Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Fanizo la Matalente
YESU akupitiriza kukambitsirana ndi atumwi ake pa Phiri la Azitona mwakuwawuza fanizo lina, lachiŵiri m’mpambo wa atatu. Masiku oŵerengeka pasadakhale, pamene anali ku Yeriko, anasimba fanizo la ndalama kusonyeza kuti Ufumuwo udaakali kutali mtsogolo. Fanizo limene akufotokoza tsopano, pokhala ndi mbali zingapo zofanana, likulongosola kukwaniritsidwa kwa zochitika zake m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu mu ulamuliro wa Ufumu. Ilo limapereka fanizo lakuti ophunzira ake ayenera kugwira ntchito pamene adakali pa dziko lapansi kuti awonjezere “chuma chake.”
Yesu akuyamba nati: “Pakuti [ziri, kutanthauza mikhalidwe yogwirizana ndi Ufumuwo] monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.” Yesu ali munthuyo amene, asananke ulendo wa kumwamba, akuikiza kwa akapolo ake—ophunzira okhala pa mzera wa Ufumu wakumwamba—chuma chake. Chuma chimenechi sichiri zinthu zakuthupi koma chimaimira munda wolimidwa umene iye waikamo chidaliro cha kututamo ophunzira owonjezereka.
Yesu akuikiza chuma chake kwa akapolo ake mwamsanga asanakwere kumwamba. Kodi akutero motani? Mwakuwalangiza kupitirizabe kugwira ntchito m’munda wolimidwawo mwakulalikira uthenga wa Ufumu ku malekezero ake a dziko lapansi. Monga mmene Yesu akunenera kuti: “Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye.”
Motero matalente asanu ndi atatuwo—chuma cha Kristu—akugaŵiridwa molingana ndi maluso, kapena kuthekera kwauzimu, kwa akapolowo. Akapolowo akuimira magulu a ophunzira. M’zaka za zana loyamba, gulu limene linalandira matalente asanu mowonekeratu linaphatikizapo atumwi. Yesu akupitiriza kulongosola kuti akapolo amene analandira matalente asanu ndi matalente aŵiri onse anawaŵirikiza kaŵiri mwa kulalikira kwawo Ufumu ndi kupanga ophunzira. Komabe, kapolo amene analandira talente limodzi analibisa pansi.
“Itapita nthaŵi yaikulu,” Yesu akupitiriza, “anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi.” Sizinachitike kufikira zaka za zana la 20, zaka 1,900 pambuyo pake, kuti Kristu anabwerera kukaŵerengera nawo, ndipo zinalidi tero, “itapita nthaŵi yaikulu.” Ndiyeno Yesu akulongosola kuti:
“Uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; loŵa iwe m’chikondwero cha mbuye wako.” Kapolo amene analandira matalente aŵiri nayenso anaŵirikiza kaŵiri matalente ake, ndipo analandira chiyamikiro ndi mphotho yofananayo.
Ngakhale ndi tero, kodi ndimotani mmene akapolowa akuloŵera m’chikondwero cha Mbuye wawo? Chabwino, chikondwero cha Mbuye wawo, Yesu Kristu, chinali chija cha kulandira Ufumu pamene ananka ulendo kwa Atate wake kumwamba. Ponena za akapolo okhulupirika m’nthaŵi zamakono, ali ndi chikondwero chachikulu m’kukhala oikizidwa mathayo owonjezereka a Ufumu, ndipo pamene akumaliza moyo wawo wapadziko lapansi, adzakhala ndi chikondwerero chachikulu cha kuukitsidwira ku Ufumu wakumwamba. Koma bwanji ponena za kapolo wachitatu?
“Mbuye, ndinakudziŵani inu kuti ndinu munthu wouma mtima,” akudandaula tero kapoloyu. “Ndinawopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.” Kapoloyo anakana dala kugwira ntchito m’munda wolimidwawo mwakulalikira ndi kupanga ophunzira. Chotero mbuyeyo akumutcha “woipa ndi waulesi” ndikulengeza chiweruzo nati: “Chotsani kwa iye ndalamayo . . . Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.” Awo a gulu la kapolo woipa limeneli, pokhala oponyedwa kunja, akumanidwa chikondwero chirichonse chauzimu.
Izi zikupereka phunziro lowopsya kwa onse odzinenera kukhala atsatiri a Kristu. Iwo ayenera kugwirira ntchito pa kuwonjezera chuma cha Mbuye wawo wakumwamba mwakukhala ndi phande mokwanira m’ntchito yolalikira ngati ati asangalale ndi chiyamikiro chake ndi mphotho ndiponso ngati ati apeŵe kuponyedwa ku mdima wakunja ndi chiwonongeko chotheratu. Kodi ndinu wakhama kugwiritsira ntchito maluso anu m’zimenezi? Mateyu 25:14-30.
◆ Kodi ndi phunziro lotani limene fanizo lotsatirali likuphunzitsa?
◆ Kodi akapolowo ndani, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chuma chimene akuikizidwacho?
◆ Kodi nliti pamene mbuyeyo akubwera kudzaŵerengera nawo, ndipo kodi iye akupezanji?
◆ Kodi nchiyani chimene chiri chikondwero m’mene kapolo wokhulupirikayo akuloŵa, ndipo kodi nchiyani chikuchitika kwa kapolo woipawo?