pafakitale ina yaikulu. Inuyo ndi maneba anu mumalandira ndalama zambiri ndipo mumakhala moyo wabwino. Koma tsiku lina fakitaleyo ikutsekedwa chifukwa bwana anayamba zakatangale ndipo wawononga ndalama moti fakitaleyo singathenso kubweza ngongole. Mwadzidzidzi inu ndi anzanu ntchito yakutherani moti mukuvutika kupeza zinthu zofunika pa moyo. Mabanja anu ndiponso anthu amene fakitaleyo ikufunika kuwapatsa ndalama akuvutika chifukwa cha katangale wa munthu mmodzi. Koma mwamwayi munthu wina wolemera kwambiri waganiza zothandizapo. Iye akuchita zimenezi chifukwa akudziwa kuti kampaniyo imathandiza anthu ambiri. Komanso akumvera chisoni anthu ambirimbiri ogwira ntchito pakampaniyo limodzi ndi mabanja awo. Choncho waganiza zobweza ngongole ya fakitaleyo n’kuitsegulanso. Kulipira ngongoleyo kukuthandiza antchito ambirimbiri, mabanja awo ndiponso anthu amene fakitaleyo imafunika kuwapatsa ndalama. Mofanana ndi zimenezi, kulipira ngongole ya Adamu kukuthandiza anthu mamiliyoni ambiri.
Kodi Ndi Ndani Anapereka Dipo?
13, 14. (a) Kodi Yehova anachita chiyani kuti apereke dipo lowombola anthu? (b) Kodi dipo linaperekedwa kwa ndani, nanga zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?
13 Ndi Yehova yekha yemwe akanapereka “Mwanawankhosa . . . amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yohane 1:29) Koma sikuti Mulungu anangotumiza mngelo wina aliyense kuti adzapulumutse anthu. Iye anatumiza mngelo amene akanapereka yankho labwino kwambiri pa zabodza zomwe Satana ananena zokhudza atumiki a Yehova. Yehova anadzimana kwambiri pololera kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, yemwe ‘ankasangalala naye kwambiri.’ (Miyambo 8:30) Mofunitsitsa, Mwana wa Mulungu “anasiya zonse zimene anali nazo” kumwamba. (Afilipi 2:7) Yehova anasamutsa modabwitsa moyo wa Mwana wake woyamba kubadwa n’kuuika m’mimba mwa namwali wa Chiyuda dzina lake Mariya. (Luka 1:27, 35) Atabadwa monga munthu, ankatchedwa Yesu. Koma mwalamulo ankatchedwa kuti Adamu wachiwiri chifukwa anali wofanana ndendende ndi Adamu. (1 Akorinto 15:45, 47) Choncho Yesu anatha kupereka nsembe kuti akhale dipo la anthu ochimwa.
14 Kodi dipolo linkayenera kuperekedwa kwa ndani? Lemba la Salimo 49:7 limanena mosapita m’mbali kuti dipo limayenera kuperekedwa “kwa Mulungu.” Koma kodi si Mulungu yemweyo amene anakonza zoti pakhale dipo? Inde. Komabe, zimenezi sizichititsa kuti kupereka dipo kukhale kosafunika kwenikweni, ngati kuti munthu wangochotsa ndalama m’thumba ili n’kuziika m’thumba linali. Tiyenera kumvetsa kuti dipo si kungosinthanitsa zinthu chabe, koma ndi nkhani yokhudza zamalamulo. Pokonza zoti dipo liperekedwe ngakhale kuti analuzapo zinthu zambiri, Yehova anasonyeza kuti nthawi zonse amatsatira mfundo zake zokhudza chilungamo.—Genesis 22:7, 8, 11-13; Aheberi 11:17; Yakobo 1:17.
15. N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu avutike ndiponso kufa?
15 Chakumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., mofunitsitsa Yesu Khristu analola kuti azunzike kwambiri n’cholinga choti dipo liperekedwe. Analolera kumangidwa pamilandu yabodza, kuweruzidwa kuti anali wolakwa ndiponso kukhomeredwa pamtengo wozunzikirapo. Koma kodi Yesu ankafunikadi kuvutika chonchi? Inde, chifukwa nkhani yokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu inkafunika kuthetsedwa. N’zochititsa chidwi kuti Mulungu sanalole kuti Herode aphe Yesu ali wakhanda. (Mateyu 2:13-18) Koma pamene Yesu anali munthu wamkulu, anatha kupirira mayesero onse a Satana ndipo ankadziwa bwino nkhani zimene Satana anayambitsa.b Pamene ankazunzidwa mwankhanza, Yesu anakhalabe “wokhulupirika, wosalakwa, wosaipitsidwa, wosiyana ndi anthu ochimwa.” Zimenezi zinapereka umboni wosatsutsika wakuti Yehova ali ndi atumiki ake amene amakhalabe okhulupirika akamayesedwa. (Aheberi 7:26) N’chifukwa chake atatsala pang’ono kufa, Yesu ananena mawu osonyeza kuti wapambana akuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”—Yohane 19:30.
Kumaliza Ntchito Yake Yowombola Anthu
16, 17. (a) Kodi Yesu anachita chiyani pomalizitsa ntchito yake yowombola anthu? (b) N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu akaonekere “pamaso pa Mulungu m’malo mwa ifeyo”?
16 Komabe Yesu ankafunika kumaliza ntchito yake yowombola anthu. Pa tsiku lachitatu kuchokera pamene anafa, Yehova anamuukitsa. (Machitidwe 3:15; 10:40) Pochita zinthu zosaiwalika zimenezi, sikuti Yehova anangopatsa mphoto Mwana wake chifukwa chomutumikira mokhulupirika, koma anamupatsanso mwayi woti amalizitse ntchito yowombola anthu monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu. (Aroma 1:4; 1 Akorinto 15:3-8) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe, . . . analowa m’malo oyera ndi magazi ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya. Khristu sanalowe m’malo oyera opangidwa ndi manja a anthu, amene ndi chithunzi cha malo enieniwo, koma analowa kumwamba kwenikweniko. Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu m’malo mwa ifeyo.”—Aheberi 9:11, 12, 24.
17 Khristu sakanatenga magazi ake enieni n’kupita nawo kumwamba. (1 Akorinto 15:50) Koma anatenga chimene magaziwo amaimira. Magaziwo amaimira ufulu wokhala ndi moyo padziko lapansi monga munthu wangwiro ndipo Yesu analolera kudzimana ufulu umenewu. Kenako anapita kwa Mulungu n’kukapereka mtengo wa moyowo ngati dipo powombola anthu ochimwa. Kodi Yehova analandira nsembeyo? Inde, ndipo umboni wa zimenezi ndi zimene zinachitika ku Yerusalemu pa Pentekosite wa mu 33 C.E. pamene ophunzira pafupifupi 120 analandira mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4) Ngakhale kuti zimenezi zinali zosangalatsa kwambiri, zinali chiyambi chabe cha madalitso obwera chifukwa cha dipo.
Mmene Dipo Limathandizira Anthu
18, 19. (a) Kodi ndi magulu awiri ati a anthu amene apindula ndi kugwirizanitsidwa kumene kumatheka chifukwa cha magazi a Khristu? (b) Kodi dipo likuthandiza bwanji a “khamu lalikulu” panopa, nanga lidzawathandiza bwanji m’tsogolo?
18 M’kalata yomwe analembera Akhristu a ku Kolose, Paulo anafotokoza kuti Mulungu anaona kuti ndi bwino kuti kudzera mwa Khristu, agwirizanitse zinthu zina zonse ndi iyeyo pokhazikitsa mtendere. Kuti achite zimenezi, anagwiritsa ntchito magazi amene Yesu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo. Paulo anafotokozanso kuti kugwirizanitsa kumeneku kukukhudza magulu awiri a anthu, omwe ndi “zakumwamba” ndi “zapadziko lapansi.” (Akolose 1:19, 20; Aefeso 1:10) Gulu loyamba lili ndi Akhristu okwanira 144,000 amene apatsidwa chiyembekezo choti akakhale ansembe kumwamba komanso mafumu n’kumalamulira padziko lapansi limodzi ndi Khristu Yesu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:4; 14:1-3) Kudzera mwa iwowa, anthu omvera adzapindula ndi dipo kwa zaka 1,000.—1 Akorinto 15:24-26; Chivumbulutso 20:6; 21:3, 4.
19 Zinthu “zapadziko lapansi” ndi anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wangwiro m’Paradaiso padzikoli. Lemba la Chivumbulutso 7:9-17 limanena kuti anthuwa ndi “khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuke “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. Komatu dipo limawathandiza ngakhale panopa. Iwo ‘achapa kale mikanjo yawo n’kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.’ Popeza amakhulupirira dipo, anayamba kale kupeza madalitso ambiri. Mwachitsanzo, Yehova amawaona kuti ndi olungama komanso anzake. (Yakobo 2:23) Chifukwa cha nsembe ya Yesu, anthuwa amatha ‘kufika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo amapemphera ndi ufulu wa kulankhula.’ (Aheberi 4:14-16) Akachita tchimo, Mulungu amawakhululukira. (Aefeso 1:7) Ngakhale kuti si angwiro, amakhala ndi chikumbumtima chabwino. (Aheberi 9:9; 10:22; 1 Petulo 3:21) Choncho anthu sakuchita kufunika kudikira kuti adzagwirizanitsidwe ndi Mulungu m’tsogolo, akugwirizanitsidwa naye panopa. (2 Akorinto 5:19, 20) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, pang’ono ndi pang’ono ‘azidzamasulidwa ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka’ ndipo kenako ‘adzakhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.
20. Kodi inuyo mumamva bwanji mukamaganizira mozama zokhudza dipo?
20 Tikuthokoza Mulungu “kudzera mwa Yesu Khristu” potipatsa dipo. (Aroma 7:25) Timagoma tikaganizira kuti linaperekedwa m’njira yosavuta koma yosonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri. (Aroma 11:33) Tikamaganizira mozama za dipo, zimatikhudza mtima kwambiri moti ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba. Mofanana ndi wolemba masalimo wina, tili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova, yemwe “amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.”—Salimo 33:5.
a Dipo silingathandize kuti Adamu ndi Hava amasulidwe ku uchimo. M’Chilamulo cha Mose munali mfundo iyi yokhudza wopha munthu mwadala: “Musamalandire dipo lowombolera moyo wa munthu amene wapha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa.” (Numeri 35:31) Choncho n’zoonekeratu kuti Adamu ndi Hava ankafunika kufa chifukwa sanamvere Mulungu mwa kufuna kwawo ndipo ankadziwa zomwe ankachita. Pamenepa anataya chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha.
b Kuti apereke moyo wake ngati dipo lofanana ndendende ndi moyo umene Adamu anataya, Yesu ankafunika kufa ali munthu wamkulu wangwiro osati mwana wangwiro. Kumbukirani kuti Adamu anachimwa mwadala ndipo ankadziwa kuopsa kwa zimene ankachitazo komanso zotsatira zake. Choncho kuti Yesu akhale “Adamu womalizira” n’kuphimba tchimolo, ankafunika kukhala munthu wamkulu woti angathe kusankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova akudziwa zimene akuchita. (1 Akorinto 15:45, 47) N’chifukwa chake zinthu zonse zokhulupirika zimene Yesu anachita kuphatikizapo kupereka moyo wake, zinali ngati “kuchita chinthu chimodzi cholungama.”—Aroma 5:18, 19.