NYIMBO 113
Yehova Amatipatsa Mtendere
Losindikizidwa
1. Tamandani
Yehova wamtendereyo.
Wapatsa Yesu mphamvu
zothetsa nkhondo.
Adzakonzadi zinthu
mwachilungamo.
Mtendere udzakhala
padziko lonse.
2. Tasiya kulankhula
zokhumudwitsa.
Malupanga, mikondo,
zonse tataya.
Timasunga mtendere
pokhululuka
Monga nkhosa za
Yesu zamtenderedi.
3. Mtendere ndi
umboni wa madalitso.
Tasunga malamulo a
M’lungu wathu.
Timakonda mtendere.
Tiusonyeze
Mpaka m’Paradaiso
wamtendereyo.
(Onaninso Sal. 46:9; Yes. 2:4; Yak. 3:17, 18.)