Kodi Mumatsutsa Dziko mwa Chikhulupiriro Chanu?
“Ndi chikhulupiriro Nowa . . . anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a mnyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi.”—AHEBRI 11:7.
1, 2. Kodi nchiyani chimene tingaphunzire mwa kusanthula moyo wa Nowa?
YEHOVA anapatsa Nowa ndi banja lake—chiŵerengero cha asanu ndi atatu okha—mwaŵi wa kukhala anthu okha odzapulumuka Chigumula. Miyoyo ya anthu a mumbadwo wa Nowa inafupikitsidwa pamene Mulungu anawamiza m’manda a madzi. Chotero popeza kuti Nowa ali kholo lathu, tiyenera kukhala oyamikira koposa za chikhulupiriro chimene iye anasonyeza.
2 Tingaphunzire zambiri kuchokera m’kusanthula moyo wa Nowa. Malemba amatiwuza ife chifukwa chimene Mulungu anamuyanjira ndi chipulumutso pamene Iye anawononga anthu a mbadwo wa Nowa. Cholembera chaumulungu chimodzimodzichi chimasonyeza mowonekera kuti mbadwo wathu ukuyang’anizana ndi chiweruzo chofananacho chochitidwa ndi Mulungu. Ponena za ichi, Yesu ananena kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, NW) Mwa kutsanzira chikhulupiriro cha Nowa, tingakhale ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kupulumuka chiwonongeko chomayandikira cha dongosolo loipa liripoli.—Aroma 15:4; yerekezani ndi Ahebri 13:7.
3. Kodi nchifukwa ninji Yehova anabweretsa Chigumula?
3 M’zaka 1,656 kuyambira pa kulengedwa kwa Adamu kufika ku Chigumula, anthu ochepera kwenikweni anali ndi chikhoterero cha kuchita zabwino. Makhalidwe abwino ananyonyotsoka kufika ku mlingo wotsika kwenikweni. “Anawona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” (Genesis 6:5) Chiwawa, kufunafuna zosangulutsa, ndi kukhalapo kwa angelo osandulika omwe anakwatira akazi ndi kubala zimphona zinali pakati pa zochititsa zimene zinatsogolera ku kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu pa dziko lakale limenelo la anthu. Kwa Nowa, Yehova ananena kuti: “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo.” Kuleza mtima kwa Mlengi, “Woweruza wa dziko lapansi,” kunali kutatha.—Genesis 6:13; 18:25.
Nowa Anayenda Ndi Mulungu
4. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anawonera Nowa, ndipo nchifukwa ninji? (b) Pamene kuli kwakuti chilungamo cha Mulungu chinafunikira kuwononga dziko loipa limenelo, kodi ndimotani mmene chikondi chake chinawonetsedwera kwa Nowa ndi banja lake?
4 Nowa anali wosiyana chotani nanga ndi anthu a m’tsiku lake! Iye “anapeza ufulu pamaso pa Yehova. . . . Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:8, 9) Kodi ndimotani mmene Nowa anayendera ndi Mulungu? Mwakuchita zinthu zabwino zoterozo zonga ngati kulalikira monga m’chirikizi wa chilungamo ndi kumanga chingalawa mokhulupirika ndi momvera. Chotero, ngakhale kuti dziko lakale limenelo linawonongedwa chifukwa chakuti linaipa kotheratu, Mulungu “anasunga Nowa mlaliki wachilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.” (2 Petro 2:5) Inde, Mulungu wathu wachikondi ndi wolungama, Yehova, sanawononge olungama limodzi ndi oipa. Iye analangiza Nowa kumanga chingalawa chachikulu cha kudzipulumutsira iyemwini, amnyumba yake, ndi unyinji wa nyama, zonsezo kuti zikadzazenso dziko lapansi pambuyo pa Chigumula. Ndipo Nowa “momwemonso anachita.”—Genesis 6:22.
5. Kodi ndimotani mmene Malemba amalongosolera chilungamo ndi chikhulupiriro cha Nowa?
5 Chitamalizidwa chingalawa, Mulungu anamuwuza Nowa kuti: “Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuwona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno.” Paulo akuika nkhanizo mofupikira mwanjira iyi: “Ndi chikhulupiriro, Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo amnyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala woloŵa nyumba wachilungamo chiri monga mwa chikhulupiriro.”—Genesis 7:1; Ahebri 11:7.
6. Kodi ndimotani mmene Nowa anatsutsira dziko la tsiku lake mwa chikhulupiriro chake?
6 Nowa anali ndi chikhulupiriro chapadera. Iye anakhulupirira chimene Mulungu ananena ponena za kuwononga mbadwo umenewo. Nowa anali ndi mantha akuya a kusakondweretsa Yehova ndipo anamanga chingalawa mwachimvero mogwirizana ndi malamulo operekedwa ndi Mulungu. Kuwonjezerapo, monga mlaliki wachilungamo, Nowa anawawuza ena ponena za chiwonongeko chomayandikiracho. Ngakhale kuti iwo sanalabadire mawu ake, iye sanalole dziko loipa limenelo ‘kumupanikiza iye m’chikombole chake.’ (Aroma 12:2, Phillips) M’mwalomwake, mwa chikhulupiriro chake, Nowa anatsutsa dziko chifukwa cha kuipa kwake ndipo anasonyeza kuti linayenerera chiwonongeko. Ntchito zake za chimvero ndi chilungamo zinasonyeza kuti ena kuchotsapo iye ndi banja lake akanapulumuka ngati anali ofunitsitsa kusintha njira yawo ya moyo. Ndithudi, Nowa anatsimikizira kuti, mosasamala kanthu za zitsenderezo za thupi lake lopanda ungwiro, dziko loipa lomuzungulira, ndi Mdyerekezi, chinali chothekera kukhala ndi moyo womwe unakondweretsa Mulungu.
Chifukwa Chimene Mulungu Adzawonongera Dongosolo Lino
7. Kodi timadziŵa motani kuti tikukhala m’masiku otsiriza?
7 Zaka khumi zirizonse za zaka za zana la 20 lino zawona dziko likumizidwa mwakuya m’kuipa. Ichi chakhaladi tero makamaka chiyambire chiyambi cha Nkhondo ya Dziko ya I. Anthu akhala omwerekera koposa m’zinthu zonga ngati chisembwere cha kugonana, upandu, chiwawa, nkhondo, udani, umbombo, ndi kugwiritsira ntchito mwazi molakwa kotero kuti okonda chomwe chiri chabwino amazizwa ngati mikhalidweyo ingaipirepo kuposa apo. Komabe, Baibulo linaneneratu zochitika mu mbadwo wathu wa kuipa kopambanitsa, zikumapereka umboni wowonjezereka wakuti tikukhala “m’masiku otsiriza.”—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:34.
8. Kodi nchiyani chimene ena anena ponena za kuzindikira chimo?
8 Lerolino, kudziŵa uchimo kwathetsedwa m’maganizo a unyinji wokulira. Zaka 40 zapitazo, Papa Pius XII anati: “Chimo la zaka za zana lino liri kusazindikira konse kwa chimo.” Mbadwo wamakono umakana kuvomera uchimo ndi liwongo. M’bukhu lake lakuti Whatever Became of Sin? Dr. Karl Menninger ananena kuti: “Liwu lenilenilo lakuti ‘chimo’ . . . lafika pafupi kuzimiririka—liwulo, limodzi ndi kumveka kwake. Chifukwa ninji? Kodi aliyense walekeratu kuchimwa?” Ambiri ataya luntha la kuzindikira chabwino pa choipa. Koma sitikudabwitsidwa ndi ichi, popeza kuti Yesu ananeneratu zochitika zoterozo pamene anali kulongosola ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake’ mu “nthaŵi ya chimaliziro.”—Mateyu 24:3; Danieli 12:4.
Chitsanzo cha Chiweruzo Chokhazikitsidwa m’Tsiku la Nowa
9. Kodi ndimotani mmene Yesu anayerekezera tsiku la Nowa ndi chimene chikachitika mkati mwa kukhalapo Kwake?
9 Yesu anasonyeza kufanana pakati pa zochitika za m’tsiku la Nowa ndi zimene zikachitika mkati mwa kukhalapo Kwake mu mphamvu ya Ufumu, kodzayamba mu 1914. Iye ananena kuti: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu [Yesu]. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.
10. Kodi ndimotani mmene anthu kaŵirikaŵiri samadziŵira kanthu za zochitika zapadera zogwirizana ndi kukhalapo kwa Kristu?
10 Inde, monga mmene zinaliri m’tsiku la Nowa, anthu lerolino sakudziŵa kanthu. Pokhala otanganitsidwa ndi kukhala ndi moyo kwa tsiku ndi tsiku ndi zolondola zadyera, iwo amakana kuzindikira kuti mikhalidwe yamakono imasiyana mwapadera ndi ija ya kumbuyo ndipo imayenerera ndendende ndi chimene Yesu ananena kuti chikazindikiritsa nthaŵi yachimaliziro. Kwa zaka zakutizakuti, Mboni za Yehova zakhala zikuwuza mbadwo wamakono kuti kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu Yaumesiya m’mwamba kunayamba mu 1914 ndipo kukuyendera limodzi ndi “mathedwe a dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3, NW) Anthu ambiri amaseka uthenga Waufumu, koma chimenechinso chinanenedweratu pamene mtumwi Petro analemba kuti: “Ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”—2 Petro 3:3, 4.
11. Kodi nchifukwa ninji mbadwo wamakono sudzakhala ndi chodzikhululukira pamene chisautso chachikulu chifika?
11 Chikhalirechobe, mbadwo wamakono sudzakhala ndi chodzikhululukira pamene chisautso chachikulu chifika. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pali zolembera za Baibulo za ziweruzo zakale zaumulungu zomwe zimakhazikitsa chitsanzo cha chimene Mulungu adzachita m’tsiku lathu. (Yuda 5-7) Ulosi Wabaibulo womwe ukukwaniritsidwa akuwona ndi maso umasonyeza kotheratu pamene tiri m’nyengo ya nthaŵi. Mbadwo uno ulinso ndi ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova ndi mbiri yawo ya kusunga umphumphu yofanana ndi Nowa.
12. Monga nsonga, kodi ndimotani mmene Petro akuyerekezera chiwonongeko cha dziko la tsiku la Nowa ndi chija chomwe chidzadza pa “miyamba ndi dziko lamasiku ano”?
12 Petro akulongosola zimene zidzachitika kwa awo omwe sakudziŵa kanthu ponena za nsongazi. Mofanana ndi Yesu, mtumwiyo akuchita tero mwa kulozera ku zimene zinachitika m’tsiku la Nowa, akumanena kuti: “Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidawungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizidwa ndi madzi, lidawonongeka; koma miyamba ndi dziko lamasiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:5-7.
13. Podziŵa zochitika za mu mbiri zomwe ziri kutsogoloku, ndi uphungu wotani wa Petro womwe uyenera kulabadiridwa?
13 Ndi chiweruzo chotsimikizirika chimenechi cha Mulungu chiri pafupi kutichitikira, tisanyengedwe kapena kuwopsyezedwa ndi oseka. Sitifunikira kugawana ndi chiyembekezo chawo. Petro akulangiza kuti: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la [Yehova], m’menemo, miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu. Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:11-13.
Tsanzirani Chikhulupiriro cha Nowa kuti Mupulumuke
14. Kodi ndi mafunso otani omwe angatithandize kudzisanthula ife eni?
14 Lerolino, tikuyang’anizana ndi zitokoso zimodzimodzizo zonga zimene zinayang’anizidwa ndi Nowa ndi banja lake m’kupitirizabe ndi kukhala anthu odzapulumuka. Mofanana ndi Nowa, Mboni za Yehova zikutsutsa dziko mwa chikhulupiriro chawo chochirikizidwa ndi ntchito zabwino. Koma aliyense wa ife angadzifunse iyemwini kuti: ‘Kodi ine mwaumwini ndikuchita motani? Ngati chisautso chachikulu chidati chidze mawa, kodi Mulungu akandiweruza ine kukhala woyenera kupulumuka? Mofanana ndi Nowa, yemwe anali “munthu wolungama m’mibadwo yake,” kodi ndiri ndi kulimba mtima kwa kukhala wosiyana ndi dziko? Kapena kodi nthaŵi zina chimakhala chovuta kuwona kusiyana pakati pa ine ndi munthu wakudziko chifukwa cha mmene ndimachitira, kulankhula, kapena kuvala?’ (Genesis 6:9) Yesu ananena za ophunzira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.”—Yohane 17:16; yerekezani ndi 1 Yohane 4:4-6.
15. (a) Mogwirizana ndi 1 Petro 4:3, 4, kodi ndimotani mmene tiyenera kuwonera kuganiza kwathu kwakale kwakudziko ndi mikhalidwe? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita pamene tasulizidwa ndi mabwenzi akale akudziko?
15 Petro akulangiza kuti: “Nthaŵi yapitayi idafikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; m’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano.” (1 Petro 4:3, 4) Mabwenzi anu akale akudziko angalankhule mwamwano kwa inu chifukwa chakuti mukuyenda ndi Mulungu ndipo simuthamanganso nawo. Koma, mofanana ndi Nowa, mungawatsutse mwa chikhulupiriro chanu ndi ntchito zabwino zochitidwa modzichepetsa.—Mika 6:8.
16. Kodi ndimotani mmene Mulungu anawonera Nowa, ndipo kodi ndi mafunso otani amene angatithandize kusanthula maganizo ndi mikhalidwe yathu?
16 Mulungu analingalira Nowa kukhala munthu wolungama. Kholo lokhulupirika limenelo “linapeza ufulu pamaso pa Yehova.” (Genesis 6:8) Pamene musanthula maganizo anu ndi mikhalidwe mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu, kodi mumadzimva kuti iye amavomereza zimene mukuchita, ndi malo onse amene mumapitako? Kodi nthaŵi zina mumadziloŵetsa m’zosangulutsa zoipa, zomwe ziri zofalikira chotero tsopano? Mawu a Mulungu amanena kuti tiyenera kuganizira zinthu zoyera, zabwino, ndi zomangirira. (Afilipi 4:8) Kodi mukuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama kotero kuti ‘muphunzitse mphamvu zanu za kuzindikira zosiyanitsira chabwino ndi choipa’? (Ahebri 5:14) Kodi mumakana oyanjana nawo oipa ndi kukonda kuyanjana ndi alambiri a Yehova anzanu pa misonkhano Yachikristu ndi zochitika zina?—1 Akorinto 15:33; Ahebri 10:24, 25; Yakobo 4:4.
17. Monga Mboni za Yehova, kodi ndimotani mmene tingafananire ndi Nowa?
17 Pambuyo posimba kumalizidwa kwa chingalawa, Malemba amanena kuti: “Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:22) Munthu wa Mulungu ameneyo analinso wakhama m’kulalikira monga mboni ya Yehova. Mofanana ndi Nowa, mungakhale m’chirikizi wachangu wa chimene chiri chabwino monga mlaliki wokhazikika wa chilungamo. Limbikirani m’kulengeza chenjezo lonena za mapeto a dziko loipa iri, ngakhale kuti ochepera ndi amene amamvetsera. Gwirani ntchito mogwirizana ndi akhulupiriri anzanu kupangitsa ntchito yopanga ophunzira kuchitidwa mapeto asanadze.—Mateyu 28:19, 20.
18. Kodi ndi pamaziko otani pamene Yehova akugamulira amene ayenera kupulumuka chisautso chachikulu?
18 Kugwiritsira ntchito miyezo yolunjika ndi yolungama imodzimodziyo monga mmene iye anachitira m’tsiku la Nowa, Mulungu tsopano akugamulapo omwe ayenera kupulumuka ndi omwe ayenera kuwonongeka pa nthaŵi ya chisautso chachikulu. Yesu anafanizira ntchito yamakono yakupatula ku kulekanitsa kwa nkhosa ndi mbuzi kochitidwa ndi mbusa. (Mateyu 25:31-46) Anthu omwe amazika miyoyo yawo pa zilakolako ndi zolondola zadyera samafuna kuti dziko lakaleli lithe ndipo sadzapulumuka. Koma awo amene amapeŵa kuloŵetsedwa m’kuipa kwa dziko iri, omwe amasungirira chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu, ndi omwe amapitiriza kulalikira uthenga Waufumu, kupereka chenjezo la kudza kwa chiweruzo cha Yehova, adzasangalala ndi chiyanjo chaumulungu monga opulumuka. Anatero Yesu kuti: “Pomwepo adzakhala aŵiri m’munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: aŵiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.”—Mateyu 24:40, 41; 2 Atesalonika 1:6-9; Chibvumbulutso 22:12-15.
Landirani Madalitso Ndi Nowa
19. Kodi ndi kusonkhanitsa kwa masiku otsiriza kotani kumene Yesaya ndi Mika ananeneratu?
19 M’maulosi olingana, aneneri a Mulungu Yesaya ndi Mika onsewo analongosola chomwe chikachitika mkati mwa masiku otsiriza. Iwo anawoneratu chomwe tikuwona chikukwaniritsidwa lerolino—khamu la anthu owona mtima akutuluka m’dziko lakale ndi kupita ku phiri lophiphiritsira la kulambira kowona. Kwa ena iwo akupereka chiitano chakuti: “Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:2, 3; Mika 4:1, 2) Kodi mukuyenda limodzi ndi gulu lachimwemwe limeneli?
20. Kodi ndi madalitso otani amene adzasangalalidwa ndi aja omwe akutsutsa dziko mwa chikhulupiriro chawo?
20 Yesaya ndi Mika anatchulanso madalitso odzasangalalidwa ndi awo omwe amatsutsa dziko mwa chikhulupiriro chawo. Mtendere weniweni ndi chilungamo zidzafalikira pakati pawo, ndipo sadzaphunziranso nkhondo. Iwo adzakhala ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha choloŵa kuchokera kwa Yehova ndipo “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake.” Koma munthu aliyense ayenera kupanga chosankha cholimba, popeza kuti Mika akusonyeza kuti njira ziŵiri ziri zothekera, akumanena kuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.”—Mika 4:3-5; Yesaya 2:4.
21. Kodi ndimotani mmene mungagawanire madalitso aakulu a moyo wosatha pa dziko lapansi?
21 Malemba amasonyeza momvekera chomwe chikufunikira kuti tipulumuke chisautso chachikulu: chikhulupiriro cholimba. Nowa anali ndi chikhulupiriro choterocho, koma kodi muli nacho? Ngati muli nacho, mofanana ndi iye mudzakhala “woloŵa nyumba wachilungamo chiri monga mwa chikhulupiriro.” (Ahebri 11:7) Nowa anapulumuka chiwonongeko chobweretsedwa ndi Mulungu chomwe chinadza pa mbadwo wake. Iye sanakhale ndi moyo zaka 350 zokha pambuyo pa Chigumula koma iye adzawukitsidwa ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo pa dziko lapansi kosatha. Ndi dalitso lalikulu chotani nanga! (Ahebri 11:13-16) Inu mungagawane m’dalitso limenelo ndi Nowa, banja lake, ndi mamiliyoni ena omwe amakonda chilungamo. Motani? Mwa kupirira kufika kumapeto ndi kutsutsa dziko mwa chikhulupiriro chanu.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuphunzira za moyo wa Nowa kuli kofunika kwa Akristu?
◻ Kodi anthu a mbadwo uno sakudziŵa kanthu ponena za chiyani, chotsogolera ku chiwonongeko chawo?
◻ Mofanana ndi Nowa, kodi ndimotani mmene tingatsutsire dziko iri?
◻ Kodi ndimotani mmene tingafananire ndi Nowa monga mlaliki wachilungamo?