Kodi Anthu Abwino Onse Amapita Kumwamba?
“MALIRO anatha koma osati kuzizwitsidwa kozizira monga madzi owumako. . . . Chinawoneka chosakhulupirika kuti kokha milungu yochepa kumayambiriroko mnyamata wanga wachichepere anali kutenga masitepi oyambirira, nkhope yake yaing’ono iri yowala ndi chikondwerero cha chipambano. Koma tsopano Andrew anali wakufa! . . .
“Ndinapitirizabe kuima pa zenero, kyang’ana kunja mu mdima, kufunafuna kumwamba. ‘Kodi mnyamata wachichepereyo ali kuti tsopano?’ Ndinadabwa. ‘Kodi iye ali kwinakwake kumwamba kumeneko pakati pa nyenezi?’”
IMFA ya mwana mwinamwake iri chokumana nacho chothetsa nzeru chachikulu kwambiri chimene makolo angakhale nacho. ‘Kodi mwana wathu ali kuti tsopano?’ iwo amadabwa. ‘Kumwamba kapena kumalo ena?’ Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti ana omwe amafa amapita kumwamba. Mu Johannesburg, South Africa, mawu olembedwa pa mwala umodzi wa pa manda amaŵerenga kuti: “Mulungu anafuna duwa lotsegulira, mngelo wake anatenga lathu limodzi.” Koma wina angadabwe: ‘Nchifukwa ninji Mulungu akafuna “duwa lotsegulira” pamene, mogwirizana ndi chikhulupiriro chofala, iye ali nawo kale ambiri?’ Ndipo anthu osaŵerengeka amadabwa . . .
‘Kodi Kumwamba Kuli Monga Chiyani?’
Anthu ambiri ali kokha ndi lingaliro losadziŵika bwino la kumwamba. Ena mopepuka mtima amalankhula za “mkhalidwe mkati mwa mitambo pamene mufa.” Koma nchiyani chimene Baibulo limanena? Versi lake loyambirira lenilenilo limanena kuti: “Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Ichi chimalozera kumwamba kwa kuthupi, chiwonetsero cha ulemerero wa nyenyezi ndi milalang’amba. (Deuteronomo 4:19) Koma palinso kumwamba kwauzimu. Chotero, Baibulo limalankhula za “pokhala pokwezeka poyera ndi pa ulemerero” pa Yehova.—Yesaya 63:15, NW.
Ndani yemwe anali woyambirira “kukhala pokwezeka” pamenepa pa Atate wathu wa kumwamba? Mwana wake wokondedwa, Yesu Kirstu. Iye ananena kuti: “Kulibe munthu anakwera kumwamba koma iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) Ichi mwachiwonekere chiamsonyeza kuti palibe zolengedwa zaumunthu zomwe zinapitapo kumwamba. Koma Yesu analonjeza kuti anthu ena adzapita kumeneko. Nthaŵi yochepa asanakwere kupita kumwamba, iye anati kwa ophunzira ake okhulupirika: “Ndipita kukukonzerani inu malo . . . ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha, kuti kumene kuli ineko mukakhale inunso.”—John 14:2, 3.
Mwachidziŵikire, chotero, anthu ena abwino amapita kumwamba. Koma kodi anthu onse abwino amapita kumwamba? Bwanji ponena za kwawo kwa munthu—dziko lapansi? Kodi ilo likayenera kuwonongedwa ndi nkhondo ya nyukliya kukhala phulusa lowotchedwa lomayandama mu mlengalenga? Ndithudi ayi. Baibulo limanena kuti: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.” (Mlaliki 1:4) Ndipo nchifukwa ninji Mlengi ayenera kuwononga dziko lapansi lokongola iri, ngakhale kuti mbali za ilo zaipitsidwa ndi munthu wadyera? Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Machidziŵikire, chotero, dziko lapansi liri ndi mtsogolo mosangalatsa. Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu ananeneratu kuti: “Odala ali akufatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) M’kuwonjezerapo, bukhu lomalizira la Baibulo, Chivumbulutso, limasonyeza kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Ponena za mtundu wa anthu womvera, limanena kuti: “Mulungu yekha adzakhala nawo. Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira kapena chowawitsa zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3,4.
Kuchokera ku zomwe takambitsiranazi, chingawonedwe kuti anthu ena abwino amapita kumwaba, pamene kuli kwakuti ena adzasangalala ndi moyo pa dziko lapansi. Ichi chikutanthauza kuti pali magulu aŵiri osiyana a anthu okhudzidwa. Kodi chimenecho chiri chothekera motani? M’kuwonjezerapo, mofanana ndi mayi wa Andrew, ambiri amadandaula ponena za zimene zimachitika kwa ana awo omwe afa osabatizidwa. Aroma Katolika amaphunzitsidwa kuti iwo amapita ku malo otchedwa Limbo. Kodi kulidi malo oterowo? Kodi ana amapita kumeneko? Mayankho okhutiritsa ndi otonthoza akuperekedwa m’nkhani yotsatira.