Mutu 4
Iye Amene Aneneri Onse Anamuchitira Umboni
“ATATE akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha.” (Yohane 5:20) Mwanayu analitu kusangalala kwambiri ndi ubwenzi wabwino umene anali nawo ndi Atate ake, Yehova! Kugwirizana kwawo kunayamba iye atangolengedwa, zaka zikwi zosaŵerengeka asanabadwe monga munthu padziko lapansi. Anali Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, mwana yekhayo amene Yehova mwiniyo anamulenga mwachindunji. China chilichonse m’mwamba ndiponso padziko lapansi chinalengedwa pogwiritsa ntchito Mwana woyamba kubadwa wokondeka kwambiri ameneyu. (Akolose 1:15, 16) Analinso Mawu a Mulungu, kapena kuti Womulankhulira, amene kudzera mwa iye Mulungu anafotokozera ena chifuniro Chake. Mwana amene anali kusekeretsa Mulungu ameneyu, ndiye amene anakhala munthu wotchedwa kuti Yesu Kristu.—Miyambo 8:22-30; Yohane 1:14, 18; 12:49, 50.
2 Maulosi ouziridwa ambirimbiri okhudza Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu ameneyu analembedwa mayi ake aumunthu asanakhale ndi pathupi pake mozizwitsa. Mtumwi Petro anapereka umboni kwa Korneliyo kuti: “Ameneyu aneneri onse amuchitira umboni.” (Machitidwe 10:43) Udindo wa Yesu unatchulidwa kwambiri m’Baibulo moti mngelo wina anauza mtumwi Yohane kuti: “Umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.” (Chivumbulutso 19:10) Maulosi amenewo anasonyeza bwino kuti iye ndiye Mesiya. Ananena za maudindo osiyanasiyana amene akakhala nawo pokwaniritsa zolinga za Mulungu. Zonsezi ziyenera kutichititsa chidwi kwambiri lerolino.
Zomwe Maulosi Anavumbula
3 Ulosi woyamba mwa maulosi amenewo unanenedwa anthu atapanduka mu Edene. Yehova anauza njoka kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Kwenikweni ulosiwu unali kunenedwa kwa Satana, amene anaimiridwa ndi njoka. “Mkaziyo” ndi gulu lokhulupirika la kumwamba la Yehova, lomwe lili ngati mkazi wake wokhulupirika. ‘Mbewu ya njoka’ ikuphatikizapo angelo onse ndi anthu onse amene amaonetsa mtima wonga wa Satana, aja amene amatsutsana ndi Yehova ndi anthu Ake. ‘Kulalira mutu wa njoka’ kukutanthauza kuwonongedwa kwa Satana wopandukayo, yemwe ananamizira Yehova ndi kubweretsa chisoni chachikulu pa anthu. Koma kodi mbali yoyambirira ya “mbewu” imene idzalalira mutuwo tingaidziŵe bwanji? Kwa zaka mazana ambiri mbaliyi inali “chinsinsi.”—Aroma 16:20, 25, 26.
4 Patatha zaka ngati 2,000 za mbiri ya anthu, Yehova anapereka mfundo zinanso. Anati Mbewuyo idzabadwa kubanja la Abrahamu. (Genesis 22:15-18) Komabe, kuti munthu akhale kholo lotsatira pa mzere wa makolo a Mbewuyo, sizinadalire kuti wabadwira kubanja limenelo koma anali kuchita kusankhidwa ndi Mulungu. Ngakhale kuti Abrahamu anali kumukonda mwana wake Ismayeli, yemwe anabereka ndi Hagara, Yehova anati: “Pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isake, amene Sara adzakubalira iwe.” (Genesis 17:18-21) Kenako anatsimikiza za panganolo, osati kwa Esau, mwana woyamba kubadwa wa Isake, koma kwa Yakobo, yemwe anali kholo la mafuko 12 a Israyeli. (Genesis 28:10-14) M’kupita kwa nthaŵi, anati Mbewuyo idzabadwira mu fuko la Yuda, kubanja la Davide.—Genesis 49:10; 1 Mbiri 17:3, 4, 11-14.
5 Kodi ndi mbali zina ziti zimene zinaperekedwa zodziŵira Mbewuyo? Kudakali zaka zoposa 700 kutsogolo, Baibulo linati pamene Mbewu yolonjezedwayo idzakhala munthu adzabadwira ku Betelehemu. Linavumbulanso kuti Mbewuyo inalipo kale “kuyambira nthaŵi yosayamba,” kuchokera pa kulengedwa kwake kumwamba. (Mika 5:2) Nthaŵi yeniyeni imene ikaonekera padziko lapansi monga Mesiya nayonso inanenedweratu, kudzera mwa mneneri Danieli. (Danieli 9:24-26) Ndipo pamene Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera, nakhala Wodzozedwa wa Yehova, mawu a Mulungu mwiniyo ochokera kumwamba ananena momveka bwino kuti iye ndi Mwana Wake. (Mateyu 3:16, 17) Mbewu ija inavumbulika! Motero Filipo anatha kunena n’chidaliro chonse kuti: “Iye amene Mose analembera za Iye m’chilamulo, ndi aneneri, tam’peza, ndiye Yesu.”—Yohane 1:45.
6 Pambuyo pake, otsatira a Yesu anadzazindikira kuti m’Malemba ouziridwa muli maulosi ambiri zedi onena za iye. (Luka 24:27) Zinadziŵika bwino kwambiri kuti Yesu ndiye mbali yoyambirira ya ‘mbewu ya mkazi,’ imene idzalalira mutu wa njoka, kuwononga Satana kuti asakhaleponso. Mwa Yesu, zonse zimene Mulungu analonjeza anthu, zinthu zonse zimene timazilakalaka, zidzakwaniritsidwa.—2 Akorinto 1:20.
7 Kodi kudziŵa zimenezi kuyenera kutikhudza motani? Baibulo limatiuza za mdindo wina wa ku Aitiopiya amene anali ataŵerenga ena mwa maulosi ameneŵa onena za Momboli ndi Mesiya yemwe anali kubwera. Maulosiwo atamuzunguza, anafunsa mlaliki Filipo kuti: “Mneneri anena ichi za yani?” Koma mdindoyu atapatsidwa yankho la funso lake sanaisiyire pomwepa nkhaniyi. Atamvetsera bwinobwino zimene Filipo analongosola, anazindikira kuti chifukwa chomvetsetsa ulosi umenewu womwe unali utakwaniritsidwa anayenera kuchitapo kanthu. Anazindikira kuti anafunika kubatizidwa. (Machitidwe 8:32-38; Yesaya 53:3-9) Kodi ifenso timalabadira mofananamo?
8 Talingaliraninso nkhani yokhudza mtima ya Abrahamu pamene anayesa kupereka nsembe Isake, mwana wake mmodzi yekhayo yemwe anabereka ndi Sara. (Genesis 22:1-18) Zimenezi zinaimira zomwe Yehova anali kudzachita—kupereka nsembe Mwana wake wobadwa yekha: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Izi zimatipatsa chidaliro chakuti monga momwe Yehova anaperekera Mwana wake wobadwa yekha kuti akwaniritse cholinga Chake, Iye ‘adzatipatsanso zinthu zonse kwaulere.’ (Aroma 8:32) Kodi n’chiyani chimene ifeyo tikufunika kuchita? Malinga ndi zomwe zili pa Genesis 22:18, Yehova anauza Abrahamu kuti mitundu yonse idzadalitsidwa kupyolera mwa Mbewu ‘chifukwa Abrahamu anamvera mawu a Mulungu.’ Ifenso tikufunika kumvera Yehova ndi Mwana wake: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”—Yohane 3:36.
9 Ngati timayamikira chiyembekezo cha moyo wosatha chimene tili nacho chifukwa cha nsembe ya Yesu, tidzafuna kuchita zimene Yehova watiuza kupyolera mwa Yesu. Zimenezi zimakhudza kukonda Mulungu ndi anzathu. (Mateyu 22:37-39) Yesu anasonyeza kuti kukonda kwathu Yehova kudzatichititsa kuphunzitsa ena ‘kusunga zinthu zonse zimene Yesuyo watilamulira.’ (Mateyu 28:19, 20) Ndipo tifunika kumakondananso ndi atumiki a Yehova anzathu mwa “kusonkhana kwathu pamodzi” nthaŵi zonse. (Ahebri 10:25; Agalatiya 6:10) Komanso, pamene tikumvera Mulungu ndi Mwana wake, sitiyenera kuganiza kuti iwo amafuna kuti tizichita zinthu mwangwiro. Ahebri 4:15 amati Yesu, monga Mkulu wa Ansembe wathu, amatha “kumva chifundo ndi zofooka zathu.” Izitu n’zolimbikitsa kwambiri, makamaka pamene tipempha Mulungu m’pemphero kudzera mwa Kristu kuti atithandize kugonjetsa zofooka zathu.—Mateyu 6:12.
Khulupirirani Kristu
10 Atauza khoti lalikulu la Ayuda ku Yerusalemu kuti ulosi wa Baibulo unakwaniritsidwa mwa Yesu, mtumwi Petro anati ndi mawu amphamvu: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Popeza kuti ana onse a Adamu ndi ochimwa, imfa yawo ilibe phindu lililonse ndipo singakhale dipo loombolera wina aliyense. Koma Yesu anali wangwiro, ndipo moyo wake unali nsembe yamtengo wapatali. (Salmo 49:6-9; Ahebri 2:9) Anapereka kwa Mulungu dipo limene mtengo wake unali wolingana ndendende ndi moyo wangwiro umene Adamu anautaya. (1 Timoteo 2:5, 6) Izi zinatsegula njira yoti tidzapezere moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.
11 Dipo linatsegulanso njira yoti ngakhale panopa tizipindulanso mbali zina. Mwachitsanzo, ngakhale kuti ndife ochimwa, nsembe ya Yesu imatithandiza kukhala ndi chikumbumtima choyera chifukwa machimo athu amakhululukidwa. Izi zimene zikutheka ndi nsembeyi n’zoposa zomwe zinali kutheka ndi nsembe zanyama zimene Aisrayeli anali kupereka mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose. (Machitidwe 13:38, 39; Ahebri 9:13, 14; 10:22) Komabe, kuti atikhululukire moteromo timafunika kuvomereza moona mtima kuti nsembe ya Kristu ndi yofunika kwambiri kwa ife: “Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi. Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.”—1 Yohane 1:8, 9.
12 Kodi anthu ochimwa angachitenji kuti asonyeze kuti akukhulupirira Kristu ndi nsembe yake? Anthu a mu zaka 100 zoyambirira ankati akakhala okhulupirira, ankaonetsa zimenezo pagulu. Motani? Anali kubatizidwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yesu analamula kuti ophunzira ake onse azibatizidwa. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 8:12; 18:8) Munthu sazengereza kuchita zimenezi pamene mtima wake wakhudzidwa ndi makonzedwe amene Yehova anapanga mwa Yesu chifukwa chotikonda. Amasintha chilichonse chofunika kusintha pamoyo wake, amadzipatulira kwa Mulungu m’pemphero, ndipo amasonyeza kuti anadzipatulira mwa kumizidwa m’madzi. Mwa kusonyeza chikhulupiriro m’njira imeneyi, iye ‘amafunsa chikumbumtima chokoma kwa Mulungu.’—1 Petro 3:21.
13 Inde, ngakhale pambuyo pobatizidwa khalidwe lauchimo lidzaonekabe. Ndiyeno zikatero? Mtumwi Yohane anati: “Izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu.” (1 Yohane 2:1, 2) Kodi izi zikutanthauza kuti mosasamala kanthu za chimene tachita, ngati tipemphera kwa Mulungu kuti atikhululukire ndiye kuti basi zonse zikhala bwino? Si choncho ayi. Kuti Mulungu atikhululukire, chinsinsi chake ndi kulapa moona mtima. Tingafunikenso kuthandizidwa ndi anthu achikulire omwenso azoloŵerana ndi zambiri mu mpingo wachikristu. Tiyenera kuzindikira kulakwika kwa zimene tinachita ndi kumva nazo chisoni kuchokera pansi pa mtima kotero kuti tiyesetse kusazibwereza. (Machitidwe 3:19; Yakobo 5:13-16) Ngati tichita zimenezi, Yesu adzatithandizadi ndipo Yehova adzatiyanjanso.
14 Nsembe ya Yesu yatsegula njira yokakhala ndi moyo wamuyaya kumwamba kwa a “kagulu ka nkhosa,” omwe ali mbali yachiŵiri ya mbewu yotchulidwa pa Genesis 3:15. (Luka 12:32; Agalatiya 3:26-29) Yatsegulanso njira yokhala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi la paradaiso kwa anthu ena mabiliyoni ambirimbiri. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 20:11, 12; 21:3, 4) Moyo wamuyaya ndi “mphatso yaulere ya Mulungu . . . mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23; Aefeso 2:8-10) Ngati tikukhulupirira mphatso imeneyo ndipo tikuyamikira njira yomwe tinapatsidwira mphatsoyo, tidzasonyeza zimenezi. Pozindikira kuti Yehova wagwiritsa ntchito Yesu modabwitsa kuti akwaniritse chifuniro Chake ndiponso kuti tonse tifunika kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa, utumiki wachikristu tidzauona kukhala ina mwa ntchito zofunika kwambiri pa moyo wathu. Chikhulupiriro chathu chidzaonekeratu mu kulankhula kwathu kwa mtima wonse pamene tiuza ena za mphatso yapamwamba imeneyi yochokera kwa Mulungu.—Machitidwe 20:24.
15 Chikhulupiriro choterocho n’chabwino kwambiri ndipo chimathandiza anthu kugwirizana. Mwa chikhulupiriro chimenechi, timayandikana kwambiri ndi Yehova, Mwana wake, ndiponso ndi anzathu mu mpingo wachikristu. (1 Yohane 3:23, 24) Ndipo chifukwa cha chikhulupiriro chimenechi timasangalala poona kuti Yehova mokoma mtima wapatsa Mwana wake “dzina limene liposa mayina onse [kupatulapo dzina la Mulungu], kuti m’dzina la Yesu, bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afilipi 2:9-11.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Pamene Mesiya anaonekera, n’chifukwa chiyani amene anali kukhulupiriradi Mawu a Mulungu anamuzindikira bwinobwino?
• Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tiyenera kuchita posonyeza kuyamikira nsembe ya Yesu?
• Kodi nsembe ya Yesu yatipindulitsa kale m’njira zotani? Kodi zimenezi zimatithandiza motani pamene tikupemphera kwa Yehova kuti atikhululukire machimo?
[Mafunso]
1. Kodi mfundo zokhudza moyo wa Yesu asanakhale munthu zimasonyezanji za ubwenzi wake ndi Yehova?
2. Kodi maulosi a Baibulo anena za Yesu kufika pati?
3. (a) Mu ulosi wa pa Genesis 3:15, ndani amene akuimiridwa ndi njoka, “mkaziyo,” ndi ‘mbewu ya njoka’? (b) N’chifukwa chiyani ‘kulalira mutu wa njoka’ n’kochititsa chidwi kwambiri kwa atumiki a Yehova?
4. Kodi mzere wa makolo ake a Yesu unathandiza motani kuti iye adziŵike kuti anali Mbewu yolonjezedwayo?
5. Pamene Yesu anayamba utumiki wake padziko lapansi, n’chiyani chinasonyeza kuti anali Mesiya?
6. (a) Malinga n’kunena kwa Luka 24:27, kodi otsatira a Yesu anadzazindikira chiyani? (b) Kodi mbali yoyambirira ya ‘mbewu ya mkazi’ ndani, nanga zikutanthauzanji kuti adzalalira mutu wa njoka?
7. Kuwonjezera pa kudziŵa Yemwe maulosi ananena za iye, n’chiyaninso chimene chingakhale chothandiza kuchizindikira?
8. (a) Kodi pamene Abrahamu anayesa kupereka nsembe Isake zinaimira chiyani? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anauza Abrahamu kuti mitundu yonse idzadalitsidwa kupyolera mwa Mbewu, nanga zimenezi zikutikhudza motani lerolino?
9. Ngati timayamikira chiyembekezo cha moyo wosatha chimene tili nacho chifukwa cha nsembe ya Yesu, tidzachitanji?
10. N’chifukwa chiyani palibe wina angatipulumutse koma Yesu Kristu yekha?
11. Fotokozani mmene tingapindulire kwambiri ndi nsembe ya Yesu.
12. N’chifukwa chiyani kumizidwa m’madzi kuli kofunika kuti munthu akhale ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu?
13. Tikazindikira kuti tachita tchimo, kodi tiyenera kuchitapo chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutero?
14. (a) Fotokozani njira yofunika yomwe nsembe ya Yesu yatipindulitsira. (b) Ngati tilidi ndi chikhulupiriro, n’chiyani chimene tiyenera kuchita?
15. Kodi kukhulupirira Yesu Kristu kumatithandiza bwanji kugwirizana?
[Chithunzi patsamba 36]
Yesu anauza otsatira ake kuti aphunzitse ena kusunga Malamulo a Mulungu