Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Anthu a Mulungu akufunikira ‘kusamalira awo a mbumba yawo,’ chotero ndimotani mmene Abrahamu anangotumiza Hagara ndi Ismayeli m’chipululu?
Ziri ponse paŵiri chikondi ndi choyenera kwa atumiki a Mulungu kusamalira kaamba ka ziwalo zosowa za banja lawo. Ponena za makolo Achikristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.”—1 Timoteo 5:8.
Tingakhale otsimikizira kuti njira ya Abrahamu sinali yotsutsana ndi mzimu wa uphungu waumulungu woterowo, popeza iye anaika chitsanzo cha chikhulupiriro chowona, kukhala “bwenzi la Yehova.”—Yakobo 2:23; Ahebri 11:8-19.
Mulungu analonjeza dalitso kupyolera mwa mbewu ya Abrahamu, kapena mlowa m’malo. Pamene Sara anali wachikulire ndipo anali wosabala, iye anauza Abrahamu kutulutsa mwana kupyolera mwa mdzakazi wake wa Chiigupto Hagara. Pambuyo pake, pamene Hagara anali ndi pakati, iye anayamba kuchita mwamtonzo kulinga kwa Sara komwe kunakhoza kulongosoledwa monga “chiŵaŵa,” kapena chimo lankhalwe motsutsana ndi mkazi wokondedwa wa Abrahamu. (Eksodo 23:1; 2 Samueli 22:49; Masalmo 11:5) Abrahamu anamlola Sara kuika Hagara m’malo ake, mwakutero Hagara anathaŵa kupita ku chipululu, mwinamwake kumabwerera ku Igupto. Mbiriyo sikunena kuti anatenga chakudya limodzi naye, chotero iye angakhale anadziŵa kuti akapeza chakudya ndi madzi pamalo a chigono ena, monga ngati kuchokera ku magulu a Anthu Okhala m’Chipululu.—Genesis 12:1-3, 7; 16:1-6.
Mngelo analowereramo ndi kumuuza Hagara kuti ayenera kubwerera, kuti iye adzakhala ndi mbadwa zambiri, ndipo kuti ‘dzanja la mwana wake Ismayeli lidzatsutsana ndi wina aliyense.’ (Genesis 16:7-12) Osati zaka zambiri pambuyo pake, Ismayeli anatsimikizira kukhala wotsutsana ndi Isake wachichepere, mbadwa yolowa m’malo yeniyeni ya Abrahamu kwa Sara. Ismayeli anayamba ‘kutonza’, kapena kunyazitsa, Isake. Ichi chinali chowopsya kwambiri kuposa mkangano wa pachibale. Mawu a Mulungu amachizindikiritsa kukhala “kuzunza” mbewu yonenedweratu mwaumulungu ya Abrahamu. Chotero kachitidwe kamphamvu kanali koyenerera.—Genesis 21:1-9; Agalatiya 4:29-31.
Yehova anauza Abrahamu kulabadira kaimidwe ka mkazi wake pa chimene chinafunikira kuchitidwa, ‘kumuchotsa Hagara ndi mwana wake.’ Ngakhale kuti Abrahamu sanasangalatsidwe ndi ziyembekezo za kuchoka kwa Hagara ndi mwana wake, Abrahamu anapanga maperekedwe a zakuthupi kaamba ka iwo. Ndi kusiyana kothekera ndi nthaŵi yoyambirira pamene Hagara anapita m’chipululu, panthaŵiyi iye anachoka ndi mkate (mwinamwake kutanthauza zakudya zosiyanasiyana) ndi madzi—zoperekedwa ndi Abrahamu. Iye mwachiwonekere anataika kwina kwake “m’chipululu cha Beereseba,” ndipo zakudya zake zinatha asanapeze chitsime chimodzi m’deralo. Koma tsoka lake silinali kuchinyazitso cha Abrahamu, popeza iye ‘anapereka zakudya kaamba ka awo omwe anali ake,’ ngakhale m’chiyang’aniro cha khalidwe lawo loipa lomwe linafunikira kuchotsedwa kwawo kuchokera ku banjalo.—Genesis 21:10-21.
[Mapu/Chithunzi patsamba 31]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Great Sea
Mount Carmel
Megiddo
Jerusalem
Hebron
Beer-sheba
Dead Sea
Negeb
[Mawu a Chithunzi]
Based on a map copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi]
Wadi Zini, chigwa cha mtsinje wouma kum’mwera kwa Beereseba