MUTU 23
“Mulungu Ndi Amene Anayamba Kutikonda”
1-3. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa kuti imfa ya Yesu ikhale yosiyana ndi imfa ya munthu aliyense?
TSIKU lina zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, munthu wina wosalakwa anaimbidwa mlandu, anamupeza wolakwa pa milandu imene sanapalamule ndipo kenako anamuzunza mpaka kumupha. Sanali munthu woyamba kuphedwa mwankhanza ndiponso mopanda chilungamo, koma n’zomvetsa chisoni kuti sanalinso womaliza. Komabe imfa yake inali yosiyana kwambiri ndi imfa ya munthu aliyense.
2 Pamene munthuyo ankavutika kwambiri, kutatsala maola ochepa kuti afe, kumwamba kunachitika zinthu zodabwitsa zomwe zinasonyeza kuti imfa yake inali yapadera. Ngakhale kuti anali masana, mwadzidzidzi kunagwa mdima. Wolemba mbiri wina anati pa tsikulo “dzuwa linachita mdima.” (Luka 23:44, 45) Munthuyo atangotsala pang’ono kufa ananena mawu osaiwalika akuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” Zoonadi, imfa yake inakwaniritsa chinthu chofunika kwambiri. Nsembe imene iye anapereka inali njira yaikulu kwambiri yosonyezera chikondi yoti palibe munthu aliyense anachitapo.—Yohane 15:13; 19:30.
3 Munthuyu ndi Yesu Khristu. Anthu ambiri amadziwa bwino mmene anavutikira ndiponso mmene anafera pa Nisani 14, mu 33 C.E., pa tsiku lamdimali. Komabe, nthawi zambiri anthuwa amanyalanyaza mfundo yofunika kwambiri. Ngakhale kuti Yesu anavutika kwambiri, Yehova ndi amene anavutika kuposa pamenepa. Pa tsikuli, iye analolera kudzimana kwambiri ndipo anasonyeza chikondi chachikulu kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo. Kodi anachita chiyani? Yankho la funsoli litiphunzitsa zambiri zokhudza khalidwe lofunika la Yehovayo, lomwe ndi chikondi.
Njira Yaikulu Kwambiri Imene Yehova anasonyezera Chikondi
4. Kodi msilikali wa Chiroma anadziwa bwanji kuti Yesu sanali munthu wamba, nanga ananena kuti chiyani?
4 Mtsogoleri wa asilikali a Roma yemwe ankayang’anira kuphedwa kwa Yesu anadabwa kwambiri ndi mdima umene unagwa Yesu asanafe ndiponso chivomerezi champhamvu chimene chinachitika Yesuyo atangofa. Iye ananena kuti: “Ndithu, uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Mateyu 27:54) N’zodziwikiratu kuti Yesu sanali munthu wamba. Msilikaliyo anathandiza pakuphedwa kwa Mwana wobadwa yekha wa Mulungu Wam’mwambamwamba. Koma kodi Mwana ameneyu anali wofunika bwanji kwa Atate ake?
5. Kodi Yehova ndi Mwana wake anakhala limodzi kumwamba kwa nthawi yaitali bwanji?
5 Baibulo limati Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Tangoganizani, Mwana wa Mulunguyu anali ndi moyo zinthu zonse zimene timaona m’chilengedwechi zisanakhalepo. Ndiye kodi Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kwa nthawi yaitali bwanji? Asayansi ena amakhulupirira kuti chilengedwechi chakhala chilipo kwa zaka 13 biliyoni. Kwa anthufe, n’zovuta kumvetsa kuti nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji. Komabe ngati zimene asayansi amanenazi ndi zoona, ndiye kuti Mwana wa Mulungu wakhala alipo kwa zaka zoposa 13 biliyoni. Ndiye kodi ankachita chiyani pa nthawi yonseyi?
6. (a) Kodi Mwana wa Yehova ankatani asanabwere padzikoli? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi Mwana wake amakondana kwambiri?
6 Mwana ameneyu ankagwira ntchito mosangalala ngati “mmisiri waluso” wa Atate ake. (Miyambo 8:30) Baibulo limati: “Palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda [Mwanayo].” (Yohane 1:3) Choncho Yehova ndi Mwana wake anagwira ntchito limodzi popanga zinthu zina zonse. Imeneyitu inali nthawi yosangalatsa kwambiri. Tonsefe timadziwa kuti kholo limakondana kwambiri ndi mwana. Ndipo chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Choncho popeza Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kwa nthawi yaitali, ankakondana kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Apa n’zodziwikiratu kuti chikondi chinagwirizanitsa kwambiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake kuposa mmene zilili ndi anthu alionse omwe anagwirizanapo.
7. Yesu atabatizidwa, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anasangalala ndi zimene Mwanayu anachita?
7 Ngakhale zinali choncho, Atate anatumiza Mwana wake padzikoli kuti adzabadwe ngati mwana wakhanda. Zimenezi zikusonyeza kuti kwa zaka zambiri Yehova analolera kuti asakhale ndi Mwana wakeyu kumwamba. Ali kumwambako, ankaona pamene Yesu ankakula n’kukhala munthu wangwiro ndipo ankachita chidwi ndi zimene zinkachitika pa moyo wake. Ali ndi zaka pafupifupi 30, Yesu anabatizidwa. Kodi Yehova anamva bwanji Mwana wakeyu atachita zimenezi? Iye analankhula kuchokera kumwamba kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa ndipo amandisangalatsa kwambiri.” (Mateyu 3:17) Yehova anasangalala kwambiri ataona kuti Yesu wachita mokhulupirika zonse zimene zinanenedweratu ndiponso zonse zimene anamuuza kuti adzachite.—Yohane 5:36; 17:4.
8, 9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitikira Yesu pa Nisani 14, 33 C.E., nanga Atate ake akumwamba zinawakhudza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani Yehova analola Mwana wake kuti avutike ndiponso kufa?
8 Koma kodi Yehova anamva bwanji pa Nisani 14, mu 33 C.E.? Mwachitsanzo, kodi anamva bwanji pamene Yesu anaperekedwa komanso pamene gulu la anthu linabwera n’kudzamugwira usiku? Nanga anamva bwanji pomwe anzake anamuthawa kenako n’kuyamba kuzengedwa mlandu mosemphana ndi malamulo? Kodi anamva pamene ankamunyoza, kumulavulira, kumumenya ndiponso kumukwapula mpaka kumsana kwake kumatuluka magazi? Nanga anamva bwanji pamene ankakhomerera manja ndi miyendo yake pamtengo, n’kumusiya pompo anthu akumunyoza? Kodi Yehova anamva bwanji pamene Mwana wake wokondedwa anamulirira pamene ankamva ululu woopsa? Nanga anamva bwanji pamene Yesu anamalizika? Ndipo kodi anamva bwanji pamene kwa nthawi yoyamba kuchokera pamene zinthu zonse zinalengedwa, Mwana wake wokondedwayu kunalibeko?—Mateyu 26:14-16, 46, 47, 56, 59, 67; 27:38-44, 46; Yohane 19:1.
9 Timasowa chonena ndipo sitingathe kufotokoza ululu umene Yehova anamva pamene ankaona mwana wake akuzunzidwa komanso kufa. Zimene tingathe kufotokoza ndi chifukwa chake Yehova analola kuti zimenezi zichitike. N’chifukwa chiyani Yehova analolera kuti amve kupweteka chonchi? Iye akutiuza chifukwa chake pa Yohane 3:16, vesi lofunika kwambiri limene ena amati ndi chidule cha uthenga wonse wabwino wonena za Yesu. Vesili limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” Choncho Yehova anachita zonsezi chifukwa cha chikondi. Anasonyeza chikondi chachikulu kuposa wina aliyense pamene anatipatsa mphatso yapadera. Iye anatumiza Mwana wake kuti adzavutike n’kutifera.
“Mulungu . . . anapereka Mwana wake wobadwa yekha”
Tanthauzo la Chikondi
10. Kodi anthu amafunika chiyani, nanga n’chifukwa chiyani n’zovuta kudziwa tanthauzo lenileni la mawu akuti “chikondi”?
10 Kodi mawu akuti “chikondi” amatanthauza chiyani? Ambiri amanena kuti anthu amafunikira kwambiri chikondi kuposa chilichonse. Kuchokera pamene abadwa mpaka pa nthawi yomwalira, anthu amafunitsitsa kukondedwa, amasangalala akamakondedwa komanso amawonda mwinanso kufa kumene chifukwa chosowa chikondi. Ngakhale zili choncho, n’zovuta kwambiri kufotokoza kuti chikondi n’chiyani. Anthu amalankhula zambiri zokhudza chikondi. Pali mabuku, ndakatulo ndiponso nyimbo zambirimbiri za chikondi. Koma si nthawi zonse pamene zimenezi zimathandiza anthu kudziwa tanthauzo la chikondi. Kungoti mawuwa amagwiritsidwa ntchito kwambiri moti tanthauzo lake lenileni limaoneka kuti silingadziwike.
11, 12. (a) Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la chikondi? (b) Kodi ndi mitundu iti ya chikondi yomwe inkatchulidwa m’Chigiriki chakale, nanga ndi mawu ati otanthauza “chikondi” amene anagwiritsidwa ntchito kwambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu? (Onaninso mawu am’munsi.) (c) Kodi mawu akuti a·gaʹpe amatanthauza chiyani?
11 Komabe, Baibulo limatithandiza kumvetsa bwino kuti chikondi n’chiyani. Dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo inati: “Chikondi chimadziwika ndi ntchito zake.” (Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words) Baibulo limatiuza zambiri zokhudza zimene Yehova anachita posonyeza anthu chikondi ndiponso kukoma mtima. Mwachitsanzo, n’chiyaninso chingatithandize kumvetsa khalidweli kuposa chinthu chamtengo wapatali chimene Yehova anachita chomwe takambirana chija? M’mitu ikubwerayi, tiona zitsanzo zinanso zofotokoza mmene Yehova anasonyezera chikondi. Tingaphunzirenso zambiri kuchokera pa mawu a chilankhulo choyambirira omwe m’Baibulo anawamasulira kuti “chikondi.” M’Chigiriki chakale munali mawu 4 otanthauza “chikondi.”a Pa mawu amenewa, mawu amene anawagwiritsa ntchito kwambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu ndi akuti a·gaʹpe. Dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo imati amenewa ndi “mawu amphamvu kwambiri onena za chikondi omwe munthu angawaganizire.” Chifukwa chiyani tikutero?
12 Mawu akuti a·gaʹpe amanena za chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa chotsatira mfundo zinazake. Choncho sikuti munthu amasonyeza chikondichi chifukwa chongotengeka. Timachita kusankha kuti tisonyeze chikondi chimenechi chifukwa timadziwa kuti kuchita zimenezi n’koyenera. Munthu amene ali ndi chikondi cha a·gaʹpe amaganizira kwambiri zofuna za ena kuposa zake. Mwachitsanzo, taonaninso lemba la Yohane 3:16. Kodi “dziko” limene Mulungu analikonda kwambiri moti mpaka anapereka Mwana wake wobadwa yekha ndi chiyani? Amenewa ndi anthu amene akhoza kuwomboledwa. Ena mwa anthu amenewa amachita zinthu zosasangalatsa Mulungu. Kodi Yehova amakonda aliyense wa anthuwa ngati mnzake wapamtima, mofanana ndi mmene ankakondera Abulahamu? (Yakobo 2:23) Ayi, koma mwachikondi Yehova amachitira zabwino aliyense, ngakhale pamene zingachititse kuti aluze zambiri. Amafuna kuti anthu onse alape n’kusiya kuchita zoipa. (2 Petulo 3:9) Ambiri amachitadi zimenezi ndipo iye amasangalala n’kuyamba kuwaona kuti ndi anzake.
13, 14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti nthawi zambiri chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mmene munthu akumvera komanso chimakhala chochokera mumtima?
13 Komabe anthu ena ali ndi maganizo olakwika okhudza chikondi cha a·gaʹpe. Amaganiza kuti ndi chikondi chimene anthu amangochisonyeza potengera zimene akudziwa osati chifukwa cha mmene akumvera mumtima mwawo. Komatu zoona n’zakuti nthawi zambiri chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mmene munthu akumvera. Mwachitsanzo, pamene Yohane analemba kuti, “Atate amakonda Mwana,” anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti a·gaʹpe. (Yohane 3:35) Kodi chikondi chimenechi ndi chongosonyezedwa potengera zomwe ukudziwa osati kuchokera mumtima? Ayi. Pa Yohane 5:20, pamene Yohane analemba mawu a Yesu akuti “Atatewo amakonda Mwana,” anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti phi·leʹo. Choncho chikondi chimene Yehova amasonyeza, nthawi zambiri chimakhudza mmene akumvera komanso chimakhala chochokera mumtima. Komabe sikuti amachisonyeza chifukwa chongotengeka maganizo. Nthawi zonse amachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo zake zanzeru zomwenso ndi zolungama.
14 Monga taonera, makhalidwe onse a Yehova ndi apamwamba komanso osangalatsa. Koma khalidwe lake losangalatsa kwambiri ndi chikondi. Palibe chimene chimatichititsa kuti tizifuna kukhala anzake a Yehova kuposa chikondi. N’zosangalatsanso kuti chikondi ndi khalidwe lake lalikulu kwambiri. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
“Mulungu Ndi Chikondi”
15. Kodi Baibulo limanena chiyani zokhudza chikondi cha Yehova zomwe silinena likamafotokoza za makhalidwe ake ena akuluakulu? (Onaninso mawu am’munsi.)
15 Baibulo limatiuza mfundo ina yokhudza chikondi, koma silitchula mfundoyi ponena za makhalidwe ena akuluakulu a Yehova. Malemba sanena kuti Mulungu ndi mphamvu, Mulungu ndi chilungamo kapenanso kuti Mulungu ndi nzeru. Iye ali ndi makhalidwe amenewo, makhalidwewa amachokera kwa iye ndipo palibe amene amasonyeza kwambiri makhalidwe atatuwa kuposa iyeyo. Koma Baibulo limanena chinthu china chokhudza chikondi, lomwe ndi khalidwe lake la nambala 4. Limati: “Mulungu ndi chikondi.”b (1 Yohane 4:8) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?
16-18. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “Mulungu ndi chikondi”? (b) Pa zolengedwa zonse zapadzikoli, n’chifukwa chiyani m’pake kuti munthu ndi amene amaimira chikondi cha Yehova?
16 Kunena kuti “Mulungu ndi chikondi” n’kosiyana ndi kungonena kuti chinthu ichi n’chofanana ndi ichi. Mwachitsanzo, sitinganene kuti “Mulungu ndi wofanana ndi chikondi.” Komanso kungakhale kulakwitsa kutembenuza mawuwa n’kunena kuti “chikondi ndi Mulungu.” Yehova ndi weniweni osati khalidwe basi. Iye ndi Mulungu amene amaganiza, amasangalala kapena kukhumudwa komanso ali ndi makhalidwe ena kuwonjezera pa chikondi. Komabe khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Choncho buku lina ponena za vesili limati: “Mulungu ndi wachikondi pa chilichonse.” Kuti timvetse bwino zimenezi, taganizirani izi: Mphamvu za Yehova zimamuthandiza kuti akwanitse kuchita zinthu. Chilungamo ndi nzeru zake zimamuthandiza kudziwa njira imene angachitire zinthuzo. Koma chikondi ndi chimene chimamupangitsa kuti achite zinthuzo. Ndipo nthawi zonse akamasonyeza makhalidwe enawo, amasonyezanso chikondi.
17 Nthawi zambiri timanena kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi. Choncho ngati tikufuna kuphunzira chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, tiyenera kuphunzira za Yehova. Koma anthu nawonso amatha kusonyeza khalidwe labwinoli. N’chifukwa chiyani zili choncho? Pa nthawi imene ankalenga zinthu, Yehova analankhula mawu awa ndipo ayenera kuti ankauza Mwana wake: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe.” (Genesis 1:26) Pa zolengedwa zonse zapadzikoli, ndi anthu okha amene angasankhe kuti azikonda ena ndipo akamachita zimenezi amakhala kuti akutsanzira Atate awo akumwamba. Kumbukirani kuti Yehova anasankha zolengedwa zosiyanasiyana kuti ziziimira makhalidwe ake akuluakulu. Koma iye anasankha munthu, yemwe ndi wapamwamba pa zolengedwa zonse zapadzikoli, kuti aziimira chikondi, lomwe ndi khalidwe lake lalikulu.—Ezekieli 1:10.
18 Tikamasonyeza chikondi chopanda dyera komanso tikamachisonyeza chifukwa choti tikutsatira mfundo za m’Baibulo, timasonyeza khalidwe lalikulu la Yehova. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene mtumwi Yohane analemba kuti: “Timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Koma kodi Yehova anayamba ndi iyeyo kutikonda m’njira ziti?
Yehova Ndi Amene Anayamba Kusonyeza Chikondi
19. N’chiyani chinalimbikitsa Yehova kuti ayambe kulenga zinthu zamoyo?
19 Chikondi sichinayambe lero. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani funso ili: N’chiyani chinachititsa Yehova kuti ayambe kulenga zinthu zamoyo? Sikuti ankasowa wocheza naye. Yehova ndi wokwanira payekha ndipo ali ndi zonse, moti safunikira kuti winawake amupatse chinachake. Koma chikondi, chomwe ndi khalidwe limene limalimbikitsa munthu kuchitira ena zabwino, chinamulimbikitsa kuti apatse moyo anthu ndi angelo kuti nawonso azisangalala. Choyamba, iye analenga Mwana wake wobadwa yekha, yemwe ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Kenako Yehova anagwiritsa ntchito Mmisiri Walusoyu polenga zinthu zina zonse, kuyambira angelo. (Yobu 38:4, 7; Akolose 1:16) Yehova anapatsa angelo amphamvuwa ufulu ndi nzeru komanso anawalenga m’njira yoti azitha kukhumudwa kapena kusangalala ndi zinthu. Zimenezi zimawachititsa kuti azitha kusonyeza chikondi ndiponso kugwirizana, koma chofunika kwambiri n’chakuti amathanso kukhala anzake a Yehova Mulungu. (2 Akorinto 3:17) Choncho iwo amakonda ena chifukwa choti Yehova ndi amene anayamba kuwakonda.
20, 21. N’chiyani chikanathandiza Adamu ndi Hava kudziwa kuti Yehova amawakonda, koma kodi iwo anachita zotani?
20 Ndi mmenenso zinalili ndi anthu. Yehova atangolenga Adamu ndi Hava, anawasonyeza kuti ankawakonda m’njira zambiri. Chilichonse chomwe ankaona m’Paradaiso m’munda wa Edeni chinkasonyeza kuti Atate awo amawakonda. Taonani zimene Baibulo limanena: “Yehova Mulungu anadzala munda ku Edeni, chakum’mawa, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumba uja.” (Genesis 2:8) Kodi munayamba mwapitako kumalo enaake okongola kwambiri? N’chiyani chinakusangalatsani kwambiri kumeneko? Kodi kunali kuwala kwa dzuwa komwe kunkadutsa m’masamba a mitengo? Kapena kukongola kochititsa chidwi kwa maluwa osiyanasiyana? Kodi kanali kaphokoso kapansipansi ka madzi akuyenda mumtsinje, kapena kulira kwa mbalame ndi tizilombo tina? Kapenanso kanali kafungo kabwino ka mitengo, zipatso komanso maluwa? Kaya zinthu zinali bwanji, masiku ano kulibe malo okongola amene tingawayerekezere ndi munda wa Edeni. N’chifukwa chiyani tikutero?
21 Yehova anadzala yekha munda umenewo. Choncho uyenera kuti unali wokongola kwambiri. M’mundawo munali mitengo yonse yokongola komanso ya zipatso zokoma kwambiri. Mundawo unali waukulu, munali mitsinje komanso nyama zambiri zosangalatsa. Adamu ndi Hava anali ndi chilichonse chowachititsa kukhala osangalala ndiponso okhutira, kuphatikizapo ntchito yosangalatsa komanso banja labwino. Yehova ndi amene anayamba kuwakonda, choncho iwonso ankafunika kumukonda. Komatu analephera kuchita zimenezi. M’malo momvera Atate wawo wakumwamba chifukwa chomukonda, anamupandukira chifukwa chodzikonda.—Genesis, chaputala 2.
22. Kodi zimene Yehova anachita Adamu ndi Hava atamupandukira zinasonyeza bwanji kuti chikondi chake ndi chokhulupirika?
22 Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yehova. Koma kodi zinamuchititsa kuti asiye kukonda anthu? Ayi. “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.” (Salimo 136:1) Choncho nthawi yomweyo anakonza njira yopulumutsira ana a Adamu ndi Hava omwe angakhale ndi mtima wabwino. Monga taonera, chinthu chimodzi chomwe Yehova anachita kuti apulumutse anthu ndi kupereka dipo la Mwana wake wokondedwa, ngakhale kuti zimenezi zinamupweteka kwambiri.—1 Yohane 4:10.
23. Kodi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa kuti Yehova akhale “Mulungu wachimwemwe” n’chiyani, nanga ndi funso lofunika kwambiri liti limene liyankhidwe m’mutu wotsatira?
23 N’zosachita kufunsa kuti kuchokera pachiyambi Yehova wakhala akuyamba ndi iyeyo kusonyeza chikondi kwa anthu. Yehova wasonyeza m’njira zosawerengeka kuti iye “ndi amene anayamba kutikonda.” Chikondi chimachititsa kuti anthu azigwirizana ndiponso azisangalala, choncho n’zosadabwitsa kuti Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Komabe mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova amandikonda ineyo pandekha?’ Mutu wotsatira uyankha funso limeneli.
a Mawu akuti phi·leʹo, amene amanena za kukonda mnzako kapena m’bale wako, amapezekanso m’mavesi ambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu. Mawu akuti stor·geʹ omwe amanena za kukonda anthu a m’banja lako, anagwiritsidwa ntchito pa 2 Timoteyo 3:3 pofotokoza kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri sazidzakonda achibale awo. Mawu akuti eʹros, omwe amanena za chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi, sanagwiritsidwe ntchito m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu, ngakhale kuti chikondi cha mtundu umenewu chimafotokozedwanso m’Baibulo.—Miyambo 5:15-20.
b M’Baibulo muli mawu ena omwe analembedwa mofanana ndi amenewa. Mwachitsanzo, timawerenga kuti “Mulungu ndiye kuwala” ndiponso kuti “Mulungu . . . ndi moto wowononga.” (1 Yohane 1:5; Deuteronomo 4:24) Koma mawuwa tiyenera kuwaona kuti ndi ophiphiritsa chifukwa akuyerekezera Yehova ndi zinthu zooneka. Yehova ali ngati kuwala, chifukwa ndi woyera ndiponso wolungama. Kwa iye kulibe “mdima,” kapena kuti chinthu chodetsedwa. Ndipo tingamuyerekezere ndi moto chifukwa amagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga.