Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwapereka lingaliro losamalitsa ku makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati ndi tero, mwachiwonekere mungakhale okhoza kukumbukira zotsatlrazi:
◻ Kodi nchifukwa ninji Mkristu sayenera kukondwerera Krisimasi?
Chifukwa chimodzi chiri chakuti phwando la Krisimasi linayambika mu chikondwerero chachikunja cha Saturnalia, phwando la Chiroma la mulungu wa malimidwe Saturn. Mawu a Mulungu amati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana.” (2 Akorinto 6:14-17) Mkristu sangakhale wopatulidwa kwa osakhulupirira pamene iye akupitirizabe kukumbukira phwando lachikunja.—12/15, tsamba 5.
◻ Kodi nchiyani chimene chiri Chaka Choliza Lipenga cha Akristu?
Chiri chimasuko chophatikiza “chowonadi“ chomwe chingamasule anthu kuchokera ku “lamulo lachimo ndi imfa.” Chowonadi chimenechi chiri chozikidwa pa “Mwana,“ Yesu Kristu. (Yohane 8:31-36; Aroma 8:1, 2, 21)—1/1, tsamba 25.
◻Ndi liti pamene Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chimasangalalidwira?
Pa Pentekoste 33 C.E., Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chinayamba kukondwereredwa ndi awo omwe anakonzekera kaamba ka moyo kumwamba. Kwa mtundu wa anthu wokhulupirira womwe udzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi, Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chachikulu chidzakumanizidwira mkati mwa zaka chikwi, pamene zikhoterero za chimo lacholowa ndi kupanda ungwiro zidzachotsedwa.—1/1, tsamba 25, 26, 31.
◻ Ndi chifukwa ninji Mboni zaYehova sizitsogoza masukulu kaamba ka ana mu Asia ndi kwina kuli konse?
Chifukwa cha chimene Baibulo limanena, Mboni za Yehova mokulira ziyenera kukhala zodera nkhaWa ndi ntchito yawo ya kulalikira uthenga wofunika kwambiri ponena za Ufumuwa Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20 Iwo siali osadziwa ponena zakuvutika kwa anthu ndi kupanda chilungamo mu dongosolo iri la zinthu, ndipo zimathandiza monga mmene zingathere. Komabe izo zimazindikira kuti kuchiritsa kwenlkweni kuli, osati mmanja mwa anthu, koma mu chipulumutso chimene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa posachedwa. (Masalmo 146:3-10)—1/15, tsamba 7.
◻ Kodi ndi mbali ziti za chikhulupiriro zimene tingaphunzire kuchokera ku zitsanzo za Abeli, Enoke, Nowa, Abrahamu, ndi Mose?
Chikhulupiriro chonga cha Abeli chimafulumiza chiyamikiro chathu kaamba ka nsembe ya Yesu. Chikhulupiriro chowona chimatithandiza ife kukhala olimbamtima ngati Enoke. Monga ndi Nowa, chikhulupiriro chimatifutumiza ife kutsatira malangizo a Mulungu. Chikhulupiriro cha Abrahamu chimatifulumiza ife kuwona kufunika kwa kumvera Mulungu ndi kudalira mu malonjezo ake. Tiyenera kukhala opanda mawanga kuchokera ku dziko iri ndi kuima momvera ndi anthu a Mulungu, monga mmene Mose anaperekera chitsanzo.—1/15, tsamba 20.
◻Kodi ndi mwanjira yotani mmene kufunitsitsa kungakhalire kayadalitso kapena temberero?
Kufunitsitsa kwabwino ponena za Mlengi wathu, chifuno chake, ndi zolinga zake kungakhale kokhutiritsa ndi kopindulitsa, kubweretsa chimwemwe ndi kutsitsimula miyoyo yathu. Kumbali tna, kufunitsitsa kosadziletsa kungatitsogoze ife mu mkhalidwe wakuyang’anira ndi nthanthi za anthu, kusawerengera mokulira chikhulupiriro chenicheni ndi kudzipereka kwa umulungu.—2/1, tsamba 29, Chingelezi.
◻ Kodi nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene anapemphera kuti: “Atate. ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire ine.”? (Mateyu 26:39)
Yesu anali wodera nkhaWa ponena za mlandu wochitira mwano umene iye anawona kuti udzaperekedwa motsutsana ndi iye. Uwo unali mlandu woipa kwambiri umene mYuda akanakhala nawo. Imfa yake pansi pa mikhalidwe imeneyo inawonekera, chotero, kukhala yobweretsa chitonzo pa Atate wake wakumwamba.—2/15, tsamba 24.
◻ Ngati munthu akafunikira kukhala wopirira kuvutika kapena masautso, kodi ndi iti imene ingakhale njira yanzeru ya iye kuitenga?
Chiri chabwino kaamba ka iye kukhala wodikira, kuyang’ana mwachiyembekezo kwa Yehova kaamba ka mpumulo, ndi kudziyandikitsa iye mwini kufupi ndi iye. Ichi chikachipangitsa icho kukhala chopepuka kaamba ka munthuyo kupita pansi pa zokumana nazo zofananazo m’moyo popanda kutaya chiyembekezo. (Maliro 3:25-31)—2/15, tsamba 24, Chingelezi.
◻ Kodi ndani amene ali “mafuko khumi ndi awiri a Israyell” olankhulidwa ndi Yesu pa Luka 22: 28-30?
Awa amaimira anthu onse a mtundu wa anthu omwe adzaweruzidwa ndi Kristu ndi ansembe ake 144, 000 mchigwirizano ndi kubadwanso kwa zonse zimene Yehova anakonzekeretsa kaamba ka dziko iri lapansi. (Mateyu 19:28)—3/1, tsamba 29.
◻ Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mtendere wa umulungu, ndipo kodi ndimotani mmene iwo ungapezedwere?
Mtendere wa umulungu uli mkhalidwe wachete wa maganizo ndi mtima, mkhalidwe wa mkatikati waphee, mosasamala kanthu za zimene zingakhale zikumachitika. (Masalmo 4:8) Iwo ungabwere kokha kuchokera ku unansi wovomerezeka ndi Mulungu, wothekera ndi nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. (Akolose 1:19, 20)—3/15, masamba 11, 14, 15.
◻ Kodi ndi zithandizo zotani zimene tiri nazo lerolino ndi cholinga chofuna kudziwa Mulungu mwathithithi?
Tiri ndi ponse paMri Baibulo ndi kayang’anidwe kabwino ka zaka mazana akukwaniritsidwa kwa maulosi aBaibulo. Ndiponso tiri ndi mbiri yauthenga wabwino wa moyo, ntchito, ndi mawu a Yesu Kristu, . Ponena za amene Paulo analemba: “Pakuti mwa iye [Kristu] chikhalira chidzalo cha Mulungu m’thupi.” (Akolose 2:9)—4/1, tsamba 6.