Lemekezani Yehova ndi Chuma Chanu
‘NDIRIBE chuma; ndidakali wachichepere ndipo ndiri ndi zinthu zochepa.’ ‘Sindinaphunzire kwambiri; kodi ndingampatsenji Yehova?’ ‘Ndiri wolemala kwambiri; Yehova adzangondipulumutsa.’ ‘Ndakalamba; nkuchedwa kwa ine kupeza chuma.’
Kodi malingaliro onga awa abwera m’maganizo mwanu pamene mukulingalira mutu wa nkhani ino? Komabe, mwinamwake ndinu wolemera kuposa mmene mukuganizira. Kumbukirani mawu awa a Ambuye Yesu ku mpingo wa Smurna: ‘Ndidziŵa chisautso chako, ndi umphawi wako komatu uli wachuma.’ (Chibvumbulutso 2:9) Yesu ananena kuchiyambiyambi mu Ulaliki wa Paphiri kuti: ‘Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, . . . koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, . . . pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.’ (Mateyu 6:19-21) Kodi mawu awa a Ambuye wathu akukusangalatsani? Inde, mungakhale chinachake mwa inu chimene Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi Mwana wake amachilingalira kukhala chamtengo koposa. Tiyeni tisanthule.
Ulemerero wa Achichepere—Mphamvu ndi Changu
Kodi ndimotani mmene wachichepere angaperekere utumiki wamtengo wake kwa Yehova? Miyambo 20:29 ikutitsimikizira kuti achichepere ali ndi chuma chaulemerero—thanzi lakuthupi. Nkotsitsimula chotani nanga kuwona wachichepere akupereka nyonga yake ndi ubwana ku utumiki wa Mulungu wathu!
Tiyeni tisanthule masamba a mbiri kubwerera kumbuyo kuchiyambi kwa ma 1930 pamene achichepere ambiri anamva chowonadi chokhala m’Baibulo. Wa zaka 16 wina anabwereka kwa mnzake bukhu lothandizira kuphunzira Baibulo lotchedwa Creation, lofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Pamene anafika pa mutu wakuti “The New Creation” (Chilengedwe Chatsopano) ndikuŵerenga ponena za kupatulikitsidwa, pomwepo anadziŵa chomwe anafunikira kuchita ndi moyo wake. Mwamsanga, anadzipereka yekha kwa Mlengi wamphamvuyonse. Chaka chotsatira anaŵerenga bukhu lina iri, Vindication (Book One), ndikuphunzira ponena za chiyembekezo cha kugawana m’kuyeretsa dzina la Mulungu ndi ulamuliro wake. Chidziŵitsochi chinadzutsa chikhumbo chachangu mwa iye kaamba ka utumiki wa nthaŵi zonse. Chaka chimodzimodzicho anafunsira mwaŵi waupainiya, ndipo mpaka pano iye adakapitirizabe muutumiki wa nthaŵi zonse. Pamene kuli kwakuti anzake ambiri amaliza ntchito yawo ya padziko lapansi, otsalira ambiri adakasonyezabe mzimu wakudzipereka kwa moyo wonse kwa Atate wathu wakumwamba.
Kodi achichepere Achikristu lerolino amasonyeza mkhalidwe wamtengo wake wofananawu? Motsimikizirika amatero! Malipoti a mu Yearbook amasonyeza kuti khamu lochuluka monga mame tsopano likudziphatika ku ntchito yaupainiya. (Salmo 110:3) Philippines inasimba kuti 13 peresenti ya apainiya okhazikika ngamsinkhu wa zaka zosafika 20. Kodi pali kwinakwake kumene izi ziri tero? Inde, kulipo. Mwachitsanzo, kufufuza m’zilumba zazing’ono za Trinidad ndi Tobago kumavumbula kuti apainiya atsopano 282 analembetsedwa pakati pa September 1, 1986, ndi September 30, 1988. M’chiŵerengero chimenecho, 48 anali pamsinkhu wa zaka zosafika 20. Kodi mungakonde kumvetsera kwa mmodzi wa awa?
Mvetserani kwa Charmaine Francis. Mtsikanayu akuti: “Kuchokera panthaŵi yomwe ndinali mwana, makolo anga analankhula nane ponena za kutumikira Yehova ndi kukhala wokhulupirika kwa iye. Pamene makolo anga anafunsa chimene ndikachita adakaikidwa m’ndende kaamba ka kulalikira mbiri yabwino, ndinati, ‘Ndidzatumikira Yehova.’ Ndinadzipereka pamene ndinali wa zaka 13, ndipo ndinabatizidwa pamene ndinali wa zaka 14. Mwamsanga pambuyo pake, patchuthi chirichonse cha sukulu, ndinadzilowetsa mu upainiya wothandiza. Mu 1983 ndinayamba upainiya wokhazikika. M’chaka changa choyamba cha upainiya, ndinali ndi chimwemwe cha kuthandiza mayi wapanyumba kukhala mtumiki wa Yehova. Tsopano ndikutsogoza maphunziro Abaibulo asanu ndi anayi. Mmodzi akukonzekera kubatizidwa, ndipo atatu akupezeka pamisonkhano.”
Tsopano, kodi achicheperenu, simukuvomereza kuti nanunso muli ndi chinachake cha mtengo wake cholemekeza nacho Yehova? Ndithudi muli nacho! Ngakhale ngati patsopano lino simuli mu utumiki wa nthaŵi zonse, mungamulemekeze Yehova molingana ndi mikhalidwe yanu. Inu mungakhale mudakali ndi zaka zambiri muli pasukulupo. Komabe, muli ndi mwaŵi wapadera wa kutamanda Yehova kwa aphunzitsi anu ndi anzanu a m’kalasi. Christian Kalloo, yemwe ali ndi zaka khumi, anapita kusukulu ndi kope lake la bukhu la Life—How Did It Get Here—By Evolution or by Creation? Chotulukapo chake? Iye anagawira makope asanu ndi aŵiri kwa okondwerera mu nkhaniyo. Iye anagawiranso limodzi mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Inu mungachite zofananazo.—Yerekezerani ndi Mateyu 21:15, 16.
Mlangizi Wathu Wamkulu Akutiphunzitsa Ife
Mneneri Yesaya anati: “Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira.” Iye anathokoza Yehova kaamba ka luso lake la kulankhula. Iye analembanso lonjezo la Yehova lakuti: ‘Mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m’kamwa mwako sadzachoka m’kamwa mwako, pena m’kamwa mwa ana ako, pena m’kamwa mwa mbewu ya mbewu yako.’ (Yesaya 50:4; 59:21) Mongadi mmene amuna opanda maphunziro ndi anthu wamba anakhalira atumwi a Yesu ndipo Mulungu anawapanga kukhala anzeru m’nkhani zauzimu, chotero Yehova wapanganso anthu wamba kukhala anzeru lerolino.
Yearbook ya mu 1986 iri ndi chidziŵitso cholimbikitsa kwa omwe ali ndi maphunziro ochepera kapena omwe alibiretu. M’maiko ambiri Mboni za Yehova zimakonzekera makalasi a osaphunzira kuchitidwira kuphunzitsa achikulire kuŵerenga. Yehova wadalitsa chotani nanga oterewa! Pakati pa 1962 ndi 1984 mu Nigeria, anthu 19,238 anapanga kupita patsogolo kwabwino kwambiri kuphunzira kuŵerenga ndi kulemba ndipo tsopano ngokhozadi kudziŵerengera Baibulo ndi kuŵerengera omwe amachitirako umboni. Ndi madalitso olemerera chotani nanga omwe akhala nawo! Mbale wina anachita bwino kwambiri kwakuti anakhala mlangizi wa kalasi la kuŵerenga mumpingo mwake.
Lingaliraninso chokumana nacho cha Ezekiel Ovbiagele. Iye anali wosakhoza kuŵerenga pamene anabatizidwa mu 1940. Pambuyo pophunzira kuŵerenga, iye anapita patsogolo kufikira kulembetsedwa kukhala mpainiya, ndipo pambuyo pakebe, mu 1953, iye anaikidwa monga woyang’anira woyendayenda.
Palibe ziletso za msinkhu m’dongosolo la kuphunzira. Ena angagwire mawu mwambi wakale uwu: “Simungaphunzitse galu wokalamba machenjera atsopano!” Uwu ungakhale wowona kwa agalu, koma anthu sinyama. Ngakhale okalamba angaphunzire ndipo amaterodi ngati akufunadi kudziŵa Yehova ndi kumtumikira. Inu mungakhale mukudziŵa ena amene anatero. Mwachitsanzo, Alice Okon ku Nigeria analimbikitsidwa kuŵerenga Baibulo ndi kuphunzira za chiyembekezo chimene limapereka; iye anavomereza ndi kusangalala ndi chiyembekezo chimene chiri kutsogoloku. Pamsinkhu wa zaka 80, iye sanali wokalamba kosakhoza kuphunzira. Kodi simukulingalira kuti anakondweretsa mtima wa Yehova? Iye ngolemera m’chikhulupiriro. Miyambo 3:14 imatitsimikizira kuti kukhala ndi nzeru ‘kuposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka.’ Pamene munthu angalankhule chowonadi molongosoka, mawu ake amafanana ndi “zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”—Miyambo 25:11; Akolose 3:16.
Wolemera m’Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino Ngakhale Ngolemala
Munthu wobadwa wolemala kuthupi angakhale wokhumudwitsidwa pamene akula ndi kuzindikira mkhalidwe wake. Ndipo nkokhwethemula pamene munthu akhala mnkhole wa kulemala kuuchikulire. Kodi mkhalidwewu uli wopanda chiyembekezo kwa oterewa? Ayi, iwo ungakhozedi kutsegula njira yonkira ku moyo wosatha.
M’nkhondo Yadziko ya I, Edward Stead anali ndi khola labwino m’tauni yaing’ono ya Arvada, Wyoming, U.S.A., ndipo mkazi wake anali ndi hotela yaing’ono. Kugwidwa ndi matenda a Spanish flu kunafooketsa mphamvu zake zathupi zotetezera matenda, ndipo anadwala rheumatoid arthritis, yomwe inaumitsa mfundo za ziŵalo zake kwakuti thupi lake linalemazidwa mumpangidwe wa mpando wake wa magudumu. Ngakhale kuti uwu ungawonekere kukhala mkhalidwe wopanda chiyembekezo, iye ankakhozabe kulankhula, ndi kutukula pang’ono manja ake. Kwa nthaŵi yaitali analakalaka kudzipha. Pambuyo pake anakumana ndi chowonadi, ndipo anachikupatira gwagwagwa.
Poyamba ankakhala pakhomo la hotela ndikulankhula kwa alendo ponena za chikhulupiriro chake chopezedwa tsopanocho. Iye anali wokhoza kutukula manja ake mokwanira kutsegula bukhu la Baibulo kusonyeza omwe anaima kuti amvetsere. Ena omwe anayamikira kuyesayesa kwakeko anamutcha ngwazi yopunduka. Chotsatira, iye anasankhapo kuchitira umboni m’matauni ena ngati pokhala pabwino pakanapangidwira iye m’galimoto yotseguka kumbuyo. Ichi chinachitidwa, ndipo kwa zaka zambiri iye wachita upainiya mumkhalidwe wodabwitsa uwu, akumayenda mamailo zikwi zambiri pakati pa Wyoming ndi Texas, mogwirizana ndi apainiya achichepere aŵiri kapena atatu omwe anamusamalira. Kwanthaŵi imene anakhala ndi moyo, iye anali chilimbikitso chachikulu kwa onse amene anamdziŵa.
Ngati mukudzimva wokhumudwa chifukwa cha kulemala kwathupi, chonde ŵerengani nkhani ya pamasamba 22-5 mu The Watchtower ya November 15, 1986. Amuna onse otchulidwa mmenemo ndi akulu, alangizi auzimu, oyeneretsedwa kutonthoza abale awo omwe angakhale osalemala koma ofunikira kumangiriridwa mwauzimu. Ngolemera chotani nanga m’maso mwa Mulungu!—1 Timoteo 6:18.
Esterleta Dick, wa zaka 63 zakubadwa, wakhala Mboni yobatizidwa kwa zaka 16. Mu 1978 anakhala wakhungu, koma wakhala akutumikira monga mpainiya wokhazikika kwa zaka ziŵiri zapitazi. Kodi kumathekera motani? Eya, mloleni adziyankhire.
“Tsiku lina,” iye akutero, “mlongo wachipainiya wachichepere anandifunsa ine kuti: ‘Mlongo Dick, nthaŵi zonse mumafikira maola anu monga mpainiya wothandiza. Bwanji osayesera kukhala mpainiya wokhazikika?’”
Esterleta anawopa kuti akakhala chothodwetsa kwa abale, koma anakumbukira kuti woyang’anira wadera analimbikitsa utumiki wa upainiya. Iye akuti: “Ndinayamba, ndipo tsopano ndathera zaka ziŵiri muutumiki waupainiya. Ndimachita umboni wa m’khwalala ndipo ndiri ndi maulendo obwereza ambiri. Ndiponso, ndimatsogoza maphunziro Abaibulo apanyumba asanu ndi limodzi. Motani? Ndisanachezere mwininyumba, bukhu lophunziridwalo limaŵerengedwa kwa ine kunyumba limodzi ndi malemba oikidwamo, kotero kuti ndimakhala wokhoza kuthirira ndemanga paphunziropo. Ophunzira anga a Baibulo atatu amapezeka pamisonkhano limodzi nane, ndipo mmodzi ngwobatizidwa.”
Aliyense ‘Angadzaze Dzanja Lake’ Ndi Mphatso
Kodi kupatsa nkolekezera kuuzimu? Ayi. Pamene Mfumu Davide wakale ankakonzekera kumanga kachisi, iye anafunsa kuti: “Kodi ndani uyo afuna mwini kudzaza dzanja lake lerolino ndi mphatso za kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5, NW) Aliyense akanatero. Mofananamo, lerolino achichepere kapena achikulire, aumoyo wabwino kapena ayi, angafune kupereka mwaufulu chuma chakuthupi kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu. Uku kungachitidwe kupyolera mu ofesi yanthambi ya m’dziko lanu kapena kupyolera mumpingo wa kwanu. Mwanjirayi, aliyense molingana ndi mphamvu zake, angathandizire kuchepetsa zotaika ndi kutsimikizira kuti mbiri yabwino ikulalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu. Uwu ndi mwaŵi.—2 Akorinto 9:8-12.
Chofunika koposa, inu muli ndi chuma chauzimu chimene mungalemekeze nacho Yehova. Achichepere ali ndi nyonga ndi ubwana wa uchichepere. Osaphunzira angaphunzire kupereka kwa Yehova zipatso za milomo yawo. Olemala angathe ndipo apita patsogolo m’chidziŵitso, nzeru, ndi kumvetsetsa, kwakuti ambiri sali kokha atamandi anthaŵi zonse a Yehova komanso aphungu ndi abusa mumpingo Wachikristu. Kodi sindinu wolemera koposa mmene munaganizira? Chotero, lemekezani Yehova ndi chuma chanu.—Ahebri 13:15, 16.