“Chodzala ndi Maina a Mwano”
BUKHU la Baibulo la Chibvumbulutso limalongosola masomphenya a “chirombo chofiiritsa chodzala ndi maina a mwano.” Icho chikhalako kwa kanthaŵi, kenaka chiloŵa m’phompho kumene pambuyo pake chituluka. (Chibvumbulutso 17:3, 8) Mobwerezabwereza, masamba a magazini ino azindikiritsa chirombo chofiiritsa chimenechi, poyambirira, ndi Chigwirizano cha Amitundu ndipo, pambuyo pake, choloŵa m’mwalo chake, Mitundu Yogwirizana. Koma kodi nchifukwa ninji chirombo chofiiritsa chikunenedwa kukhala “chodzala ndi maina a mwano”?
Kulembedwa koyamba kwa Pangano la Chigwirizano cha Amitundu, kozikidwa pa malingaliro ogwirizana a Chibritish ndi Chiamerica, kunadziŵikitsidwa poyera pa February 14, 1919. Tsiku lotsatira, m’nkhani yokhala ndi mutu wakuti “The League of Peace,” (Chigwirizano cha Mtendere) The Times ya ku London inanena kuti: “Chiri chochititsa kunyada koyenera kuzindikira m’Panganolo ntchito yochuluka chotero ya Angelezi. . . . Tiri ofunitsitsa kunena kuti iri kalata ya mitundu yonse yofunika kwambiri yosafalitsidwapo chikhalire.” George Thayer, minisitala wa First Congregational Church of Cincinnati mu United States, anailongosola iyo kukhala “chilengezo chapamwamba koposa cha chifuno ndi chikhumbo cha anthu otsungula a dziko lapansi chomwe sichinalembedwepo ndi kalelonse.” Chitamando chinabweranso kuchokera ku manyuzipepala a zinenero zachilendo. “Iyo sirii Baibulo,” inanena tero nyuzipepala ya Chifrench L’Homme Libre, “koma iri yothekera kukhala yoposa pamenepo, popeza kuti kulibe Baibulo, kapena Mlaliki aliyense chikhalire amene analetsapo anthu kuphana wina ndi mnzake. Malingaliro asandulika kukhala chenicheni.” Nyuzipepala ya Chifrench Victoire inachilongosola icho kukhala “kuyesayesa kokulira kogwirizana komwe sikunapangidwepo kuchokera pachiyambi cha dziko lapansi kaamba ka kukhazikitsa kulingalira ndi chilungamo pa dziko lapansi.”
Pambuyo pokhazikitsa Chigwirizano cha Amitundu, Kazembe Jan Smuts, mmodzi wa oimira a Britain pa ntchito imeneyo, analemba kuti: “Panganolo liri imodzi ya makalata a ntchito koposa a mbiri ya munthu. . . . Ilo liyenera kupambana, chifukwa chakuti palibenso njira ina kaamba ka mtsogolo mwa kutsungula. . . . Mmodzi ndi mmodzi anthu okhalabe kunja kwa panganolo adzatsatira mbendera imeneyi pansi pa imene mtundu wa anthu udzayenda kutsogolo ku zilakiko za gulu lamtendere ndi kukwaniritsa.”
Ziyembekezo zonse zoterozo zinatsimikiziridwa kukhala zabodza pamene Nkhondo ya Dziko ya II inawulika mu 1939. Chigwirizanocho chinalephera. Icho chinali kokha gulu la anthu lopangidwa ndi anthu opanda ungwiro. Choteronso lero choloŵa m’malo chake, Mitundu Yogwirizana. Komabe, pa tsiku limene Tchata cha UN chinasainidwa, nkhani ya mu The New York Times inachizindikiritsa icho kukhala “mtengo wa mtendere” ndi kunena kuti, “Chiyembekezo chachikulu chabadwa . . . Zinthu zazikulu zingabwere.” Mofananamo, atsogoleri a tchalitchi azindikiritsa UN kukhala “chiyembekezo chokha” kaamba ka mtendere ndi “chiyembekezo chomalizira.”
Kulozeretsa ku magulu a munthu zinthu zimene Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzakwaniritsa kuli kuchita mwano. Chotero, Baibulo linaneneratu kuti pambuyo pa kukhalapo kwa kanthaŵi, Mitundu Yogwirizana idzapita “kuchitayiko.” Kokha boma lakumwamba langwiro la Mulungu ndilo lingakhoze kubweretsa mtendere wosatha kwa mtundu wa munthu.—Chibvumbulutso 17:11, 12; Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44.