Mfundo Zazikulu Zabaibulo Masalmo 107 mpaka 150
Mulungu Wachimwemwe, Anthu Achimwemwe!
Chimwemwe ndi chonulirapo chimene anthu ambiri satha kuchipeza. Kwa kagulu kochepa ka ena, ngakhale kuli tero, chimwemwe ndi njira yawo ya moyo. Mfungulo yawo ku icho? Kulambira kowona! Masalmo amatitsimikizira ife kuti Yehova ali Mulungu wachimwemwe, ndipo chotero tingakhale achimwemwe mwa kumlambira iye. Kuti titsimikizire chimenechi, tiyeni tiyang’ane pa Bukhu la Chisanu la Masalmo, limenelo liri, Masalmo 107 mpaka 150.
Yehova Mpulumutsi
Chonde werengani Masalmo 107 mpaka 119. Pemphero la Ayuda kaamba ka kupulumutsidwa kuchokera ku ukapolo ku Babulo layankhidwa, ndipo “wowomboledwa wa Yehova“ anasunga kubwerera mwa nyimbo. (Masalmo 107) Chifukwa cha kupulumutsidwa mwamsanga, Davide ’anapanga nyimbo’ kwa Mulungu ndikubukitsa ubwino Wake ndi chikondi. (Masalmo 108, 109) Ndi mphamvu yochokera kwa Yehova, Mbuye wa Davide, amenerali Yesu Kristu, anayenera kugonjetsa adani a Mulungu. (Masalmo 110) Kuwonjezera ku kupulumutsa anthu Ake, Yehova akudalitsa munthu wowongoka mtima womuopa iye. (Masalmo 111, 112) Pambuyo pa chipulumutso chawo kuchokera ku Babulo, Ayuda anaimba Masalmo a Haleluya, kapena nyimbo za chitamando, ku maphwando awo a chaka ndi chaka. (Masalmo 113-118) SaImo la 119 liri lalitali kuposa onse, ndipo onse kuchotsapo 2 amaversi ake 176 amaloza ku mawu kapena lamulo la Mulungu.
◆ 107:27—Ndimotani mmene ‘nzeru yawo inatsimikizira kukhala yosokonezeka’?
Monga amarinyero ogwidwa munamondwe wosakaza, nzeru ya Ayuda inatsimikizira kukhala yachabe m’mkhalidwe wawo wa ndende mu Babulo; zoyeseyesa zonse za umunthu za kupulumutsa iwo zinalephereka. Koma mwakutembenukira kwa Yehova pakati pa mkhalidwe wonga namonqiwe umenewu, chipulumutso chinafika. lye anapangitsa namondwe wophiphiritsira kuleka ndi kuwapulumutsira iwo “kudooko“ la chisungiko—dziko la Yuda.—Masalmo 107:30.
◆ 110:3—Kodi nchiyani chimene chiri chizindikiritso chokhala ndi “aubwana monga madotho amame”? (NW)
Mame amagwirizanitsidwa ndi dalitso, kutulutsidwa, ndi kuchuluka. (Genesis 27:28) Madontho amame ndi odekha, otsitsimuritsa, osangalatsa moyo, ndipo ochuluka. M’tsiku la chamuna cha Mfumu ya Umesiya, anthu ake mwamsanga, mosangalala amadzipereka iwo eni m’ziwerengero zazikulu kotero kuti iwo angayerekezedwe ndi madontho amame. Monga madontho amame otsitsimulitsa, mu gulu lonse la Yehova lerolino amuna ndi akazi ochuluka achichepere akupereka utumiki kwa Mulungu ndi kwa olambira nawo.
◆ 116:3—Kodi nchiyani chimene chiri “zingwe za imfa”?
Chinawoneka ngati kuti imfa inamanga mwamphamvu wamasalmo ndi zingwe zosakhoza kuduka kotero kuti kupulumuka kunali kosatheka. Zingwe zomangidwa mothinitsa m’thiti zimabweretsa ukali wopweteka, kapena zowawa, ndipo Greek Septuagint version imatanthauzira liwu la Chihebri kaamba ka “zingwe” monga “zowawa.” Chotero, pamene Yesu Kristu anafa, anali mkugwidwa kochititsa manjenje, kapena zowawa, za imfa. Pamene Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa, pamenepo, lye anali “kumasula zowawa za imfa.”—Machitidwe 2:24.
◆ 119:83—Kodi ndimotani mmene wamasalmo analiri monga “thumba lofukirira”?
Pamene anali kudikira Yehova kuti amusangalatse iye, wamasalmo anakhala ngati thumba lofukirira lomwe lingapachikidwe pamene sirikugwiritsidwa ntchito. Chifukwa chautsi mu hema kapena mnyumba posakhala ndi tsanja la pa moto, mtunduwu wa thumba lofukirira pang’ono ndi pang’ono limada, kuuma, ndi kukhwinyata. M’chenicheni, ichi ndi chimene chinachitika kwa wamasalmo m’manja mwa omuzunza. (Versi 84) Mkhalidwe wake wozunzidwa mwina mwake unadziwika ndi nkhope yake yovutidwa ndi yokalulidwa, ndipo mwina mwake thupi lake linayambukiridwa kotero kuti linataya madzi ake. (Yerekezani ndi Masalmo 32:4. ) Chotero iye anadzimva kukhala wachabe monga thumba lofukirira lofota lomwe ena angaike ku mbali losayenera kuikamo madzi. Komabe iye ‘sanaiwale malamulo a Yehova.’
◆ 119:119—Kodi ndimotani mmene Mulungu anapangira oipa kutha “monga thobvu laphala”?
Thobvu lopangika kuchokera mu kusungunuka kwa chitsulo kapena m’ng’anjo yosungunulira ya moto liri chotulukapo chachabe, chinthu china chake choipa choyenera kutaidwa. Mwakutero woyenga amasiyanitsa chitsulo monga golide kapena siliva kuchokera ku “thobvu laphala.” Mofananamo, Yehova amalingalira anthu oipa kukhala oyenerera kudzala ndi kuwachotsapo, kuwalekanitsa iwo kuchokera kwa awo a mtengo omwe ali oyanjidwa ndi iye.—Yerekezani ndi Ezekieli 22:17-22.
Phunziro kwa Ife: Monga Ayuda anthawi zakale, Mboni za Yehova lerolino zikuyembekezera chipulumutso—tsopano kupyola mu namondwe wa Harmagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi yoikidwiratu ya Mulungu, dongosolo iri la zinthu lidzasesedwa ndi nkhondo iyi yaikulu. Awo amene sayang’ana kwa Yehova kaamba ka chipulumutso adzakhala opanda thandizo kotheratu pamene adzakanthidwa ndi mafunde aakulu achiwonongeko. Komabe, opulumuka, “adzapereka chiyamikiro kwa Yehova chifukwa cha chikondi chake.” Chotero, m’masiku ano otsiriza, ponse pawiri otsatira odzozedwa a Yesu ndi “khamu lalikulu“ angaike chikhulupiriro chawo chonse mwa Yehova.—Masalmo 107:31; Chivumbulutso7:9.
‘Nyimbo Zokwerera’
Werengani Masalmo 120 mpaka 134. Masalmo 15 amenewa amatchedwa nyimbo “zokwerera.” Ophunzira sagwirizana ponena zatanthauzo lenileni la “kukwerera,“ koma mwina mwake masalmo amenewa anaimbidwa ndi Aisrayeli pamene anapita pamalo okwezeka, kapena kukwera, ku mzinda wokwezeka wa Yerusalemu kaamba ka maphwando awo atatu a chaka ndi chaka.—Masalmo 122:1.
◆ 120:4—Kodi nchiyani chimene chinali “mibvi yakuthwa“ ndi “makala atsanya”?
Lilime labodza lingakhale lowononga monga chida kapena moto. (Miyambo 12:18; Yakobo 3:6) Mkupereka chilango, Yehova amawona kuti lilime labodza latonthozedwa monga ngati kuti ndi mikondo ya wankhondo. Mokondweretsa, makala opangidwa kuchokera ku tsamba la mtengo tonga tsake limapsa kwambiri, kuloza ku kuwopsa kwa chiweruzo cha umulungu pa “lilime lonyenga.”—Masalmo120:2, 3.
◆ 131:2—Kodi ndimotani mmene moyo unakhalira monga “mwana womletsa kuyamwa”?
Pambuyo poletsedwa kuyamwa, khanda limafunafuna may! wake kuti likhutiritsechikhumbo chake chakudyetsedwa. Ndipo mwana woleka kuyamwa amapeza chikhutiritso, chisungiko, ndi chisangalalo m’manja mwa mayi wake. Wokhutiritsidwa kutsata njira yodzichepetsa (versi 1), wamasalmo anadzimva “kukhala woluluzidwandi wotonthozedwa,” monga mwanawoleka kuyamwa m’manja mwa maywake. Modzichepetsa kudikira pa Yehova ndi kuchita chifuniro chake kubweretsa chisungiko ndi madalitso olemerera.
Phunziro kwa Ife: Angakhale kuli kwakuti Yehova angapulumutse anthu ake kutsoka, iye samawachinjiriza iwo ku matsoka onse. Ndithudi, matsoka anapangitsa opeka kunena masalmo awa. Komabe Mulungu “sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza” koma “adzaikanso populumukirapo.” (1 Akorinto 10:13) Yehova amatichinjiriza ife kukusakaza kwa uzimu. lye mwina angayendetse zinthu kotero kuti achotse tsoka ilo lenilenilo kapena kutilimbikitsa ife koterokuti tipirire chitsenderezo. Kufikira ku utali umenewo, wotonthoza ndi wopindulitsa kwambiri uli umodzi womwe timasangalala nawo ku misonkhano yathu ya Chikristu.—Masalmo 133:1-3.
Mulungu Woyenera Chitamando
Werengani Masalmo 135 mpaka 145. Mkusiyanitsa ndi mafano omwe owapanga alingana nawo, Yehova ali Mulungu woyenera chitamando ndiponso Mpulumutsi. (Masalmo 135, 136) Ngakhale pamene anthu ake anali mu Babulo, iwo sanaiwale “nyimbo za Ziyoni. (Masalmo 137) Davide akunena kuti‘mafumu adzalemekeza Yehova’ ndikutamanda pa kapangidwe kakekodabwitsa. (Masalmo 138, 139)lye apemphera kaamba ka chinjirizola Mulungu ndi kutamanda ubwinoWake, kudziwa kuti kokha unansiwabwino ndi Yehova umabweretsa chimwemwe chenicheni.—Masalmo 140-145.
◆ 138:2—Kodi ndimotani mmene Yehova anakwezera zokamba zake kuposa dzina lake?
Pamene Yehova adziwitsa chinthu china pa maziko a dzina lake, timayembekezera zambiri m’njira ya kukwaniritsidwa Komabe, iye nthawi zonse amapambana zoyembekezera zathu, kupangitsa kuzindikira kwathu kusiyidwa kutalitali ndi zomwe tinayembekezera. Mulungu amalemekeza “mawu ake” mwakupanga zofikiritsa zake zokulira kusiyana ndi zimene tinayembekezera
◆ 139:9—Kodi nchiyani chimene, “mapiko a mbanda kucha” akutanthauza?
Kanenedwe aka kasonyeza kuwala kwa mbanda kucha, monga ngati kuti kuti mapiko, mwamsanga kufalikira pamwamba pa mitambo kuchokera kum’mawa kupita kumadzulo. Kukanakhala kuti Davide “anatenga mapiko a mbanda kucha,” ndi kufika kudera lakutali la kumadzulo, kumeneko iye akanakhalabe pansi pa chisamatiro ndi ulamuliro wa Yehova—Masalmo 139:10; yerekezani ndi Amosi 9:2, 3.
◆ 141:3—Nchifukwa ninji Davide anafuna ‘mdindo pakamwa pa milomoyake’?
Davide anadziwa kuwononga kumene lilime lingachite ndi mmene anthu opanda ungwiro ali oyesedwa kulankhula mozaza makamaka ngati aputidwa. Mose anali munthu wofatsa koposa pa dziko lonse lapansi, koma anachimwa ndi lilime lake m’chigwirizano ndi madzi a pa Meriba (Numeri 12:3; 20:9-13) Kusunga milomo kuli kofunika, pamenepo, kupewa mawu ovulazartdikusunga mtima wabwino.—Yakobo3:5-12.
◆ 142:7—Kodi ndi chifukwa ninji Davide anaganiza kuti moyo wake unali “m’ndende”?
lye anadzimva kukhala ali yekha ndi mavuto ake, monga ngati m’mdima, ndende yoopsa, wosamvedwa ndi wopatulidwa kwa anthu onse. Pamene tiri ndi malingaliro ofananawo ndi kuganiza kuti “dzanja lathu lamanja” liri lomasuka kumenya nkhondo, mwachidaliro tingaitane kwa Yehova kaamba ka thandizo.—Masalmo 142:3-7.
Phunziro kwa Ife: Mu Salmo 139, Davide analongosola chimwemwe mu luso la Mulungu la ‘kusanthula’ iye ndi “kudziwa” iye ndi njira zake. M’malo mwa kufuna kuthawa, Davide anafuna kuyedzamira mokulira ku chitsogozo ndi ulamuliro wa Yehova. lye anadziwa kuti Mulungu nthawi zonse amamuyang’ana iye. Nzeru yotero simaletsa kokha kuleka kuchita choipa komanso imapereka kwa wina chitonthozo champhamvu. Chenicheni chakuti Yehova amawona zochita zathu, amamvetsetsa mavuto athu, ndipo nthawi zonse ali wokonzeka kutithandiza ife kutulutsa mkhalidwe wa chisungiko ndi mtendere, womwe uli wofunika kaamba ka chimwemwe.
Lemekezani Yehova!
Werengani Masalmo 146 mpaka 150. Masalmo amenewa amalasa pa mutu wa Bukhu lonse la Masalmo—“Lemekezani Yehova, anthu inu!”Liri lonse la ilo limayamba ndi kutha ndi mawu aulemelero amenewa. Zonsezi zimakwera ku mawu okwezeka mu Salmo 150, lomwe liitana zolengedwa zonse “kulemekeza Yehova!”
◆ Masalmo 146:3—Nchifukwa ninji osaika chikhulupiriro mwa anthu olamulira?
Anthu olamulira ali okhoza kufa Iwo sangathe kudzipulumutsa iwo okha kapena awo amene amaika chikhulupiriro mwa iwo. Mwakutero, chikhulupiriro mwa ulamuliro wa munthu ndi wosatsimikizirika ndi matsiriziro a imfa. Koma “wodala ali iye amene. .. chiyembekezo chake chiri pa Yehova Mulungu wake.” (Masalmo 146:5, 6) Wamasalmo anawona kufunika kwa chitsogozo chokulira kuposa chimene anthu iwo eni angapereke.
◆ 148:4—Kodi nchiyani chimene chiri “madzi a pamwamba pa thambo’?
Wamasalmo mwachiwonekere anatanthauza mtambo wa madzi pamwamba pa dziko omwe amagwa okha nthawi ndi nthawi monga mvula, omwe potsirizira amabwerera ku nyanja Kazunguliridwe aka kali kofunika m’moyo, ndipo kukhalapo kwake kumapereka chitamando kwa Mlengi. Popeza mlengalenga womwe uli pakati pa dziko lapansi ndi mitambo ungatchedwe miyamba, wamasalmo anayerekeza mitambo monga ‘madzi apamwamba pa thambo.’
Masalmo apanga chowonadi ichi kukhala chozindikirika chokha: Kuti tikhale achimwemwe mowonadi, tikafunikira unansi wabwino ndi Yehova. Chotero, chifuno chenicheni cha anthu a Mulungu ndi chifukwa cha kukhalapo kwathu chingafupikitsidwe mu kuitana kotsirizira kwa wamasalmo: “Zonse zakupuma—zilemekeze Yehova. Lemekezani Yehova, anthu inu!”—Masalmo 150:6.