Mangirirani Chikhulupiriro mwa Yehova—Mwa Kuphunzira Mwakhama Mawu Ake
“Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero . . . Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.”—Deuteronomo 32:46, 47.
1, 2. (a) Ndi chiyembekezo chotani chimene chinyang’anizana ndi Israyeli pamene anamanga msasa pa zigwa za Moabu? (b) Ndi chenjezo lotani limene Mose anapereka kwa mtunduwo?
ULENDO wawo wautali m’chipululu unali pafupi kutha. Kokha Yordani wokhotakhota tsopano analenkanitsa mtunduwo kuchoka ku Dziko Lolonjezedwa loyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitaliyo. Ngakhale kuli tero, kwa mtsogoleri wa mtunduwo, Mose, chiyembekezo cha Israyeli cha kulowa dziko limenelo chinabweretsa malingaliro omvetsa chisoni. Iye anakumbukira mmene mtunduwo kamodzi unakhumudwira chifukwa cha kusoweka kwawo kwa chikhulupiriro mwa Yehova ndipo chotero unakanizidwa kulowa mu Kanani.—Numeri 13:25–14:30.
2 Chotero Mose anasonkhanitsa mtunduwo pa zigwa za Moabu. Pambuyo pa kubwereramo m’mbira yawo ya mtundu ndi kubwerezanso Lamulo la Mulungu, Mose anapereka chomwe chinatchedwa nyimbo yolembedwa ndi iye. M’chinenero cha ndakatulo yapamwamba, iye anasonkhezera Israyeli kukhulupirira ndi kumvera Yehova, “Mulungu wokhulupirika, ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” M’kumaliza, Mose akuchenjeza kuti: “Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero, kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.”—Deuteronomo 32:4, 46, 47.
‘Kuika Mitima Yawo’ ku Mawu a Mulungu
3, 4. (a) Ndi ku chiyani kumene Aisrayeli anayenera ‘kuika mitima yawo.’ ndipo kodi ichi chinaphatikizapo chiyani? (b) Ndimotani mmene mibadwo ya mtsogolo inagwiritsira ntchito uphungu wa Mose?
3 Mose anachenjeza Aisrayeli ‘kuika mitima yawo’ osati kokha ku nyimbo yake yodzutsa maganizo koma ku zolembedwa zonse zopatulika. Iwo anayenera “kupereka chilabadiro chabwino” (Knox), “kutsimikizira kumvera” (Today’s English Version), kapena “kusinkhasinkha pa” (The Living Bible) Lamulo la Mulungu. Kokha mwa kukhala ozoloŵerana kotheratu ndi iwo ndi pamene iwo ‘akalamulira ana awo kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo chinenechi.’ Pa Deuteronomo 6:6-8, Mose analemba kuti: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero azikhala pa mtima panu; ndipo mudziwaphunzitsa mwachangu ana anu . . . Ndipo mudziwamanga pa dzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu.”
4 Wochitira ndemanga wa Baibulo W.H. Davey akunena za mmene mu nthaŵi zapambuyo pake, mawu awa “anamasuliridwira m’lingaliro lenileni ndi Ayuda, ndipo chitsogozo chopezeka mu iwo chinasinthidwira ku kugwiritsira ntchito kwa malaulo, Maversi ena . . . analembedwa pa pepala lopangidwa ndi chikopa cha nyama ndi kuvalidwa pa mkono ndi pa mphumi mkati mwa nthaŵi ya pemphero.” Mipukutu yolongosola yokhala ndi malemba, kapena mabokosi aŵiri a mawu a malemba owuziridwa, inali kuvalidwa m’nthaŵi ya Yesu ndipo idakali kugwiritsiridwa ntchito ndi mipatuko ina ya Chiyuda lerolino. (Mateyu 23:5) Koma, akuwonjezera Davey: “Anthu m’kupusa kwawo anadzikhutiritsa iwo eni ndi kunyamula izo pa iwo eni makope a mawu wamba a lamulo, m’malo mosonyeza m’miyoyo yawo kusunga kwa chilamulo chosungidwa mmenemo.”
5. Nchiyani chomwe chinali kugwiritsira ntchito koyenera kwa mawu a Mose pa Deuteronomo 6:6-8?
5 Ayi, sipanali pa manja awo enieni kapena pa mphumi pamene Lamulo la Mulungu linayenera kukhala koma ‘pa mitima yawo.’ Mwa kupeza osati kokha chidziŵitso cha ilo koma chiyamikiro chozama kaamba ka ilo, Lamulo limenelo nthaŵi zonse likasungidwa m’chiyang’aniro, ngati kuti linalembedwa pagome patsogolo pa maso awo kapena kumangiriridwa pa manja awo.
Makonzedwe a Kuphunzira Lamulo la Mulungu
6, 7. (a) Ndi makonzedwe otani amene Yehova anapanga kuzoloŵeretsa Aisrayeli ndi Chilamulo cha Mose? (b) Ndimotani mmene icho chinakhaliranso chothekera kwa anthu a Mulungu m’nthaŵi zakale kukhala olangizidwa m’Mawu a Mulungu?
6 Ngakhale ndi tero, ndimotani mmene Aisrayeli akaphunzirira malamulo ena 600 a Lamulolo? Makope a ilo mosakaikira anali osawonekawoneka poyambirira. Mfumu ya mtsogolo ya Israyeli inayenera “kulemba m’bukhu kaamba ka iyemwini kope la lamulo limeneli . . . , ndipo anayenera kuŵerenga mu ilo masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire ndi kuwopa Yehova Mulungu wake kotero kuti asunge mawu onse a lamulo limeneli.” (Deuteronomo 17:18, 19) Mulungu anakonzekera kaamba ka Lamulolo kuti lidziŵerengedwa chaka cha chisanu ndi chiŵiri chirichonse pa Madyerero a Misasa. (Deuteronomo 31:10-13) Pamene kuli kwakuti chochitika choterocho mosakaikira chinali chodzutsa maganizo, chinali chosabwerezabwereza kuti chiike chidziŵitso mozamitsa.
7 Yehova anakonzanso kaamba ka fuko la Levi kuti ‘liphunzitse Yakobo malangizo a Mulungu ndi Israyeli chilamulo cha Mulungu.’ (Deuteronomo 33:8,10; yerekezani ndi Malaki 2:7.) Pa zochitika zina, Alevi anachita ndawala zophunzitsa zomwe zinatumikira mtundu wonse. (2 Mbiri 17:7-9; Nehemiya 8:7-9) Chikuwoneka kuti, m’kupita kwa nthaŵi, chifupifupi mbali za Mawu a Mulungu zinalinso zopezeka kwa anthu mwachisawawa.a Chotero, wamasalmo anakhoza kulemba kuti: “Wodala munthuyo . . . [amene] chikondwerero chake chiri m’chilamulo cha Yehova, ndipo m’chilamulo chake amalingilira usiku ndi usana.” (Masalamo 1:1, 2) Chenjezo la Mose la ‘kuika mitima yawo ku Mawu a Mulungu’ chotero linafikira ku lamulo la kupanga phunziro lakhama la Baibulo.
‘Kuika Mitima Yathu’ ku Mawu a Mulungu Lerolino
8. Ndi ku ukulu wotani umene Israyeli analabadira chenjezo la Mose, ndipo ndi zotulukapo zotani?
8 Israyeli analephera kulabadira chenjezo la Mose. Pamene mtunduwo pomalizira pake unakhazikitsa ufumu wake, mwachiwonekere ambiri a mafumu ake analephera ‘kudzilembera iwo eni kope la lamulo ndi kuŵerenga ilo masiku onse a miyoyo yawo.’ Podzafika m’zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., m’maisku a Mfumu Yosiya, “bukhu la chilamulolo” linali litataika. (2 Mafumu 22:8-13) Chitsanzo choipa ku mbali ya atsogoleri a mtunduwo mosakaikira chinafulumiza mtunduwo kugwera mu mpatuko. Mowonadi ku chenjezo la Mose, tsoka la mtunduwo linawoneka mu 607 B.C.E.—Deuteronomo 28:15-37; 32:23-35.
9. Ndimotani mmene mkhalidwe wa Akristu lerolino uliri wofanana ndi uja wa Israyeli wakale?
9 Mofanana ndi Aisrayeli akale, Akristu lerolino ali pamalire a dziko lolonjezedwa—dziko latsopano lolungama la Mulungu. (2 Petro 3:13) Zochitika zodabwitsa ziri m’chizimezime; kulengezedwa kwa “mtendere ndi chisungiko, kugwa kwa Babulo Wamkulu,” ndi kuwukira kwa “Gogi wa Magogi.’ Zochitika zimenezi zidzaika chikhulupiriro chathu mwa Yehova kuchiyeso. Chiri chofulumira, chotero, kuti ‘tiike mitima yathu ku mawu a Mulungu’ tsopano!—1 Atesalonika 5:3; Chivumbulutso, mutu 18; Ezekieli, mutu 38.
10. Nchifukwa ninji ena anganyalanyaze ni phunziro laumwini?
10 Kuchita tero, ngakhale kuli tero, kungakhale chitokoso chenicheni “m’nthaŵi zino zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1, NW) Ntchito ya kuthupi, kulera ana, sukulu, ndi mathayo a mpingo zonse zingapange zilamuliro zolemera pa nthaŵi yathu. Monga chotulukapo chake, tingayedzamire ku kudzikhululukira ife eni ndi kuzilala m’phunziro lathu la Baibulo, tikumalingalira kuti ‘Ndikuchita zokwanira kuti ndipulumuke.’ Komabe, Baibulo likuchenjeza Akristu: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale.” (1 Timoteo 4:15, 16) Tiyeni tilingalire tsopano zina za zifukwa zamphamvu zochitira tero.
Kulimbitsa Unansi Wathu Ndi Mulungu
11, 12. (a) Ndimotani mmene kupeza chidziŵitso chthithithi cha Mulungu kunayambukirira Yobu? (b) Nchifukwa ninji kawonedwe kathu ka Mulungu kangakhalire kowonekera bwino kuposa m’nthaŵi ya Yobu?
11 Yobu anali “wakuwopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” Koma pamene Yehova anadzivumbulutsa iyemwini mowonjezereka kwa iye mu mphepo ya mkuntho, Yobu ananena kuti; “Kumva ndinamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso.” (Yobu 1:1; 42:5) Kodi ife lerolino “tingawone” Mulungu, kunena kuti, kupita kupyola kuzoloŵerana wamba, mwathithithi kudziŵa mbali zambiri za umunthu wake? Ndithudi tingatero! Kupyolera m’masamba a Baibulo, Yehova wavumbula zochulukira ponena za iyemwini kuposa zimene zinadziŵika ngakhale kwa Yobu.
12 Tiri ndi kawonedwe kowunikirika ka kuzama kwa chikondi cha Mulungu, tikumadziŵa kuti iye “anakonda dziko lapansi kotero kuti anatumiza Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Kupyolera m’maulosi a Baibulo, tiri ndi ndandanda ya machitachita a Mulungu-kufikira ku mapeto a Zaka Chikwi! (Chivumbulutso, mitu 18-22) Tiri ndi mbiri ya zochita za Mulungu ndi mpingo wa Chikristu: kubweretsa kwake Akunja, kuika kwake “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti adyetse anthu ake, kuitana kwake “khamu lalikulu” ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha pa Paradaiso wa pa dziko lapansi. (Mateyu 24:45, Chivumbulutso 7:9, 14-17; Aefeso 3:3-6) Pambuyo pa kusunzumira mu zinthu zozama za Mulungu ndi kulingalira ntchito zake zozizwitsa m’malo mwathu, sitingathe kuthandiza koma kufuula kuti: “Ha! kuya kwake ndi kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!”—Aroma 11:33.
13. Ndimotani mmene ‘tingafufuzire kaamba ka Mulungu,’ ndipo ndi ati omwe ali mapindu a kuchita tero?
13 Wamasalamo ananena kuti: “Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse.” Tingachite chofananacho mwa kupanga kulingalira kwa tsiku ndi tsiku kwa nkhani za m’Malemba; kumachita zokulira kulimbikitsa chomangira chathu ndi Yehova. Phunziro lowona mtima limathandizanso kupanga njira yathu kukhala ‘yokhazikika m’kusunga malamulo a Mulungu.’—Masalmo 119:5, 10.
Kuphunzira Kumatithandiza Ife Kuchinjiriza Chikhulupiriro Chathu
14. Chitirani chitsanzo phindu la kukhala ‘okonzekera kuchinjiriza’ chiyembekezo chathu Chachikristu.
14 “Sindikufunani inu Mboni m’nyumba mwanga!” anatero mwamuna mmodzi wa ku Ghana kwa aŵiri omwe anaitanira panyumba yake. Iye mowonjezereka anachepsya Mbonizo chifukwa cha “kusalandira kuthiridwa mwazi ndi kusapereka sawatcha ku mbendra ya mtundu.” Zitsutso zoterozo zimakumanizidwa mofala mu utumiki wa m’munda. Ndi chitonzo chotani—ndi kuchepetsedwa—kumene kukakhalira ngati tinali osakhoza “kupanga chodzichinjiriza kwa yense wokufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu”! (1 Petro 3:15, NW) Mwamwaŵi, Mboni zimenezi zinali zokhoza kugwiritsira ntchito Baibulo mokhutiritsa kulongosola kawonedwe koyenera ka mwazi ndi mmene Mkristu amalinganizira ulemu kaamba ka zizindikiro za mtundu ndi kupewa kulambira mafano. Chotulukapo chake? Mwamunayo anakondweretsedwa ndi mayankho awo achindunji. Lerolino, onse aŵiri iye ndi mkazi wake ali Mboni zobatizidwa.
15. Ndimotani mmene phunziro laumwini limatikonzekeretsera ife kaamba ka utumiki wathu?
15 Paulo akufulumiza kuti: “Uchite changu kudziwonetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a chowonadi.” Phunziro laumwini lidzatithandiza ife osati kokha kukhala pa njira ya moyo ife eni komanso “okonzeka, kuchita ntchito iriyonse yabwino” kuti tithandize enanso kuchita tero.—2 Timoteo 2:15; 3:17.
Resisting Satan’s Snares
16. Ndi iti yomwe iri misampha ina ya Satana imene anthu a Yehova amakumanizana nayo?
16 Lerolino, kusatsa malonda kumatikuta ife ndi zosangalatsa ku “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi matamandidwe a moyo.” (1 Yohane 2:16) Mkhalidwe woipa wa chisembwere umalemekezedwa ndi ofalitsa nkhani ndipo kaŵirikaŵiri umapititsidwa patsogolo mokangalika ndi ogwira nawo ntchito ndi anzathu a pa sukulu. Mabukhu a mpatuko ovulaza angatumizidwe popanda chilolezo kunyumba zathu. Chidwi chawo chitadzutsidwa, abale ena aŵerenga zinthu zoipitsa zoterozo—kuwononga chikhulupiriro chawo. Palinso mzimu wadyera, wa kuthupi “womwe tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” Chiri chopepuka chotani nanga kukhala woyambukiridwa ndi iwo ndi kukulitsa mzimu wa kuipidwa, wosuliza!—Aefeso 2:2.
17, 18. Ndimotani mmene phunziro laumwini lingatichinjirizire ife ku ‘kutengeka’?
17 Ochepera, ndithudi, amaima pa njira ya kugwidwa mu msampha ndi Satana. M’malomwake, mwa kunyalanyaza phunziro laumwini, mofanana ndi bwato lomasulidwa pa makochezi ake, iwo pang’ongopang’ono “amatengeka” ndi kukhala chandamale choyambirira cha kuwukiridwa ndi Satana. (Ahebri 2:1) Mbale mmodzi wachichepere, mwachitsanzo, anakhala wodziloŵetsamo mu mkhalidwe wachisembwere ndi mtsikana wachichepere ku sukulu. “Ndinapeza,” iye akukumbukira, “kuti choyambitsa chachikulu kaamba ka ichi chinali chenicheni chakuti ndinali kusowa chakudya mwauzimu. Sindinapange phunziro laumwini. Chimenecho ndicho chifukwa chake ndinalephera kupewa chiyesocho.” Programu ya phunziro laumwini, ngakhale kuli tero, inathandiza mbaleyo kukhala wolimba mwauzimu.
18 Satana ali wogamulapo kuwononga ambiri a anthu a Mulungu monga mmene iye angathere. Mwa kudyetsa maganizo athu mokhazikika ndi zinthu zabwino zomwe zimabwera kuchokera ku Mawu a Mulungu ndi kapolo wake wokhulupirika, tingapewe kukhala ogwidwa mu msampha. (Afilipi 4:8) Zokumbutsa za kupewa kukondetsa zinthu zakuthupi, mkhalidwe woipa wa chisembwere, malingaliro a mpatuko, ndi mzimu woipa zimapezeka ponse paŵiri m’Baibulo ndi m’zofalitsidwa za Watch Tower Society. Ngati ife ndithudi tipereka choposa chisamaliro cha nthaŵi zonse, sitidzatengeka nkomwe.
Makonzedwe Kuchokera ku Gulu la Yehova Kuti Atithandize Ife
19. Mdindo wa ku Aitiopiya anachitira chitsanzo chiyani ponena za kufunikira kwathu kwa chitsogozo chauzimu?
19 Kuphunzira kuli ntchito ya kalavula gaga. Ife chotero tingakhale oyamikira kuti gulu la Yehova limatipatsa ife thandizo lokulira. M’zaka za posachedwapa ena anena kuti munthu aliyense payekha ayenera kuloledwa kutembenuza Baibulo iyemwini. Mdindo wa ku Aitopiya, ngakhale kuli tero, mwapoyera anazindikira chifuno chake cha chitsogozo chauzimu. Monga wotembenuzidwa wodulidwa, iye mosakaikira anali kale ndi chidziŵitso chokulira cha Baibulo. Chenicheni chakuti iye anayesera kuphunzira chinachake chozama monga ulosi wa Yesaya 53 cimasonyeza chimenechi. Komabe, pamene iye anafunsidwa ngati iye anamvetsetsa chimene iye anali kuŵerenga, iye anavomereza kuti: “Ndithudi, ndingachite bwanji tero popanda wina akunditsogoza?”—Machitidwe 8:26-33.
20. Ndi ati amene ali ena a makonzedwe amene gulu la Yehova lapanga kutithandiza ife m’phunziro lathu laumwini la Baibulo? Kodi mumadzimva motani ponena za makonzedwe oterowo?
20 Anthu a Yehova lerolino mofananamo amafunikira chitsogozo chauzimu. Kukhumba “Kulankhula m’chigwirizano” pamene chibwera ku nkhani zauzimu, iwo amalandira thandizo loperekedwa ndi gulu la Yehova—ndipo limenelo liri thandizo lalikulu chotani nanga! (1 Akorinto 1:10) Tiri ndi kusefukira kokhazikika kwa chidziŵitso kupyolera m’maganizi a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tiri ndi unyinji wa mabukhu ndi mabroshuwa okwaniritsa mbali zochulukira za nkhani za Baibulo. Aŵerengi olankhula Chingelezi ali odalitsidwa mwapadera kukhala ndi Watch Tower Publications Index 1930-1985, chida chomwe chingathandize munthu ‘kupitiriza kufunafuna kaamba ka nzeru monga siliva ndi monga chuma chobisika.’—Miyambo 2:2-4.
21. (a) Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anasonyezera chikondwerero m’phunziro laumwini? (b) Ndi ati amene ali ena a malingaliro a kupititsira patsogolo phunziro laumwini?
21 Kodi mukutenga mwaŵi wokwanira wa zofalitsidwa za Sosaite mwa kuzigwiritsira ntchito izo kaamba ka kuphunzira ndi kufufuza? Kapena kodi zofalitisidwa zoterozo zimatumikira mochepera monga zokometsera pa shelufu? Mosangalatsa, mtumwi Paulo kamodzi analangiza Timoteo “kubweretsa . . . mabukhu, makamaka zikopa zija zolembera” kwa iye ku Roma; mwachidziŵikire, Paulo anali kulozera ku mbali za Malemba Achihebri. (2 Timoteo 4:13) Iye mosakaikira anafuna kukhala nazo pafupi ndi cholinga cha kuyendetsa bwino phunziro ndi kufufuza. Ngati simunachite kale chimenecho, bwanji osayamba kuwunjika laibulale yanu yanu ya zofalitsidwa za teokratiki kotero kuti nanunso mungachite kufufuza? Ikani zofalitisdwa zimenezo m’malo omwe mungakhoze kuzipeza, mwandongosolo, mwaudongo, ndipo mwaukhondo. Ikhani pambali malo ophunzirira omwe ali a bata ndi owunikiridwa bwino. Ndandalitsani nthaŵi zokhazikika kaamba ka phunziro laumwini.
22. Nchifukwa ninji ‘kuika mitima yathu ku mawu a Mulungu’ kuli kofunika koposa lerolino kuposa ndi kalelonse?
22 Mofanana ndi Aisrayeli opanga misasa pa chigwa cha chonde cha Moabu, tikuima pa mphepete penipeni pa dziko latsopano. Koposa ndi kale lonse, tifunikira kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi ‘kumadzipezera nthaŵi’ kaamba ka kuphunzira, mwinamwake kudzimana zikondwerero zina, monga ngati kuwonera wailesi ya kanema. (Aefeso 5:16) “Lirani monga makanda a lero mkaka woyenera,” anachenjeza tero Petro, “kuti mukakule nawo” osati kokha kufikira ku uchikulire koma “kufikira chipulumutso.” (1 Petro 2:2; yerekezani ndi Ahebri 5:12-14.) Miyoyo yathu yeniyeniyo ikukhudzidwa. Chotero tsutsani chikhoterero chirichonse cha kunyalanyaza m’phunziro laumwini. Igwiritsireni ntchito iyo monga njira yozamitsira chikondi chanu kaamba ka Mulungu ndi chikhulupiriro chanu mwa iye; iyonso iri njira yokwezera chiyamikiro chanu kaamba ka gulu limene iye akuligwiritsira ntchito kutithandiza ife. Inde, ‘ikani mtima wanu’ ku Mawu a Mulungu, mwakhama, mokhazikika. “Sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.”
[Mawu a M’munsi]
a Zidutswa zosweka zowumba, kapena mapale, zinali kugwiritsiridwa ntchito mofala m’nthaŵi za Baibulo monga chinthu cholembapo chotsika mtengo. Ikunena tero The International Standard Bible Encyclopedia (1986): “Mapale anakhoza kugwiritsiridwa ntchito ngakhale ndi magulu osauka koposa, omwe sakanatha kugula china chirichonse cholembapo.” Kuti ndi ku mlingo wotani kumene mapale anagwiritsiridwa ntchito ndi Aisrayeli akale kaamba ka kulemba malemba a Baibulo sichikudziŵika. Mosangalatsa, ngakhale ndi tero, mapale a m’zana lachisanu ndi chiŵiri C.E., okhala ndi malemba a m’Baibulo anapezedwa m’Igupto, kupereka lingaliro la njira imodzi mwa imene anthu wamba anakhalira ndi mbali za Baibulo.
Nsonga Kaamba ka Kubwereramo
◻ Nchifukwa ninji Mose anachenjeza Aisrayeli ‘kuika mitima yawo ku Mawu a Mulungu,’ ndipo ndimotani mmene iwo anayenera kuchitira icho?
◻ Ndimotani mmene phunziro laumwini limalimbikitsira unansi wathu ndi Mulungu ndi kutithandiza ife kuchinjiriza chikhulupiriro chathu?
◻ Kodi ndi mbali yotani imene phunziro laumwini limachita m’kutsutsa kwathu misampha ya Satana?
◻ Kodi ndi makonzedwe otani amene gulu la Yehova lapanga kupititsa patsogolo kuphunzira kwathu kwa Mawu a Mulungu?
[Chithunzi patsamba 11]
M’malo molemba Lamulo la Mulungu pa mitima yawo, Ayuda anadzimangirira ndi mipukutu yokhala ndi malemba