MUTU 12
Kuthandiza Ntchito ya Ufumu ya M’dziko Lanu Komanso ya Padziko Lonse
A MBONI ZA YEHOVA akwanitsa kulalikira uthenga wabwino “mpaka kumalekezero a dziko lapansi” pokwaniritsa ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza. (Mac. 1:8; Mat. 24:14) Zimenezi zatheka chifukwa chakuti amadzipereka kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zawo pochita zinthu zauzimu. Iwo amapitiriza kuika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba m’moyo wawo chifukwa amakhulupirira kuti Yehova adzawasamalira. (Mat. 6:25-34; 1 Akor. 3:5-9) Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti Yehova akusangalala ndi utumiki wawo ndiponso akuwadalitsa.
NDALAMA ZOYENDETSERA NTCHITO YA UFUMU PADZIKO LONSE
2 Anthu ena akaona njira zimene timagwiritsa ntchito polalikira komanso akaganizira kuti timagawira anthu Mabaibulo komanso mabuku othandiza pophunzira Baibulo popanda kutchula mtengo wake, amadabwa kuti: “Zimenezi zimatheka bwanji?” N’zoona kuti kusindikiza Mabaibulo ndiponso mabuku athu kumafuna ndalama zambiri. Kumanga ndiponso kusamalira nyumba za Beteli kumene kumakhala anthu amene amagwira ntchito yosindikiza mabuku, kuyang’anira ntchito yolalikira, komanso kugwira ntchito zosiyanasiyana zopititsa patsogolo ntchito yolalikira uthenga wabwino kumafunanso ndalama. Kuwonjezera pamenepa, oyang’anira madera, amishonale, apainiya apadera ndiponso anthu ena amene ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera, amapatsidwa ndalama pang’ono komanso thandizo lina kuti apitirize utumiki wawo. Choncho ntchito yolalikira uthenga wabwino yomwe ikuchitika m’dziko lanu komanso padziko lonse, imafuna ndalama zambiri. Ndiye kodi ndalamazi zimachokera kuti?
3 Anthu ambiri amene amayamikira ntchito ya Mboni za Yehova amapereka mwakufuna kwawo ndalama zothandizira pa ntchito yapadziko lonse. Komabe ndalama zambiri zoyendetsera ntchito yathu zimaperekedwa ndi a Mboni omwe amatumiza zopereka zawo ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo. Iwo amakhala ndi mtima wofanana ndi womwe atumiki a Mulungu akale anali nawo omwe anapereka zinthu mowolowa manja pothandizira ntchito yomanga malo olambirira Yehova. (Eks. 35:20-29; 1 Mbiri 29:9) Anthu ena amaneneratu kuti katundu wawo adzaperekedwe ku ofesi ya nthambi iwowo akadzamwalira. Ndalama zina zochepa zimaperekedwa ndi anthu, mipingo ndiponso madera. Zinthu zonsezi zikaphatikizidwa zimathandiza poyendetsera ntchito ya Ufumu.
A Mboni za Yehova amaona kuti ndi mwayi wawo kugwiritsa ntchito ndalama zawo ndiponso zinthu zina pothandizira ntchito yolalikira
4 A Mboni za Yehova amaona kuti ndi mwayi wawo kugwiritsa ntchito ndalama zawo ndiponso zinthu zina pothandizira ntchito yolalikira. Yesu ndi ophunzira ake anali ndi bokosi la ndalama zomwe ankalipirira zinthu zofunika. (Yoh. 13:29) Baibulo limanenanso za azimayi amene ankatumikira Yesu ndi ophunzira ake. (Maliko 15:40, 41; Luka 8:3) Mtumwi Paulo ankayamikira mphatso zimene ankalandira kuchokera kwa anthu amene ankafuna kumuthandiza pa utumiki wake. (Afil. 4:14-16; 1 Ates. 2:9) A Mboni za Yehova masiku ano amatsatira chitsanzo cha anthu amenewa omwe ankachita utumiki wawo mwakhama komanso kupereka zinthu zawo mowolowa manja. Zimenezi zimathandiza kuti anthu oona mtima a padziko lonse athe kupatsidwa “madzi a moyo kwaulere.”—Chiv. 22:17.
KULIPIRA ZINTHU ZOFUNIKA PA MPINGO
5 Ndalama zogwiritsa ntchito pa mpingo zimakhalanso zoti anthu apereka mwa kufuna kwawo. Pa misonkhano yawo sipamayendetsedwa mbale ya zopereka, samatchula ndalama yoti aliyense apereke komanso samapemphetsa ndalama. Amaika mabokosi a zopereka pamalo awo a misonkhano kuti aliyense amene akufuna apereke “mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake.”—2 Akor. 9:7.
6 Ndalama zimene zapezeka, choyamba zimagwiritsidwa ntchito polipirira zinthu zofunikira pa nthawi ya misonkhano komanso posamalira Nyumba ya Ufumuyo. Bungwe la akulu likhoza kuona kuti ndi bwino kuti ndalama zina zitumizidwe ku ofesi ya nthambi ya m’dzikolo n’cholinga choti zithandize pa ntchito ya padziko lonse. Mpingo umayenera uvomereze kaye asanatumize ndalamazo. Mipingo yambiri imathandizira ntchito ya padziko lonse m’njira imeneyi ndipo imachita zimenezi nthawi ndi nthawi. Ngati anthu onse mumpingo akudziwa zinthu zimene zikufunikira ndalama, sizingakhale zoyenera kulengeza mobwerezabwereza kuti pakufunika zopereka.
KUSAMALIRA ZOPEREKA
7 Pambuyo pa misonkhano, abale awiri amachotsa ndalama zonse m’mabokosi a zopereka n’kulemba kuti ndi zingati. (2 Maf. 12:9, 10; 2 Akor. 8:20) Bungwe la akulu limaonetsetsa kuti ndalamazo zasungidwa bwino mpaka pamene zidzatumizidwe ku ofesi ya nthambi kapena kugwiritsidwa ntchito ndi mpingo. Mwezi uliwonse m’bale amene amasamalira ndalama za mpingo amalemba sitetimenti kuti mpingo udziwe mmene ndalama zagwirira ntchito ndipo miyezi itatu iliyonse wogwirizanitsa ntchito za akulu amakonza zoti iyeyo kapena mkulu wina awerengere mmene ndalama zagwiritsidwira ntchito.
NDALAMA ZIMENE DERA LIMALIPIRIRA ZINTHU
8 Ndalama zolipirira zofunika pa msonkhano wadera komanso zinthu zina, zimachokera kwa Mboni za Yehova za m’deralo. Pa misonkhanoyi pamakhala mabokosi a zopereka. Zimenezi zimapereka mwayi kwa anthu woti apereke ndalama zothandiza deralo. Komanso pa nthawi ina, mipingo imatha kupereka ndalama zolipirira zinthu zina.
9 Nthawi zambiri dera lingathe kulipira zinthu zonse zofunika n’kutsalanso ndi ndalama zopereka pothandiza ntchito yapadziko lonse. Koma ngati ku akaunti ya dera kulibe ndalama zokwanira kulipirira zinthu zofunika pa msonkhanowo kapena zokonzekerera msonkhano wotsatira, monga zolipirira malo odzachitira msonkhano, woyang’anira dera angauze akulu kuti adziwitse mipingo kuti pakufunikira ndalama. Bungwe la akulu la mpingo uliwonse lidzakambirana nkhaniyo n’kuona kuti mpingo wawo ungakwanitse kupereka ndalama zingati ku akaunti ya dera. Mpingo uyenera kuvomereza kaye ndalama zimene agwirizanazo.
10 Ngati pali vuto la ndalama limene akulu a m’deralo akufunika kudziwa, pa tsiku la msonkhano wadera payenera kuchitika msonkhano wa akulu a m’deralo wowadziwitsa za nkhaniyo. Akulu ayenera kuvomereza kaye nthawi iliyonse imene ndalama zadera zikugwiritsidwa ntchito, kupatulapo ngati zikugwiritsidwa ntchito polipirira zinthu zimene zimafunika nthawi zonse pa nthawi ya msonkhano. Ndalama zimenezi ziyenera kulembedwa bwinobwino n’kufunsa akulu kuti avomereze kaye zisanagwiritsidwe ntchito.
11 Pamakhala dongosolo loti pazikhala kuwerengetsera ndalama za dera pakatha nthawi inayake.
KUSAMALIRA OSAUKA
12 Ntchito ina ya bokosi la ndalama limene Yesu ndi ophunzira ake anali nalo inali kuthandizira osauka. (Maliko 14:3-5; Yoh. 13:29) Mpaka pano Akhristu ali ndi udindo umenewu chifukwa Yesu ananena kuti: “Osaukawo muli nawo nthawi zonse.” (Maliko 14:7) Kodi Mboni za Yehova masiku ano zimakwaniritsa bwanji udindo umenewu?
13 Nthawi zina, Akhristu ena mu mpingo angafunikire thandizo chifukwa cha ukalamba, matenda kapena mavuto ena omwe sangathane nawo okha. Achibale awo kapena anthu ena omwe adziwa za vutolo, angayesetse kuwathandiza. Zimenezi n’zogwirizana ndi zomwe mtumwi Yohane ananena kuti: “Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo, n’kuona m’bale wake zikumusowa, koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu? Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.” (1 Yoh. 3:17, 18; 2 Ates. 3:6-12) Kulambira koona kumaphatikizapo kusamalira anthu okhulupirika amene akufunikira thandizo.—Yak. 1:27; 2:14-17.
14 M’kalata yoyamba imene mtumwi Paulo analembera Timoteyo, anafotokoza mmene Akhristu angaperekere thandizo kwa anthu oyenera kuthandizidwa. Mungawerenge malangizo amenewa pa 1 Timoteyo 5:3-21. Udindo waukulu umapita kwa munthu aliyense wa m’banjalo. Akhristu okalamba kapena amene akudwala, ayenera kuthandizidwa ndi ana awo, zidzukulu kapena achibale awo. Nthawi zina boma komanso mabungwe amatha kuthandiza anthu oterewa, choncho achibale kapena anthu ena angathandize anthuwo kuti azilandira nawo thandizolo. Nthawi zina mpingo ungafunikire kuthandiza abale ndi alongo ena ofunika thandizo amene atumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. Ngati palibe ana kapena achibale amene angawathandize komanso ngati thandizo limene boma kapena mabungwe akupereka n’losakwanira, bungwe la akulu lingakambirane n’kuona zimene mpingo ungachite pothandiza anthuwo. Akhristu amaona kuti ndi mwayi wawo kugawana zinthu zimene ali nazo ndi anthu amene akufunika thandizo.
15 Abale ndi alongo ambiri amafunika thandizo chifukwa cha kuzunzidwa, nkhondo, zivomerezi, kusefukira kwa madzi, njala kapena mavuto ena amene akuchitika m’masiku otsiriza ovuta ano. (Mat. 24:7-9) Nthawi zambiri abale ndi alongo a m’mipingo ya m’deralo amakhala kuti alibe chilichonse choti angathandizire ena, choncho Bungwe Lolamulira limadziwitsa abale a m’madera ena komanso limatsogolera ntchito yopereka thandizo loyenerera. Njira imeneyi ikufanana ndi yomwe Akhristu a ku Asia Minor anagwiritsa ntchito potumiza chakudya kwa abale awo a ku Yudeya pa nthawi ya njala. (1 Akor. 16:1-4; 2 Akor. 9:1-5) Tikamatsatira chitsanzo chawo, timasonyeza kuti timakondadi abale athu komanso kuti ndife otsatira enieni a Yesu Khristu.—Yoh. 13:35.
KAGAWIDWE KA MABUKU
16 Baibulo komanso mabuku othandiza pophunzira Baibulo amathandiza kwambiri polengeza uthenga wa Ufumu. Nthawi zambiri bungwe la akulu limasankha mtumiki wothandiza kuti azisamalira mabuku amene mpingo umalandira. Abale amene amapatsidwa ntchito zimenezi samaona udindo wawo mopepuka. Amayesetsa kulemba chiwerengero cha mabuku amene alandira komanso amene akufunika, n’cholinga choti mpingo uzikhala ndi mabuku okwanira nthawi zonse.
17 Monga Akhristu odzipereka kwa Mulungu, timazindikira kuti nthawi yathu, luso lathu, chuma chathu, ngakhalenso moyo umene tili nawowu ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo watipatsa zonsezi n’cholinga choti tizigwiritse ntchito pomutumikira. (Luka 17:10; 1 Akor. 4:7) Tikamagwiritsa ntchito mwanzeru zinthu zimene tili nazo, timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Tiyenera kuyesetsa kulemekeza Yehova ndi zinthu za mtengo wapatali zimene tili nazo, podziwa kuti iye amasangalala ndi mphatso iliyonse imene timapereka ndi mtima wathu wonse. (Miy. 3:9; Maliko 14:3-9; Luka 21:1-4; Akol. 3:23, 24) Yesu ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mat. 10:8) Tikamadzipereka potumikira Yehova n’kumagwiritsanso ntchito zimene tili nazo pochita zimenezi, timakhala osangalala kwambiri.—Mac. 20:35.