Lipoti la Olengeza Ufumu
Kugwirizananso Kwachimwemwe mu Brazil
PA 67 a amishonale ophunzitsidwa pa Gileadi amene akutumikira mu Brazil 63 anafika pamodzi pa ofesi ya nthambi ndikuima kaamba ka chithunzi chopanga mbiri ichi. Kugwirizananso kwachimwemwe kumeneku kunachitika pa November 18, 1986, mkati mwa kuchezera kwa A. D. Schroeder, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York.
Zinali zaka zoyambirira 41 chifupifupi pa tsiku lomwelo—pa November 17, 1945—pamene omaliza maphunziro awiri a kalasi loyambirira la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anafika ku Brazil. Kwa m’modzi wa iwo, Charles Leathco (kumbuyo, kumanzere kwa pakati), uku kunali kugwirizananso kwapadera chifukwa iye ndi mlendo wake Charlotte Schroeder anali mkalasi imodzi mu Gileadi, ndipo Mbale Schroeder anali mmodzi wa aphunzitsi awo.
Kuyambira kalasi yoyamba imeneyo, chiwonkhetso cha amishonale 258 abwera ku Brazil. Pakati pa iwo panali 16 a ku Brazil. Mmodzi wa iwo, Augusto Machado (kumanzere m’zera wakutsogolo), anaphunzira chowonadi kuchokera kwa amishonale oyambirira, kupita ku Gileadi, ndi kubwerera ku Brazil. Wakhala akutumikira pa ofesi ya nthambi kwa zaka 30 zapita ndipo tsopano ali mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi. Ngakhale kuti ambiri a amishonalewo sakutumikiranso monga amishonale, ntchito yabwino imene anachita inatsalira. Mu1945 munali ofalitsa a Ufumu 344 okha mu dzikolo tsopano Brazil ikuyandikira chizindikiro cha 200, 000, kuchitira ripoti chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa 196, 948 mu chaka chautumiki cha 1986.
Chinali chimwemwe chotani nanga kwa amishonale AchiBrazil, achichepere ndi achikulire, kukumbutsanso pa kugwirizananso kwachimwemwe kumeneku ponena za ntchito yozizwitsa ya zaka 41 zapita.