MUTU 4
Mmene Zinthu Zimayendetsedwera mu Mpingo
M’KALATA yoyamba imene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Korinto, anatchula mfundo yofunika kwambiri yokhudza Mulungu yakuti: “Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.” Kenako ponena za mmene misonkhano ya mpingo iyenera kuchitikira, anati: “Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:33, 40.
2 Koyambirira kwa kalata imeneyi mtumwiyu anapereka malangizo okhudza magawano amene anali mu mpingo wa ku Korinto. Paulo anapempha abalewo kuti ‘azilankhula mogwirizana’ komanso kuti akhale ndi “mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akor. 1:10, 11) Kenako anawapatsa malangizo pa nkhani zosiyanasiyana zomwe zikanasokoneza mgwirizano wa mpingo. Poyerekezera ndi mmene thupi la munthu lilili, Paulo anasonyeza kufunika kochita zinthu mogwirizana. Analimbikitsa Akhristu onse, kaya akhale ndi udindo wotani mu mpingo, kuti ayenera kukondana. (1 Akor. 12:12-26) Ngati mpingo uli wogwirizana zimathandiza kuti uzichita zinthu mwadongosolo.
3 Ndiyeno kodi zinthu zinkayenera kuyendetsedwa bwanji mu mpingo wachikhristu? Kodi ndani ankayenera kuuyendetsa? Kodi unkafunika kutsatira dongosolo lotani? Nanga ndani anali oyenera kukhala m’maudindo? Baibulo lingatithandize kupeza mayankho omveka bwino a mafunso amenewa.—1 Akor. 4:6.
UMATSOGOLEREDWA NDI MULUNGU
4 Mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa pa tsiku la Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza mpingo woyambirirawu? Tikuphunzira kuti mpingowu unkayendetsedwa ndi kutsogoleredwa ndi Mulungu. Nkhani ya m’Baibulo yofotokoza zimene zinachitika ku Yerusalemu pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, imasonyeza kuti mpingo wa Akhristu odzozedwa unakhazikitsidwadi ndi Mulungu. (Mac. 2:1-47) Baibulo limasonyeza kuti mpingowo unali nyumba ya Mulungu komanso banja lake. (1 Akor. 3:9; Aef. 2:19) Masiku ano zinthu mu mpingo wachikhristu zimayendetsedwa motsatira mmene mpingo woyambirira unkachitira.
Masiku ano zinthu mu mpingo wachikhristu zimayendetsedwa motsatira mmene mpingo woyambirira unkachitira
5 Mpingo woyambirira unali ndi ophunzira pafupifupi 120. Anthu amenewa anali woyambirira kulandira mzimu woyera pokwaniritsa lemba la Yoweli 2:28, 29. (Mac. 2:16-18) Kenako patsiku lomwelo anthu enanso pafupifupi 3,000 anabatizidwa m’madzi n’kukhala mbali ya mpingo wa obadwa ndi mzimu. Iwo analandira mawu onena za Khristu ndipo “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” Pambuyo pake “Yehova anapitiriza kuwawonjezera anthu amene anali kuwapulumutsa.”—Mac. 2:41, 42, 47.
6 Mpingo wa ku Yerusalemu unakula kwambiri moti mkulu wina wa ansembe wachiyuda anadandaula kuti ophunzirawo anadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chawo. Ophunzira atsopano a ku Yerusalemu, anaphatikizapo anthu ambiri amene poyamba anali ansembe achiyuda.—Mac. 5:27, 28; 6:7.
7 Yesu anati: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Zimenezi zinachitika pamene ophunzira anayamba kuzunzidwa koopsa ku Yerusalemu, Sitefano ataphedwa. Ophunzirawo anabalalikira ku Yudeya ndi ku Samariya. Ndipo kulikonse kumene ankapita anapitiriza kulalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu ambiri kuphatikizapo Asamariya. (Mac. 8:1-13) Patapita nthawi uthenga wabwino unalalikidwa kwa anthu osadulidwa omwe sanali Ayuda. (Mac. 10:1-48) Ntchito yolalikirayi inachititsa kuti pakhale ophunzira ambiri komanso kuti mipingo yatsopano ikhazikitsidwe m’madera ena kunja kwa Yerusalemu.—Mac. 11:19-21; 14:21-23.
8 Kodi panakonzedwa zotani kuti mpingo uliwonse watsopano uzichita zinthu motsogoleredwa ndi Mulungu? Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu panakonzedwa zoti pakhale abusa aang’ono oti azisamalira gulu la nkhosa. Pa ulendo wawo woyamba waumishonale, Paulo ndi Baranaba anaika akulu m’mipingo imene ankachezera. (Mac. 14:23) Wolemba Baibulo Luka anafotokoza za msonkhano umene mtumwi Paulo anachita ndi akulu a mpingo wa ku Efeso. Paulo anauza akuluwo kuti: “Mukhale tcheru ndi kuyang’anira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Mac. 20:17, 28) Akulu amenewa anayenerera kukhala pa udindowu chifukwa anakwaniritsa zimene Malemba amanena kuti n’zofunika kwa munthu amene akufuna kukhala pa udindo. (1 Tim. 3:1-7) Tito yemwe ankagwira ntchito limodzi ndi Paulo anapatsidwa mphamvu yoika akulu m’mipingo ya ku Kerete.—Tito 1:5.
9 Pamene mipingo inkawonjezereka, atumwi ndi akulu a ku Yerusalemu anapitiriza kuyang’anira mpingo wonse wachikhristu womwe unkapezeka m’mayiko ambiri. Atumwi ndi akuluwo ndi amene anali m’bungwe lolamulira.
10 M’kalata imene analembera mpingo wa ku Efeso, mtumwi Paulo anafotokoza kuti mpingo wachikhristu ukamachita zinthu mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu komanso ukamagonjera Yesu Khristu monga Mutu, umakhala wogwirizana. Mtumwiyu analimbikitsa Akhristu amenewa kuti ayenera kukhala odzichepetsa n’cholinga choti ‘asunge umodzi’ pochita zinthu mwamtendere ndi anthu onse mumpingo. (Aef. 4:1-6) Ndiyeno anagwira mawu a pa Salimo 68:18 pofotokoza zimene Yehova anachita pokonza zoti abale oyenerera mwauzimu azitumikira mumpingo monga atumwi, aneneri, alaliki, abusa ndi aphunzitsi. Abalewa anali mphatso zochokera kwa Yehova ndipo ankathandiza mpingo wonse kuti ukhale wolimba mwauzimu komanso kuti uzichita zinthu zokondweretsa Mulungu.—Aef. 4:7-16.
MIPINGO IMATSATIRA ZIMENE MPINGO WOYAMBIRIRA UNKACHITA
11 Masiku ano, mipingo yonse ya Mboni za Yehova imatsatira zimene mpingo woyambirira unkachita. Mipingo yonseyi imapanga gulu limodzi logwirizana padziko lonse, lomwe linayamba ndi kagulu ka Akhristu odzozedwa. (Zek. 8:23) Zimenezi zikutheka chifukwa choti monga mmene Yesu Khristu analonjezera, wakhala ali limodzi ndi Akhristu odzozedwa “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Anthu amene masiku ano akulowa mu mpingo, amamvetsera uthenga wabwino, kudzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse komanso amabatizidwa monga ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19, 20; Maliko 1:14; Mac. 2:41) Iwo amazindikira kuti Yesu Khristu yemwe ndi “m’busa wabwino,” amatsogolera gulu lonse la nkhosa lomwe lapangidwa ndi Akhristu odzozedwa komanso a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:14, 16; Aef. 1:22, 23) “Gulu limodzi” limeneli ndi logwirizana chifukwa limazindikira kuti Khristu ndi Mutu wake ndiponso limagonjera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene Khristuyo anamuika. Choncho tiyenera kupitiriza kukhulupirira kwambiri kapoloyu amene Yesu akumugwiritsa ntchito.—Mat. 24:45.
NTCHITO YA MABUNGWE OSIYANASIYANA A M’GULU LA MULUNGU
12 M’gulu la Mulungu mwakhazikitsidwa mabungwe osiyanasiyana n’cholinga choti athandize kupereka chakudya chauzimu pa nthawi yake komanso kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe mapeto asanafike. Mabungwewa ndi ovomerezeka mogwirizana ndi malamulo a m’mayiko osiyanasiyana ndipo amachita zinthu mogwirizana. Amathandizanso kuti uthenga wabwino uzilalikidwa mosavuta padziko lonse.
NTCHITO ZIMENE MAOFESI A NTHAMBI AMAGWIRA
13 Ofesi ya nthambi ikakhazikitsidwa, pamasankhidwa Komiti ya Nthambi ya akulu atatu kapena kuposerapo kuti aziyang’anira ntchito ya m’dzikolo ndipo nthawi zina amayang’aniranso ntchito ya m’mayiko ena amene akusamaliridwa ndi ofesiyo. M’bale mmodzi m’komitiyi amatumikira monga wogwirizanitsa ntchito za Komiti ya Nthambi.
14 Mipingo imene nthambi iliyonse imayang’anira, imagawidwa kukhala madera. Maderawa amakhala aakulu mosiyanasiyana potengera malo, chinenero komanso chiwerengero cha mipingo imene nthambi imayang’anira. Woyang’anira dera amaikidwa kuti azitumikira mipingo ya m’deralo. Ofesi ya nthambi imapereka malangizo kwa woyang’anira dera okhudza mmene angagwirire ntchito yake.
15 Mipingo imatsatira ndi kuvomereza zimene gulu lakonza, zomwe zimapindulitsa aliyense. Imagonjera akulu osiyanasiyana amene aikidwa kuti ayang’anire ntchito m’maofesi a nthambi, m’madera ndi m’mipingo. Imalandira chakudya chauzimu cha pa nthawi yake chochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Nayenso kapolo wokhulupirika amagonjera Khristu monga Mutu wake, amatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo komanso amatsogoleredwa ndi mzimu woyera. Choncho tonse tikamagwira ntchito limodzi mogwirizana, tidzapezanso madalitso ochuluka ngati mmene mpingo wachikhristu woyambirira unachitira. Ponena za madalitso amene mpingowo unapeza, Baibulo limati: “Mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:5.