“Wakumva Anene, Idzani”
M’chaka chonse chikudzachi, Mboni za Yehova m’maiko oposa 200 padziko lonse zidzadzipereka mogwirizana ndi lemba lawo lachaka la 1991 lakuti: “WAKUMVA ANENE. IDZANI”
“Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”—CHIBVUMBULUTSO 22:17.
1. Kodi tikuitanidwa ‘kudza’ ku “madzi” otani?
INU mukuitanidwa kuti “idzani.” Kudzatani? Eya, idzani kudzapha ludzu lanu ndimadzi. Aŵa simadzi wamba ayi koma madzi amodzimodziwo amene Yesu Kristu anawatchula pamene anauza mkazi Wachisamariya pachitsime kuti: “Koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:14) Kodi Yesu anawatenga kuti “madzi” ameneŵa?
2. Kodi ndiati ali magwero a “madzi” ameneŵa, ndipo iwo anayenda kokha pambuyo pa chochitika chotani?
2 Mtumwi Yohane anapatsidwa mwaŵi m’masomphenya wakuwona magwero kumene “madzi” ameneŵa anachokera, monga momwe ananenera pa Chibvumbulutso 22:1 kuti: ‘Ndipo anandiwonetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.’ Inde, magwero a madzi onyezimira ngati krustalo ameneŵa okhala ndi mphamvu yopatsa moyo siwina aliyense koma Mpatsi wa Moyo, Yehova iyemwini, yemwe amawapereka kupyolera mwa Mwanawankhosayo, Yesu Kristu. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 21:6.) Popeza kuti ‘mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa’ watchulidwa, payenera kukhala pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu Waumesiya mu 1914, ndiko kuti, pambuyo pakuyamba kwa tsiku la Ambuye, pamene madzi a moyowo akuyamba kuyenda.—Chibvumbulutso 1:10.
3, 4. Kodi “madzi” ameneŵa amaimira chiyani, ndipo amakhalako kaamba ka yani?
3 Kodi madzi a moyo ameneŵa amaphiphiritsira chiyani? Amachitira chithunzi makonzedwe a Mulungu akubwezeretsa kuungwiro moyo wa anthu, moyo wosatha wangwiro pa dziko lapansi losinthidwa kukhala paradaiso. Madzi a moyowo amaimira makonzedwe onse a moyo kupyolera mwa Yesu Kristu. Kodi onse alipo tsopano? Ayi, osati onse, popeza kuti choyamba Mulungu ayenera kuchotsapo dongosolo lazinthu loipa liripoli ndi wolamulira wake wosaoneka ndi maso, Satana Mdyerekezi. Koma tingamwe “madzi” omwe alipo mwakumvetsera ndi kulabadira mbiri yabwino Yaufumu ndikuigwirizanitsa ndi miyoyo yathu.—Yohane 3:16; Aroma 12:2.
4 Motero, atasonyeza Yohane ‘mtsinje wa moyo,’ Yesu analankhula ndi Yohane ponena za chifuno Chake potumiza mngelo Wake ndi masomphenyawo. Ndiyeno Yohane anamva chilengezo chakuti: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.’ (Chibvumbulutso 22:17) Chifukwa chake, atumiki a Mulungu amatambasulira chiitanocho kwa akumva ludzu kuti ayambe kumwa m’makonzedwe a Mulungu opezera moyo wamuyaya pa dziko lapansi kupyolera mwa Mwanawankhosa wa Mulungu.—Yohane 1:29.
Chosoŵa cha Madzi a Moyo Chibuka
5. Kodi zinali motani kuti anthu anadzafunikira makonzedwe aumulungu ameneŵa?
5 Mwachisoni, makolo oyambirira abanja la anthu sanamamatire kunjira ya moyo imene ikapatsa mbadwa zawo mwaŵi wakusangalala ndi moyo waumunthu wangwiro kosatha m’mudzi waparadaiso. Moyo wosatha kaamba ka anthu unafunikiritsa kuti Adamu apange chosankha chaluntha chakutumikira Mlengi wake momvera. Mosonkhezeredwa ndi cholengedwa chauzimu chachipanduko, Hava anayamba ulendo umene unafikitsa anthu ku imfa, ndipo Adamu, mwamuna wake wangwiro, anasankha kugwirizana naye panjira yodzetsa imfa imeneyo. Chotero, monga mpatsi wa moyo wachibadwidwe ku mibadwo ya anthu yomadzayo, Adamu ndiyedi anayambitsa imfa kugwera banja lonse la anthu. Nchifukwa chake Baibulo limati: ‘Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Panali pambuyo pa kuchimwa kwa Adamu ndi Hava pamene iwo anayamba kuwonjezera ziŵalo zatsopano ku banja la anthu.—Salmo 51:5.
6. Kodi nchifukwa ninji Yehova anapanga makonzedwe akuti pakhale “madzi” ameneŵa?
6 Kodi Mulungu adatsekerezedwa kosatha m’kukwaniritsa chifuno chake cha dziko lapansi laparadaiso lodzala ndi anthu angwiro? Ndithudi, yankho Labaibulo nlakuti, ayi! Ngakhale kuli choncho, pofuna kukwaniritsa chifuno chake, Yehova anapanga makonzedwe achikondi omwe akachita motsutsa kulephera kwa Adamu kodzetsa ngozi komabe akakhala ogwirizana kotheratu ndi chiweruzo chachilungamo ndi chilungamo, zimene Zimamuimira kotheratu. Iye amachita zimenezi kupyolera mwa “mtsinje wa madzi a moyo.” Mwa umenewo, adzabwezeretsa moyo wangwiro waumunthu kwa anthu omvera, amene njira yawo yofikira Magwero a moyo inataidwa. Mtsinjewu umayenda m’lingaliro lake lenileni mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu. Chotero, mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, anthu, kuphatikizapo oukitsidwa kwa akufa, ayenera kumwa mu “mtsinje wa madzi a moyo.”—Yerekezerani ndi Ezekieli 47:1-10; Machitidwe 24:15.
7. Kodi makonzedwe a “madzi” ameneŵa akupangidwa pa maziko otani?
7 Yehova amasangalala nawo moyo wake wa iyemwini, ndipo amasangalala nakonso kupereka mwaŵi wa moyo waluntha kwa zolengedwa zake zina. Maziko a makonzedwe a Yehova operekera moyo ndiwo nsembe yadipo ya Yesu. (Marko 10:45; 1 Yohane 4:9, 10) Mawu a Mulungu akuloŵetsedwamonso, amene Baibulo nthaŵi zina limawatcha “madzi.” (Aefeso 5:26) Yehova Mulungu ngwaufulu kunena kuti, “Idzani” kwa zolengedwa zaumunthu, zimene zinataikiridwa makonzedwe oyambirira amene Mulungu anawapanga kwa anthu aŵiri angwiro, Adamu ndi Hava.
Kagulu ka Mkwatibwi Kakupereka Chiitanocho, “Idzani”
8. Kodi “madzi” ameneŵa anaperekedwa kwa yani choyamba ndipo liti?
8 Oyamba kupereka chiitano chakuti “Idzani” ndiaja opanga mkwatibwi wophiphiritsira wa Mwanawankhosa, Mwana wachisamba wauzimu wa Yehova. (Chibvumbulutso 14:1, 3, 4; 21:9) Mkwatibwi wauzimu wa Kristu sakunena kuti, “Idzani” kwa iyemwini, ndiko kuti, kwa awo amene Yehova Mulungu adzasonkhanitsabe monga mbali ya kagulu ka mkwatibwi kotero kuti apange kagulu ka 144,000. Mawu achiitanowo akuperekedwa kwa anthu oyembekezera kupata moyo waumunthu wangwiro padziko lapansi pambuyo pa Armagedo. (Chibvumbulutso 16:14, 16) Mkati mwa mapeto ano a dongosolo lazinthu liripoli chiyambire 1914, tamva chiitanocho chikuperekedwa ndi “mkwatibwi,” mogwirizana ndi mzimu woyera wa Mulungu.
9. Kodi timadziŵa motani kuti siali akagulu kakang’ono kokha?
9 Mosangalatsa, bukhu lotsirizira la Baibulo limasonyeza kuti ‘khamu lalikulu, limene palibe munthu akhoza kuliŵerenga,’ likavomereza kulengezedwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndipo likadziphatika nganganga ku mbali ya boma lachifumu limenelo. (Chibvumbulutso 7:9, 10, 16, 17) Kodi ndinu mmodzi wa khamu lalikulu limenelo? Pamenepo, “wakumva anene, Idzani.”
Mzimu ndi Mkwatibwi Anena, “Idzani”
10. Kodi madzi ophiphiritsirawo ayenera kutuluka kuti ndipo, chifukwa ninji?
10 Komano nchifukwa ninji Mulungu ndi Mkwati wophiphiritsira sakutchulidwa pa Chibvumbulutso 22:17? Choyamba, onani kuti vesilo silikunena kuti mzimuwo umagwira ntchito pansi pa chitsogozo cha yani. Komabe, kutchulidwa kwa mzimu kumapereka malingaliro athu kwa Yehova Mulungu iyemwini. Atateyo sakuchotsedwa m’chithunzicho, popeza kuti iye ndiye Magwero enieni a mzimu woyera. Chachiŵiri, Mwanayo amagwirizana kotheratu ndi Atate wake, monga momwe iyemwini akunenera kuti: ‘Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho.’ (Yohane 5:19) Ndiponso, pamene kuli kwakuti chiitano chimenechi ndicho mawu ouziridwa ochokeradi kwa Yehova Mulungu, anthu angalandire chitsogozo chaumulungu, kapena “mawu ouziridwa,” kupyolera mwa Yesu Kristu, ‘Mawu’ amenewo. (Chibvumbulutso 22:6, NW; onaninso 22:17, Reference Bible, mawu amtsinde; Yohane 1:1) Pamenepa, timagwirizanitsa Kristu, Mkwatiyo, moyenerera ndi chiitano chimenechi. Inde, tingakhale otsimikiza kuti onse aŵiri Yehova Mulungu, Atate wa Mkwatiyo, ndi Yesu Kristu, Mkwatiyo, amagwirizana ndi “mkwatibwi” kupyolera mwa mzimu woyera m’kunena kuti, “Idzani.”
11, 12. (a) Kodi panali chisonyezero choyambirira chotani chakuti chiitano chakudzamwa chikafutukulidwa? (b) Kodi ndimotani mmene nkhaniyo inakhalira yomvekera bwino mowonjezereka mkati mwa zaka?
11 Kwa zaka makumi ambiri chiitano chimenechi chakuti “idzani” chakhala chikupita kwa anthu akumva ludzu la “madzi a moyo.” Ngakhale kumbuyoko mu 1918, kagulu ka mkwatibwi kanayamba kulalikira uthenga umene kwenikweni unakhudza aja omwe akakhala padziko lapansi. Unali nkhani yapoyera yamutu wakuti “Mamiliyoni Amene Ngamoyo Tsopano Sangamwalire Konse.” Iyo inapereka chiyembekezo chakuti ambiri akapulumuka Armagedo ndiyeno pambuyo pake nkupeza moyo wamuyaya padziko lapansi Laparadaiso pansi pa Ufumu Waumesiya wa Mulungu. Koma uthenga umenewo sunasonyeze mwachindunji njira yopezera mwaŵi wachipulumutso umenewu, kusiyapo mwa chilungamo chachisawawa.
12 Kuti afikire anthu owonjezereka ndi chiitano chakuti, “Idzani” mu 1922 uthenga uwu unanka kwa onse omwe anali okondwerera kutumikira Mulungu: “Lengezani Mfumu ndi Ufumuwo.” Mu 1923 kagulu ka mkwatibwi kanamvetsetsa kuti “nkhosa” ndi “mbuzi” za m’fanizo la Yesu pa Mateyu 25:31-46 zikuwonekera Armagedo isanakanthe. Ndiyeno, mu 1929, The Watch Tower ya March 15 inali ndi nkhani yakuti “Chiitano Chachisomo.” Lemba lake la mutu linali Chibvumbulutso 22:17, ndipo inagogomezera thayo la kagulu ka mkwatibwi lopereka chiitano chakuti, “Idzani.”—Masamba 87-9.a
Nkhosa Zina Zikuloŵamo m’Kunena Kuti, “Idzani”
13, 14. M’ma 1930, kodi nchiwongolero chowonjezereka chotani chimene chinaperekedwa chakuti enanso akamwa madzi ophiphiritsirawo?
13 Kuwonjezerapo, kalelo mu 1932, The Watchtower inatchula thayo la “nkhosa zina,” nazonso, kumati, “Idzani.” (Yohane 10:16) M’kope lake la August 1, tsamba 232, ndime 29 inati: “Mboni za Yehova tsopano ziri ndi changu chonga chija cha Yehu ndipo ziyenera kulimbikitsa gulu la Yonadabu [nkhosa zina] kutsagana nazo ndikukhala ndi phande m’kulengeza kwa ena kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” Kenaka, pambuyo pogwira mawu Chibvumbulutso 22:17, ndimeyo inati: “Odzozedwa alimbikitsetu onse ofuna kukhala ndi phande m’kulengeza mbiri yabwino ya ufumuwo. Iwo satofunikira kukhala odzozedwa a Ambuye kuti alengeze uthenga wa Ambuye. Nchitonthozo chachikuludi kwa mboni za Yehova kudziŵa tsopano kuti zaloledwa kupereka madzi a moyo ku gulu la anthu amene angapulumutsidwe pa Armagedo ndikupatsidwa moyo wosatha padziko lapansi chifukwa cha kuchuluka kwa ubwino wa Yehova.”b
14 Kuchokera 1934 kunka mtsogolo, otsalira odzozedwa anasonyeza kuti nkhosa zina zimenezi ziyenera tsopano kudzipereka zokha kwa Mulungu ndikuphiphiritsa kudzipereka kumeneku ndiubatizo wa m’madzi ndiyeno nkugwirizana ndi kagulu ka mkwatibwi m’kunena kuti, “Idzani” kwa enanso akumva ludzu. Chotero, tsopano panali chiitano chachindunji choperekedwa ndi kagulu ka mkwatibwi chakusonkhanitsa nkhosa zina zakumva ludzu zimenezi mu “gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi,” Yesu Kristu. (Yohane 10:16) Mu 1935 otsalira odzozedwa anasonkhezeredwa kuphunzira pamsonkhano wawo waukulu wachaka chimenecho kuti gulu la onga nkhosa la anthu kwa amene iwo ankanena kuti, “Idzani” kwenikweni linali ‘khamu lalikulu’ la pa Chibvumbulutso 7:9-17. Izi zinapereka chisonkhezero chachikulu ku ntchito yoitanayo.
15. Kodi ndimotani mmene “mzimu” unaloŵetsedweramo m’chiitano chakuti, “Idzani”?
15 Mwakunena kuti, “Idzani” kagulu ka mkwatibwi kanagwirizana ndi mzimu wa Mulungu. Pogwiritsira ntchito mzimu wake kumasulira tanthauzo la maulosi a Mawu ake olembedwa, iye anachititsa otsalira a kagulu ka mkwatibwi kupereka chiitanocho. Maulosiŵa amene anali maziko a chiitano chawo adauziridwa ndi mzimu wa Mulungu. Chotero unalidi, kwenikweni, mzimu wa Mulungu womayenda kupyolera mwa Kristu ndi mkwatibwi wake umene unkanena kwa khamu lalikulu la nkhosa zina kuti, “Idzani.”—Chibvumbulutso 19:10.
16. Kodi mzimu ndi mkwatibwi akuphatikizidwa motani m’chiitanocho lerolino?
16 Kufikira lerolino mzimuwo ndi mkwatibwi, oimiridwa ndi otsalira, ‘akunenabe kuti, Idzani.’ Otsalira amauza nkhosa zina zimenezi kuitana enanso kuti ‘adze.’ Iwo sayenera kusunga kwa iwo okha “madzi a moyo,” pamene alipo lerolino. Ayenera kumvera lamulo lochokera kwa “mzimu ndi mkwatibwi,” lakuti: “Wakumva anene, Idzani.” Onse akupha ludzu lawo ayenera kupereka chiitanocho. Ayenera kuchipereka kwa aliyense mosasankha fuko, mtundu, chinenero, kapena chipembedzo—aliyense kulikonse! “Madzi a moyo” amene alipo panthaŵi ino ndamene Mboni za Yehova zikuitanira ndikuthandiza anthu onse kudzamwa, kwaulere!
17. Kodi ndi “madzi” amtundu wanji amene alipo lerolino?
17 Padziko lonse lapansi, Mwanawankhosayo, Yesu Kristu, akutsogoleradi khamu lalikulu ku “akasupe a madzi a moyo.” (Chibvumbulutso 7:17) Iwoŵa sali konse madzi oipitsidwa, koma ali madzi oyera, ozizirira, abwino ochokera mwachindunji ku Magwero ake. Madzi ophiphiritsira ameneŵa amatanthauza zochuluka kuposa madzi m’lingaliro la kumvetsetsa chowonadi cha Baibulo; amatanthauza makonzedwe onse a Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu omwe amayamba ngakhale tsopano kuika khamu lalikulu panjira yonkira ku moyo wangwiro wamuyaya wachimwemwe.
Loŵanimo Tsopano m’Chilengezocho
18. Kodi chiitanocho nchachikulu motani m’nthaŵi yathu?
18 Khamu lalikulu limeneli lafika kale chiŵerengero cha mamiliyoni angapo. Iwo akupitirizabe mwachangu kumalengeza mbiri yabwino ya Ufumuwo padziko lonse lokhalidwa ndi anthu. Iwo amachitira lipoti ntchito zawo zakumunda mokhazikika polalikira mbiri yabwino ya Ufumu, imene tsopano yafika ku maiko 212. Malinga ndi mmene nthaŵi ya mkati mwa chimaliziro cha dongosolo lazinthu ikulolera, chiitanocho chidzapitirizabe mogwirizana ndi kuleza mtima ndi chipiriro cha Yehova Mulungu, Wosunga Nthaŵi Wamkulu. Iye adzadziŵa pamene nthaŵi idzakwanira ndi pamene mphindi yauchamuna idzafika yakudzidziŵitsa kwa onse kuti iye ndiye Yehova, monga momwe walonjezera kutero m’ndemanga zobwerezedwabwerezedwa za ulosi wa Baibulo.—Ezekieli 36:23; 38:21-23; 39:7.
19. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti “madzi” ameneŵa amaperekedwa kwaulere?
19 Komabe, pamene nthaŵi ikadalipo, ziŵalo za khamu lalikulu zimakhala ndi phande mwachisangalalo pamodzi ndi otsalira a kagulu ka mkwatibwi m’kunena kuti: ‘Idzani mudzamwe madzi a moyo kwaulere!’ Olengeza mbiri yabwino yopulumutsa moyo imeneyi akupereka chilengezocho kwaulere, osalipiritsa mautumiki awo omwe amawapereka polengeza uthenga Waufumu kuzungulira padziko lonse.
20. Kodi nchiyani chidzakhala chotulukapo chifukwa chakukhalapo kwa “madzi” ameneŵa?
20 Madzi a moyo tsopano akupezeka kuzungulira dziko lonse, kotero kuti anthu ofuna kuŵamwa angatero ndikukhutiritsidwa mokwanira ndi zotulukapo zopulumutsa moyo. Anthu owomboledwa adzasangalala ndi moyo wopanda malire pompano padziko lapansi, limene lidzasandulizidwa kukhala paradaiso, kulemekeza chifuno chamtengo wapatali cha Yehova. Mlengi wathu sanapanga dziko lapansi kwachabe koma kuti likhale munda wa Edene wokuta dziko lonse, kapena Paradaiso wa chisangalalo, wokhalidwa ndi zolengedwa zaumunthu zangwiro m’chifaniziro ndi chifanefane cha Mulungu.
21. Kodi chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chidzakwaniritsidwa motani?
21 Motsimikizirikadi, udzakhala mwaŵi waukulu wosaneneka ndi chisangalalo kukhala m’dziko latsopano loterolo! Pamenepo ntchito imene Mulungu anawapatsa anthu aŵiri oyambirira pa Genesis 1:27, 28 idzakwaniritsidwa mokulira. Chithokozo chinketu ku kasamaliridwe kaukatswiri ka Yehova ka tsoka limene linagwera banja la anthu, dziko lapansi lidzagonjetsedwa kuukulu wokhala paradaiso ndipo lidzadzazidwa ndi fuko la anthu angwiro. Inde, Mulungu adzayang’ana zonse wazipangazo, ndipo, tawonani, zidzakhala zabwino kwambiri. Kodi mudzakhalako? Ngati nditero, pamenepo muyenera kuyamba tsopano kumwa mwachiyamikiro madzi a moyo kwaulere. “Idzani” ndikumwa mmene mungafunire ndikupha ludzu lanu ndi madzi a moyo amene tsopano ayamba kuyenda ndipo adzayenda mokwanira mkati mwa Zaka Chikwi zirinkudza. Ndipo lolani yense wakumva chiitano chabwino chimenechi anene: “Idzani.”
[Mawu a M’munsi]
a Mwazinthu zina, nkhani imeneyi inanena kuti: “Sipanakhalepo umboni waukulu motere wa chowonadi monga mkati mwa zaka zoŵerengeka zapitazo. . . . Otsalira akuwabweretsera uthenga wachisangalalo, namati kwa iwo: ‘Ndipo amene afuna, amwe madzi a moyo kwaulere.’ Iwo akuuzidwa kuti tsopano angaime ku mbali ya Ambuye, ndimotsutsana ndi Mdyerekezi, ndikulandira dalitso. Kodi sigulu la anthu oterowo amene tsopano angafunefune chifatso ndi chilungamo, ndi kubisidwa m’tsiku lakusonyeza mkwiyo wake, ndikuwolotsedwa m’nkhondo yaikulu ya Armagedo ndiyeno kukhala ndimoyo kosatha osafa? (Zef. 2:3) . . . Kagulu ka otsalira okhulupirika kamaloŵamo m’chiitano chachisomo ndikunena, ‘Idzani.’ Uthenga umenewu uyenera kulengezedwa kwa awo okhala ndi chikhumbo cha chilungamo ndi chowonadi. Ziyenera kuchitidwa tsopanoli.”
b The Watchtower ya August 15, 1934, nayonso inasonya ku thayo la nkhosa zina ndipo patsamba 249, ndime 31 inati: “Gulu la Yonadabu ndiamene ‘amamva’ uthenga wa chowonadi, ndiamene ayenera kunena kwa owamvetsera kuti: ‘Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.’ (Chibv. 22:17) A gulu la Yonadabu ayenera kupitira limodzi ndi a kagulu ka Yehu kophiphiritsiridwa, ndiwo, odzozedwa, ndikulengeza uthenga wa ufumuwo, ngakhale kuti sali mboni zodzozedwa za Yehova.”
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi ndi “madzi” otani omwe akutchulidwa pa Chibvumbulutso 22:17?
◻ Kodi ndiati ali magwero a “madzi” ameneŵa?
◻ Kodi nchifukwa ninji “madzi” amenewo ali ofunika, ndipo kodi nliti kokha pamene iwo anayamba kuyenda?
◻ M’lemba lathu, kodi kutchula “mzimu” kumasonyeza chiyani, ndipo kodi ndimotani mmene “mkwatibwi” akuloŵetsedweramo?
◻ Kodi ndani amene angamwe “madzi” amenewo, ndipo ndichotulukapo chotani?