Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kumvera Chifundo Aumphaŵi
PAMBUYO pakutsutsa Afarisi kaamba ka miyambo yawo yodzitumikira, Yesu akuchoka ndi ophunzira ake. Osati kale kwambiri, mungakumbukire, kuyesayesa kwake kwa kuchoka ndi iwo kukapuma pang’ono kunasokonezedwa pamene khamu linawapeza iwo. Tsopano, ndi ophunzira ake, iye akutuluka kupita ku mbali za Turo ndi Sidoni, mamailosi ambiri kumpoto. Uwu mwachiwonekere uli ulendo wokha umene Yesu apanga ndi ophunzira ake kupyola malire a Israyeli.
Pambuyo pa kupeza nyumba yoti akhalemo, Yesu akuchilola icho kudziŵika kuti sakufuna aliyense kudziŵa kumene iye ali. Komabe, ngakhale m’gawo iri losakhala la Chiisrayeli, iye sangapulumuke kuzindikiridwa. Mkazi wa Chigriki, wobadwira muno mu Foinike wa ku Syria, akumapeza iye ndi kuyamba kupempha: “Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi wagwidwa koposa ndi chiwanda.” Yesu, ngakhale kuli tero, sakunena liwu liri lonse m’kuyankha.
Kenaka, ophunzira ake akumuuza Yesu: “Muuzeni amuke, pakuti afuula pambuyo pathu.”
Akulongosola chifukwa chake kaamba ka kunyalanyazira iye, Yesu akuti: “Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotaika za banja la Israyeli.”
Ngakhale kuli tero, mkaziyo sanalefuke. Iye akumfikira Yesu, akugwada pamaso pake, ndi kuchondelera, “Ambuye, ndithangateni ine!”
Ndimotani nanga mmene mtima wa Yesu unafulumizidwira ndi kupempha kowona mtima kwa mkaziyo! Komabe, iye kachiŵirinso akuloza ku thayo lake loyamba, kutumikira anthu a Mulungu Aisrayeli. Panthaŵi imodzimodziyo, mwachiwonekere kufuna kuyesa chikhulupiriro chake, akusonyeza kawonedwe konyada ka Ayuda ka awo amene anali a mitundu ina, akumanena kuti: “Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagaru.”
Ndi kamvekedwe kake ka mawu kachikondi, ndi kalongosoledwe kapamaso, Yesu motsimikizirika akutsimikizira malingaliro ake ofewa kulinga kwa awo omwe sali Ayuda. Iye akudekhetsa ngakhale kuyerekeza konyada kwa amitundu ndi agaru mwa kulozera kwa iwo monga “tiagaru,” kapena ana a garu. M’malo mobwezera, mkaziyo akubwereka mawu pa kulozera kwa Yesu ku kunyada kwa Ayuda ndi kupanga kawonedwe kodzichepetsa: “Etu, Ambuye; pakutinso tiagaru timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye awo.”
“Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu,” Yesu akuyankha. “Chikhale kwa iye monga momwe wafunira.” Ndipo chatero! Pamene iye abwerera kunyumba yake, apeza mwana wake wamkazi ali pakama, wochiritsidwa kotheratu.
Kuchokera kumbali ya kugombe ya Sidoni, Yesu ndi ophunzira ake apita kudutsa dzikolo kulinga ku madzi a Mtsinje wa Yordano. Iwo mwachiwonekere akudutsa Yordano kwinakwake ku mtunda kwa Nyanja ya Galileya ndi kulowa m’gawo la Dekapoli, kum’mawa kwa nyanja. Kumeneko iwo akwera phiri, koma khamu liwapeza iwo ndi kubweretsa kwa Yesu opunduka awo, opanda miyendo, akhungu, ndi osalankhula, ndi ambiri omwe anali odwala ndi opunduka. Iwo anawaponya iwo pa mapazi a Yesu, ndipo iye anawachiritsa. Anthuwo anazizwa pakuwona osalankhula akulankhula, opunduka miyendo akuyenda, ndi akhungu akupenya, ndipo analemekeza Mulungu wa Israyeli.
Mwamuna mmodzi yemwe ali wogontha ndi wachibwibwi akupatsidwa chisamaliro chapadera cha Yesu. Ogontha kaŵirikaŵiri amachititsidwa manyazi, makamaka m’khamu. Yesu angakhale anadziŵa kunjenjemera kwapadera kwa munthuyo. Chotero Yesu mwachikondi anampatula pa khamu la anthu pa yekha. Pamene ali okha, Yesu akusonyeza chimene akachita kwa iye. Iye akulonga zala zake m’makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake. Kenaka, akuyang’ana kumwamba, Yesu akuusa moyo molimba nanena: “Tseguka.” Pamenepo, mphamvu za kumva za munthuyo zabwezeretsedwa, ndipo ali wokhoza kulankhula mwachibadwa.
Pamene Yesu apanga kuchiritsa kwambiri kumeneku, makamuwo akuyankha ndi chiyamikiro: “Wachita iye zonse zabwino. Ngakhale ogontha awamvetsa ndi osalankhula awalankhulitsa.” Mateyu 15:21-31; Marko 7:24-37.
◻ Nchifukwa ninji Yesu sakuchiritsa mwamsanga mwana wa mkazi wa Chigriki?
◻ Pambuyo pake, ndi kuti kumene Yesu akutenga ophunzira ake?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu mwachikondi akuchiritsa munthu wogontha amene ali wachibwibwi?