MUTU 11
Abulahamu Anasonyeza Kuti Anali Wokhulupirika
Abulahamu anaphunzitsa mwana wake Isaki kuti azikonda Yehova komanso kukhulupirira malonjezo ake onse. Koma Isaki ali ndi zaka pafupifupi 25, Yehova anapempha Abulahamu kuti achite zinthu zovuta kwambiri. Kodi anamuuza kuti achite chiyani?
Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupereke nsembe kuphiri la Moriya.’ Abulahamu sankadziwa chifukwa chake Yehova anamuuza kuti achite zimenezi, komabe iye anamvera.
M’mawa wa tsiku lotsatira, anatenga Isaki komanso antchito ake awiri n’kuyamba ulendo wopita kuphiri la Moriya. Atayenda kwa masiku atatu, anayamba kuona phirilo chapatali. Abulahamu anauza antchito ake aja kuti adikire penapake, pamene iye ndi Isaki akukapereka nsembe. Abulahamu anapatsa Isaki nkhuni kuti anyamule ndipo iye anatenga mpeni. Koma Isaki anafunsa bambo akewo kuti: ‘Nanga nkhosa yokapereka nsembeyo ili kuti?’ Abulahamu anayankha kuti: ‘Mwana wanga, Yehova apereka nkhosa yoti tipereke nsembe.’
Atafika paphiripo, anamanga guwa loti aperekerepo nsembe. Ndiyeno Abulahamu anamanga Isaki manja ndi miyendo n’kumugoneka paguwapo.
Kenako anatenga mpeni kuti amuphe. Koma nthawi yomweyo, anamva mngelo wa Yehova akufuula kuti: ‘Abulahamu, usamuvulaze mwanayo. Tsopano ndadziwa kuti umakhulupirira Mulungu chifukwa umafuna kupereka nsembe mwana wako.’ Zitatero, Abulahamu anaona nkhosa itakodwa m’ziyangoyango, chapafupi. Mwamsanga anamasula Isaki ndipo anatenga nkhosayo n’kuipereka nsembe.
Kuyambira tsiku limenelo, Yehova anayamba kutchula Abulahamu kuti mnzake. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Ndi chifukwa choti Abulahamu ankachita zilizonse zimene Yehova ankafuna ngakhale zitakhala kuti sakuzimvetsa.
Yehova anabwerezanso lonjezo limene anamuuza Abulahamu kuti: ‘Ndidzakudalitsa komanso ndidzachulukitsa ana ako kapena kuti mbadwa zako.’ Apa Yehova ankatanthauza kuti adzadalitsa anthu onse abwino kudzera m’banja la Abulahamu.
“Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16