Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Chilangizo Chotsazikira
CHAKUDYA chachikumbukiro chatha, koma Yesu ndi atumwi ake adakali m’chipinda chosanjacho. Ngakhale kuti Yesu adzapita posachedwapa, iye ali ndi zinthu zambiri zonena. Iye awatonthoza kuti, ‘Mtima wanu usavutike. Mukhulupirira Mulungu.’ Koma zambiri zikufunikira. “Khulupirirani Inenso,” iye awonjezera tero.
“M’nyumba mwa Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri,” Yesu apitiriza tero. “Pakuti ndipita kukukonzerani inu malo . . . kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” Atumwiwo sakuzindikira kuti Yesu akulankhula ponena za kupita kumwamba, chotero Tomasi afunsa kuti: “Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji?”
‘Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo,’ Yesu ayankha. Inde, mwa kumuvomereza kokha ndi kutsanzira njira yake ya moyo mpamene aliyense angaloŵe m’nyumba yakumwambayo ya Atate chifukwa chakuti, monga mmene Yesu akunenera kuti: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.”
“Ambuye, tionetsereni ife Atate,” Filipo afunsa tero, ‘ndipo chitikwanira.’ Mwachionekere Filipo akufuna kuti Yesu awonetsere Mulungu, monga mmene kunachitidwira m’nthaŵi zakalekale m’masomphenya kwa Mose, Eliya, ndi Yesaya. Koma, kwenikweni, atumwiwo ali ndi chinachake chabwino koposa masomphenya amtundu umenewo, monga momwe Yesu akunenera kuti: ‘Kodi ndiri ndi inu nthaŵi yaikulu yotero, ndipo sunandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate.’
Yesu amaunikira mwangwiro umunthu wa Atate wake kwakuti kukhala naye ndi kumuona, m’chenicheni, nkofananadi ndi kuona Atate. Komabe, Atate ngwamkulu pa Mwana, monga mmene Yesu akuvomerezera motere: ‘Mawu amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha.’ Yesu akupereka chitamando chonse cha kuphunzitsa kwake kwa Atate wake wakumwamba molondola.
Nkolimbikitsa chotani nanga mmene kuyenera kukhalira kwa atumwiwo kumva Yesu tsopano akuwauza kuti: ‘Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi’! Yesu sakutanthauza kuti atsatiri ake adzachita ntchito zazikulu zozizwitsa kumposa. Ayi, koma iye akutanthauza kuti iwo adzachita uminisitala kwanthaŵi yaitali, m’dera lokulira, ndipo kwa anthu ambiri.
Yesu sadzawasiya ophunzira ake atachokapo. ‘Ndipo chimene chirichonse mukafunse m’dzina langa,’ iye akuwalonjeza, ‘ndidzachita.’ Mowonjezera, iye akuti: ‘Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu nkhoswe ina, kuti ikhale ndi inu ku nthaŵi yonse, ndiyo mzimu wachowonadi.’ Pambuyo pake, atakwera kumwamba, Yesu atsanulira pa ophunzira ake mzimu woyera, nkhoswe ina imeneyi.
Kuchokapo kwa Yesu kuli pafupi, monga mmene iye akunenera motere: “Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine.” Yesu adzakhala cholengedwa chauzimu chimene palibe munthu angachione. Koma kachiŵirinso Yesu akulonjeza atumwi ake okhulupirika kuti: “Koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.” Inde, Yesu sadzaonekera kokha kwa iwo monga munthu pambuyo pa kuukitsidwa koma m’kupita kwanthaŵi iye adzawaukitsira kumoyo ndi iye kumwamba monga zolengedwa zauzimu.
Tsopano Yesu akunena lamulo lokhweka kuti: ‘Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.’
Pakumva izi mtumwi Yudase, yemwe akumutchanso Tadeyo aloŵerera kuti: ‘Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?’
“Ngati wina akonda Ine,” ayankha Yesu, ‘adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzamkonda . . . Wosandikonda Ine sasunga mawu anga.’ Mosafanana ndi atsatiri ake omverawo, dziko linyalanyaza ziphunzitso za Kristu. Chotero iye sakudzivumbula mwini kwa iwo.
Mkati mwa uminisitala wake wa padziko lapansi, Yesu waphunzitsa atumwi ake zinthu zambiri. Kodi iwo adzazikumbukira bwanji zonsezo, makamaka popeza kuti, ngakhale kufikira panthaŵiyi, iwo adakalepherabe kuzindikira zambiri? Mwachimwemwe, Yesu alonjeza kuti: ‘Nkhosweyo, mzimu woyera, umene Atate adzautuma m’dzina langa, iwowo udzaphunzitsa inu zonse, nudzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.’
Powatonthozanso, Yesu akuti: ‘Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani. . . . Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.’ Zowona, Yesu akupita, koma iye alongosola kuti: ‘Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.’
Nthaŵi yotsala ya Yesu ndi iwo njaifupi. “Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu,” iye akutero, ‘pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine.’ Satana Mdyerekezi, amene anali wokhoza kuloŵa mwa Yudase ndi kumgwira, ndiye mkulu wa dziko. Koma palibe chifooko chauchimo mwa Yesu kuti Satana achidyerere masuku kumpatutsa pa kutumikira Mulungu. Yohane 14:1-31; 13:27; Luka 22:3, 4; Eksodo 24:10; 1 Mafumu 19:9-13; Yesaya 6:1-5.
▪ Kodi Yesu akupita kuti, ndipo kodi Tomasi akulandira yankho lotani ponena za njira yonkira kumeneko?
▪ Mwapempho lake, nchiyani chimene Filipo mwachionekere akufuna kuti Yesu achite?
▪ Kodi yemwe waona Yesu amaonanso bwanji Atate?
▪ Kodi ndimotani mmene atsatiri a Yesu amachitira ntchito zazikulu kumuposa?
▪ Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Satana aliri wopanda ulamuliro pa Yesu?