Mutu 28
N’chifukwa Chiyani Atsikana Samandifuna?
Zimene ndikumuuzazi zichititsa kuti afe nane mutu. Ndamuuza zonse, katundu amene ndili naye, malo amene ndayenda ndiponso anthu amene ndimadziwana nawo. Sindikukayika kuti akuchita kuona kuchedwa kuti ndimufunsire.
Zimene akuchitazi zandikwana kwambiri. Ndayesa kumuuza mwaulemu kuti sindikumufuna koma sakumva. Ndiye ndimuuze bwanji mwamphamvu koma moti asakhumudwe?
TIYEREKEZE kuti ndinu wamkulu ndithu moti mukhoza kukhala ndi chibwenzi. Mukulakalaka mutapeza mtsikana wooneka bwino ndiponso wofanana naye chikhulupiriro. (1 Akorinto 7:39) Koma m’mbuyomu mwayesapo kuti mupeze chibwenzi koma mumangowomba khoma. Kodi vuto ndi chiyani? Kapena atsikana amangofuna anyamata ooneka bwino okha? Mtsikana wina, dzina lake Lisa, ananena kuti: “Ndimakonda anyamata okhala ndi masozi.” Komabe atsikana ambiri samangokopeka ndi maonekedwe. Carrie wazaka 18, ananena kuti: “Nthawi zambiri anyamata ooneka bwino samakhala akhalidwe.”
Kodi atsikana amafuna anyamata akhalidwe lotani? Ngati mukufuna kufunsira mtsikana winawake kodi muyenera kuganizira zinthu ziti? Nanga ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene muyenera kuzikumbukira?
Zoyenera Kuchita Musanayambe Chibwenzi
Musanaganize zofufuza mtsikana, pali zinthu zingapo zofunika zimene muyenera kuchita ndipo zingakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi aliyense. Tiyeni tikambirane zinthu zimenezi.
● Yesetsani kukhala ndi makhalidwe abwino. Baibulo limanena kuti chikondi “sichichita zosayenera.” (1 Akorinto 13:5) Khalidwe labwino limasonyeza kuti mumalemekeza anthu ena ndiponso kuti mukukula mwauzimu ndipo mwayamba kutengera makhalidwe a Khristu. Komabe makhalidwe abwino sali ngati suti imene umangovala kuti anthu ena akugomere kenako n’kukaivula ukafika kunyumba. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimasonyeza makhalidwe abwino ndikamachita zinthu ndi abale anga?’ Ngati simusonyeza khalidwe labwino ndi abale anu zingakhale zovuta kuti muzisonyeza khalidwe labwino pochita zinthu ndi anthu ena. Kumbukirani kuti mtsikana wozindikira adzafuna kuona mmene inuyo mumachitira zinthu ndi abale anu kuti adziwe kuti ndinu munthu wotani.—Aefeso 6:1, 2.
Zimene atsikana amanena: “Ndimakopeka ndi mnyamata amene amasonyeza khalidwe labwino pondichitira zinthu zing’onozing’ono ngati kunditsegulira chitseko ndiponso zinthu zikuluzikulu ngati kuchita zinthu mondiganizira komanso moganizira abale anga.”—Anatero Tina.
“Sindisangalala ngati munthu amene ndangokumana naye koyamba akundifunsa zinthu zimene munthu sungamasuke kumangouza aliyense ngati zoti ‘Kodi uli ndi chibwenzi?’ ndiponso ‘Kodi uli ndi zolinga zotani?’ Ndimaona kuti si ulemu, moti ndimamangika kwambiri munthu akamandifunsa zimenezi.”—Anatero Kathy.
“Ndimaona kuti si ulemu anyamata akamaganiza kuti akhoza kumangotiseweretsa maganizo pomachita zinthu ngati atifunsira, koma ayi. Amakhala ngati sasamala za mmene tikumvera mumtima komanso amaona ngati tonse timangoganizira za banja basi, moti timafuna kuti azitimvera chisoni.”—Anatero Alexis.
● Muzikhala aukhondo nthawi zonse. Kukhala waukhondo kumasonyeza kuti mumalemekeza anthu ena komanso mumalemekeza thupi lanu. (Mateyu 7:12) Ngati mumadzilemekeza nokha n’zosavuta kuti anthu enanso azikulemekezani. Koma ngati mulibe ukhondo, olo mutayesetsa bwanji n’zovuta kuti mtsikana akopeke nanu.
Zimene atsikana amanena: “Mnyamata wina amene ankandifuna ankanunkha mkamwa. Fungo lake linali lamphamvu kwambiri moti zinali zosatheka kulipirira.”—Anatero Kelly.
● Muzidziwa kuchezetsa. Kulankhulana bwino n’kumene kumathandiza kuti chibwenzi kapena banja likhale lolimba. Muyenera kukambirana zomwe inuyo mumakonda komanso zimene mnzanuyo amakonda. (Afilipi 2:3, 4) Muyenera kumvetsera pamene iyeyo akulankhula ndiponso muzilemekeza maganizo ake.
Zimene atsikana amanena: “Ndimasangalala mnyamata akamacheza nane momasuka. Ayenera kumakumbukira zinthu zimene ndinamuuza komanso azifunsa mafunso amene angathandize kuti tizipitiriza kucheza.”—Anatero Christine.
“Ndimaganiza kuti anyamata amakopeka ndi zimene amaona pamene atsikana amakopeka ndi zimene amamva.”—Anatero Laura.
“Mnyamata akamakupatsa mphatso zimakhala bwino koma mnyamata yemwe ukhoza kukopeka naye mosavuta ndi amene amadziwa kuchezetsa komanso amakuuza mawu olimbikitsa.”—Anatero Amy.
“Ndikudziwa mnyamata winawake yemwe ndi waulemu komanso samakumasukira kwambiri. Timatha kucheza nkhani zabwinobwino iyeyo osakuuza zinthu ngati zoti, ‘Komatu ndiye ukununkhira bwino’ kapena ‘Lero ndiye watchenatu.’ Amamvetsera mwachidwi ndikamalankhula ndipo ndikukhulupirira kuti mtsikana aliyense angasangalale kucheza ndi munthu wotere.”—Anatero Beth.
“Ndikhoza kulola kukhala pa chibwenzi ndi munthu amene amakambako tinthabwala koma osati nthawi zonse. Pena muzikambiranako zinthu za phindu koma asamakambe nkhani zimenezi mongofuna kuti akukope.”—Anatero Kelly.
● Muzisonyeza kuti ndinu woganiza bwino. Baibulo limati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.” (Agalatiya 6:5) Palibe mtsikana amene angakopeke ndi mnyamata yemwe sachedwa kuchotsedwa ntchito chifukwa choti ndi waulesi kapena chifukwa chakuti amangokhalira kucheza.
Zimene atsikana amanena: “Kuli bwino kuti anyamata azichita zinthu mozindikira chifukwa akapanda kutero atsikana sangawafune.”—Anatero Carrie.
“Anyamata ena alibe zolinga zenizeni. Akamamufuna mtsikana winawake amamufunsa zolinga zake kenako amvekere, ‘Tafanana, ndi zimene nanenso ndikufuna ndidzachite.’ Koma zimene amachita sizigwirizana ndi zonena zawo.”—Anatero Beth.
Zitsanzo zimene zili pamwambazi zikusonyeza kuti kukhala munthu wodalirika komanso woganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi ena. Koma kodi mungatani ngati mukuona kuti ndinu wokonzeka kuyamba chibwenzi ndi mtsikana winawake?
Zinthu Zina Zimene Muyenera Kuchita
● Muuzeni maganizo anu. Ngati mukuona kuti mtsikana amene mumacheza naye angakhale mkazi wabwino, muuzeni kuti mukumufuna. Fotokozani maganizo anu momveka bwino komanso mosazungulira. Ndi zoona kuti zimenezi si zophweka chifukwa mungamaope kuti akukanani. Koma kulimba kwanu mtima kufotokoza maganizo anu ndi umboni wakuti mwakula. Komabe dziwani kuti mukufunsira chibwenzi osati banja. Choncho, muzichita zinthu mwanzeru. Kulankhula mwaulemu kwambiri kapena momangika kukhoza kuchititsa mtsikanayo kukuopani m’malo moti akopeke nanu.
Zimene atsikana amanena: “Sindingadziwe zimene munthu akuganiza ndiye ngati mnyamata akundifuna, kulibwino angondiuza bwinobwino.”—Anatero Nina.
“N’zovuta kuti musinthe n’kuyamba kuonana ngati chibwenzi makamaka ngati mwakhala mukungocheza kwa nthawi yaitali. Komabe ndingakonde ngati mnyamatayo atangondiuza maganizo ake.”—Anatero Helen.
● Muzilemekeza maganizo a mtsikanayo. Kodi mungatani ngati mtsikana yemwe mumacheza naye atakana zoti mukhale naye pa chibwenzi? Mungasonyeze kuti mumamulemekeza ngati mutakhulupirira kuti iyeyo akudziwa zimene zili mumtima mwake ndipo ayi wake akutanthauzadi ayi. Mungasonyeze kuti ndinu munthu wachibwana ngati mutakakamirabe kuti akuloleni. Ndipo ngati mutanyalanyaza zimene iye wanena momveka bwino kuti sakukufunani, mwinanso mpaka kumukwiyira chifukwa chakuti wakukanani, kodi zingasonyeze kuti mumamuganiziradi kapena mumangoganizira zofuna zanu?—1 Akorinto 13:11.
Zimene atsikana amanena: “Zimandikwana kwambiri ndikamukana mnyamata momveka bwino koma iyeyo n’kumakakamirabe.”—Anatero Colleen.
“Mnyamata wina nditamukana ankakakamirabe kuti ndim’patse nambala yanga ya foni. Ndinkafuna kumuyankha mwaulemu pozindikira kuti anasonyeza kulimba mtima kuti akwanitse kundiuza maganizo ake. Koma kenako ndinaona kuti ndikufunika kumuuza mwamphamvu kuti andisiye.”—Anatero Sarah.
Zimene Simuyenera Kuchita
Anyamata ena amaona ngati sizingawavute kufunsira mtsikana kapena kumukopa kuti ayambe kuwafuna. Ndipo nthawi zina amapikisana ndi anzawo kuti aone munthu amene akhoza kukopa atsikana ambiri. Komatu mpikisano wotero si wabwino ndipo ungakuipitsireni mbiri. (Miyambo 20:11) Mukhoza kupewa zimenezi ngati mutatsatira mfundo zotsatirazi.
● Musamakope atsikana. Munthu amene amakopa anzake amalankhula zinthu zachinyengo komanso amagwiritsa ntchito thupi lake m’njira yoti akope anthu ena. Munthu wotere sakhala ndi cholinga chokhala pa chibwenzi cholongosoka. Kuchita zimenezi kumakhala kunyalanyaza mfundo ya m’Baibulo yakuti tiziona ‘akazi achitsikana . . . ngati alongo athu, ndipo pochita zimenezi tisakhale ndi maganizo alionse oipa.’ (1 Timoteyo 5:2) Munthu amene amakopa ena samakhala ndi anzake odalirika komanso banja lake silimayenda bwino. Atsikana anzeru amadziwa zimenezi.
Zimene atsikana amanena: “Ndikukhulupirira kuti palibe mtsikana amene angakopeke ndi mnyamata yemwe wamuuza mawu okopa koma n’kudziwa kuti mnyamatayo ananenanso zomwezo kwa mtsikana wina mwezi watha.”—Anatero Helen.
“Pali mnyamata wina wooneka bwino yemwe anayamba kundiuza mawu okopa ndipo nthawi zambiri ankangodzichemerera. Koma kenako pamene tinalipo panabweranso mtsikana wina ndipo iye anayambanso kunena zomwe zija kwa mtsikanayo. Kenako panabweranso mtsikana wina ndipo anachitanso chimodzimodzi. Zimenezi sizinandisangalatse ngakhale pang’ono.”—Anatero Tina.
● Musamangopusitsa atsikana. Musamaganize kuti mmene mumachezera ndi anyamata n’chimodzimodzi ndi mmene mungachezera ndi mtsikana. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani izi: Ngati mutamuuza mnyamata mnzanu kuti akuoneka bwino ndi suti yatsopano imene wagula kapena ngati mumamuuza zakukhosi kwanu kawirikawiri sangaganize kuti mukumufuna. Koma ngati mutayamikira mtsikana chifukwa cha mmene akuonekera kapena ngati kawirikawiri mumamuuza zakukhosi kwanu, akhoza kuyamba kuganiza kuti mukumufuna.
Zimene atsikana amanena: “Ndikukayikira ngati anyamata amadziwa zoti sangacheze ndi mtsikana mofanana ndi mmene amachezera ndi anyamata anzawo.”—Anatero Sheryl.
“Nthawi zina mnyamata akhoza kupeza nambala yanga kenako n’kunditumizira meseji. Munthu umayamba kudzifunsa kuti cholinga chake ndi chani. Nthawi zina anthu amatha kuyamba kucheza kwambiri chifukwa cha mameseji omwe amatumizirana n’kuyamba kufunana, koma kodi munthu anganene zambiri bwanji pa foni?”—Anatero Mallory.
“Anyamata ambiri sadziwa kuti mtsikana sachedwa kukopeka makamaka ngati mnyamatayo akuoneka kuti amawaganizira komanso ndi wochezeka. Si kuti mtsikanayo amakhala kuti watopa ndi umbeta. Ndikuganiza kuti atsikana ambiri amachita zimenezi chifukwa amafuna atakhala ndi chibwenzi ndipo nthawi zonse amakhala akusakasaka mwamuna woyenerera.”—Anatero Alison.
KUTI MUMVE ZAMBIRI WERENGANI MUTU 3, M’BUKU LACHIWIRI
Kodi chikondi chenicheni mungachidziwe bwanji?
LEMBA
‘Valani umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.’—Aefeso 4:24.
MFUNDO YOTHANDIZA
Funsani munthu wina wachikulire kuti akuuzeni khalidwe lofunika kwambiri limene mnyamata ayenera kukhala nalo. Kenako onani ngati inuyo mukufunika kuyesetsa kukonza mbali imeneyi.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Kukhala ndi makhalidwe abwino n’kofunika kwambiri kuposa maonekedwe anu.
ZOTI NDICHITE
Ndikufunika kukhala waulemu pochita zinthu izi: ․․․․․
Kuti ndizicheza bwino ndi anthu ena ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumadzilemekeza?
● Kodi mukamacheza ndi mtsikana mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza maganizo ake komanso mmene akumvera?
[Mawu Otsindika patsamba 198]
“Anyamata amaganiza kuti atsikana angakopeke nawo ngati amavala mwanjira inayake kapena ngati ali ooneka bwino. Ngakhale kuti atsikana ena akhoza kukopekadi ndi zimenezi, atsikana ambiri amakopeka ndi mnyamata amene ali ndi makhalidwe abwino.”—Anatero Kate
[Chithunzi patsamba 197]
Makhalidwe abwino sali ngati suti imene umangovala kuti anthu ena akugomere kenako n’kukaivula ukafika kunyumba