MUTU 80
Yesu Anasankha Atumwi 12
Yesu atalalikira pafupifupi kwa chaka ndi hafu, ankafunika kusankha zinthu zina zofunika kwambiri. Anafunika kusankha anthu apadera oti azigwira nawo ntchito yolalikira. Anthuwa anafunikanso kuwaphunzitsa kuti adzathe kutsogolera mpingo wa Chikhristu iye akadzapita kumwamba. Yesu anaona kuti m’pofunika kuti Yehova amutsogolere posankha anthuwo. Choncho anapita kuphiri kwayekhayekha ndipo anapemphera usiku wonse. Kutacha, anaitana ophunzira ake ena ndipo anasankhapo anthu 12 oti akhale atumwi. Kodi ukukumbukira mayina awo? Anali Petulo, Andireya, Yakobo, Yohane, Filipo, Batolomeyo, Tomasi, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni ndi Yudasi Isikariyoti.
Atumwi 12 amenewa ankayenda ndi Yesu. Kenako atawaphunzitsa, anayamba kumapita okha. Yehova anawapatsa mphamvu kuti azitha kutulutsa ziwanda komanso kuchiritsa odwala.
Yesu ankaona kuti atumwi 12 amenewa ndi anzake ndipo ankawakhulupirira. Koma Afarisi ankaganiza kuti atumwiwo anali osaphunzira komanso anthu wamba. Komatu Yesu anawaphunzitsa kuti azigwira bwino ntchito yawo. Atumwiwo anakhalabe ndi Yesu pa nthawi yofunika kwambiri pa moyo wake. Mwachitsanzo, analipo Yesu atatsala pang’ono kuphedwa komanso ataukitsidwa. Mofanana ndi Yesu ambiri mwa atumwiwa anali ochokera ku Galileya. Ndipo ena anali okwatira.
Koma atumwiwa sanali angwiro ngati ife tomwe ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Pena ankalankhula asanaganize ndiponso ankasankha molakwika. Nthawi zinanso sankaleza mtima komanso ankakangana kuti wamkulu ndi ndani. Komabe atumwiwa anali anthu abwino ndipo ankakonda Yehova. Iwo ndi amene anali anthu oyamba kukhala mumpingo wa Chikhristu Yesu atapita kumwamba.
“Ndakutchulani kuti anzanga, chifukwa ndakudziwitsani zinthu zonse zimene ndamva kwa Atate wanga.”—Yohane 15:15