MUTU 69
Kodi Atate Wawo Anali Abulahamu Kapena Mdyerekezi?
AYUDA ANKANENA KUTI ABULAHAMU ANALI ATATE WAWO
YESU ANALIPO KALE ABULAHAMU ASANAKHALEPO
Yesu anapitirizabe kuphunzitsa anthu mfundo zofunika za choonadi pamene anali ku Chikondwerero cha Misasa (kapena kuti Chikondwerero cha Zokolola) ku Yerusalemu. Ayuda ena omwe analipo pa nthawiyo anali atangouza Yesu kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu ndipo sitinakhalepo akapolo.” Koma Yesu anawayankha kuti: “Ndikudziwa kuti ndinu ana a Abulahamu, koma mukufuna kundipha, chifukwa mawu anga sakukhazikika mwa inu. Zimene ndinaziona kwa Atate wanga ndi zimene ndimalankhula. Chotero inunso mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.”—Yohane 8:33, 37, 38.
Pamenepatu mfundo ya Yesu inali yakuti: Atate ake anali osiyana ndi Atate a Ayudawo. Chifukwa chakuti Ayudawo sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza anabwerezanso kuti: “Atate wathu ndi Abulahamu.” (Yohane 8:39; Yesaya 41:8) N’zoona kuti Ayudawo analidi zidzukulu za Abulahamu ndipo chifukwa cha zimenezi ankaona kuti nawonso anali ndi chikhulupiriro ngati cha Abulahamu, yemwe anali bwenzi la Mulungu.
Komabe zimene Yesu anawayankha zinawadabwitsa kwambiri chifukwa ananena kuti: “Ngati ndinu ana a Abulahamu, chitani ntchito za Abulahamu.” Mfundo imeneyi inali yomveka chifukwa mwana amatengera zochita za bambo ake. Yesu ananenanso kuti: “Koma tsopano mukufuna kundipha ine, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu. Abulahamu sanachite zimenezi.” Kenako zimene Yesu ananena zinawasokoneza kwambiri. Iye anati: “Inu mumachita ntchito za atate wanu.”—Yohane 8:39-41.
Ayudawo sanamvetsebe kuti Yesu ankanena za ndani ponena mawu amenewa. Iwo ankanena kuti sanali ana apathengo chifukwa ananena kuti: “Ife sitinabadwe m’chigololo, tili ndi Atate mmodzi, ndiye Mulungu.” Koma kodi Mulungu analidi Atate wawo? Yesu ananena kuti: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda, pakuti ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.” Kenako Yesu anafunsa funso n’kuliyankhanso yekha. Iye anati: “N’chifukwa chiyani mukulephera kuzindikira zimene ine ndikunena? N’chifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga.”—Yohane 8:41-43.
Yesu anafotokoza mfundo zonsezi pofuna kuthandiza anthuwo kuti amvetse kuopsa kosamukhulupirira. Ndiyeno anawauza mosapita m’mbali kuti: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.” Kenako Yesu anafotokoza momveka bwino kuti Atate wawo anali otani. Ananena kuti: “Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi.” Ndiyeno ananenanso kuti: “Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu. Ndiye chifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa sindinu ochokera kwa Mulungu.”—Yohane 8:44, 47.
Zimene Yesu ananenazi zinakwiyitsa kwambiri Ayudawa ndipo anamuyankha kuti: “Kodi tikamanena kuti, Ndiwe Msamariya ndipo uli ndi chiwanda, tikulakwitsa ngati?” Potchula Yesu kuti “Msamariya,” Ayudawo anasonyeza kuti ankadana naye kwambiri. Koma Yesu sanaganizire kwambiri zinthu zachipongwe zimene ananenazo. Iye anawauza kuti: “Ndilibe chiwanda ine, ndimalemekeza Atate wanga, koma inu mukundinyoza.” Zimene Ayudawa ankachita pokana Yesu inali nkhani yaikulu. Tikutero chifukwa cha mawu amphamvu amene kenako Yesu ananena akuti: “Ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa.” Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza kuti atumwi ake komanso anthu ena amene ankamutsatira sadzafadi? Ayi. Iye ankatanthauza kuti anthuwo sadzafa “imfa yachiwiri.” Anthu amene adzafe imfa yachiwiri ndi amene alibe chiyembekezo chodzaukitsidwa.—Yohane 8:48-51; Chivumbulutso 21:8.
Yesu atanena kuti amene akusunga mawu ake sadzaona imfa, Ayudawo anaganiza kuti Yesu ankatanthauza kuti anthuwo sadzafa moti ananena kuti: “Tsopano tadziwa ndithu kuti uli ndi chiwanda. Abulahamu anamwalira, ndiponso aneneri. Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga sadzalawa imfa.’ Kodi iweyo ndiwe wamkulu kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? . . . Ndiye iweyo ukudziyesa ndani?”—Yohane 8:52, 53.
Pamenepatu n’zoonekeratu kuti Yesu ankanena kuti iyeyo ndi Mesiya. Koma m’malo moyankha kuti iye ndi ndani, Yesu ananena kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza, amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, chikhalirecho simukumudziwa. Koma ine ndikumudziwa. Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza, kufanana ndi inuyo.”—Yohane 8:54, 55.
Kenako Yesu anayamba kufotokoza za Abulahamu, yemwe anali wokhulupirika komanso kholo lawo, kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwera.” Chifukwa chakuti Abulahamu ankakhulupirira zimene Mulungu analonjeza, ankayembekezera kuona Mesiya. Ayudawo sanakhulupirire zimenezi moti anamufunsa kuti: “Zaka 50 zakubadwa sunakwanitse n’komwe, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?” Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.” Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti asanabadwe monga munthu anali mngelo wamphamvu kumwamba.—Yohane 8:56-58.
Yesu atangonena zimenezi, Ayudawo anakwiya kwambiri moti anatola miyala kuti amugende. Koma sanamugende moti Yesu anachokapo ali bwinobwino.