Mutu 5
Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
1, 2. (a) Kodi Akhristu amakumana ndi mavuto otani pa nkhani ya anthu ocheza nawo? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi mmene Yeremiya ankasankhira anthu oti akhale anzake?
KODI mungatani ngati anzanu akuntchito, oyandikana nawo nyumba kapena akusukulu atakupemphani kuti mukakhale nawo paphwando la Khirisimasi? Nanga mungatani ngati abwana anu atakuuzani kuti munene bodza kapena muchite zinthu zophwanya malamulo? Kapena mungatani ngati akuluakulu a boma atakuuzani kuti muchite zinthu zomwe zingakuchititseni kulowerera pa ndale kapena pa nkhondo? Mwina chikumbumtima chanu sichingakuloleni kuchita zimenezi, ngakhale kuti munganyozedwe kapena kuzunzidwa.
2 M’nkhani ino tiona kuti Yeremiya ankakumana ndi mavuto ngati amenewa kawirikawiri. Mosakayikira zitithandiza kwambiri tikaganizira anthu osiyanasiyana amene Yeremiya anachita nawo zinthu pa zaka zonse zimene ankachita utumiki wake. Ena mwa anthu amenewa ankayesetsa kumufooketsa kuti asiye utumiki wakewo. Nthawi zina Yeremiya ankachita zinthu zina ndi anthu amenewa, koma iye sanasankhe kuti iwo akhale anzake. Choncho, zingatithandize ngati titaona anthu amene Yeremiya anasankha kuti akhale anzake. Iye anasankha anthu amene ankamuthandiza komanso kumulimbikitsa kuti akhalebe wokhulupirika. Zoonadi, Yeremiya ndi chitsanzo chabwino kwa ife pa nkhani yosankha anthu ocheza nawo.
KODI MUMASANKHA ANTHU OTANI KUTI AKHALE ANZANU?
3. Kodi Zedekiya ankafuna chiyani kwa Yeremiya, ndipo Yeremiyayo anachita chiyani?
3 Mfumu Zedekiya analankhulana ndi Yeremiya maulendo angapo mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mfumuyi inkafuna kumva mawu olimbikitsa pa zimene inkafunsa zokhudza tsogolo la ufumu wake. Iyo inkafuna kuti Yeremiya anene kuti Mulungu adzapulumutsa dziko la Yuda kwa adani ake. Zedekiya anatuma nthumwi kuti zikapemphe Yeremiya kuti: “Chonde tifunsire kwa Yehova chifukwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo akufuna kumenyana nafe nkhondo. Mwina Yehova adzatichitira imodzi mwa ntchito zake zamphamvu kuti Nebukadirezarayo atichokere.” (Yer. 21:2) Mfumuyi sinafune kutsatira malangizo a Mulungu akuti igonjere Ababulo. Katswiri wina wa Baibulo anayerekezera Zedekiya ndi “munthu wodwala amene amapita kwa dokotala mobwerezabwereza kuti akamuthandize, koma osafuna kumwa mankhwala amene wapatsidwa.” Kodi Yeremiya anachita chiyani? Iye sanauze Zedekiya zinthu zimene ankafuna kumva ngakhale kuti Zedekiyayo akanayamba kumukonda akanamuuza zimenezo. Kodi n’chifukwa chiyani Yeremiya sanasinthe uthenga wake kuti zinthu zimuyendere bwino? N’chifukwa chakuti Yehova anali atamuuza kuti alengeze uthenga wakuti Yerusalemu adzawonongedwa.—Werengani Yeremiya 32:1-5.
4. Kodi tingafunike kuganizira mfundo ziti pa nkhani yocheza ndi anthu osiyanasiyana, monga akuntchito kwathu?
4 M’njira zina, mmene zinthu zilili kwa inu n’chimodzimodzi ndi mmene zinalili ndi Yeremiya. Mosakayikira inunso mumachita zinthu zina ndi anthu oyandikana nawo nyumba, anzanu akuntchito, kapenanso akusukulu, amene tinganene kuti ndi anansi anu. Koma kodi mungafune kuti muzolowerane nawo kwambiri mpaka kufika pokhala anzanu ngakhale kuti asonyeza kuti safuna kumva kapena kutsatira malangizo a Mulungu? Yeremiya sakanasiyiratu kulankhula ndi Zedekiya chifukwa anali adakali mfumu ngakhale kuti iye ankakana kutsatira malangizo a Mulungu. Komabe, Yeremiya sanalolere kuchita zinthu zogwirizana ndi maganizo opotoka a mfumuyo ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti mfumuyo isamukonde. Koma ngati iye akanachita zinthu zogwirizana ndi maganizo a Mfumu Zedekiya, n’zodziwikiratu kuti mfumuyo ikanamupatsa mphatso zambirimbiri ndiponso zinthu zina. Ngakhale zinali choncho, Yeremiya anakaniratu kuchita zinthu zosangalatsa mfumuyo ndipo sanalole kuti Zedekiya akhale mnzake. N’chifukwa chiyani Yeremiya anachita zimenezi? N’chifukwa chakuti iye sakanalola ngakhale pang’ono kusintha uthenga umene Yehova anamuuza. Chitsanzo cha Yeremiya chiyenera kutithandiza ifeyo kudziunika kuti tione ngati anthu amene timasankha kukhala anzathu amatilimbikitsa kuti tikhale okhulupirika kwa Mulungu. N’zoona kuti simungapeweretu kulankhulana kapena kuchita zinthu zina ndi anthu amene satumikira Mulungu, monga anthu akuntchito kwanu, kusukulu kapena anthu amene mwayandikana nawo nyumba. (1 Akor. 5:9, 10) Komabe, mukudziwa bwino kuti ngati mungasankhe anthu amenewo kukhala anzanu, mwina mungachite zinthu zina zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu.
KODI ANTHU OSAKHULUPIRIRA MAWU A MULUNGU ANGAKHALE ANZANU?
5, 6. Kodi anthu ena anachita chiyani pofuna kuti Yeremiya asiye kunenera?
5 Si Zedekiya yekha amene ankayesetsa kuchita zinthu zimene zikanafooketsa Yeremiya. Wansembe wina dzina lake Pasuri “anamenya” Yeremiya, mwina zikoti 39. (Yer. 20:2; Deut. 25:3) Nawonso akalonga ena a ku Yuda anamenya Yeremiya, kenako n’kumutsekera “m’ndende.” Mneneriyu anaikidwa m’ndende yapansi yoipa kwambiri, moti atakhalamo masiku ambiri, anayamba kuona kuti afera momwemo. (Werengani Yeremiya 37:3, 15, 16.) Kenako Yeremiya anatulutsidwa m’ndendemo, koma patapita nthawi, akalonga ena anakapempha Zedekiya kuti Yeremiya aphedwe. Akalongawo anachita zimenezi chifukwa ankaona kuti Yeremiya akufooketsa asilikali achiyuda. Zimenezi zinachititsa kuti mneneriyu aponyedwe m’chitsime cha matope n’cholinga choti afere momwemo. (Yer. 38:1-4) Mwawerenga kale kuti Yeremiya anapulumutsidwa ku chiwembu choopsachi ndipo sanafe. Zinthu zoipa zimene anthuwo anachita zikusonyeza kuti iwo anayamba kukayikira zimene mneneri wa Mulunguyo ankanena. Choncho iwo anamuukira, ngakhale kuti anayenera kudziwa kuti zimene ankachitazo zinali zoipa.
6 Si akuluakulu a boma okha amene anali adani a Yeremiya. Pa nthawi ina, anthu a mumzinda wa Anatoti, kwawo kwenikweni kwa Yeremiya, anamuopseza kuti asiye kunenera ngati akufuna kuti asamuphe. (Yer. 11:21) Iwo anamuopseza chonchi chifukwa sankasangalala ndi uthenga umene iye ankalengeza. Ngakhale zinali choncho, Yeremiya anasankha Yehova kuti akhale mnzake weniweni, osati anthu a mumzinda wakwawo. Kenako anthu ena anayamba kumuchitira zinthu zina zankhanza. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yeremiya anagwiritsa ntchito goli lathabwa monga chizindikiro chooneka polimbikitsa Ayuda kuti alowe m’goli la mfumu ya ku Babulo kuti asaphedwe. Koma Hananiya anachotsa golilo m’khosi mwa Yeremiya n’kulithyola. Mneneri wonyengayo anauza anthu kuti Yehova wanena kuti: “Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.” Komatu Hananiya anamwalira m’chaka chomwecho, ndipo zinadziwika kuti Yeremiya ndiye mneneri amene ankanena zoona. (Yer. 28:1-11, 17) Komanso Yerusalemu atawonongedwa mogwirizana ndi zimene Yeremiya analosera, Yohanani ndi akuluakulu ena a asilikali anakana kumvera lamulo limene Mulungu anapereka loti asachoke m’dziko la Yuda. Iwo anauza Yeremiya kuti: “Ukunena zabodza. Yehova Mulungu wathu sanakutume kudzatiuza kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko.’” Iwo anapitiriza kusamvera Yehova moti pamene ankapita ku Iguputo anagwira Yeremiya ndi Baruki n’kupita nawo limodzi.—Yer. 42:1–43:7.
Kodi Yeremiya ankalengeza uthenga wake kwa anthu otani? Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yeremiya?
7. Kodi vuto lina limene mungakumane nalo pamene mukuyesetsa kuti mukhalebe okhulupirika kwa Yehova ndi lotani?
7 Kwa zaka zambiri, Yeremiya anakhala ndi anthu amene sankakhulupirira uthenga umene iye ankalengeza komanso omwe ankamutsutsa. Tikaganizira mmene zinthu zinalili pa moyo wake, tingathe kuona kuti zikanakhala zosavuta kuti iye agonje n’kuyamba kucheza ndi anthu omwe sankalemekeza Mulungu kapenanso Mawu ake. Ndipotu anthu oterowo anali paliponse. Nanga bwanji inuyo masiku ano? N’kutheka kuti nanunso mumafunika kuchita zinthu zina ndi zina ndi anthu ofanana ndi a m’nthawi ya Yeremiya. Mwina anthuwo amakutsutsani mwaukali kapena amatsutsa uthenga wa Mulungu wanu, kapenanso mwina amaoneka kuti ndi anthu abwino ndithu. Koma kodi mudzasankha anthu otero kuti akhale anzanu? Kodi chingakhale chinthu chanzeru kumacheza ndi anthu amene sakhulupirira kwenikweni maulosi a Mulungu? Ngati Yeremiya akanakhalapo m’nthawi yathu ino, kodi iye akanasankha kucheza ndi anthu amene moyo wawo umasonyeza kuti amakana choonadi cha m’Mawu a Mulungu, kapenanso anthu amene amakhulupirira kwambiri anthu anzawo? (2 Mbiri 19:2) Mulungu anauza Yeremiya mosapita m’mbali zimene zidzachitikire anthu omwe amakhulupirira anthu anzawo m’malo mokhulupirira Mulunguyo. (Werengani Yeremiya 17:5, 6.) Kodi inuyo mukuiona bwanji nkhani imeneyi?
8. Fotokozani mavuto amene Akhristu a m’dera lanu angakumane nawo.
8 Akhristu ena aganizapo zoti bizinezi yawo kapena ntchito yawo ingapite patsogolo ngati atamachereza makasitomala awo amene si a Mboni. Komatu kuchita zimenezo kungachititse Akhristuwo kucheza ndi anthu oipa, omwe amalankhula nkhani zowola ndiponso amene amamwa mowa kwambiri. Mukhoza kumvetsa chifukwa chake Akhristu ambiri amene akanatha kuchereza anthu otero amasankha kusawachereza pofuna kupewa kucheza ndi anthu oipa. Iwo amasankha kuchita zimenezi ngakhale kuti zingawatayitse mwayi wopititsa patsogolo bizinezi kapena ntchito yawo. Nthawi zina zingachitikenso kuti abwana kapena anzanu amene mumagwira nawo ntchito ali ndi chizolowezi chochitira makasitomala zinthu zachinyengo. Ngakhale zitakhala choncho, Akhristu oona ayenera kupewa kutengera zochita za anthu ena. Nthawi zina kusankha zochita pa nkhani ngati zimenezi kumakhala kovuta. Komabe tili ndi mwayi chifukwa tili ndi zitsanzo zabwino, monga Yeremiya. Iye anapitirizabe kuchita zinthu zomwe zinam’thandiza kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri.
9. Kodi kukhala ndi mtima wofuna kuchita zinthu zimene anthu ambiri akuchita, n’koopsa motani?
9 Ayuda ena anayamba kunyoza Yeremiya chifukwa cha kulimba mtima kwake komanso chikhulupiriro chake. (Yer. 18:18) Ngakhale kuti iye ankanyozedwa, analolera kukhala wosiyana ndi anthu a m’nthawi yakewo, omwe ankatsatira ‘njira imene anthu ambiri ankaitsatira.’ (Yer. 8:5, 6) Nthawi zina Yeremiya ankalolera ‘kukhala yekhayekha.’ Iye ankaona kuti ndi bwino kukhala yekhayekha m’malo mocheza ndi anthu oipa, omwe akanatha kum’sokoneza. (Werengani Yeremiya 9:4, 5; 15:17.) Nanga bwanji inuyo? Mofanana ndi m’nthawi ya Yeremiya, masiku ano anthu ambiri ndi osakhulupirika kwa Mulungu. Ndipotu kuyambira kale kwambiri, atumiki a Yehova amafunika kukhala osamala posankha anthu ocheza nawo. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Yeremiya analibe anzake. Tikutero chifukwa panali anthu ena amene ankamuteteza ndiponso kumuthandiza. Kodi anthu amenewo anali ndani? Kudziwa anthu amenewo kungakuthandizeni kwambiri.
KODI YEREMIYA ANASANKHA ANTHU OTANI KUTI AKHALE ANZAKE?
10, 11. (a) Kodi Yeremiya ankayendera mfundo ziti posankha anthu ocheza nawo? (b) Kodi anzake a Yeremiya anali ndani, ndipo tiyenera kufunsa mafunso otani okhudza anzakewo?
10 Kodi Yeremiya anasankha anthu otani kuti akhale anzake? Molangizidwa ndi Yehova, iye anadzudzula mobwerezabwereza anthu oipa, achinyengo, opanda chilungamo, achiwawa, ankhanza ndiponso achiwerewere. Anthu omwe ankachita makhalidwe amenewa ankachita uhule mwauzimu chifukwa anasiya kulambira koona n’kuyamba kulambira mafano. Yeremiya analimbikitsa Ayuda anzake kuti: “Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.” (Yer. 18:11) Ngakhale pamene Yerusalemu anawonongedwa, Yeremiya anatamanda Mulungu chifukwa cha “kukoma mtima [kwake] kosatha,” chifukwa cha “chifundo” chake ndiponso chifukwa cha ‘kukhulupirika’ kwake. (Maliro 3:22-24) Yeremiya ankasankha anthu okhawo amene anali atumiki okhulupirika a Yehova kuti akhale anzake.—Werengani Yeremiya 17:7.
11 Ndipotu tikudziwako anthu ena amene Yeremiya anawasankha kuti akhale anzake. Ena mwa anthu amenewa, monga Ebedi-meleki, Baruki, Seraya komanso ana a Safani, anamuthandiza kwambiri. Mwina tingafunse kuti: ‘Kodi anthu amenewa anali otani? Kodi ubwenzi wawo unali wotani ndi Yeremiya? N’chifukwa chiyani tinganene kuti iwo anali anzake abwino? Komanso kodi anathandiza bwanji Yeremiya kuti apitirizebe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika?’ Tikamakambirana mayankho a mafunso amenewa, tiganizire mmene zinthu zilili pa moyo wathu masiku ano.
12. (a) Kodi Yeremiya ndi Baruki, amene tikuwaona pachithunzi cha patsamba 58, anali ofanana m’njira ziti? (b) Kodi Seraya anali ndani, ndipo tikudziwa zotani za iye?
12 Zikuoneka kuti mnzake wapamtima wa mneneriyu anali Baruki, mwana wa Neriya. Yeremiya ankamudalira kwambiri Baruki ndipo anam’patsa ntchito yoti azilemba uthenga wachiweruzo wochokera kwa Yehova umene mneneriyu ankamuuza. Kenako Yeremiya anauza Baruki kuti akawerenge mpukutu umene analembawo, choyamba pamaso pa anthu ndipo kenako kwa akalonga a ku Yuda. (Yer. 36:4-8, 14, 15) Baruki anali ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Yeremiya moti sankakayikira kuti zimene Mulungu ananena zidzachitikadi. Anthu amenewa anakumana ndi zinthu zofanana pa zaka 18 zomalizira za ufumu wa Yuda, pamene zinthu zinali zovuta kwambiri m’dzikolo. Kwa nthawi yaitali iwo ankagwirira limodzi ntchito imene Mulungu anawapatsa. Onse anakumana ndi mavuto ndipo nthawi zina ankafunika kubisala kuti adani asawapeze. Komanso onsewa, aliyense payekha analandira uthenga wachindunji wochokera kwa Yehova womulimbikitsa. Zikuoneka kuti Baruki ankachokera ku banja lotchuka la alembi m’dziko la Yuda. Malemba amanena kuti iye anali “mlembi,” ndipo m’bale wake Seraya anali ndi udindo waukulu m’boma. Mofanana ndi Baruki, patapita nthawi Seraya anagwiranso ntchito ndi Yeremiya polengeza mauthenga aulosi ochokera kwa Yehova. (Yer. 36:32; 51:59-64) Ana awiri amenewa a Neriya anagwira ntchito mofunitsitsa limodzi ndi Yeremiya m’nthawi yovutayo, ndipo zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsa kwambiri mneneriyu. Inunso mungalimbikitsidwe ndi anthu okhulupirika amene akutumikira Yehova pamodzi nanu.
Kodi mukuphunzirapo chiyani mukaona anthu amene Yeremiya anasankha kuti akhale anzake?
13. Malinga ndi chithunzi chimene chili patsamba 63, kodi Ebedi-meleki anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wapamtima wa Yeremiya?
13 Munthu wina amene anathandiza kwambiri Yeremiya anali Ebedi-meleki. Mwachitsanzo, pamene akalonga okwiya anaponyera Yeremiya m’chitsime chopanda madzi kuti afere momwemo, Ebedi-meleki, amene anali wochokera ku Itiyopiya osati ku Yuda, ndi amene analimba mtima kuti amupulumutse. Iye anali nduna ya panyumba ya mfumu, ndipo anapita mosabisa kwa Zedekiya amene anali atakhala pa Chipata cha Benjamini. Ndiyeno molimba mtima, Ebedi-meleki anapempha Zedekiya kuti amulole kukapulumutsa Yeremiya amene anaponyedwa m’chitsime cha matope. Popita kukapulumutsa Yeremiya, Ebedi-meleki anatenga amuna 30. Zimenezi zikusonyeza kuti mwina iye ankayembekezera kuti adani a Yeremiya angathe kulimbana naye. (Yer. 38:7-13) Sitikudziwa kuti Ebedi-meleki ankacheza kwambiri bwanji ndi Yeremiya. Koma tikaganizira mfundo yakuti onse anali mabwenzi a Yehova, sitingalakwitse kuganiza kuti Ebedi-meleki analinso mnzake wapamtima wa Yeremiya. Iye ankadziwa kuti Yeremiya anali mneneri wa Yehova. Ebedi-meleki ananena kuti zimene akalonga aja anachita zinali “zoipa,” ndipo anali wokonzeka kuchita zinthu zoyenera ngakhale kuti akanatha kuchotsedwa nazo ntchito. Zoonadi, Ebedi-meleki anali munthu wabwino. Umboni wa zimenezi ndi wakuti Yehova anamutsimikizira kuti: “Ndidzakulanditsa [pa tsiku limene Yerusalemu adzawonongedwe] . . . chifukwa chakuti wandikhulupirira.” (Werengani Yeremiya 39:15-18.) Amenewatu anali mawu olimbikitsa kwambiri ochokera kwa Yehova. Kodi inunso simungafune anthu otere kuti akhale anzanu?
14. Kodi tikudziwa chiyani za anthu a m’banja la Safani ndi zimene ankachitira Yeremiya?
14 Anthu ena amene anali anzake a Yeremiya anali ana atatu a Safani ndi mdzukulu wake mmodzi. Anthu amenewa ankachokera m’banja lolemekezeka, chifukwa Safani anagwirapo ntchito ngati mlembi wa Mfumu Yosiya. Pa nthawi yoyamba imene adani a Yeremiya ankafuna kupha mneneriyu, ‘Ahikamu, mwana wa Safani anateteza Yeremiya kuti anthu asamuphe.’ (Yer. 26:24) Ahikamu anali ndi mchimwene wake dzina lake Gemariya. Pamene Baruki ankawerenga uthenga wa chiweruzo cha Mulungu pamaso pa anthu, Mikaya mwana wa Gemariya anali pomwepo, ndipo anapita kukadziwitsa bambo ake ndi akalonga ena. Ndiyeno iwo anachenjeza Yeremiya ndi Baruki kuti akabisale poopa kuti Yehoyakimu angawachitire zoipa. Komanso mfumu itakana kumvetsera uthenga wochokera kwa Mulungu, Gemariya anali m’gulu la anthu amene anachonderera mfumuyo kuti isatenthe mpukutu wa uthengawo. (Yer. 36:9-25) Yeremiya anatumiza Elasa, mwana wina wa Safani, kuti akapereke kalata yaulosi kwa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo. (Yer. 29:1-3) Choncho tikuona kuti panali ana atatu a Safani ndi mdzukulu wake mmodzi amene ankathandiza mneneri wa Mulunguyu. Yeremiya ayenera kuti ankayamikira kwambiri anthu amenewa. Anthuwa anali anzake, koma osati chifukwa choti ankakonda zinthu zofanana, monga chakudya, zakumwa kapena zosangalatsa. Panali zinthu zambiri zimene zinachititsa kuti anthuwa akhale anzake.
MUZISANKHA MWANZERU ANTHU OTI AKHALE ANZANU
15. Kodi Yeremiya anapereka chitsanzo chabwino chiti pa nkhani yosankha anthu ocheza nawo?
15 Mungatengere chitsanzo kwa Yeremiya cha mmene ankachitira zinthu ndi anthu abwino komanso oipa m’nthawi yake. Yeremiya ankakakamizidwa ndi anthu osiyanasiyana, monga mfumu, akalonga ambiri, aneneri onyenga komanso akuluakulu a asilikali, kuti asinthe uthenga wake. Koma Yeremiya sanasinthe, ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthuwo azidana naye. Komabe Yeremiya sanadandaule nazo chifukwa sankalakalaka kuti anthu amenewo akhale anzake. Yehova ndi amene anali mnzake wapamtima nthawi zonse. Yeremiya anatsimikiza ndi mtima wonse kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, ngakhale anthu atayamba kumuzunza chifukwa cha zimenezi. (Werengani Maliro 3:52-59.) Koma monga taonera, si Yeremiya yekha amene anali wotsimikiza ndi mtima wonse kutumikira Yehova.
16, 17. (a) Kodi mtumiki wa Yehova angathandizidwe bwanji ndi mnzake wapamtima? (b) Kaya mukukhala m’dziko liti, kodi anzanu apamtima mungawapeze kuti?
16 Ebedi-meleki anali mnzake wapamtima wa Yeremiya chifukwa chakuti ankakhulupirira Yehova komanso ankamudalira. Munthu ameneyu anali wolimba mtima ndipo anachita zinthu mosazengereza populumutsa Yeremiya. Mofunitsitsa, nayenso Baruki anakhala ndi Yeremiya kwa nthawi yaitali ndipo anamuthandiza kulengeza uthenga wochokera kwa Yehova. Anthu amene ndi mabwenzi apamtima mumpingo wachikhristu masiku ano angamadalirane kwambiri ngati mmene ankachitira Yeremiya ndi anzakewo. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka 20 amene ndi mpainiya wokhazikika, dzina lake Cameron, amayamikira kwambiri mmene mlongo Kara, amenenso ndi mpainiya, anamuthandizira. Cameron ananena kuti: “Kara anandilimbikitsa kuti ndiziika Yehova poyamba m’moyo wanga. Iye anachita zimenezi pondisonyeza chitsanzo chabwino komanso pondiuza mawu olimbikitsa.” Alongo awiriwa ankakhala m’madera otalikirana, komabe Kara ankaimbira foni Cameron pafupipafupi kapena kumulembera makalata kuti adziwe mmene mnzakeyo alili komanso kuti alimbikitsane. Cameron ananena kuti: “Mlongoyu ankadziwa mavuto onse amene tinkakumana nawo pa banja pathu. Ankadziwa zimene mkulu wanga ankachita komanso mmene zinandipwetekera mkulu wangayu atasiya choonadi. Kara anali nane pamene ndinkakumana ndi mavuto onsewa, ndipo sindikudziwa kuti ndikanatani pakanapanda mlongoyu, amene ankandilimbikitsa kwambiri. Ndithudi, Kara anandithandiza kwabasi.”
17 Mumpingo wachikhristu muli anthu amene angathe kukhala anzanu apamtima, kaya a msinkhu wanu kapena ayi. Abale ndi alongo anu ali ndi chikhulupiriro ngati chanu, ali ndi makhalidwe achikhristu ofanana ndi anu, amakonda Yehova ngati inu nomwe, ali ndi chiyembekezo ngati chanu, ndipo n’kutheka kuti akukumana ndi mavuto amene inunso mukukumana nawo. Mungathe kuchitira nawo limodzi utumiki wachikhristu. Iwo angakulimbikitseni pamene mukukumana ndi mavuto, ndipo inunso mungawalimbikitse. Iwo adzasangalala nanu limodzi zinthu zikamakuyenderani bwino potumikira Yehova. Kuwonjezera pamenepo, anthu amenewa angakhale anzanu kwamuyaya.—Miy. 17:17; 18:24; 27:9.
18. Kodi mukuphunzira chiyani kwa Yeremiya pa nkhani yosankha anthu oti akhale anzanu?
18 Zimene tikuphunzira kwa Yeremiya pa nkhani yosankha anthu oti akhale anzathu n’zodziwikiratu. Nthawi zonse tizikumbukira mfundo yosatsutsika yakuti: N’zosatheka kuti mukhalebe okhulupirika kwa Mulungu ngati mumakonda kucheza ndi anthu amene amakhulupirira zinthu zosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Choncho kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo imeneyi n’kofunika kwambiri masiku ano mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Yeremiya. Yeremiya analolera kuti akhale wosiyana ndi anthu ambiri a m’nthawi yake n’cholinga choti agwire mokhulupirika ntchito imene anapatsidwa ndiponso kuti azithandizidwa ndi Yehova. Kodi inunso ndinu okonzeka kuchita zimenezi? Yeremiya ankakonda kucheza ndi anthu amene anali ndi chikhulupiriro chofanana ndi chake ndiponso amene ankamuthandiza pochita utumiki wake. Inde, Mkhristu aliyense wokhulupirika masiku ano ayenera kutengera chitsanzo cha Yeremiya pa nkhani yosankha mwanzeru anthu oti akhale anzake.—Miy. 13:20; 22:17.
Kodi mungatsanzire bwanji Yeremiya posankha anthu oti akhale anzanu komanso amene simukufuna kuti akhale anzanu?