Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pamene Kristu Adza Mumphamvu ya Ufumu
YESU adakali ndi ophunzira ake pa Phiri la Azitona. Poyankha pempho lawo la chizindikiro cha kufika kwake ndi cha mathedwe a dongosolo la zinthu, iye tsopano akuwauza lotsirizira mumpambo wa mafanizo atatu. “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake ndi angelo onse pamodzi naye,” Yesu akuyamba motero, “pomwepo iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake.”
Anthu sangawawone angelo muulemerero wawo wakumwamba. Chotero kudza kwa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, ndi angelo kuyenera kukhala kosawoneka kwa anthu. Kudzako kuchitika mu chaka cha 1914. Koma kodi kaamba ka chifuno chotani? Yesu akulongosola kuti: “Ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu amitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”
Pofotokoza chomwe chidzachitikira awo olekanitsidwira kumbali yoyanjidwa, Yesu akuti: “Pomwepo mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, idzani kuno inu odalitsika a atate wanga, loŵani ufumu wokonzedwera kwa inu pachikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Nkhosazo sizidzalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba koma zidzaloŵa mu Ufumuwo m’lingaliro la kukhala nzika za padziko lapansi. “Chikhazikiro chake cha dziko lapansi” chinachitika pamene Adamu ndi Hava poyambapo anabala ana amene akapindula ndi makonzedwe a Mulungu a kuombola anthu.
Koma kodi nchifukwa ninji nkhosazo zalekanitsidwira kudzanja lamanja lachiyanjo la Mfumuyo? “Pakuti ndinali ndi njala,” mfumuyo ikuyankha motero, “ndipo munandipatsa ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza ine; wamaliseche ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi ine; ndinali m’nyumba ya ndende, ndipo munadza kwa ine.”
Popeza kuti nkhosazo ziri padziko lapansi, izo zikufuna kudziŵa mmene zinachitira ntchito zabwino zoterozo kwa Mfumu yawo yakumwamba. “Ambuye, tinakuwonani inu liti wanjala, ndikukudyetsani,” zikufunsa motero, “kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinawona inu liti mlendo ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndikukuvekani? Ndipo tinakuwonani inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa inu?”
“Indetu ndinena kwa inu,” Mfumuyo ikuyankha, “chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale aang’onong’ono aŵa, munandichitira ichi ine.” Abale a Kristu ndiwo otsalira a 144,000 padziko lapansi omwe adzalamulira ndi iye kumwamba. Ndipo Yesu akuti, kuŵachitira zabwino, nkofanana ndi kumchitira zabwino.
Kenaka, Mfumuyo ilankhula kwa mbuzi. “Chokani kwa ine otembereredwa inu kumoto wa nthaŵi zonse wokolezedwera Mdyerekezi ndi amithenga ake; pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira ine; wamaliseche ndipo simunandiveka ine; wodwala, ndi m’nyumba ya ndende: ndipo simunadza kundiwona ine.”
Komabe, mbuzizo, zikudandaula kuti: “Ambuye, tinakuwonani liti wanjala kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena wodwala, kapena m’nyumba ya ndende, ndipo ife sitinakutumikirani inu?” Mbuzizo zikuweruzidwa moipa pamaziko amodzimodziwo amene nkhosa zaweruzidwira moyanjidwa. “Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang’onong’ono [a abale anga],” Yesu akuyankha motero, “Munalibe kundichitira ichi ine.”
Chotero kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu ya Ufumu, mwamsanga mapeto a dongosolo iri lazinthu asanachitike pa chisautso chachikulu, kudzakhala nthaŵi ya chiweruzo. Mbuzi “zidzapita kukulikhidwa kosatha, koma olungama [nkhosa] kumoyo wosatha.” Mateyu 25:31-46; Chivumbulutso 14:1-3.
◆ Kodi nchifukwa ninji kukhalapo kwa Kristu kuyenera kukhala kosawoneka, ndipo kodi iye akuchita ntchito yotani panthaŵiyo?
◆ Kodi ndimlingaliro lotani mmene nkhosa zikuloŵera mu Ufumu?
◆ Kodi ndiliti pamene “chikhazikitsiro cha dziko lapansi” chinachitika, ndipo kodi nchifukwa ninji panthaŵiyo?
◆ Kodi ndi pamaziko otani pa amene anthu akuweruzidwirapo kaya kukhala nkhosa kapena mbuzi?