Mutu 16
“Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni”
NTHAŴI yoyamba imene anthu amafika pa msonkhano wa Mboni za Yehova, amachita chidwi ndi chikondi chimene amachiona kumeneko. Amatero chifukwa kumeneko amawalandira bwino ndipo kumakhala macheza abwino. Alendo amene amafika pa misonkhano yathu yaikulu amaonanso chikondi chimenechi. Mtolankhani wina analemba zimene anaona pamsonkhano wachigawo. Iye anati: ‘Panalibe woledzera mowa kapena mankhwala osokoneza bongo. Panalibe wolalata kapena wolankhula mokalipa. Panalibe kukankhana, kubwanyulana, kutukwanana kapena kunyozana. Kunalibe nthabwala zonyansa kapena kulankhula zolaula. Panalibe wosuta fodya. Sanabe. Sanatayire zitini pa kapinga. Zinali zachilendo kwabasi.’ Zonsezi ndi umboni wa chikondi, chimene “sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha.”—1 Akorinto 13:4-8.
2 Chikondi cha pa abale n’chimene Akristu enieni amadziŵika nacho. (Yohane 13:35) Tikamakula mwauzimu, timaphunzira kusonyeza chikondi kwambiri. Mtumwi Paulo anapempherera Akristu anzake kuti chikondi chawo ‘chisefukire chiwonjezeke.’ (Afilipi 1:9) Ndipo mtumwi Yohane anasonyeza kuti chikondi chathu chifunika kukhala chodzimana. Analemba kuti: “Umo tizindikira chikondi, popeza [Mwana wa Mulungu] anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” (1 Yohane 3:16; Yohane 15:12, 13) Kodi ife tingathedi kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu? Pamene nthaŵi zambiri sitingafunikire kutero, kodi timachita zinthu mpaka pati pofuna kuwathandiza panopa ngakhale kuti kuteroko sikutikhalira bwino ifeyo?
3 Kuwonjezera pa ntchito zathu zimene zimasonyeza kuti tili ndi mzimu wodzimana, mtima wathu wonse uyeneranso kukhala pa abale athu. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni.” (Aroma 12:10) Tonsefe timatero kwa anthu enaake. Koma kodi tingaphunzire kukonda enanso ndi mtima wonse? Chifukwa chakuti mapeto a dziko lakaleli ayandikira, tifunika kuyandikana kwambiri ndi Akristu anzathu. Baibulo limati: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi. . . . Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.”—1 Petro 4:7, 8.
Pakabuka Mavuto
4 Zoona, chifukwa cha kupanda kwathu ungwiro, nthaŵi zina tidzachitabe zinthu zokhumudwitsa ena. Abale athunso angatilakwire m’njira zambiri. (1 Yohane 1:8) Zimenezi zikakuchitikirani muyenera kuchitanji? Malemba amatipatsa malangizo ake. Koma zimene amanena zingasiyane ndi zimene ife anthu opanda ungwiro timakonda kuchita. (Aroma 7:21-23) Ngakhale ndi choncho, ngati tiyesetsa kutsatira uphungu umene Baibulo limapereka, tidzasonyeza kuti tikufuna kukondweretsa Yehova ndi mtima wathu wonse. Ndiponso tikatero, chikondi chathu pa ena chidzalimba.
5 Anthu ukawalakwira, iwo nthaŵi zina amafuna kuthana nawe basi. Koma zimenezo sizithandiza. Zimangoipitsa zinthu. Ngati pakufunika kubwezera, nkhani imeneyo tiisiye m’manja mwa Mulungu. (Miyambo 24:29; Aroma 12:17-21) Ena amayesa kupeŵa munthu amene wawalakwirayo. Koma sitifunika kutero ndi olambira anzathu. Chifukwa chake n’chakuti kukonda abale athu ndiyo mbali ina imene imachititsa kulambira kwathu kukhala kovomerezeka. (1 Yohane 4:20) N’kuona Paulo analemba kuti: ‘Loleranani wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni nokha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.’ (Akolose 3:13) Kodi mungatero?
6 Nanga bwanji ngati wina amatilakwira mobwerezabwereza koma osati kuti amachita tchimo lalikulu lofunika kuti achotsedwe nalo mu mpingo? Pa machimo aang’ono ngati amenewo, mtumwi Petro ananena maganizo ake kuti m’pofunika kukhululuka “kasanu ndi kaŵiri.” Koma Yesu anati: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” Iye anagogomeza kukula kwa mangaŵa amene tili nawo kwa Mulungu poyerekeza ndi amene munthu wina aliyense angakhale nawo kwa ife. (Mateyu 18:21-35) Mulungu timam’lakwira masiku onse—nthaŵi zina chifukwa cha dyera, nthaŵi zina zimene timanena kapena zimene timaganiza, kapenanso kulephera kuchita zinazake—ndipotu sitizindikira n’komwe kuti tikulakwa. (Aroma 3:23) Komabe, Mulungu amatichitira chifundo. (Salmo 103:10-14; 130:3, 4) Amafunanso kuti ife tichite chimodzimodzi kwa ena. (Mateyu 6:14, 15; Aefeso 4:1-3) Tikatero, ndiye kuti tizisonyeza chikondi chimene “sichilingirira zoipa.”—1 Akorinto 13:4, 5; 1 Petro 3:8, 9.
7 Nthaŵi zina zimachitika kuti taona kuti mbale wathu ali nafe chifukwa ngakhale kuti ifeyo tilibe naye chifukwa. Zikatero, tingasankhe kutenga chifukwacho ndi ‘kuchikwirira ndi chikondano,’ ngati mmene 1 Petro 4:8 amanenera. Mwinanso tingaganize zolankhula naye ndi kuyesa kukonza ubwenzi wathu kuti ukhalenso wamtendere.—Mateyu 5:23, 24.
8 N’kutheka kuti wokhulupirira mnzanu akuchita zinthu zimene inuyo ndi anthu ena simukondwera nazo. Kodi si bwino kukambirana naye nkhaniyo? Ee, tingati zimenezo n’zabwino ndithu. Ngati mungam’fotokozere vutolo mokoma mtima, zikhoza kuthandiza. Koma choyamba mudzifunse kuti: ‘Kodi zimene amachitazo n’zosemphanadi ndi Malemba? Kapena kodi vutolo langokhala ineyo chifukwa chakuti kumene ineyo ndimachokera ndi mmene ndinakulira zikusiyana ndi iyeyo?’ Samalani kuti simukukhazikitsa miyezo yanuyanu n’kumaweruza nayo ena. (Yakobo 4:11, 12) Yehova amalandira anthu a mafuko osiyanasiyana mopanda tsankho ndipo amaleza nawo mtima pamene iwo akukula mwauzimu.
9 Wina mumpingo akachita tchimo lalikulu, monga la chiwerewere, m’pofunika kuisamalira msanga nkhaniyo. Ndani ayenera kuisamalira? Akulu. (Yakobo 5:14, 15) Komabe, ngati wina walakwira mnzake, mwina pa zamalonda kapena chifukwa chosalankhula bwino, uja amene mnzake wam’lakwira afunika kupita kwa amene walakwayo kuti akambirane mseri. (Mateyu 18:15) Ngati nkhani imeneyo yakanika kutha atakambirana, afunika kuchitanso zina zomwe zanenedwa pa Mateyu 18:16, 17. Ngati timakonda mbale wathu amene walakwayo ndipo tikufunitsitsa ‘kum’bweza,’ zidzatithandiza kuchita zimenezo m’njira yoti n’kum’fika pa mtima.—Miyambo 16:23.
10 Pakabuka vuto lililonse, lalikulu kapena laling’ono, zimathandiza kuyesa kuliona mmene Yehova amalionera. Iye safuna tchimo lamtundu uliwonse, ndipo nthaŵi yake ikakwana, anthu amene mosalapa amachita machimo aakulu amachotsedwa m’gulu lake pofuna kuti likhale loyera. Koma tonsefe tisaiŵale kuti timachita machimo aang’ono m’njira zambiri ndipo timafuna kuti atilezere mtima ndi kutichitira chifundo. Choncho Yehova amatiikira chitsanzo chimene tiyenera kutsatira ena akatilakwira. Tikawachitira chifundo, ndiye kuti tikusonyeza chikondi chake.—Aefeso 5:1, 2.
Funani Njira ‘Zokulitsira’ Chikondi
11 Paulo anakhala miyezi yambiri akulimbikitsa mpingo wa ku Korinto, ku Girisi. Anachita khama kuthandiza abale kumeneko, ndipo anawakonda kwambiri. Koma ena mwa iwo sanali kum’konda ndi mtima wonse. Anali kungom’peza zifukwa. Iye anawalimbikitsa ‘kukulitsa’ chikondi chawo. (2 Akorinto 6:11-13; 12:15) Ndiye tonsefe tingachite bwino kuona mmene timasonyezera chikondi kwa ena ndi kupeza njira zimene tingachikulitsire.—1 Yohane 3:14.
12 Kodi alipo ena mumpingo amene zimativuta kuwayandikira? Ngati tingayesetse kuiŵalako maumunthu awo—zimene timafuna kuti iwonso atichitire—zingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iwowo. Ndiponso mtima wathu ungayambe kuwakonda ngati tifunafuna mbali zimene amachita bwino n’kumayang’ana zomwezo basi. Chifukwa cha zimenezi chikondi chathu pa iwo chidzakula.—Luka 6:32, 33, 36.
13 Zoona, pali zina zimene sizitheka kuchitira ena. Sizingatheke kupatsa moni wina aliyense pamsonkhano. Poitana mabwenzi kuti adzadye chakudya kunyumba kwathu, sikungatheke kuitana wina aliyense. Koma kodi tingakulitse chikondi mwa kupatula mphindi zoŵerengeka chabe kuti tidziŵane bwino ndi wina mumpingo? Kodi nthaŵi zina tingapemphe wina amene sitikum’dziŵa bwino kuti tipite naye mu utumiki wa kumunda?
14 Misonkhano ikuluikulu yachikristu imapereka mpata wabwino wokulitsa chikondi chathu. Pamakhala anthu zikwizikwi. Ngakhale kuti onsewo sitingacheze nawo, titha kuchita zinthu m’njira yoonetsa kuti tikuika ubwino wa ena patsogolo pa ubwino wathu. Nthaŵi yopuma, tingasonyeze kukonda ena mwa kuyamba ifeyo kucheza ndi anthu amene atizungulira pamene takhalapo. Tsiku lina anthu onse padziko lapansi adzakhala abale ndi alongo, ogwirizana pa kulambira Mulungu woona ndi Atate wa onse. Komatu ndiye panthaŵiyo tidzasangalala kwambiri kudziŵana ndi ena! Chikondano chenicheni chidzatilimbikitsa kuchita zimenezo. Bwanji osayamba panopa?
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi pakabuka mavuto pakati pa Akristu ayenera kuwathetsa bwanji, nanga n’chifukwa chiyani?
• Tikamakula mwauzimu, ndi motaninso mmene chikondi chathu chiyenera kukulira?
• Kodi zingatheke bwanji kusonyeza chikondano chenicheni kwa onse osati chabe kwa mabwenzi apamtima?
[Mafunso]
1. Kodi chimene chimachititsa chidwi atsopano pamisonkhano ya Mboni za Yehova n’chiyani?
2. (a) Kodi kasonyezedwe kathu ka chikondi kayenera kukhala kotani m’kupita kwa nthaŵi? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi chikondi chotani potsanzira Kristu?
3. (a) Kodi chikondi chathu tingachisonyeze kwambiri motani? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kukondana ndi chikondano chenicheni panopa?
4. (a) Kodi n’chifukwa chiyani pangabuke mavuto pakati pa anthu mumpingo? (b) Kodi timapeza phindu lotani mwa kutsatira uphungu wa m’Baibulo ngakhale kuti nthaŵi zina sitingakonde kutero?
5. Wina akatilakwira, n’chifukwa chiyani sitiyenera kubwezera?
6. (a) Kodi mbale wathu tiyenera kum’khululukira kangati? (b) Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuzindikira chomwe chidzatithandiza wina akatilakwira?
7. Kodi tiyenera kuchitanji ngati mbale wathu ali nafe chifukwa?
8. Ngati wokhulupirira mnzathu amachita zinthu zimene sitikondwera nazo, kodi tingachitepo chiyani?
9. (a) Kodi amene amasamalira milandu mumpingo wina akachita tchimo lalikulu ndani? (b) Nanga ndi liti pamene wolakwiridwa amafunika kuyamba iyeyo kuchitapo kanthu, ndipo cholinga chake n’chiyani?
10. Pakabuka vuto lililonse, n’chiyani chidzatithandiza kuona bwino nkhaniyo?
11. N’chifukwa chiyani Paulo analimbikitsa Akorinto ‘kukulitsa’ chikondi chawo?
12. Kodi chikondi chathu pa onse mumpingo tingachikulitse bwanji?
13. Kodi tingachitenji kuti tikulitse chikondi chathu pa abale mumpingo wathu?
14. Tikakhala pakati pa Akristu anzathu amene sitinakumanepo nawo, tingasonyeze bwanji chikondano chenicheni?
[Chithunzi patsamba 148]
Chikondi chachikristu chimasonyezedwa m’njira zambiri, monga pamisonkhano ya mpingo