MUTU 1
Mauthenga Awiri Ochokera kwa Mulungu
MNGELO GABIRIELI ANANENERATU ZA KUBADWA KWA YOHANE M’BATIZI
GABIRIELI ANAUZIRATU MARIYA ZA KUBADWA KWA YESU
Tinganene kuti Baibulo ndi uthenga wochokera kwa Mulungu. Atate wathu wakumwamba anatipatsa bukuli kuti tizipezamo malangizo othandiza. Tsopano tiyeni tione mauthenga awiri apadera amene anaperekedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo. Mngelo Gabirieli, yemwe ‘amaima pamaso pa Mulungu,’ ndi amene anapereka mauthenga amenewa. (Luka 1:19) Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi imene mngeloyu ankapereka mauthenga ofunikawa?
Uthenga woyamba unaperekedwa cha m’ma 3 B.C.E. ndipo unaperekedwa kwa Zekariya yemwe anali wansembe wa Yehova. Zekariya ankakhala ku mapiri a ku Yudeya, mwina chapafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Iye ndi mkazi wake Elizabeti anali okalamba kwambiri ndipo analibe ana. Gabirieli anaonekera kwa Zekariya pa nthawi imene anali ku kachisi wa Mulungu ku Yerusalemu chifukwa inali nthawi yake yoti akatumikire monga wansembe. Ali m’kachisimo, Gabirieli anaonekera mwadzidzidzi ataima pafupi ndi guwa lansembe zofukiza.
Mosakayikira Zekariya ayenera kuti anachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo anamukhazika mtima pansi ndipo anamuuza kuti: “Usachite mantha Zekariya, chifukwa pembedzero lako lamveka ndithu. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera mwana wamwamuna, ndipo udzamutche Yohane.” Gabirieli ananenanso kuti Yohane “adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova” ndipo ‘adzasonkhanitsira Yehova anthu okonzedwa.’—Luka 1:13-17.
Zekariya anaona kuti zimenezi n’zosatheka chifukwa iye ndi mkazi wake anali okalamba kwambiri. Choncho Gabirieli anamuuza kuti: “Udzakhala chete, osatha kulankhula mpaka tsiku limene zimenezi zidzachitike. Izi zidzachitika chifukwa sunakhulupirire mawu anga.”—Luka 1:20.
Pamene zimenezi zinkachitika, anthu omwe anali kunja kwa kachisiyo ankaona kuti Zekariya akuchedwa kutuluka. Kenako Zekariya anatuluka koma atasiya kulankhula ndipo ankagwiritsa ntchito manja polankhula nawo. Anthuwo ataona zimenezi anadziwa kuti waona masomphenya pa nthawi imene anali m’kachisimo.
Zekariya atamaliza kugwira ntchito yake ya pa kachisi anabwerera kwawo. Ndipo pasanapite nthawi yaitali Elizabeti anakhala ndi pakati. Akuyembekezera kubadwa kwa mwanayo, Elizabeti anakhala pakhomo kwa miyezi 5, osaonekera kwa anthu ena.
Kenako Gabirieli anaonekera ulendo wachiwiri. Kodi pa nthawiyi anaonekera kwa ndani? Anaonekera kwa mtsikana wina wosakwatiwa, dzina lake Mariya, yemwe ankakhala m’tauni ya Nazareti, m’chigawo cha Galileya chomwe chinali kumpoto kwa Yerusalemu. Kodi mngeloyo anamuuza chiyani Mariya? Anamuuza kuti: “Mulungu wakukomera mtima.” Anamuuzanso kuti: “Mvetsera! Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Udzam’patse dzina lakuti Yesu.” Anawonjezeranso kuti: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. . . . Adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.”—Luka 1:30-33.
Mungathe kuona kuti Gabirieli anali ndi mwayi waukulu wopereka mauthenga awiriwa. Pamene tikupitiriza kuphunzira zambiri za Yohane komanso Yesu, m’pamenenso tingamvetse chifukwa chake mauthenga ochokera kumwambawa ali ofunika kwambiri.