Kodi Munthu Akuchitanji ndi Dziko Lapansi?
ZAKA mazana atatu zapitazo, munthu anali womvana kwenikweni ndi chilengedwe. Kwakukulukulu, iye sankawopsyezedwa ndi masinthidwe ochititsidwa ndi munthu mmalo ozungulira a dziko lapansi m’njira imene akuchitira lerolino. Masinthidwe ochititsidwa ndi maindasitale adali asanayambike. Kunalibe nyumba zoperekera magetsi, mafakitale, magalimoto, kapena magwero ena ochititsa kuipitsa kofalikiraku. Lingaliro lakuti munthu akawononga dziko lonse lapansi linali losakhulupiririka kwa iye.
Komabe, ngakhale kumbuyoko, chenjezo lonena za kuwononga dziko lapansi linkafalitsidwa. Chenjezo limenelo linapezeka m’bukhu lomalizira la Baibulo, ndipo linaneneratu za nthaŵi pamene Mulungu akaloŵerera m’zochita za munthu mwa “kuononga iwo akuononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:17, 18.
Nkotonthoza chotani nanga kwa onse odera nkhaŵa ndi kusasamalira kwa munthu dziko lapansi m’tsiku lathu kudziŵa kuti Mlengi wa planeti lathu lokongolali adzalipulumutsa kukuwonongedwa! ‘Koma,’ inu mungadabwe kuti, ‘kodi tafikapodi pa mkhalidwe woipitsitsa woterowo wofunikira kuloŵereramo kwa Mulungu?’ Eya, lingalirani zina za nsonga ndi kudziweruzira nokha.
Nkhalango
Nkhalango zimakongoletsa dziko lapansi ndipo zimapereka zakudya ndi pogona kwa mamiliyoni angapo a mitundu yosiyanasiyana ya zolengedwa. Pamene mitengo ikula ndi kupanga zakudya, iyo imakhala ikuchitanso ntchito zina zofunika koposa, monga ngati kuyeretsa mpweya womwe timapumira kunja ndikutulutsa mpweya wofunika womwe timapumira mkati. Chotero, National Geographic ikuti, “iyo imapereka kuchiritsa kumodzi ku chitungu cha padziko lonse chomwe chikuwopsyeza moyo pa dziko lapansi monga momwe tikuchidziŵira.”
Koma munthu akuwononga choloŵa chake cha nkhalango. Nkhalango za Kumpoto kwa Amereka ndi ku Ulaya zikufa ndi kuipitsa. Ndipo kuitanitsa maoda kwa maiko okhala ndi maindasitale kukuwononga nkhalango zakumalo otentha. Nyuzipepala ya ku Afirika inalongosola kuti mu 1989, “mtunda wa mamita 66 miliyoni m’mbali zonse zitatu [wa mitengo yakumalo otentha] unayembekezera kugulitsidwa kunja kwa dziko—48 peresenti ku Japan, 40 peresenti ku Ulaya.”
Ndiponso, m’maiko ena, alimi amaotcha nkhalango kuti apange munda. Nthaka ya nkhalango yosalimbayo imatha mphamvu yake mofulumira, ndipo alimiwo amaotchabe nkhalango ina. Kwayerekezedwa kuti m’zaka za zana lino lokha, pafupifupi theka la nkhalango yadziko inazimiririka.
Nyanja
Nyanja zadziko lapansi zimachitanso mbali yokulira yoyeretsa mpweya, ndipo ntchito za munthu zikuiwononga. Mpweya wambiri womwe timapumira kunja umayeretsedwa ndi nyanja. Zitatero, zomera zamnyanja zimayeretseratu mpweya womwe timapumira kunjawo ndi kutulutsa mpweya womwe timapumira mkati. Dr. George Small akulongosola zungulirezunglire wochilikiza moyoyu motere: “70 peresenti ya mpweya womwe timapumira mkati wowonjezeredwa ku mpweya wadziko chaka chirichonse umachokera ku tizirombo ndi zomera zamnyanja.” Chikhalirechobe, asayansi ena akuchenjeza kuti umoyo wa zomera zamnyanja ungachepetsedwe mowopsya chifukwa cha kuchepera kwa magwero ampweya m’dziko, komwe kwakhulupiriridwa kuti kukuchititsidwa ndi munthu.
Ndiponso, munthu amatayira zinyalala, mafuta, ndipo ngakhale zinthu zotayidwa zopatsa ululu m’nyanja. Pamene kuli kwakuti maiko ena amavomereza kuchepetsa zoipa zimene zimaloledwa kutayidwa m’nyanja, ena amakana. Dziko lina la Kumadzulo lafikira pa kukhala ndi kuyenera kwa kutaya zoipa za nyukliya m’nyanja. Wofufuza nyanja wotchuka Jacques Cousteau akuchenjeza kuti: “Tiyenera kupulumutsa nyanja ngati tikufuna kupulumutsa anthu.”
Madzi Akumwa
Munthu akuwononga ngakhale madzi ake akumwa! M’maiko osauka, anthu mamiliyoni ambiri amafa chaka chirichonse chifukwa cha madzi oipitsidwa. M’maiko olemera, pakati pa zinthu zina, magwero operekera madzi amaipitsidwa ndi feteleza ndi mankhwala ophera tizirombo omwe amakokoledwera m’mitsinje ndikukakhala pansi pa madzi. Mu 1986 dziko linapanga matani 2.3 miliyoni ya mankhwala ophera tizirombo, ndipo chiŵerengero cha kuwonjezeka chasimbidwa kukhala 12 peresenti chaka chirichonse.
Magwero ena a kuipitsa ndiwo mankhwala (chemicals) otaidwa. “Migolo yachitsulo yodzala ndi mankhwala,” ikulongosola tero Scientific American, “njofanana ndi bomba lotcheredwa lomwe lidzaphulika atachita dzimbiri.” Magazinewo akuwonjezera kuti, mtundu uwu wa kuipitsa ukuchitika “padziko lonse mwa mankhwala otaidwa zikwi zambiri.”
Kodi chotulukapo chake nchiti? Padziko lonse lapansi, mitsinje yomwe idali yoyera ikusinthidwa kukhala dzala la maindasitale. Kwayerekezedwa kuti anthu a ku Ulaya 20 miliyoni amamwa madzi a m’Rhine, komatu mtsinje umenewu ngwoipitsidwa kwenikweni kwakuti matope otengedwa m’mphepete mwake ngoipa kwenikweni kuŵagwiritsira ntchito monga ndowe!
Ntchito Zamalimidwe
Mowopsya, munthu akuwonongadi munda wake. Mogwirizana ndi Scientific American, mu United States mokha, 20 peresenti ya minda yopatulidwira kutsirira yawonongedwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kutsirira kopambanitsa kumawonjezera mchere wambiri kunthaka. Maiko ambiri awononga nthaka yambiri ya chonde mwanjirayi. “Minda yambiri tsopano ikutheredwa chonde chake chifukwa cha kuikidwa mchere wopambanitsa kuposa yomwe ikukhalitsidwa yachonde ndi maprojekiti otsirira atsopano,” yatero The Earth Report. Vuto lina lofalikira nlakulima munda panyengo yaitali, komwe kungakhale kukuchititsa kufutukuka kwa zipululu.
Magalimoto Ambirimbiri
Zinthu zonsezo kaamba ka minda ndi madzi a planeti lathu. Koma bwanji ponena za mpweya wake? Uwu ukuwonongedwanso, ndipo amaliŵongo ngambiri. Kungotchula mmodzi yekha, lingalirani galimoto. Machenjezo otsatirawa achokera m’magazine atatu a sayansi achisonkhezero: “Magalimoto amabweretsa kuipitsa mpweya kwambiri kuposa ntchito iriyonse ya munthu.” (New Scientist) “Pakali pano pali magalimoto 500 miliyoni olembetsedwa paplaneti . . . Matanki awo amamwa pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu za mafuta adziko. . . . Chiŵerengero cha magalimoto chikuwonjezeka mofulumira kwenikweni kuposa cha anthu.” (Scientific American) “Kupangidwa, kugwiritsiridwa ntchito ndi kutaidwa kwa petulo pamlingo uliwonse ndiko magwero aakulu a kuipiraipira kwa dziko ndi matenda.”—The Ecologist.
Inde, planeti lathu likuipitsidwa, kuwonongedwa. Nyanja zake, madzi ake akumwa, minda yake, ndipo ngakhale mpweya wake zikuipitsidwa kwakukulu. Ndithudi, chimenechi chokha chingavomereze kuti nthaŵi iripafupi yakuti Mulungu aloŵerere ndi “kuononga iwo akuononga dziko.” (Chibvumbulutso 11:18) Komabe, pali njira zina, zoipitsitsadi, m’zimene dziko lapansi likuwonongedwera. Tiyeni tiwone kuti izo nziti.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“Tiyenera kupulumutsa nyanja ngati tikufuna kupulumutsa anthu.”—Jacques Cousteau