Mutu 6
Mlandu Umene Tonse Tiyenera Kuyankhapo
PALI mlandu wofunika kwambiri pa milandu yonse imene anthu ayankhapo. Mlanduwo ukukukhudzani. Tsogolo lanu losatha likudalira kuti inu mukhala mbali iti pamlandu umenewu. Kupanduka kumene kunachitika mu Edene ndiko kunayambitsa mlanduwu. Panthaŵiyo Satana anafunsa Hava kuti: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava anayankha kuti Mulungu ananena za mtengo wina umodzi wokha kuti: “Musadye umenewo . . . mungadzafe.” Ndiyeno mosapita m’mbali, Satana anaimba Yehova mlandu wa kunena zabodza, anati sizoona kuti moyo wa Hava kapena wa Adamu unali kudalira kumvera Mulungu. M’kunena kwake Satana anati Mulungu anamana zolengedwa zake chinthu chabwino, mphamvu yodziikira miyezo imene akufuna pamoyo. Satana anatsindika kuti: “Adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:1-5.
2 Kwenikweni, Satana anali kunena kuti anthu angachite bwino kwambiri kumadzisankhira zochita m’malo motsatira malamulo a Mulungu. Motero iye anatsutsa kalamuliridwe ka Mulungu. Zimenezi zinadzutsa nkhani yofunika kwambiri ya mlanduwu yakuti kaya Mulungu ayenera kulamulira chilengedwe chonse kapena ayi, ndiko kuti, ngati ali ndi ufulu wolamulira. Panabuka funso lakuti: Kodi chabwino n’chiyani kwa anthu, kalamuliridwe ka Yehova kapena ulamuliro wina wosadalira Yehovayo? Inde, Yehova akanatha kupha Adamu ndi Hava nthaŵi yomweyo, koma zimenezo sizikanathetsa mogwira mtima nkhani ya ulamuliro. Mwa kupatsa anthu nthaŵi yoti achulukane, Mulungu akanasonyeza zimene zingatsatire ngati anthu akhala mosadalira iye ndi malamulo ake.
3 Kuukira kwa Satana ufulu wolamulira wa Yehova sikunathere pa zimene zinachitika mu Edene. Anakayikira ngati pali amene angakhale wokhulupirika kwa Yehova. Iyi inakhala nkhani yachiŵiri ya mlandu uja. Anakayikira aliyense, ana a Adamu ndi Hava ndiponso ana onse auzimu a Mulungu, ngakhalenso Mwana woyamba kubadwa wokondedwa kwambiri wa Yehova. Mwachitsanzo, m’masiku a Yobu, Satana anati amene amatumikira Yehova amatero osati chifukwa chokonda Mulungu ndi kalamuliridwe kake, koma chifukwa cha dyera. Ananenetsa kuti pamene iwo akumana ndi mavuto, onse akhoza kulephera kupitiriza pogonjera zokhumba zawo.—Yobu 2:1-6; Chivumbulutso 12:10.
Zimene Mbiri Yasonyeza
4 Mfundo yofunika kwambiri pankhani ya ulamuliro ndi iyi: Mulungu sanalenge anthu kuti azitha kuyendetsa zinthu bwinobwino popanda kulamuliridwa ndi iye. Chifukwa chowaganizira, anawapanga kuti azidalira malamulo ake olungama. Mneneri Yeremiya anavomereza kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.” (Yeremiya 10:23, 24) Motero Mawu a Mulungu amatilangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Monga mmene Mulungu anapangira kuti anthu azitsatira malamulo ake amene chilengedwe chimayendera kuti athe kukhala ndi moyo, anapanganso malamulo a makhalidwe abwino, amene ngati atsatiridwa angapangitse anthu kukhala ogwirizana.
5 N’zachionekere kuti Mulungu anadziŵa kuti anthu sangathe kuyendetsa zinthu bwino popanda kulamuliridwa ndi iye. Poyesa mosaphula kanthu kuti asadalire ulamuliro wa Mulungu, anthu akhazikitsa magulu osiyanasiyana a ndale, a zachuma, ndiponso a zipembedzo. Kusiyana kumeneku kwachititsa anthu kukangana nthaŵi zonse, ndipo zotsatira zake zakhala chiwawa, nkhondo, ndi kuphana. ‘[Munthu] wapweteka mnzake pomulamulira.’ (Mlaliki 8:9) Izi n’zimene zachitikadi m’mbiri yonse ya anthu. Monga ananeneratu Mawu a Mulungu, anthu oipa ndi onyenga akhalabe ‘oipa chiipire.’ (2 Timoteo 3:13) Ndipo m’zaka za m’ma 1900, nthaŵi imene anthu anafikadi patali ndi ntchito zasayansi komanso zamafakitale, munachitika masoka oipitsitsa kusiyana n’kale lonse. Mawu a Yeremiya 10:23 aoneka kukhaladi oona kwambiri, anthu sanalengedwe kuti azilongosola mapazi awo.
6 Zotsatirapo zomvetsa chisoni komanso zotenga nthaŵi yaitali za kukhala ndi ufulu wodzilamulira m’malo molamuliridwa ndi Mulungu zasonyeza bwino kuti ulamuliro wa anthu sungaphule kanthu. Njira yokha yopezera chimwemwe, umodzi, thanzi labwino, ndiponso moyo ndiyo kulamuliridwa ndi Mulungu. Ndipo Mawu a Mulungu amasonyeza kuti nthaŵi yoti Yehova alolere anthu kukhala ndi ufulu wodzilamulira yatsala pang’ono kutha. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5) Posachedwa adzaloŵererapo pa zochita za anthu kuti asonyeze ulamuliro wake padziko lapansi. Ulosi wa Baibulo umati: “Masiku a mafumu aja [maulamuliro a anthu amene alipo tsopanoli] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [anthu sadzalamuliranso dziko lapansi], koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipo tsopanoli]. Nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Kupulumuka Kuloŵa M’dziko Latsopano la Mulungu
7 Kodi ndani adzapulumuka pamene ulamuliro wa Mulungu uthetsa ulamuliro wa anthu? Baibulo limati: “Owongoka mtima [amene amachirikiza ufulu wolamulira wa Mulungu] adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa [amene sachirikiza ufulu wolamulira wa Mulungu] adzalikhidwa m’dziko.” (Miyambo 2:21, 22) Wamasalmo ananena mofananamo kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:10, 29.
8 Dziko la Satana litawonongedwa, Mulungu adzabweretsa dziko lake latsopano lomwe lidzathetseratu chiwawa, nkhondo, umphaŵi, kuvutika, matenda, ndi imfa zomwe zasautsa anthu kwa zaka masauzande ambiri. Baibulo limafotokoza bwino madalitso amene anthu omvera adzakhala nawo. Limati: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Mwa boma la Ufumu wake wakumwamba lolamuliridwa ndi Kristu, Mulungu adzatsimikizira kotheratu ufulu wake wokhala Wolamulira wathu Wamkulu.—Aroma 16:20; 2 Petro 3:10-13; Chivumbulutso 20:1-6.
Mmene Ena Anayankhirapo pa Mlanduwu
9 M’mbiri yonse ya anthu, pakhala amuna ndi akazi achikhulupiriro amene asonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova monga Wolamulira Wamkulu. Iwo anadziŵa kuti miyoyo yawo inadalira kumvera ndi kutsatira zonena zake. Mmodzi mwa iwo anali Nowa. Mulungu anauza Nowa kuti: “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga . . . Udzipangire wekha chingalawa.” Ndipo Nowa anatsatira malangizo a Yehova. Ngakhale kuti anthu ena masiku amenewo anachenjezedwa, anali kungokhala ngati kuti panalibe chachilendo chimene chinali kudzachitika. Koma Nowa anamanga chingalawa chachikulu ndipo anatanganidwa ndi kulalikira njira zolungama za Yehova kwa ena. Nkhaniyi imapitiriza kunena kuti: “Anachita Nowa, monga mwa zonse anamulamulira iye Mulungu, momwemo anachita.”—Genesis 6:13-22; Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5.
10 Abrahamu ndi Sara analinso zitsanzo zabwino pochirikiza ulamuliro wa Yehova; anali kuchita chilichonse chimene Mulungu anawalamulira. Ankakhala mumzinda wotukuka wa Uri wa kwa Akaldayo. Koma pamene Yehova anauza Abrahamu kuti apite ku dziko lina, dziko limene linali lachilendo kwa iye, Abrahamu ‘anamuka monga Yehova ananena kwa iye.’ Mosakayikira Sara anali ndi moyo wosangalatsa—anali ndi nyumba, anzake, ndiponso achibale. Komatu anali wogonjera kwa Yehova ndi kwa mwamuna wake ndipo anapita kudziko la Kanani, ngakhale kuti sanadziŵe zomwe akakumana nazo kumeneko.—Genesis 11:31–12:4; Machitidwe 7:2-4.
11 Mose anali munthu winanso amene anachirikiza ulamuliro wa Yehova. Ndipo anachita zimenezi m’mikhalidwe yovuta kwambiri, anali kuonana pamaso m’pamaso ndi Farao wa ku Igupto. Si kuti Mose anali kudzidalira ayi. Iye anakayikira ngati angathe kulankhula zomveka. Komatu anamvera Yehova. Mothandizidwa ndi Yehova ndi mbale wake Aroni, Mose analankhula mobwerezabwereza mawu a Yehova kwa Farao wouma mtimayo. Ngakhale ana ena a Israyeli anali kumutsutsa kwambiri Mose. Komabe, mokhulupirika Mose anachita zonse zimene Yehova anamulamula, moti kudzera mwa iye Israyeli anamasulidwa ku Igupto.—Eksodo 7:6; 12:50, 51; Ahebri 11:24-27.
12 Amene anali okhulupirika kwa Yehova sanalingalire kuti zimene anafunika kumvera ndi zimene Mulungu analemba zokha. Pamene mkazi wa Potifara anayesa kunyengerera Yosefe kuti achite naye chisembwere, panalibe lamulo lolembedwa la Mulungu loletsa chigololo. Komabe, Yosefe anali kudziŵa makonzedwe a ukwati omwe Yehova anakhazikitsa mu Edene. Anali kudziŵa kuti Mulungu sangasangalale ngati atagona ndi mkazi wa mwini wake. Yosefe sanafune kuona kuti Mulungu angamulole kufanana ndi Aigupto mpaka pati. Anatsatira njira ya Yehova mwa kulingalira zimene Mulungu anakhala akuchita ndi anthu ndiyeno anagwiritsa ntchito mosamalitsa zimene iye anaona kuti ndizo zofuna za Mulungu.—Genesis 39:7-12; Salmo 77:11, 12.
13 Amene amam’dziŵadi Yehova samusiya ngakhale atayesedwa kwambiri. Satana anati ngati chuma chochuluka cha Yobu chitawonongeka kapena ngati atadwala kwambiri, Yobu—amene Yehova anamuyamikira—akanasiya Mulungu. Koma Yobu anasonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza, ngakhale kuti Yobu mwiniyo sanali kudziŵa chifukwa chake anali kukumana ndi masoka. (Yobu 2:9, 10) Patadutsa zaka zambirimbiri, poyesabe kutsimikizira mfundo yake, Satana anachititsa mfumu ya Babulo yomwe inakalipa kwambiri kuti iopseze anyamata atatu achihebri kuti aponyedwa m’ng’anjo yamoto kuti afe ngati sagwadira fano limene mfumuyo inaimika. Atakakamizidwa kusankhapo kumvera lamulo la mfumu kapena kumvera lamulo la Yehova loletsa kulambira mafano, iwo molimba mtima anaonetsa kuti anali kutumikira Yehova ndi kuti iye anali Mfumu yawo Yaikulukulu. Kukhala wokhulupirika kwa Mulungu kunali kwa mtengo wapatali kwa iwo kuposa moyo umene anali nawo.—Danieli 3:14-18.
14 Mwa zitsanzo zimenezi, kodi tiyenera kuganiza kuti, munthu kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova ayenera kukhala wangwiro kapena munthu amene waphonya penapake ndiye kuti basi walephereratu? Si choncho ayi! Baibulo limatiuza kuti nthaŵi zina Mose anali kulephera. Ngakhale kuti sizinali kumukondweretsa Yehova, iye sanakane Mose. Nawonso atumwi a Yesu Kristu anali ndi zofooka zawo. Polingalira kuti tinabadwa opanda ungwiro, Yehova amasangalala ngati sitinyalanyaza mwadala zofuna zake pa mbali iliyonse. Ngati titachita cholakwa chifukwa chofooka, n’kofunika kwambiri kulapa moona mtima ndipo tisazoloŵere kuchita cholakwacho. Mwa kutero timasonyeza kuti timakondadi zimene Yehova amati n’zabwino ndipo timada zimene iye amati n’zoipa. Chifukwa chokhulupirira nsembe ya Yesu yotetezera machimo, tikhoza kukhala ndi khalidwe loyera pamaso pa Mulungu.—Amosi 5:15; Machitidwe 3:19; Ahebri 9:14.
15 Komabe, kodi mwina n’zosatheka kuti anthu amvere ulamuliro wa Yehova mosaphonyetsako kalikonse? Yankho la funso limeneli linali monga “chinsinsi” kwa zaka ngati 4,000. (1 Timoteo 3:16) Ngakhale kuti Adamu analengedwa wangwiro, iye sanapereke chitsanzo chabwino chokhala wodzipereka kwa Mulungu. Ndiyeno ndani akanapereka chitsanzo chotero? Ndithudi sichikanaperekedwa ndi wina aliyense wa ana ake ochimwa. Munthu yekha amene akanachita zimenezi anali Yesu Kristu. (Ahebri 4:15) Zomwe Yesu anakwanitsa kuchita zinasonyeza kuti Adamu, amene anali m’mikhalidwe yabwino kwambiri, akanatha kukhala wokhulupirika bwinobwino akanafuna kutero. Vuto silinali ndi ntchito ya kulenga ya Mulungu. Motero Yesu Kristu ndiye chitsanzo chimene timafuna kutsanzira posonyeza osati kokha kumvera lamulo la Mulungu, komanso posonyeza kuti ndife odzipereka kwa Yehova, Wolamulira Wamkuluyo.—Deuteronomo 32:4, 5.
Kodi Ife Tiyankha Kuti Chiyani?
16 Aliyense lerolino ayenera kuyankhapo pa mlandu wa kulamulira chilengedwe chonse. Ngati talengeza kuti tikuima ku mbali ya Yehova pa mlanduwu, Satana amalimbana nafe. Amatibweretsera mavuto kuchokera kumbali iliyonse ndipo adzapitiriza kuchita zimenezi mpaka dziko lake loipali litatha. Tiyenera kukhala tcheru nthaŵi zonse. (1 Petro 5:8) Khalidwe lathu limasonyeza mbali imene tili pa nkhani yaikulu ya ulamuliro wa Yehova ndiponso pa nkhani yachiŵiri ya kukhulupirika kwa Mulungu poyesedwa. Tingalakwitse ngati tiona kuti kusakhulupirika n’kosafunika chifukwa chakuti n’kofala m’dzikoli. Kukhalabe okhulupirika kumafuna kuti tiyesetse kugwiritsa ntchito miyezo yolungama ya Yehova pa mbali iliyonse ya moyo.
17 Mwachitsanzo, sitingatsanzire Satana amene ali “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Tiyenera kukhala oona m’zochita zathu zonse. M’dziko la Satanali, kaŵirikaŵiri achinyamata sanena zoona kwa makolo awo. Koma achinyamata achikristu amapeŵa zimenezi, ndipo motero amasonyeza kuti zonena za Satana zakuti anthu a Mulungu sangakhale okhulupirika pamene akuyesedwa n’zabodza. (Yobu 1:9-11; Miyambo 6:16-19) Ndiyeno pali nkhani zabizinesi zimene zingasonyeze kuti munthu akugwirizana ndi “atate wake wa bodza” m’malo mogwirizana ndi Mulungu wa choonadi. Timazipeŵa zimenezi. (Mika 6:11, 12) Ndiponso, kuba kulikonseko n’kosayenera, ngakhale munthuyo ataba chifukwa chosoŵa kapena ngakhale woberedwayo atakhala wolemera. (Miyambo 6:30, 31; 1 Petro 4:15) Ngakhale limeneli litakhala khalidwe lofala m’dera la kwathu kapenanso ngakhale chimene tatengacho chitakhala chaching’ono, kuba ndi kuswa malamulo a Mulungu basi.—Luka 16:10; Aroma 12:2; Aefeso 4:28.
18 Panthaŵi ya Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000, Satana ndi ziwanda zake adzakhala ali m’phompho moti sadzatha kusonkhezera zochita za anthu. Kudzakhalatu kumasuka kwabasi! Koma pambuyo pa zaka 1,000, iwo adzamasulidwa kwa kanthaŵi. Satana ndi otsatira ake adzavutitsa anthu obwezeretsedwa amene akukhala okhulupirika kwa Mulungu. (Chivumbulutso 20:7-10) Ngati tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo nthaŵi imeneyo, kodi tidzachitanji pa nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse? Popeza kuti anthu onse panthaŵiyo adzakhala angwiro, kusakhulupirika kulikonse kudzakhala kwadala ndipo chotsatira chake chidzakhala kuwonongeka kosadzakhalanso ndi moyo. N’kofunikatu kwambiri kuti pakali pano tikhale n’chizoloŵezi chomvera malangizo alionse amene Yehova akutipatsa, kaya kudzera m’Mawu ake kapena kudzera m’gulu lake. Mwa kuchita zimenezi timasonyeza kuti ndifedi odzipereka kwa iye monga Wolamulira Wamkulu.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi nkhani yaikulu ya mlandu umene tonse tifunika kuyankhapo ndi iti? Kodi tinakhudzidwa nawo motani?
• Kodi chochititsa chidwi n’chiyani pa zomwe amuna ndi akazi akale anachita posonyeza kukhulupirika kwawo kwa Yehova?
• N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti tsiku lililonse khalidwe lathu lizilemekeza Yehova?
[Mafunso]
1, 2. (a) Kodi Satana anayambitsa mlandu wotani mu Edene? (b) Kodi nkhani yomwe ikukambidwa pa mlanduwu ikusonyezedwa motani ndi zomwe ananena?
3. Kodi nkhani yachiŵiri imene Satana anadzutsa ndi iti?
4, 5. Kodi mbiri yasonyezanji pa za kulongosola mapazi ake kwa munthu?
6. Kodi posachedwapa Mulungu adzachitanji pothetsa ufulu wa anthu wodzilamulira mosadalira iye?
7. Kodi ndani adzapulumuka pamene ulamuliro wa Mulungu uthetsa ulamuliro wa anthu?
8. Kodi Mulungu adzatsimikizira kotheratu kuti ndi woyenera kulamulira mwa kuchitanji?
9. (a) Kodi amene akhalabe okhulupirika kwa Yehova awaona motani mawu ake? (b) Kodi Nowa anasonyeza motani kuti anali wokhulupirika, nanga tingapindule motani ndi chitsanzo chake?
10. (a) Kodi Abrahamu ndi Sara anachirikiza motani ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi tingapindule motani ndi zitsanzo za Abrahamu ndi Sara?
11. (a) Kodi Mose anachirikiza ulamuliro wa Yehova m’mikhalidwe yotani? (b) Kodi chitsanzo cha Mose chingatipindulitse motani?
12. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova kumaphatikizapo zambiri osati kungochita zimene Mulungu wazilemba basi? (b) Kodi kumvetsetsa kukhulupirika kotereku kungatithandize motani kugwiritsa ntchito 1 Yohane 2:15?
13. Kodi Mdyerekezi anasonyezedwa kuti ndi wabodza motani ndi (a) Yobu? (b) Ahebri atatu?
14. Kodi n’zotheka bwanji kwa ife anthu opanda ungwiro kusonyeza kuti tilidi okhulupirika kwa Yehova?
15. (a) Kodi ndani pa anthu onse amene anali wokhulupirika kwa Mulungu mosaphonyetsako kalikonse, nanga zimenezi zinasonyezanji? (b) Kodi zimene Yesu anachita zimatithandiza motani?
16. N’chifukwa chiyani nkhani ya ulamuliro wa Yehova tifunika kukhala nayo tcheru nthaŵi zonse?
17. Kodi bodza ndi kuba zinayamba bwanji kuti ife tizizipeŵa?
18. (a) Pa mapeto a Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000, kodi anthu onse adzayesedwa motani? (b) Kodi tikhale n’chizoloŵezi chotani pakali pano?