Chikhulupiriro Chingasunthe Mapiri!
KHAMU linali m’malere. Atate angobweretsa kumene mwana wakhunyu kwa amuna amene akukhulupiriridwa kukhala okhoza kum’chiritsa iye. Mofunitsitsa, kuchiritsa kunayembekezeredwa. Koma palibe chimene chachitika! Mokhumudwitsidwa, tateyo anatembenukira kumbali.
Panthaŵi imeneyo amuna ena anayi anawonekera ndipo pakati pawo pali mtsogoleri wawo, Yesu wa ku Nazarete. Akuthamangira kwa iye, tateyo anadandaula kuti: “Chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m’madzi. Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa.”
“Idzani naye kwa ine kuno,” anatero Yesu. Chotulukapo chake? “Ndipo Yesu anachidzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.” Inde, chozizwitsa china! Koma nchifukwa ninji ophunzira a Yesu analephera?
Yesu analongosola chifukwa chake, akumati: “Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching’ono.” Kenaka iye anapitiriza: “Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, ‘Senderapo umuke kuja,’ ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosachitika.”—Mateyu 17:14-20.
Kuchokera ku chokumana nacho cha umoyo chenicheni ichi, chiri chotsimikizirika kuti chikhulupiriro chiri champhamvu. Koma kodi nchiyani chimene chiri chikhulupiriro? Kodi icho chingamangiriridwe ndi kulimbikitsidwa? Kodi icho kwenikwenidi chingasunthe mapiri?
Kodi Chikhulupiriro Nchiyani?
Mtumwi Paulo analongosola chikhulupiriro monga “chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa, chisonyezero chowoneka bwino cha zinthu [kapena, chiyembekezo chotsimikiziridwa] zosapenyeka.” (Ahebri11:1, NW) M’mawu ena, chikhulupiriro chiri chitsimikiziro chokhutiritsa cha chinachake chosawonedwa. Icho sichiri chozikidwa pa manenanena opanda pake koma chiri ndi maziko olimba. Chotero, chikhulupiriro chimasiyana ndi kukhulupirira. Bukhu lotanthauzira mawu limodzi limalongosola kukhulupirira monga “chikhulupiriro kapena kukonzekera kwa kukhulupirira, maka [maka] pazinthu zochepa kapena chitsimikiziro chosatsimikizirika.” Mosiyanitsa, munthu wokhala ndi chikhulupiriro chowona ali ndi chitsimikiziro cholimba cha zimene amakhulupirira. Chotero, iye angakuuzeni inu chifukwa chimene iye ali wokhutiritsidwa kuti chinthu chinachake chidzachitika, Atate wotchulidwa poyambirirayo anali ndi chitsimikiziro chokhutiritsa mwa iye kuti Yesu angachiritse mwana wake. Ndi chitsimikiziro chotani? Chabwino, Yesu anali atapangapo zozizwitsa kwa zaka zoposa ziwiri, ndipo kutchuka kwake kunali kutafalikira ku zigawo zochuluka za Palestina.—Luka 7:17; Yohane 10:25.
Chikhulupiriro chalongosoledwanso monga “chitsimikiziro chokhazikika mwalamulo cha zinthu zoyembekezeredwa.” Munthu amene amagula malo akutali ndipo ali ndi chitsimikiziro chokhazikika mwalamulo m’manja mwake ali ndi chitsimikiziro chokhutiritsa chakuti malowo alikodi ndipo kuti alidi ake, ngakhale kutiiye angakhale asanawone iwo. Chotero, kachiŵirinso, munthu yemwe ali ndi chikhulupiriro angabweretse chitsimikiziro chowoneka cha zimene iye amakhulupirira. Mwachitsanzo, tayerekezani kuti iye ali ndi chikhulupiriro kuti Yehova Mulungu adzabweretsa mtendere weniweni padziko iri lapansi kupyolera mwa Ufumu Wake. Kenaka munthuyu ayenera kukhala ndi chitsimikiziro chakuti Mulungu alipo ndikuti ali ndi mphamvu, chifuno, ndi nzeru yofunikira kubweretsa mtendere ndikuti Iye wakhazikitsa Ufumu wake kaamba ka cholinga chimenecho. Chitsimikiziro choterocho chiyenera kukhala champhamvu kotero kuti chikhutiritse osati kokha munthu wokhala ndi chikhulupiriro komanso ndi ena omwe ‘angafune chifukwa cha chiyembekezo chake’ kaamba ka mtendere.—1 Petro 3:15.
Chikhulupiriro Chingasunthe Mapiri!
Komabe, wina angafunse, ‘Kodi Yesu anatanthauza kuti chikhulupiriro choterocho mchenicheni chingasunthe mapiri?’ Yesu angakhale anaphatikiza chimenecho, koma iye kaŵirikaŵiri anagwiritsira ntchito mafanizo. (Mateyu 13:34) Chotero iye mwinamwake anali ndi zokhumudwitsa m’malingaliro zomwe zingakhale ngati mapiri kwa wokhulupirira. Mchenicheni, liwu lakuti “mapiri” kaŵikaŵiri limagwiritsiridwa ntchito kutanthauza unyinji waukulu, monga ngati “phiri la ngongole.” Kuti chikhulupiriro chowona chingasamutse kapena kusuntha zokhumudwitsa zonga mapiri chatsimikiziridwa ndi zokumana nazo zambiri zamakono.
Mwachitsanzo, kodi simungavomereze kuti kukhala wakufa kuchokera kukhosi kufika kunsi kungakhale konga phiri? Komabe, munthu wakufa ponse pawiri miyendo ndi mikono wokhala mu Vancouver, B. C. , Canada, sanaphunzire kokha kupaka utoto, kaya ndi bulasho kapena ndi mpeni wogwiririra kukamwa kwake, komanso amadzichirikiza iyemwini mwakugulitsa zopakidwa utoto zake. Kuwonjezerapo, chikhulupiriro chake chimamufulumiza iye kulankhula kwa ena ponena za zimene iye waphunzira kuchokera mu Baibulo, akumachita tero kaya ali pa mpando wake wa mugudumu kapena mwakulemba makalata. Iye amataipa makalata ake mwa kumenya makiyi a typewriter ndi ndodo yogwiridwa kukamwa kwake. Iye amapezekanso pa misonkhano Yachikristu mokhazikika ndi kupereka nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki yotsogozedwa ndi Mboni za Yehova. Chitsanzo chake cha chikhulupiriro, chogwirizana ndi kugwira ntchito molimbika ndi kulimbika mtima, chiri magwero achilimbikitso kwa awo omuzinga iye.
Chikhulupiriro mu Mawu a Mulungu ndi malonjezo ake mofananamo chathandiza ena Mwachitsanzo, chathandiza ambiri kugonjetsa zizolowezi zosakhala zachikristu ndi miyambo, monga ngati machitachita a bizinesi a mu mdima, kuba, kusuta, kutchova njuga, kuledzera, kukhulupirira mizimu, khalidwe la chisembwere la kugonana, ndi machitachita achipembedzo chonyenga. Nsonga yeniyeni mu zokumana nazo zonse zoterozo inali kupezedwa kwa chitsimikiziro chokhutiritsa chakuti Yehova Mulungu alipo, kuti Baibulo liri Mawu ake olembedwa, ndikuti malonjezo ake okhazikitsidwa m’Malemba ali odalirika ndipo adzakwaniritsidwa. Chikhulupiriro choterocho chingasunthe mapiri