Pamene Yehova Anaphunzitsa Mafumu Maphunziro
“Ntchito zake zonse nzowona ndi njira zake m’chiweruzo, ndi oyenda m’kudzikuza kwawo iye akhoza kuwachepetsa.”—DANIELI 4:37.
1. Ndi mikhalidwe iti ya Yehova imene Elihu akuitanira chisamaliro?
“TAWONANI! Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake; mphunzitsi wakunga iye ndani?” Mawu amenewa a Elihu olunjikitsidwa kwa Yobu wovutika amaitanira chisamaliro ku umodzi wa mikhalidwe yapadera ya Mlengi, Yehova Mulungu. Palibe aliyense amene angayerekezedwe ndi iye pamene chibwera u kulangiza, kapena kuphunzitsa, ena.—Yobu 36:22.
2, 3. (a) Ndi liti limene liri limodzi la maphunziro limene Yehova analipeza kukhala loyenerera kuphunzitsa anthu? (b) Ndani m’nthaŵi ya Mose amene anali wolamulira mmodzi amene Yehova anayenera kuphunzitsa phunziro iri, ndipo kupyolera mwa chiyani? (c) Ndi mobwerezabwereza motani m’Mawu ake mmene Mulungu amanenera chifuno chake cha kuphunzitsa anthu phunziroli?
2 Pakati pa zinthu zomwe chinakhala choyenera kwa Mulungu kuphunzitsa anthu ndi mitundu uli unansi wawo woyenera kulinga kwa iye. Ichi chawunikiridwa ndi mawu a wamasalmo Davide pa Salmo 9:19, 20: “Ukani, Yehova! Asalimbike munthu. Amitundu aŵeruzidwe pa nkhope panu. Muwachititse mantha, Yehova, adziŵe amitundu kuti ali anthu.”
3 Farao wa nthaŵi ya Mose anali pakati pa olamulira a pa dziko lapansi kwa amene Yehova Mulungu anachipeza icho kukhala choyenera kumuphunzitsa phunziro iri. Mulungu anachita tero mwa kugwiritsira ntchito miliri imene iye anaitumiza pa Aigupto. Ndiponso, Yehova anawuza Farao wodzikweza ameneyo kuti: “Koma ndithu, chifukwa chake ndakuimikira kuti ndikuwonetse mphamvu yanga ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.” (Eksodo 9:16) M’kuwonjezerapo, zoposa nthaŵi 70, kuchokera pa Eksodo 6:7 mpaka Yoweli 3:17, Yehova akunena m’Mawu ake kuti iye adzachita ntchito zamphamvu zofananazo kotero kuti mafumu, anthu, ndi mitundu akadziŵe kuti iye ali Yehova, Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.
4. M’nthaŵi ya Danieli, ndi olamulira atatu ati amene anaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo kupyolera mwa chiyani?
4 Unyinji wa zitsanzo zosangalatsa za mmene Yehova anaphunzitsira mafumu zalembedwa m’bukhu la Danieli. Olamulira amenewa anali Nebukadinezara, Belisazara, ndi Dariyo. Ndi liti pamene anawaphunzitsa iwo? Mwachidziŵikire pakati pa 617 B.C.E. ndi 535 B.C.E. Ndipo motani? Kupyolera mwa maloto ndi kumasulira kwawo ndi mwa zisonyezero za mphamvu yake. Yehova anaphunzitsa olamulira a umunthu amenewa kuti iye ali Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe ndi kuti iwo anali kokha anthu wamba—maphunziro amene alamulira a dziko a nthaŵi ino ayeneranso kuphunzira.
5. Ndi kupyolera mwa umboni wotani umene awo amene amakaikira kuwona kwa bukhu la Danieli angatsutsidwire?
5 Koma kodi kuwona kwa bukhu la Danieli sikumakaikiridwa ndi osuliza ambiri amakono? Mkuyankha osuliza amenewa, wophunzira Baibulo wina analongosola bwino kuti: “Zozizwitsa zimene limagwiritsira ntchito, maulosi amene limatsimikizira kukhala owona, kukhala analembedwa ndi Danieli munthu wamoyo. Chotero kaya tiri ndi zozizwitsa zowona ndi ulosi wowona, kapena sitiyenera kukhala ndi china chirichonse koma chosakhala chowonadi.” (Daniel the Prophet, lolembedwa ndi E. B. Pusey, tsamba 75) Nkulekeranji, popeza kwa nthaŵi ndi nthaŵi wolemba wa bukhulo amadzizindikiritsa iyemwini, monga ngati mwa kunena kuti, “Ine, Danieli”! (Danieli 8:15; 9:2; 10:2) Kodi zonsezi zinali zobera? Chenicheni chiri chakuti isanafike mbali yoyambirira ya zana la 18, ukonzi wa bukhu la Danieli sunakaikiridwe ndi Ayuda kapenanso Akristu. Ngakhale kuli tero, wotenga mphamvu yokulira kuposa lingaliro la wophunzira Baibulo aliyense wamakono uli umboni wa m”malemba wonena za bukhu la Danieli. Chotero, timapeza Danieli akutchulidwa nthaŵi zitatu m’bukhu la Ezekieli. (Ezekieli 14:14, 20; 28:3) Othetsa nkhani pa onse ali mawu a Yesu, Mwana wa Mulungu, monga mmene alembedwera pa Mateyu 24:15, 16: “Chifukwa chake mmene mukadzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli mneneri, chitaima m’malo oyera, (iye amene aŵerenga m’kalata azindikire,) pomwepo iwo ali m’Yudeya athaŵire ku mapiri.”a
Nebukadinezara Aphunzira Amene Mulungu Wowona Ali
6. Nchiyani chomwe chingakhale chinathetsa kunyada kwa mfumu ya Babulo, ndipo nchiyani chimene iye ananena ponena za iyemwini m’zolemba zake?
6 Monga mmene mneneri Yesaya akusonyezera, mafumu a Babulo anali anthu onyada kwambiri. (Yesaya 14:4-23) Nebukadinezara analinso munthu wa chipembedzo koposa. M’zolemba zake iye ananena za “mapulojekiti ake omanga ndi chisamaliro chake ku milungu ya Chibabulo.” Mosakaikira icho chinafika m’mutu mwake kuti iye anapambana m’kutenga Yerusalemu ndi Yuda yense pambuyo pakuti Sanakeribu mosakaza analephera m’kuyesera kwake kuchita ichi.
7. Ndi chokumana nacho chotani chosimbidwa mu Danieli mutu 1 chomwe chingakhale chinaphunzitsa Nebukadinezara kulemekeza Mulungu wa Ahebri?
7 Pambuyo pakuti Danieli ndi mabwenzi ake atatu a Chihebriwo anawonekera pamaso pa Nebukadinezara, iye motsimikizirika anali ndi chifukwa cha kulemekezera Mulungu wawo, popeza “mawu aliwonse a nzeru ndi a luntha amene mfumu inawafunsira, inawapeza koposa [nthaŵi khumi, NW] alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.” Inde, anzeru onse omwe anali ndi Yehova monga Mulungu wawo mokulira anapambana awo onse omwe anali kulambira milungu ina. Nebukadinezara sakanalephera kuzindikira nsonga imeneyo.—Danieli 1:20.
8. Ndi kupyolera mwa njira yotani imene Yehova anavumbulutsira anthu anzeru a ku Babulo kukhala opanda chidziŵitso chapadera?
8 Yehova anali ndi zowonjezereka za kuphunzitsa Mfumu Nebukadinezara. Phunziro lotsatira linalembedwa mu Danieli mutu 2. Mulungu anapangitsa mfumuyo kukhala ndi loto lowopsya ndipo kenaka kumpangitsa iye kuliiwala ilo. Loto limeneli linakwiyitsa mokulira mfumu ya Babulo, ndipo iye anaitana kaamba ka amuna ake anzeru onse kumuuza iye lotolo ndi kumasulira kwake. Ndithudi, iwo sakanavumbula lotolo, kutalitali m’kupereka kumasulira kwake, mwakutero kuvomereza mwa kachetechete kuti iwo analibe chidziŵitso chapadera. Ichi chinapangitsa mfumuyo kukwiya kotero kuti inalamulira kuphedwa kwa iwo onse. Pamene Danieli ndi mabwenzi ake anawuzidwa lamulo la mfumulo, Danieli anafunsa kaamba ka kanthaŵi kena, komwe iye anapatsidwa. Kenaka iye ndi mabwenzi ake atatu anaipanga iyo kukhala nkhani ya pemphero lofunitsitsa, ndi chotulukapo chakuti Yehova anavumbula lotolo ndi tanthauzo lake kwa Danieli.—Danieli 2:16-20.
9. (a) Ndi yekha amene anali wokhoza kumasulira loto la Nebukadinezara, ndipo ndi kumasulira kwa mtundu wotani kumene Ameneyu anapereka? (b) Monga chotulukapo chake, ndi kumapeto otani kumene mfumuyo inafika?
9 Pamene Danieli anabweretsedwa pamaso pa mfumu, Nebukadinezara anamfunsa iye: “Ukhoza kodi kundidziŵitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake?” Pambuyo pa kukumbutsa mfumu yonyadayo kuti amuna ake anzeru anali osakhoza kumuuza iye chinsinsi cha loto lake ndi kumasulira kwake, Danieli ananena kuti: “Kuli Mulungu kumwamba Wakuvumbulutsa chinsinsi, iye ndiye wadziŵitsa Mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza.” Akumapitiriza, Danieli anawuza mfumuyo ponena za chifano chachikulu chimene iye anachilota ndi chimene icho chinatanthauza. Mfumuyo inasangalatsidwa mokulira kotero kuti iye analengeza kuti: “Zowona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu ndi Mbuye wa mafumu ndi Wakuvumbulutsa zinsinsi, popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.” Chotero Yehova anaphunzitsa Mfumu Nebukadinezara kuti Iye ali Mulungu mmodzi wowona.—Danieli 2:26, 28, 47.
10, 11. (a) M’kunyada kwake kwakukulu, nchiyani chimene Mfumu Nebukadinezara anapanga, kotsatiridwa ndi lamulo lotani? (b) Mwa kukana kulabadira lamulo la mfumu, ndi nkhani yotani imene Ahebri atatu anawutsa, ndipo ndi chotulukapo chotani?
10 Ngakhale kuti Mfumu Nebukadinezara mosakaikira anasangalatsidwa ndi chidziŵitso ndi nzeru ya Mulungu wa Ahebri, iye anali adakali ndi zambiri zophunzira. M’kunyada kwake, iye anakhazikitsa chifano chachikulu cha golidi pa chigwa cha dura. Chifanocho chinali cha msinkhu wa mikono 60 ndi thunthu lake la mikono 6, kuitanira ku maganizo athu nambala ya 666 yomwe iri chizindikiro cha “chiromba” cha Satana chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:18. (Mkono ukumakhala chifupifupi mamita 0.5, chifanocho chinali cha chifupifupi msinkhu wa mamita 27 ndi thunthu la chifupifupi mamita 2.7.) Mfumuyo inalamulira nduna zonse za ulamuliro wake kuti “abwere kuzulura fanoli” ndi kulamulira kuti pamene oyimba anayimba, onse anayenera kugwa pansi ndi kulambira fanolo. Nduna za Akasidi zina zokhumbira, powona kuti Ahebri atatuwo omwe analipo sanagawane mu mwambowo, anawaneneza iwo kwa mfumu.—Danieli 3:1, 2.
11 Iyi inali nkhani yowopsya kwambiri kwa Nebukadinezara, popeza iye anali atanyada kuti anali “amene anaika m’kamwa mwa anthu ulemu kaamba ka milungu yaikulu.” Chotero, ponse paŵiri ukulu wa ulamuliro wa Nebukadinezara ndi kudzipereka kwake kwa chipembedzo zinalakwiridwa mokulira. Akumayankha mu mkwiyo ndi ukali, mfumu yodzikwezayo inapatsa Ahebri atatuwo mwaŵi wina koma ndi lamulo lokulira iri: “Mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthaŵi yomweyo mkati mwa ng’anjo yotentha ya moto. Ndipo mulungu amene adzakulanditsani m’manja mwanga ndani?” Chabwino, Nebukadinezara anayenera kupeza kuti Mulungu wawo analidi wokhoza kupulumutsa atumiki Ake kuchoka m’dzanja la mfumu yopanda pakeyo ndi kuti palibe mulungu wina aliyense yemwe angapulumutse mofanana ndi Mulungu wa Ahebriwo.—Danieli 3:15.
Loto la Mtengo
12, 13. (a) Ndi kumasulira kotani kumene Danieli anapatsa Nebukadinezara ponena za loto lake la mtengo? (b) Ndimotani mmene Nebukadinezara anasonyezera kuti kumasulira kwa lotolo kunalibe chotulukapo cha kudzichepetsa kwa iye?
12 Ndimotani mmene kuphunzira maphunziro amenewo kukanakuyambukirirani inu? Mowonekera, maphunziro atatu amenewa sanali okwanira kupanga Mfumu Nebukadinezara kudziŵa malo ake. Chotero Yehova anayenera kumuphunzitsa iye phunziro linanso. Kachiŵirinso, loto linaloŵetsedwamo, ndipo kachiŵirinso, palibe aliyense wa anzeru a Babulo yemwe anali wokhoza ulimasulira ilo. Potsirizira pake, Danieli anaitanidwa, ndipo iye anali wokhoza kuuza mfumu tanthauzo la lotolo, lotchedwa, kuti kwa zaka zisanu ndi ziŵiri iye akakhala ngati “nyama za kuthengo,” ndipo kenaka iye akabwerera ku umoyo wake wabwino.—Danieli 4:1-37.
13 Kuchokera ku zimene zinatsatira, chiri chodziŵikiratu kuti lotolo linalephera kukhala ndi chotulukapo chodzichepetsa pa Nebukadinezara. Chotero, chifupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, pamene mfumuyo inali kuyendayenda m’nyumba yake yachifumu, iye monyada anadzitukumula kuti: “Suyu Babulo Wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu ndi mphamvu yanga yaikulu uwoneke ulemerero wa chifumu changa?” Ndi lingaliro lotani nanga! Chotero kunali kuti pa nthaŵi yomweyo liwu linamveka kuchokera kumwamba kuuza wolamulira wodzikwezayo kuti ufumu wake ukachotsedwa kwa iye ndipo akakhala ndi zirombo za kuthengo kwa nthaŵi zisanu ndi ziŵiri, “mpaka udzadziŵa kuti Wam’mwambamwamba Alamulira mu ufumu wa anthu.”—Danieli 4:30-32.
14. Ndimotani mmene loto lonena za mtengo linakwaniritsidwira, ndipo ndi chotulukapo chotani pa Nebukadinezara?
14 Pambuyo pakuti Nebukadinezara anakhala monga nyama kwa nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zimenezo, kapena zaka, Yehova anabwezeretsa kumvetsetsa kwake ndipo iye anayenera kuvomereza ‘kuti palibe angapulumuke dzanja la Wam’mwambamwamba kapena kunena kwa iye kuti: Nchiyani chimene unali kuchita?’ Choposa chimenecho, wolamulira wa Chibabuloyo anasonyeza kuti iye mowonjezereka anaphunzira phunziro lake, mwa kunena kuti: “Tsono ine, Nebukadinezara, ndiyamika nid kukuza ndi kulemekeza Mfumu ya kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzowona, ndi njira zake n’chiŵeruzo ndi oyenda m’kudzikuza kwawo”—monga mmene mfumuyo inachitira—“iye akhoza kuwachepetsa.” Kodi umboni wonse woterowo ponena za njira mu imene Yehova mobwerezabwereza anakhazikitsira nkhani ya ulamuliro yeniyeniyo suli umboni wamphamvu m’mikhalidwe yonse kuti zolembedwa zimenezi siziri mbali za malingaliro a wina wake koma ziri ntchito za wolemba wowuziridwa ndi Mulungu kulemba mbiri yakale yeniyeni?—Danieli 4:35, 37.
Belisazara Awona Dzanja Lolemba pa Khoma
15. Ndimotani mmene Belisazara anasonyezera chitonzo kaamba ka Mulungu wowona, Yehova?
15 Mfumu ina imene Yehova anali ndi nthaŵi ya kuphunzitsa anali Belisazara. Iye anali mwana ndi m’lowa m’malo wa Mfumu Nabonidasi, iyemwini mwana wa Nebukadinezara. Pa chochitika cha phwando lalikulu, Belisazara anali ndi kulimba mtima kwa kulamula kuti zotengera za golidi zimene atate wake anazitenga mu kachisi wa Yehova m’Yerusalemu zibweretsedwe kotero kuti iye, akulu ake, azikazi ake, ndi akazi ake ang’ono amweremo. Chotero “iwo anamwa vinyo, nalemekeza milungu ya golidi ndi ya siliva, m’kuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala.”—Danieli 5:3, 4.
16, 17. (a) Ndi kupyolera mwa chiyani mmene Yehova anaikira mantha mwa Belisazara? (b) Ndi kumasulira kotani kumene Danieli anapereka ponena za dzanja lolemba pa khoma, ndipo ndimotani mmene kunatsimikizidwira kukhala kowona?
16 Nthaŵi ya Mulungu inabwera kutsiriza ulamuliro wa Babulo. Chotero, iye anapangitsa dzanja lolemba lachilendo kuwoneka pa khoma. Chozizwitsa chimenechi chinadodometsa mokulira mfumuyo kotero kuti nthaŵi yomweyo anaitana kaamba ka amuna ake anzeru onse kumasulira ilo. Palibe ndi mmodzi wa iwo amene anatha. Kenaka mayi wake anamukumbutsa iye kuti Danieli, yemwe anamasulira maloto kwa Nebukadinezara, akakhala wokhoza kumasulira dzanja lolembalo. (Danieli 5:10-12) Pamene anaitanidwa ndi kufunsidwa ngati iye angachite tero, Danieli anakumbutsa mfumuyo za mmene Mulungu anachepetsera agogo ake amuna onyada kotero kuti iye akadziŵe kuti Wam’mwambamwamba Alamulira mu ufumu wa anthu.—Danieli 5:20, 21.
17 Danieli mowonjezereka anauza Belisazara: “Mulungu amene m’dzanja lake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse yemweyo simunamchitira ulemu.” (Danieli 5:23) Chotero dzanja lolembalo linatumikira monga chidziŵitso pa wolamulira wa Chibabuloyo kuti masiku a ufumu wake afika kumapeto, kuti iye anayesedwa ndi kupezeka woperewera, ndi kuti ufumu wake ukayenera kuperekedwa kwa Amedi ndi Aperesi. Ndipo usiku womwewo, pambuyo pakuti Yehova anaphunzitsa mfumu yodzikwezayo phunziro lofunikira koposa limeneli, Belisazara, mfumu ya Akasidi, anaphedwa.—Danieli 5:30.
18. Ndi kupyolera mwa chiyani mmene Yehova adzaphunzitsira olamulira a dziko a lerolino maphunziro ofananawo ponena za ulamuliro wake ndi mphamvu ya kupulumutsa?
18 Mongadi mmene Yehova anaphunzitsira mafumu onyada Nebukadinezara ndi Belisazara maphunziro ponena za ulamuliro wake ndi mphamvu yake yopulumutsa, choteronso pa Armagedo Mulungu adzapangitsa olamulira onse a dziko lapansi kudziŵa kuti iye ali Wolamulira Wamkulu, Mfumu ya Chilengedwe Chonse yamphamvuyonse. Moyo wanu udzayambukiridwa. Motani? Chifukwa chakuti pa nthaŵi imeneyo Yehova adzapulumutsanso atumiki ake okhulupirika, mongadi mmene iye anapulumutsira Ahebri atatu kuchokera ku ng’anjo ya moto.—Danieli 3:26-30.
Dariyo Aphunzira Ponena za Mphamvu Yopulumutsa ya Yehova
19, 20. Ndi chochitika chotani m’moyo wa Danieli chimene chinaphunzitsa Dariyo ponena za mphamvu yopulumutsa ya Yehova?
19 Danieli mutu 6 amanena za chochitika china m’chimene Yehova anaphunzitsa mfumu, Dariyo, phunziro—lija la mphamvu yopulumutsa ya Mulungu. Chiwembu chinatulukapo m’kupangitsa mfumuyo kuponya Danieli m’dzenje la mikango, mokulira molimbana ndi chifuno cha mfumuyo. Iye sanali mmodzi amene monyada anadzikweza iyemwini molimbana ndi Mulungu wowona. Mosangalatsa, ngakhale kuti Dariyo anatsimikizira Danieli kuti Mulungu wake akamupulumutsa iye, iye m’chenicheni sanawonekere kukhulupirira ichi mokwanira. Kupanda apo, nchifukwa ninji iye anakhala wosagona usiku wonse ndi kudera nkhaŵa kufikira mbandakucha, pamene iye anathamangira ku dzenje la mikango? Iye kenaka anaitana: “Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza wakhoza kukulanditsa kwa mikango?”—Danieli 6:18-20.
20 Inde, Mulungu anali wokhoza kutetezera Danieli. Mfumu Dariyo anali wosangalala kwambiri kotero kuti iye anapereka lamulo iri: “M’maiko onse a ufumu wanga, anthu anjenjemere naope pamaso pa Mulungu wa Danieli. Pakuti iye ndiye Mulungu wamoyo Wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngosawonongeka . . . Iye apulumutsa nalanditsa nachita zizindikiro ndi zozizwa m’mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Danieli ku mphamvu ya mikango.”—Danieli 6:26, 27.
21. (a) Kodi mitu yoyambirira isanu ndi umodzi ya bukhu la Danieli imapereka zitsanzo zosangalatsa zotani? (b) Ndi chiyambukiro chotani chimene cholembera cha zinthu izi chiyenera kukhala nacho pa ife?
21 Mitu isanu ndi umodzi yoyambirira ya bukhu la Danieli mowonadi imatipatsa ife zitsanzo zosangalatsa za mmene Yehova, pokhala wachangu—inde, wansanje—kaamba ka dzina lake anaphunzitsa mafumu amphamvu a dziko iri kuti iye ndithudi ali m’Modzi wa mphamvu zonse, Wolamulira Wachilengedwe Chonse, wokhoza kuchepetsa olamulira odzikweza pamene iye akupulumutsa atumiki ake okhulupirika. Zolembera zimenezi ziyenera kuika mwa ife mantha owona a Mulungu ndi ulemu kaamba ka mphamvu zonse ndi ulamuliro wa Yehova. Pa nthaŵi imodzimodziyo, cholembedwa chowuziridwa chimenechi chiri cholimbikitsa chikhulupliriro koposa chifukwa chakuti chimapereka zitsanzo zabwino kwambiri za atumiki a Yehova Mulungu omwe anasonyeza chikhulupiriro chokulira ndi kulimba mtima, monga mmene nkhani yotsatirayi idzasonyeza mowonekera.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda, October 1, 1986, masamba 3-7.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Ndi phunziro lotani limene lakhala loyenerera kwa Yehova kuphunzitsa olamulira a dziko?
◻ Nchiyan chomwe chinganenedwe ponena za kuwona kwa bukhu la Danieli?
◻ Ndi liti lomwe linali phunziro limene mowonjezereka linachepetsa Mfumu Nebukadinezara?
◻ Ndi chiyambukiro chotani chimene kuphunzitsa mafumu maphunziro kwa Yehova kuyenera kukhala nako pa ife?