Kumaliza Maphunziro kwa Kalasi ya Gileadi ya 85 Chochitika Chosangalatsa
KUTSATIRA kuperekedwa kwa kachisi zaka zina 3,000 zapitazo, Solomo “anawauza anthu apite ku mahema awo, akusekera ndi kukondwera mu mtima mwawo.” (2 Mbiri 7:10) Mawu amenewo amalongosola bwino kudzimva kwa anthu oposa 4,000 pamene anali kuchoka pa Jersey City Assembly Hall of Jehovah’s Witnesses pa September 11, 1988. Chochitikacho? Kumaliza maphunziro kwa kalasi la 85 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower.
Pambuyo pa nyimbo, programu inatsegulidwa ndi pemphero lochokera mu mtima ndi W. L. Barry, chiwalo cha Bungwe Lolamulira. T. Jaracz, nayenso wa Bungwe Lolamulira, anachita monga tcheyamani kaamba ka tsikulo. ‘Kuti chochitikachi chikhale chipatsa mpumulo mowonadi ndi chomangirira mwauzimu,’ anatero Jaracz, ‘mzimu wa Yehova ndi madalitso ake akufunikira.’ Ndithudi, zimenezi zinali zowonekera pamene programuyo inafutukuka.
Kutsatira ndemanga zolonjera zimenezi, omaliza maphunzirowo analandira uphungu wa kulekana m’mipambo ya nkhani zazifupi, zogwira ntchito. R. L. Rains wa Komiti ya Beteli analankhula choyamba. Akumazika ndemanga zake pa Genesis 12:1, 2, Rains anachenjeza ophunzirawo kuti: ‘Tsimikizirani kukhala dalitso m’gawo lanu la umishonale.’ Ndipo ndimotani mmene angachitire tero? ‘Chiri mwa njira yanu ya moyo mwamsanga mutafika kumeneko,’ iye anagogomezera. Iye kenaka anawunikira nsonga ziŵiri zomwe zikathandiza mokulira: (1) Iwo ayenera kuzindikira kuti afunikira kupanga masinthidwe ena ndi cholinga chofuna kusinthira ku magawo awo atsopano; ndipo (2) ayenera kusungirira unansi wa mtendere ndi ena.
M’njira yotentha, yolimbikitsa, J. E. Barr wa Bungwe Lolamulira analankhula potsatira, akumalankhula ndi omaliza maphunzirowo pa mutu wakuti “Tipatseni Chikhulupiriro Chowonjezereka,” yozikidwa pa Luka 17:5. ‘Kumbukirani tsiku lirilonse,’ Barr anachenjeza tero, ‘kufunsa Yehova kukupatsani chikhulupiriro chowonjezereka.’ Iwo nthaŵi zonse ayenera kusunga m’maganizo chifukwa chenicheni chimene Yehova wawatumizira iwo ku magawo awo. ‘Zindikirani mphamvu ya gulu losawoneka limodzinso ndi lowoneka la Mulungu yokuchirikizani inu nthaŵi zonse, usana ndi usiku,’ anafulumiza tero Barr. ‘Simungapemphe mobwerezabwereza koposa m’mapemphero anu, “Yehova, chonde ndipatseni chikhulupiriro chowonjezereka.”’
Chikhumbo chofuna kudziŵa chinadzutsidwa pamene tcheyamani analengeza mutu wa mlankhuli wotsatira, F. D. Songer wa Komiti ya Fakitale: “Choikiza Chapadera ndi Mfungulo Yapadera.” Songer anatenga ndemanga zake kuchokera pa 1 Mbiri 9:26, 27 ndi chimene chanenedwa pamenepo ponena za odikira pa zipata a Chilevi. ‘Ntchito yawo inali chimodzi cha zoikiza zapadera,’ analongosola tero Songer. Iwo anali ndi mfungulo—chiwiya chosonyeza mphamvu yeniyeni ya kulamulira pa zipata ku malo opatulika a kachisi. Iwo anali odalirika, akumatsegula zipatazo modalirika m’mawa mulimonse. M’kumaliza, Songer anawuza omaliza maphunzirowo: ‘Mwapatsidwa choikiza chapadera ndi mfungulo yapadera, monga momwe kunaliri, zimene mukatsegulira, m’mawa mulimonse, kwa awo ofuna kulowa ku mabwalo a kulambira kowona. Chinjirizani choikiza cimenecho bwino lomwe ndipo gwiritsirani ntchito mfunguloyo modalirika.’
Chotsatira, M. G. Henschel wa Bungwe Lolamulira analankhula pa mutu wakuti “Gwirani Chitsanzo cha Mawu a Moyo.” Akumalozera ku 2 Timoteo 1:13, 14, Mbale Henschel analongosola kuti uphungu wopatukana wa Paulo kwa Timoteo unali wakuti: ‘Gwiritsira ntchito chitsanzo cha mawu a moyo chomwe walandira kuchokera kwa ine, ndipo chichinjirize monga chuma, [choikizidwa, NW].’ Omaliza maphunzirowo, nawonso, analandira chuma. Popeza kwa miyezi isanu yapitayo, iwo anaphunzira Baibulo ndi nkhani zokhudza utumiki. ‘Malangizo amenewa, chitsanzo chimenechi cha mawu a moyo,’ analongosola tero Henschel, ‘chiri chinachake chimene Mulungu wachiika m’manja mwanu kuchigwiritsira ntchito, osati kokha kwa inu eni, ayi, koma kwa ena.’
Ndi uphungu wopatukana wotani umene alangizi aŵiri a sukuluyo ali nawo kaamba ka ophunzira awo? J. D. Redford analankhula choyamba pa mutu wakuti “Vomerezani Zolakwa Zanu.” Redford anadziŵitsa kuti ngakhale kuti timadziŵa kuti “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri,” ngati tiimbidwa mlandu wa kupanga cholakwa, timakhoterera pa kudzilungamitsa ife eni. (Yakobo 3:2) ‘Kukana kuvomereza zolakwa zathu kuli kofanana ndi kudzinenera kukhala wangwiro,’ anatero Redford. Kuvomereza zolakwa zathu iri njira yanzeru. Tero motani? Mlankhuliyo analongosola kuti: ‘Palibe wina aliyense amene angasungilire ulemu wa ena ngati awumirira kuti ali wolondola ngakhale pamene akumanizana ndi cholakwa chodziŵikiratu. Ndimotani mmene wina aliyense angakhalire ndi chidaliro mwa munthu amene akudziŵa kuchokera ku chokumana nacho kuti angapereke ngakhale chowona kokha kuti apereke kawonekedwe kakuti ali wolondola? Kuvomereza cholakwa kumamangilira mwa ife mphamvu, ulemu wa umwini. Koma kulephera kuchita tero kuli mantha, ndipo kumatumikira kutifooketsa ife mwa makhalidwe abwino.’ Kugwiritsira ntchito uphungu wogwira ntchito woterowo mosakaikira kudzathandiza omaliza maphunzirowo kukhala bwino ndi ena.
U. V. Glass, mlangizi wina ndi registrar wa sukuluyo anazika chenjezo lake lomalizira pa mbiri ya Baibulo ya Gideoni, amene Yehova anamgwiritsira ntchito kupulumutsa Aisrayeli kuchoka m’dzanja la Amidyani. (Oweruza, mitu 6-8) Gideoni anasonyeza kuti chidaliro cha Yehova mwa iye sichinaikidwe molakwika, popeza kuti pamene anthu anafuna kupanga iye kukhala mfumu, iye anakana, akumanena kuti: “Yehova adzalamulira inu.” (Oweruza 8:23) ‘Nanunso,’ anatero Glass, ‘simufuna kukwezedwa. Mwadzitsimikizira inu eni. Koma ichi sichimatanthauza kuti inu ndi amene mukumenya nkhondo. Ali Yehova yemwe akukuchirikizani.’
Mlankhuli womalizira wa m’mawamo anali A. D. Schroeder wa Bungwe Lolamulira, ndipo chinali chachidziŵikire pamene iye analankhula kuti Sukulu ya Gileadi iri mu mtima mwake. Ndipo kaamb ka chifukwa chabwino—iye anali registrar pamene sukuluyo inakhazikitsidwa mu 1943. Mbale Schroeder anakulitsa mutu wakuti “Khalani Okhulupirika,” wozikidwa pa 1 Akorinto 4:2. Kodi kukhala okhulupirirka kumaphatikizanji? ‘Kumalongosola kukhala kwa wina wodzazidwa ndi chikhulupiriro mu zilengezo ndi malonjezo a mtengo wapatali a Yehova Mulungu,’ analongosola tero Schroeder. ‘Kumatanthauzanso kuti wina ali wowona, wokhazikika, wokhulupirika kwa Yehova.’ Kodi pali zitsanzo zina zirizonse za awo omwe apezedwa kale kukhala okhulupirika? Panali amuna ndi akazi a nthaŵi ya Chikristu isanafike otchulidwa pa Ahebri mutu 11; Yesu Kristu; ndi atumwi ndi ophunzira ena odzozedwa a zana loyamba C.E. Pambuyo pa kuitanira chisamaliro ku zitsanzo zina zamakono, Mbale Schroeder anafunsa kuti: ‘Bwanji ponena za ife?’ Iye anawonjezera kuti: ‘Imangokhala nkhani ya kaya muli okhulupirika kapena muli osakhulupirika. Kaya tiri a odzozedwa kapena a khamu lalikulu, tonsefe, magulu onse aŵiriwo, tiyenera kukhala mofananamo okhulupirika ku chiitano chathu.’
Kutsatira ndemanga za Mbale Schroeder, tcheyamaniyo anapereka moni wolandiridwa kuchokera ku maiko osiyanasiyana. Nthaŵi tsopano inafika kaamba ka ophunzirawo kulandira madipuloma awo. Ophunzira 22 anabwera kuchokera ku maiko asanu ndi limodzi—Canada, Finland, Germany, Great Britain, Sweden, ndi United States. Magawo awo, ngakhale ndi tero, akawatumiza iwo ku maiko osiyanasiyana 11—Belize, Dominica, Ecuador, El Salvador, Hong Kong, Lesotho, Pakistan, Paraguay, Puerto Rico, Senegal, ndi Taiwan. Ndipo nchiyani chimene omaliza maphunzirowo anali nacho chonena pa tsiku lawo la kumaliza maphunziro? Mmodzi wa ophunzirawo anaŵerenga kalata yolemberedwa ku Bungwe Lolamulira ndi banja la Beteli, yomwe inanena m’mbali kuti: “Tikuyamikirani nonsenu kachiŵirinso kaamba ka kupanga miyezi isanu iyi kukhala yokumbukirika koposa m’miyoyo yathu yonse.”
Pambuyo pa kupuma, W. L. Van De Wall wa Komiti ya Dipartmenti Yautumiki anayamba programu ya masana mwa kutsogoza Phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda. Kutsatira ichi, ophunzirawo anapanga programu yachidule, kuchitira chitsanzo zokumana nazo zoŵerengeka zosangalatsa—ndipo nthaŵi zina zoseketsa—zomwe anali nazo pamene anali kucitira umboni mu Mzinda wa New York. Kenaka, onse opezekapo, kuphatikizapo kalasi la 85, anasangalala ndi programu yapadera yokhala ndi mutu wakuti “Kuzolowerana Bwino Ndi Amishonale Athu Achangu.” Kupyolera mu zithunzithunzi ndi zojambulidwa, khamulo linali lokhoza kuwona—ndi kumva—amishonale ena a nthaŵi zakale.
Monga mapeto oyenerera, ophunzirawo anaika chitsanzo cha Baibulo atavala zovala akugogomezera kufunika kwa kuchita chifuno cha Mulungu ndi changu. Pambuyo pa nyimbo yomalizira, mmodzi ndi onse anakhudzidwa mozama pamene F. W. Franz, prezidenti wa zaka 95 zakubadwa wa Watchtower Society, anapereka pamphero lotsekera la mtima wonse. Kutsatira ichi, onse anapita “m’mahema awo, akusekera ndi kukondwera mu mtima mwawo.”
Yokhazikitsidwa mu 1943, Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower imaphunzitsa ndi kutumiza amishonale ku mbali zonse za dziko lapansi. Kwa makalasi 35 oyambirira, sukuluyo inali pa Kingdom Farm ya Watchtower Society, pafupi ndi South Lansing, New York. Ndi kalasi ya 36, kuyambira February 6, 1961, sukuluyo inasamutsidwira ku malikulu a Sosaite mu Brooklyn, New York, kumene yakhala ikugwira ntchito kufikira tsopano. Ngakhale kuli tero, ndi kuyambika kwa kalasi ya 86 pa October 17, 1988, sukuluyo ikusamutsidwira ku Watchtower Farms, pafupi ndi Pine Bush, New York.
[Bokosi patsamba 21]
Chiŵerengero cha Kalasi:
Avereji ya zaka: 29.1
Avereji ya zaka m’chowonadi: 13.4
Avereji ya zaka mu utumiki wa nthaŵi zonse: 9.1
Chiŵerengero cha abale osakwatira: 2
Chiŵerengero cha okwatirana: 10
[Chithunzi patsamba 23]
Kalasi ya Omaliza Maphunziro ya 85 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
Mu ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kunka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera ku lamanzere kunka ku lamanja mumzera uliwonse.
(1) Johnston, Y.; Kuismin, S.; Ugarte, Z.; Williams, Z.; Grischkewitz, G. (2) Powers, E.; D’Angelo, L.; Honsberger, J.; Williams, J.; James, J. (3) Kuismin, V.; Grischkewitz, U.; Ugarte, R.; Rogerson, A.; Lantunen, K.; James, D. (4) Rogerson, M.; Johnston, R.; D’Angelo, T.; Honsberger, T.; Powers, T.; Danielson, M.