MUTU 1
Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Mulungu?
1, 2. Kodi nthawi zambiri anthu amakhala ndi mafunso okhudza chiyani?
ANA amakonda kufunsa mafunso. Mukhoza kuwafotokozera zinthu koma nthawi zambiri amafunsa kuti, ‘Chifukwa?’ Ndipo mukayesetsa kuyankha funsolo mwina angakufunseninso kuti, ‘Chifukwa chiyani?’
2 Kaya ndife ana kapena akuluakulu, tonsefe timafunsa mafunso. Timafunsa zokhudza zinthu zimene tikufuna kudya, kuvala kapena kugula. Nthawi zinanso timafunsa mafunso ofunika okhudza moyo komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Koma ngati sitikupeza mayankho ogwira mtima pa mafunso amenewa, mwina tingasiye kufunafuna mayankho.
3. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti sangapeze mayankho a mafunso ofunika omwe amakhala nawo?
3 Kodi m’Baibulo muli mayankho a mafunso ofunika amene timafunsa? Inde, koma anthu ena amaona kuti Baibulo ndi lovuta kulimvetsa. Iwo amaona kuti amene angayankhe mafunso awo ndi atsogoleri achipembedzo. Ndipo ena amachita manyazi kuti akafunsa aoneka ngati otsalira. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
4, 5. Kodi ndi mafunso ofunika ati amene mungafunse? Nanga n’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kufufuza mayankho ake?
4 Muyenera kuti mumafuna kupeza mayankho a mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani ndili ndi moyo? Kodi chidzandichitikire n’chiyani ndikadzamwalira? Kodi Mulungu ali ndi makhalidwe otani? Yesu, yemwe ndi Mphunzitsi wotchuka, anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Mateyu 7:7) Choncho musasiye kufufuza mpaka mutapeza mayankho ogwira mtima.
5 Lemba la Mateyu 7:7 likusonyeza kuti Baibulo lili ndi mayankho ndipo mukhoza kuwapeza ngati ‘mutapitiriza kufunafuna.’ (Miyambo 2:1-5) Mayankho a m’Baibulo amakhala osavuta. Zimene mukuphunzira m’Baibulo zingakuthandizeni kukhala wosangalala panopo komanso kudzapeza moyo wosatha m’tsogolo. Tiyeni tikambirane funso limene limasokoneza maganizo anthu ambiri.
KODI MULUNGU AMATIGANIZIRA KAPENA NDI WOPANDA CHISONI?
6. N’chiyani chimachititsa anthu ambiri kuganiza kuti Mulungu sawaganizira?
6 Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu satiganizira. Iwo amati akanakhala kuti Mulungu amatiganizira zinthu sizikanakhala mmene zililimu. Zinthu monga nkhondo, chidani komanso mavuto osiyanasiyana zili ponseponse. Anthufe timadwala, timavutika ndiponso timafa. Anthu ambiri amadabwa kuti, ‘Ngati Mulungu amatiganizira, n’chifukwa chiyani saletsa zinthu zoipa kuti zisamachitike?’
7. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo amachititsa bwanji anthu kuganiza kuti Mulungu sawaganizira? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti si Mulungu amene amachititsa zinthu zoipa zimene zimatichitikira?
7 Nthawi zina atsogoleri achipembedzo ndi amene amachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu sawaganizira. Mwachitsanzo, anthu akakumana ndi mavuto enaake, amati ndi chifuniro cha Mulungu. Iwo amanena kuti ndi zimene Mulungu wakonza kuti zichitike. Akamanena zimenezi amakhala akumuimba mlandu Mulungu kuti ndi amene amachititsa mavuto. Koma Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. Lemba la Yakobo 1:13 limafotokoza kuti Mulungu sangayese munthu ndi zinthu zoipa. Lembali limati: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Zimenezi zikusonyeza kuti ngakhale kuti Mulungu saletsa zinthu zoipa kuti zisamachitike, iye si amene amazichititsa. (Werengani Yobu 34:10-12.) Tiyeni tione chitsanzo.
8, 9. N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwa kuimba Mulungu mlandu chifukwa cha mavuto athu? Perekani chitsanzo.
8 Taganizirani za mnyamata amene akukhala ndi makolo ake. Bambo ake amamukonda kwambiri ndipo anamuphunzitsa mmene angasankhire bwino zochita. Kenako mnyamata uja akuyamba kuchita zinthu zosamvera bambo ake ndipo akusankha kuchoka pakhomo. Akuyamba kuchita makhalidwe oipa kenako akukumana ndi mavuto. Kodi tinganene kuti bambo akewo ndi amene achititsa mavutowo chifukwa choti anamulola kuchoka pakhomo? Ayi. (Luka 15:11-13) Mofanana ndi bambo ameneyu, Mulungu saletsa anthu akasankha kuchita zinthu zosamumvera komanso akamachita zoipa. Choncho munthu akakumana ndi mavuto, ayenera kukumbukira kuti si Mulungu amene wachititsa mavutowo. Kungakhale kulakwa kumuimba mlandu Mulungu kuti ndi amene amachititsa mavuto.
9 Mulungu ali ndi chifukwa chomveka chimene walolera kuti zinthu zoipa zizichitikabe mpaka pano. M’Mutu 11 mudzaphunzira zambiri zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. Koma muyenera kudziwa kuti Mulungu amatikonda ndipo si amene amachititsa mavuto amene timakumana nawo. M’malomwake, iye ndi amene amatithandiza tikakumana ndi mavuto.—Yesaya 33:2.
10. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Mulungu adzakonza zinthu zonse zimene zawonongedwa ndi anthu oipa?
10 Mulungu ndi woyera. (Yesaya 6:3) Tingathe kumukhulupirira chifukwa zilizonse zimene amachita zimakhala zoyera komanso zabwino. Koma anthu sitingawakhulupirire choncho chifukwa nthawi zina amachita zinthu zoipa. Ngakhale atsogoleri amene amayesetsa kuchita zinthu moona mtima sakhala ndi mphamvu zoti n’kukonza zinthu zonse zomwe zawonongedwa ndi anthu oipa. Palibe munthu amene ali ndi mphamvu ngati za Mulungu. Iye ndi amene angakonze zinthu zonse zimene zinawonongeka ndipo adzachotsa anthu onse amene amachita zoipa.—Werengani Salimo 37:9-11.
KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI AKAONA ANTHU AKUVUTIKA?
11. Kodi Mulungu amamva bwanji inuyo mukamavutika?
11 Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli komanso mavuto omwe inuyo mukukumana nawo? Baibulo limanena kuti Mulungu “amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) Choncho iye amakhudzidwa ndi zinthu zabwino kapena zoipa zimene anthu amachita. Zimenezi zikusonyeza kuti iye amadana ndi zoti anthu azivutika. Baibulo limafotokoza kuti nthawi ina m’mbuyomu Mulungu “zinam’pweteka kwambiri mumtima” ataona kuti dziko lapansi ladzaza ndi anthu ochita zoipa. (Genesis 6:5, 6) Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Baibulo limanena kuti Mulungu amatidera nkhawa.—Werengani 1 Petulo 5:7.
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani timatha kukonda anthu ena, nanga timamva bwanji tikaona mavuto omwe ali m’dzikoli? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Mulungu adzathetsa mavuto ndi zinthu zonse zopanda chilungamo?
12 Baibulo limanenanso kuti Mulungu anatilenga m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu anatilenga ndi makhalidwe abwino ofanana ndi amene iyeyo ali nawo. Choncho ngati inuyo zimakukhudzani mukaona anthu osalakwa akuvutika, dziwani kuti Mulungu ndi amene zimam’khudza kwambiri. Kodi timadziwa bwanji zimenezi?
13 Baibulo limatiphunzitsa kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Chilichonse chimene amachita, amachita chifukwa cha chikondi. Choncho timakonda ena chifukwa tinatengera khalidwe lake la chikondi. Taganizirani izi: Mukanakhala kuti muli ndi mphamvu, kodi mukanathetsa mavuto ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika m’dzikoli? Tikukhulupirira kuti mukanatero chifukwa mumakonda anthu. Ndiye kuli bwanji Mulungu? Iye ali ndi mphamvu komanso amatikonda, choncho adzathetsa mavuto ndi zinthu zonse zopanda chilungamo. Simuyenera kukayikira kuti malonjezo onse a Mulungu amene ali kumayambiriro kwa bukuli adzakwaniritsidwa. Koma kuti tizikhulupirira malonjezo amenewa tiyenera kudziwa zambiri zokhudza Mulungu.
MULUNGU AMAFUNA KUTI MUMUDZIWE
14. Kodi dzina la Mulungu ndi ndani, ndipo tikudziwa bwanji zoti amafuna kuti tiziligwiritsa ntchito?
14 Kodi mumatani mukafuna kuti munthu wina akudziweni? Choyamba mumamuuza dzina lanu. Kodi Mulungu ali ndi dzina? Zipembedzo zambiri zimanena kuti dzina lake ndi Mulungu kapena Ambuye, komatu amenewa si mayina ake enieni. Angokhala mayina audindo ngati mmene zilili ndi dzina lakuti “mfumu” kapena “pulezidenti.” Mulungu amatiuza kuti dzina lake ndi Yehova. Lemba la Salimo 83:18 limati: “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Anthu amene analemba Baibulo anagwiritsa ntchito dzina la Mulungu kambirimbiri. Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake ndipo muziligwiritsa ntchito. Iye amakuuzani dzina lake n’cholinga choti akhale mnzanu.
15. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani?
15 Dzina la Mulungu lakuti Yehova, lili ndi tanthauzo lofunika kwambiri. Dzinali limatanthauza kuti Mulungu akhoza kukwaniritsa lonjezo lililonse komanso akhoza kukwaniritsa cholinga chilichonse chomwe angakhale nacho ndipo palibe chimene chingamulepheretse kuchita zimenezi. Choncho ndi Yehova yekha amene ayenera kukhala ndi dzina limeneli.a
16, 17. Kodi mayina audindo otsatirawa amatanthauza chiyani: (a) “Wamphamvuyonse”? (b) “Mfumu yamuyaya”? (c) “Mlengi”?
16 Monga mmene taonera m’ndime zapitazi, pofotokoza za Yehova, lemba la Salimo 83:18 limati: “Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba.” Komanso lemba la Chivumbulutso 15:3 limati: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya.” Kodi dzina laudindo lakuti “Wamphamvuyonse” limatanthauza chiyani? Limatanthauza kuti Yehova ali ndi mphamvu kuposa wina aliyense. Dzina laudindo lakuti “Mfumu yamuyaya” limatanthauza kuti Yehova alibe chiyambi komanso adzakhalapo mpaka kalekale. Lemba la Salimo 90:2 limafotokoza kuti iye ndi Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale. Zimenezitu n’zochititsa chidwi kwambiri.
17 Yehova yekha ndi amene ali Mlengi. Lemba la Chivumbulutso 4:11 limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Choncho Yehova ndi amene analenga zinthu zonse kuyambira angelo akumwamba, nyenyezi, zipatso komanso nsomba za m’nyanja.
YEHOVA AKHOZA KUKHALA MNZANU
18. N’chifukwa chiyani anthu ena amaganiza kuti sangakhale pa ubwenzi ndi Mulungu? Nanga Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?
18 Anthu ena akadziwa za makhalidwe odabwitsa a Yehova, amachita mantha ndipo amayamba kuganiza kuti, ‘Popeza Mulungu ndi wamphamvu zonse, wapamwamba kwambiri komanso amakhala kutali, kodi n’zotheka kuti azindiganizira?’ Koma kodi Mulungu amafuna kuti tizimuona choncho? Ayi. Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Baibulo limanena kuti Mulungu “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Choncho Mulungu amafuna kuti muzimuyandikira ndipo akulonjeza kuti “iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
19. (a) Kodi mungatani kuti Mulungu akhale mnzanu? (b) Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu omwe amakusangalatsani kwambiri?
19 Kodi mungatani kuti Mulungu akhale mnzanu? Yesu ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Choncho pitirizani kuphunzira Baibulo ndipo mudzadziwa za Yehova komanso Yesu. Mukatero mukhoza kudzapeza moyo wosatha. Mwachitsanzo, taphunzira kale kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:16) Komatu Mulungu ali ndi makhalidwe enanso abwino. Baibulo limanena kuti Yehova ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Ekisodo 34:6) Yehova ndi ‘wabwino ndipo ndi wokonzeka kukhululuka.’ (Salimo 86:5) Komanso Mulungu ndi woleza mtima ndiponso wokhulupirika. (2 Petulo 3:9; Chivumbulutso 15:4) Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadziwa zambiri zokhudza makhalidwe abwino amene Mulungu ali nawo.
20, 21. Kodi zingatheke bwanji kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe sitimuona?
20 Kodi n’zotheka kumuyandikira Mulungu ngakhale kuti sitingathe kumuona? (Yohane 1:18; 4:24; 1 Timoteyo 1:17) Mukamaphunzira za Yehova m’Baibulo mudzadziwa kuti iye ndi weniweni. (Salimo 27:4; Aroma 1:20) Mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, mudzayamba kumukonda kwambiri ndipo adzakhala mnzanu wapamtima.
21 Mudzamvetsa chifukwa chake timaona Yehova monga Atate wathu. (Mateyu 6:9) Iye anatipatsa moyo ndipotu amafuna kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. Izi n’zofanana ndi zimene bambo wachikondi angafunire ana ake. (Salimo 36:9) Baibulo limatiphunzitsa kuti n’zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Yakobo 2:23) N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova, yemwe analenga zinthu zonse, akufuna kuti mukhale mnzake.
22. Kodi mungatani ngati anthu ena atakuuzani kuti musiye kuphunzira Baibulo?
22 Anthu ena angafune kukuletsani kuphunzira Baibulo. Iwo angachite zimenezi chifukwa choopa kuti musiya chipembedzo chanu. Koma musalole kuti wina aliyense akulepheretseni kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa iye ndi mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense.
23, 24. (a) N’chifukwa chiyani simuyenera kusiya kufunsa mafunso? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu wotsatira?
23 Pamene mukuphunzira Baibulo, mudzapeza kuti zinthu zina ndi zovuta kuzimvetsa. Choncho musamachite manyazi kufunsa mafunso. Yesu ananena kuti tiyenera kukhala odzichepetsa ngati ana. (Mateyu 18:2-4) Ndipotu ana amafunsa mafunso ambiri. Mulungu amafuna kuti mupeze mayankho a mafunso anu. Choncho pamene mukuphunzira Baibulo, yesetsani kufufuza kuti mutsimikizire kuti zimene mukuphunzirazo ndi zoona.—Werengani Machitidwe 17:11.
24 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Yehova muyenera kuphunzira Baibulo. Mutu wotsatira utithandiza kudziwa kusiyana kumene kulipo pakati pa Baibulo ndi mabuku ena onse.
a Ngati m’Baibulo lanu mulibe dzina lakuti Yehova ndipo mukufuna kudziwa zambiri ponena za tanthauzo la dzinali komanso katchulidwe kake, onani Mawu Akumapeto 1.