Khalani Okonzeka Kaamba ka Tsiku la Yehova!
Mfundo Zazikulu Zochokera mu Atesalonika Woyamba
TSIKU la Yehova! Akristu a m’Tesalonika wakale analingalira kuti linayandikira. Kodi iwo anali olondola? Kodi ilo likadza liti? Imeneyo inali nkhani yaikulu imene mtumwi Paulo analembera Atesalonika m’kalata yake yoyamba, yotumizidwa kuchokera ku Korinto pafupifupi chaka cha 50 cha Nyengo Yathu ino.
Paulo ndi Sila anakhazikitsa mpingo m’Tesalonika, likulu la chigawo cha Roma cha Makedoniya. (Machitidwe 17:1-4) Pambuyo pake, m’kalata yake yoyamba kwa Atesalonika, Paulo anayamikira, kupereka chilangizo, ndikukamba za tsiku la Yehova. Nafenso tingapindule ndi kalata imeneyi, makamaka tsopano pamene tsiku la Yehova layandikira kwenikweni.
Yamikirani ndi Kulimbikitsa
Paulo choyamba anawayamikira Atesalonika. (1:1-10) Chiyamikiro chinaperekedwa chifukwa cha ntchito yawo yokhulupirika ndi chipiriro. Kunali koyamikirikanso, kuti iwo ‘analandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha mzimu woyera.’ Kodi mumawayamikira ena, monga momwe Paulo anachitira?
Mtumwiyo anakhazikitsa chitsanzo chabwino. (2:1-12) Mosasamala kanthu ndikuchitiridwa chipongwe m’Filipi, iye ‘analimbika pakamwa mwa Mulungu kulankhula uthenga wabwino’ kwa Atesalonika. Iye anatsutsa kusyasyalika, chisiriro, ndi kufunafuna ulemerero. Paulo sanakhale vuto lodya ndalama koma anali wodekha kwa iwo monga momwe nakubala amalerera mwana wake. Nchitsanzo chabwino chotani nanga kwa akulu lerolino!
Mawu otsatira a Paulo analimbikitsa Atesalonika kukhalabe olimba pamene akuzunzidwa. (2:13–3:13) Iwo adapirira chizunzo pamanja a anthu a m’dziko lawo, ndipo Timoteo anabweretsa lipoti labwino kwa Paulo lonena za mkhalidwe wawo wauzimu. Mtumwiyo anawapempherera kuti achuluke m’chikondi ndikuti mitima yawo ilimbitsidwe. Mofananamo, Mboni za Yehova tsopano zimapempherera alambiri anzawo omazunzidwa, kuwalimbikitsa ngati kuli kotheka, ndikusangalala ndi malipoti a kukhulupirika kwawo.
Khalanibe Ogalamuka Mwauzimu!
Chotsatira Atesalonika analandira uphungu. (4:1-18) Iwo anafunikira kuyenda kotheratu m’njira yokondweretsa Mulungu, akumasonyeza chikondi chaubale chowonjezereka ndikugwira ntchito ndi manja awo kudzipezera zosoŵa. Ndiponso, iwo anafunikira kumatonthozana ndi chiyembekezo chakuti m’nthaŵi yakukhalapo kwa Yesu okhulupirira odzozedwa ndi mzimu omwe adamwalira akaukitsidwa choyamba ndi kugwirizanitsidwa naye. Pambuyo pake, odzozedwa okhalabe ndi moyo akaukitsidwa pa imfa yawo ndikugwirizana ndi Kristu ndi awo omwe adaukitsidwira kale ku moyo wakumwamba.
Kenaka Paulo akulankhula za tsiku la Yehova ndi kupereka uphungu wowonjezereka. (5:1-28) Tsiku la Yehova linkadza ngati mbala, ndi chiwonongeko chamwadzidzidzi chotsimikizirika pambuyo pa mfuu yakuti: “Mtendere ndi mosatekeseka.” Chotero Atesalonika anafunikira kukhalabe ogalamuka mwauzimu, otetezeredwa ndi chapachifuŵa cha chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyembekezo cha chipulumutso monga chisoti. Iwo anafunikira kukhala ndi ulemu wozama kwa otsogoza mumpingo ndipo anafunikira kupeŵa zoipa, monga ifenso.
Kalata yoyamba ya Paulo kwa Atesalonika iyenera kutifulumiza kuyamikira ndi kulimbikitsa okhulupirira anzathu. Iyeneranso kutisonkhezera kupereka chitsanzo chabwino m’mayendedwe ndi maganizo. Ndipo motsimikizirikadi uphungu wake ungatithandize kukhala okonzekera kaamba ka tsiku la Yehova.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]
Chapachifuŵa ndi Chisoti: Polimbikitsa kukhala maso kwauzimu, Paulo analemba kuti: ‘Tivale chapachifuŵa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chiri chiyembekezo cha chipulumutso.’ (1 Atesalonika 5:8) Chapachifuŵa chinali chida cha wankhondo chotetezera chifuŵa, chokhala ndi zikamba, unyolo, kapena chitsulo cholimba. Mofananamo, chapachifuŵa cha chikhulupiriro chimatitetezera mwauzimu. Ndipo bwanji ponena za chisoti chamakedzana? Kaŵirikaŵiri chopangidwa ndi chitsulo, chinali chovala chankhondo chakumutu cholinganizidwira kutetezera womenya nkhondo mkati mwa nkhondo. Monga momwe chisoti chinatetezerera mutu wa wankhondo, momwemonso chiyembekezo cha chipulumutso chimatetezera mphamvu za kulingalira, motero kukhozetsa Mkristu kusunga umphumphu. Ha, nkofunika kwambiri chotani nanga kuti anthu a Yehova avale chida chauzimu choterocho!—Aefeso 6:11-17.