Lemekezani Yehova—Chifukwa Ninji Ndipo Motani?
“Amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.”—1 SAMUELI 2:30.
1. Kodi ndani omwe amapatsidwa mphotho zotchuka zapadziko lonse za Nobel, kodi izo zimaphatikizaponji, ndipo kodi ambiri amazilingalira motani mphothozi?
CHAKA chirichonse ziungwe zinayi za ku Scandinavia zimapereka mphotho za Nobel kwa anthu amene ‘anapatsa anthu phindu lalikulu koposa m’chaka chapita.’ Mphothozo zimaperekedwa kaamba ka zomwe zakwaniritsidwa m’zigawo zisanu ndi chimodzi za mautumiki. Mphotho ya Nobel imalingaliridwa ndi anthu ambiri kukhala ulemu waukulu wothokoza nawo munthu aliyense.
2. Kodi ofupa mphotho za Nobel amanyalanyaza ndani, ndipo kodi nchifukwa ninji Iye ali makamaka woyenerera kuchitiridwa ulemu?
2 Pamene kuli kwakuti sikulakwa kuchitira ulemu anthu owuyenerera, kodi anthu opereka ulemuwo amalingalirapo konse zolemekeza munthu wamkulu Wochitira Zabwino anthu? Wochitira Zabwino ameneyu ndiye wapereka madalitso osaneneka kwa anthu kuyambira pamene analenga mwamuna ndi mkazi oyamba pafupifupi zaka 6,000 zapitazo. Kulephera kobwerezabwereza kumlemekeza kungatikumbutse mawu a Elihu, bwenzi la Yobu wakale, yemwe anati: “Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga, Wakupatsa nyimbo usiku?” (Yobu 35:10) Wochitira Zabwino wamkuluyu amapitirizabe kuchita ‘zabwino, natipatsa zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima ndi chakudya ndi chikondwero.’ (Machitidwe 14:16, 17; Mateyu 5:45) Zowonadi Yehova ndiye Mpatsi wa ‘mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro.’—Yakobo 1:17.
Chimene Kuchitira Ulemu Kumatanthauza
3. Kodi ndi mawu a Chihebri ndi Chigiriki ati omwe amatembenuzidwa monga “kulemekeza,” ndipo kodi matanthauzo awo ngotani?
3 Liwu loyambirira Lachihebri lakuti kulemekeza, ka·vohdhʹ, kwenikweni limatanthauza “kulemera.” Chotero munthu wolemekezedwayo amalingaliridwa kukhala wolemera, wolemekezeka, kapena yemwe ndibwana. Mwachiwonekere, liwu Lachihebri limeneli, ka·vohdhʹ, limatembenuzidwanso kaŵirikaŵiri m’Malemba monga “ulemerero,” kusonyezanso mmene munthu wolemekezedwayo amalingaliridwira kukhala wolemekezeka kapena wofunika. Liwu lina Lachihebri lakuti, yeqarʹ, lotembenuzidwa “kulemekeza” m’Malemba, limatembenuzidwanso monga “chamtengo” ndi “zinthu zamtengo.” Chotero m’Malemba Achihebri, liwu lakuti kulemekeza nlogwirizana nlakuti ulemerero ndi lakuti chamtengo. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kulemekeza” m’Baibulo ndilo ti·meʹ, ndipo nalonso liri ndi tanthauzo la kukwezeka, phindu, ndi chamtengo.
4, 5. (a) Kodi kuchitira munthu ulemu kumatanthauzanji? (b) Kodi nchochitika chotani chosimbidwa mu Estere 6:1-9 chomwe chimafotokoza mwafanizo chomwe chikuphatikizidwa m’kuchitira ulemu?
4 Chotero munthu amalemekeza mnzake mwakumpatsa munthuyo ulemu waukulu ndikumkweza. Kuti tifotokoze mwafanizo, lingalirani mkhalidwe wosimbidwa m’Baibulo wokhudza Moredekai Wachiyuda wokhulupirika. Nthaŵi ina Moredekai anavumbula chiwembu chofuna kupha Mfumu Ahaswero wa Perisiya yakale. Pambuyo pake, usiku pamene tulo tidamwazikira mfumu, kachitidwe ka Moredekai kadakadziŵitsidwa kwa mfumu. Chotero iyo inafunsa anyamata ake kuti: ‘Anamchitira Moredekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi?’ Iwo anayankha kuti: ‘Sanamchitira kanthu.’ Nchachisoni chotani nanga! Moredekai anapulumutsa mfumu, ndipotu mfumuyo inalephera kumuyamikira.—Estere 6:1-3.
5 Chotero, pamene mwaŵi unamgwera, Ahaswero anafunsa nduna yake yaikulu, Hamani, mmene angalemekezere bwino munthu yemwe mfumu yakondwera naye. Mosataya nthaŵi Hamani analingalira mumtima mwake nati: ‘Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine?’ Chotero Hamani ananena kuti munthuyo ayenera kuvekedwa ‘chovala chachifumu’ ndi kukwera “kavalo amakwerapo mfumu.” Iye anamaliza nati: ‘Namuyendetse pa kavaloyo m’khwalala la m’mudzi, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.’ (Estere 6:4-9) Munthu wolemekezedwa motero akakwezedwa kwambiri ndi anthu onse.
Chifukwa Chimene Yehova Ngwoyenerera Ulemu
6. (a) Kodi ndani woposa onse amene amayenerera kuti timulemekeze? (b) Kodi nchifukwa ninji liwu lakuti “wamkulu” likumufotokoza bwino Yehova?
6 M’mbiri yonse yakale anthu akhala akuchitiridwa ulemu, kaŵirikaŵiri omwe asonyezedwa samauyenerera. (Machitidwe 12:21-23) Komabe kodi ndani yemwe amayenerera kulemekezedwa kuposa onse? Eya, ndithudi ndiye Yehova Mulungu! Iye amauyenerera ulemu wathu chifukwa chakuti ngwamkuludi. Kaŵirikaŵiri liwu lakuti “wamkulu” limagwiritsiridwa ntchito kwa iye. Iye Ngwamkulu, Mpangi Wamkulu, Mlengi Wamkulu, Mfumu Yaikulu, Mlangizi Wamkulu, Mbuye Wamkulu. (Salmo 48:2; Mlaliki 12:1, NW; Yesaya 30:20; 42:5; 54:5, NW; Hoseya 12:14, NW) Munthu wamkulu ngwokwezeka, wolemekezeka, womveka, woduma, wotchuka, ndi wowopsa. Yehova ngwosayerekezeka, alibe wolingana naye, iye ngwoposa onse. Mfundoyi anaichitira umboni mwiniyekha, nati: “Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?”—Yesaya 46:5.
7. Kodi ndim’njira pafupifupi zingati zosiyana zomwe kunganenedwe kuti Yehova Mulungu ngwapadera, ndipo kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti ulamuliro wake ngwosayerekezeka?
7 Yehova Mulungu ngwosayerekezeka pafupifupi m’njira zisanu ndi ziŵiri zapadera, zomwe zimapereka zifukwa zenizeni zomulemekezera. Choyamba, Yehova Mulungu amayenerera ulemu waukulu chifukwa chakuti ulamuliro wake ngwosafanana ndi uliwonse. Ambuye Yehova ndiye Mfumu Yachilengedwe Chonse—ngwamkulukulu. Iye ndiye Woweruza wathu, Mpatsi wa lamulo, ndi Mfumu. Anthu onse okhala kumwamba ndi padziko lapansi amaŵerengera kwa Iye; chikhalirechobe iye samaŵerengera kwa munthu aliyense. Iye wafotokozedwa bwino kukhala ‘wamkulu, wamphamvu, ndi wowopsa.’—Deuteronomo 10:17; Yesaya 33:22; Danieli 4:35.
8. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti palibe angafanane ndi Yehova (a) ponena za udindo wake? (b) ponena za umuyaya wake?
8 Chachiŵiri, Yehova Mulungu ngwoyenerera ulemu waukulu chifukwa chakuti udindo wake ngwosafanana ndi wa munthu aliyense. Iye ‘Ngwamtali Wotukulidwa,’ Wam’mwambamwamba. Iye ngwoposa kwambiri zolengedwa zake zonse zapadziko lapansi! (Yesaya 40:15; 57:15; Salmo 83:18) Chachitatu, Yehova Mulungu ayenera kulemekezedwa kuposa onse chifukwa chakuti umuyaya wake ngwosatha. Ndiyekhayu amene alibe chiyambi, pokhala wa kunthaŵi zonka muyaya.—Salmo 90:2; 1 Timoteo 1:17.
9. Kodi ndim’njira iti mmene Yehova aliri wosayerekezeka (a) ponena za ulemerero wake? (b) ponena za mikhalidwe yake yaikulu?
9 Chachinayi, Yehova Mulungu ngwoyenerera ulemu waukulu chifukwa cha ukulu wa ulemerero wake. Iye ndiye “Atate wa mauniko.” Thupi lake nlonyezimira kwambiri kwakuti palibe munthu angathe kumpenya ndi kukhalabe ndi moyo. Iye ngwowopsadi. (Yakobo 1:17; Eksodo 33:22; Salmo 24:10) Chachisanu, timafunikira kumchitira ulemu waukulu Yehova Mulungu chifukwa cha mikhalidwe yake yodabwitsa. Iye ngwamphamvuzonse, mphamvu zake nzachiyaya; iye ngwodziŵa zonse, nzeru zake nzachiyaya; iye ngwangwiro kotheratu m’chiweruzo; ndipo mwiniyo nchikondi.—Yobu 37:23; Miyambo 3:19; Danieli 4:37; 1 Yohane 4:8.
10. Kodi ndim’njira yotani mmene Yehova sangafananire ndi aliyense (a) ponena za ntchito zolenga ndi chuma? (b) ponena za dzina lake ndikutchuka?
10 Chachisanu ndi chimodzi, Yehova Mulungu ngwoyenerera kuchitiridwa ulemu waukulu kwambiri chifukwa cha ntchito zake zazikulu zachilengedwe. Monga Mlengi wa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi, iye panthaŵi imodzimodziyo ndiye Mwiniwake Wamkulu wa zinthu zonse. Pa Salmo 89:11 timaŵerenga kuti: “Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu.” Chachisanu ndi chiŵiri, Yehova Mulungu wathu ngwoyenerera ulemu kuposa onse chifukwa chakuti, dzina lake ndi kutchuka kwake nzosatha, zosafanana ndi aliyense. Ndiyekhayo yemwe ali ndi dzina lakuti Yehova, lotanthauza “Iye Amachititsa kuti Zikhaleko.”—Onani Genesis 2:4, NW, mawu amtsinde.
Mmene Mungalemekezere Yehova
11. (a) Kodi ndinjira zina ziti zimene tingalemekeze nazo Yehova? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti tikulemekezadi Yehova mwa kumkhulupirira iye?
11 Polingalira mikhalidwe yonse ya Yehova, kodi tingamlemekeze motani? Monga momwe tidzawonera, tingamlemekeze mwakumuwopa mwaulemu, mwa kumumvera, mwakumuvomereza m’njira zathu zonse, mwakupereka mphatso, mwakumutsanzira, ndi mwakumupempha. Tingamlemekezenso mwakuika chikhulupiriro mwa iye, mwakumudalira ngakhale kuti zinthu zivute zitani. Tikufulumizidwa kuti, “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” Chotero timalemekeza Yehova Mulungu mwakulabadira mawu ake. Mwachitsanzo, iye akuti: “Usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata.” (Miyambo 3:5; Yesaya 41:10) Kulephera kumkhulupirira kotheratu kukakhala kumnyoza.
12. Kodi chimvero ndi mantha zimachita mbali yanji m’kulemekeza Yehova?
12 Njira yapafupi imene tingamlemekeze nayo Yehova Mulungu njakumumvera. Ndipo chofunika kwambiri pakumverako ndicho mantha aumulungu, inde, kuwopa kusamkondweretsa Mulungu. Osonyeza kugwirizana kokhala pakati pa kuwopa ndi kumvera ndiwo mawu a Yehova kwa Abrahamu pamene Abrahamu momvera anayesa kupereka nsembe Isake, mwana wake. “Tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu,” anatero Yehova. (Genesis 22:12) Pofotokoza zimene ana amaŵerengera kwa makolo awo, mtumwi Paulo anasonyezanso kuti chimvero ndi kulemekeza zimayendera limodzi. (Aefeso 6:1-3) Chotero mwakumvera malamulo a Mulungu, omwe ngosalemetsa, timalemekeza Yehova. Mosakaikira, kusamvera Yehova Mulungu kukakhala kumnyoza.—1 Yohane 5:3.
13. Kodi kulemekeza Mulungu kudzatichititsa kukhala ndi mkhalidwe wotani wamaganizo ponena za ntchito ndi makonzedwe athu?
13 Kuwonjezera apa, tingamchitire ulemu Yehova Mulungu mwa kulabadira uphungu wa pa Miyambo 3:6 wakuti: “Umlemekeze m’njira zako zonse [inde, kumuvomereza], ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Wophunzira Yakobo akutipatsa uphungu wabwino pamfundoyi. Mmalo mwakukhalabe modzidalira tsiku ndi tsiku, kukhulupirira mphamvu zathu, tifunikira kumanena kuti: ‘Akalola Yehova, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakuti kakuti.’ (Yakobo 4:15) Unali mwambo zaka zambiri zapitazo kwa Ophunzira Baibulo Amitundu Yonse kuwonjezera zilembo zachidule izi D.V. pandemanga iriyonse yokhudza zamtsogolo, zomwe zimaimira Deo volente, kutanthauza “akalola Mulungu.”
14. (a) Kodi ndimkhalidwe wamaganizo wotani womvana ndi kuyesayesa kwathu umene tiyenera kutenga kuti tilemekeze Mulungu? (b) Kodi ndinjira yotani yomwe imasonyezedwa m’chigwirizano ndi kufalitsa mabuku a Watch Tower Society?
14 Timalemekezanso Yehova Mulungu mwakusonyeza mkhalidwe wodzichepetsa, tikumathokoza Mulungu ndi zipambano zirizonse zimene tingakhale tikusangalala nazo. Ponena za uminisitala wake mtumwi Paulo anati moyenerera: ‘Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.’ (1 Akorinto 3:6, 7) Zowonadi, Paulo anali wodera nkhaŵa ndikuchitira ulemu woyenera Mulungu, osati kudzichitira iyemwini kapena kuchitira munthu wina. Chotero, lerolino, mabuku a Watch Tower Society samadziŵitsa anthu omwe amaŵalemba, ndipo olembawo amapeŵa kulola ena kudziŵa zomwe athandizirako. Mwanjira imeneyi, chisamaliro chimasumikidwa pachidziŵitsocho, chomwe chalinganizidwira kulemekeza Yehova, ndipo osati munthu aliyense.
15. Kodi nchitsanzo chiti chomwe chimafotokoza mwafanizo mavuto amene anthu ena amakhala nawo pomvetsetsa kudzichepetsa kwa Mboni za Yehova?
15 Lamulo ili la kusumika chisamaliro pa Yehova, ndikumlemekeza mwakuteroko, limaŵadabwitsa ena. Zaka zoŵerengeka zapitazo, poika ziwiya zokuzira mawu kaamba ka nkhani yapoyera mu Central Park ya mu Mzinda wa New York, Mboni zinkaseŵera matepi a Kingdom Melodies monga choyesera zokuzira mawuzo. Okwatirana ovala mwaudongo anafunsa mmodzi wa Mbonizo kuti zinali nyimbo zotani. Popeza analingalira kuti okwatiranawo anali Mboni, iye anaŵayankha kuti: “Imeneyo ndiyo Kingdom Melodies Na. 4.” “Tamva, koma kodi ndani analemba nyimbozi?” iwo anafunsabe tero. Mboniyo inayankha kuti: “Pepani, wolembayo satchulidwa dzina.” Okwatiranawo anayankha kuti: “Anthu omwe amalemba nyimbo zamtundu umenewu samatero popanda kutchulidwa maina.” Mboniyo inayankha kuti: “Komatu Mboni za Yehova zimatero.” Inde, iwo amachita zimenezi kotero kuti ulemu wonse unke kwa Yehova Mulungu!
16. Kodi mawu athu tingaŵagwiritsire ntchito kulemekezera Yehova Mulungu m’njira zosiyanasiyana zotani?
16 Njira ina yolemekezera Yehova njakugwiritsira ntchito milomo yathu kuchitira umboni za iye. Ngati tiridi odera nkhaŵa kumuchitira ulemu, pamenepo tidzakhala osamalitsa pofalitsa mbiri yabwino ya Ufumu. Ichi tingachichite mwa kupita kunyumba ndi nyumba ndikupyolera m’njira zina zirizonse zomwe ziripo kwa ife, osanyalanyaza mwaŵi wa kuchitira umboni mwamwaŵi. (Yohane 4:6-26; Machitidwe 5:42; 20:20) Kuwonjezera apa, tiri ndi mwaŵi wa kulemekeza Mulungu wathu ndi mawu athu pamisonkhano yathu yampingo, ponse paŵiri mwakuthirira ndemanga ndi mwakukhalamo ndi phande m’kuimba kochokera mumtima nyimbo zathu za Ufumu. (Ahebri 2:12; 10:24, 25) M’kulankhulana kwathu kwatsiku ndi tsiku, tingalemekezenso Yehova Mulungu ndi milomo yathu. Mwa kuyesayesa pang’ono, tingasinthe kukambirana kukhala kwauzimu, ndipo ichi chidzatulukapo kulemekeza Yehova Mulungu.—Salmo 145:2.
17. (a) Kodi mkhalidwe wabwino uli ndi mbali yotani m’kuchitira kwathu ulemu Yehova? (b) Kodi mkhalidwe woipa umayambukira motani?
17 Monga momwe kuliri kwabwino kulemekeza Yehova Mulungu ndi milomo yathu, kulinso koyenerera kumulemekeza ndi makhalidwe athu. Yesu anawakana anthu omwe, ngakhale kuti ankalemekeza Mulungu ndi milomo yawo, mitima yawo inali kutali ndi Iye. (Marko 7:6) Mkhalidwe woipa umakhoterera kunyoza Yehova Mulungu. Mwachitsanzo, pa Aroma 2:23, 24, timaŵerenga kuti: ‘Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu.’ M’zaka zaposachedwapa anthu zikwi zambiri akhala akuchotsedwa chaka ndi chaka mumpingo wa anthu a Yehova. Mwachidziŵikire, anthu ambiri omwe anadziloŵetsa m’makhalidwe onyoza sanachotsedwe chifukwa chakuti anasonyeza mkhalidwe wa kulapa kwenikweni. Anthu onsewa ankalemekeza Yehova ndi milomo yawo, koma analephera kuchita tero ndi makhalidwe awo.
18. (a) Kodi ndi nkhaŵa yotani imene anthu ena oyanjidwa kwambiri ayenera kukhala nayo ngati ati amchitire ulemu woyenerera Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wa ansembe ena m’tsiku la Malaki umafotokozera mwafanizo nkhaŵa yofunikira?
18 Awo omwe ngotanganitsidwa m’mbali zosiyanasiyana za utumiki wanthaŵi zonse—kaya pa Beteli, m’ntchito yoyendayenda kapena yaumishonale, kapena monga apainiya—ngoyanjidwa kwakukulu ponena za mwaŵi wawo wa kuthandizira kulemekeza Yehova. Thayo lawo nlakuchita zabwino koposa pantchito iriyonse yomwe apatsidwa kuichita, kukhala ‘wokhulupirika m’chaching’ono ndi chachikulu.’ (Luka 16:10) M’njira zina malo awo olemekezeka anachitiridwa fanizo, koma osati kuphiphiritsidwa, ndi a ansembe ndi Alevi mu Israyeli wakale. Komabe, chifukwa cha kusasamala kwa ansembe ena m’tsiku la Malaki, Yehova anati kwa iwo: “Ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti?” (Malaki 1:6) Ansembewo ankanyoza dzina la Mulungu mwakupereka nyama zakhungu, zolemala, ndi zodwala monga nsembe. Pokhapo ngati omwe ali ndi mwaŵi wapadera wautumiki lerolino akalamira kuchita bwino kwambiri, iwo angayenereredi kusumulula kumene Yehova Mulungu anapatsa ansembe aja. Iwo angakhale akulemekeza Mulungu mosakwanira.
19. (a) Monga momwe kwawonedwera pa Miyambo 3:9, kodi ndiiti yomwe iri njira yowonjezereka yolemekezera Yehova? (b) Kodi ndiiti imene iri njira ina yofunika yolemekezera Yehova?
19 Njira ina yomwe tingalemekeze nayo Yehova Mulungu njakuthandizira ndalama kuntchito yolalikira padziko lonse imene iye wailamulira. ‘Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha,’ tikufulumizidwa motero. (Miyambo 3:9) Mwaŵi wa kuthandizira zopereka zoterozo ndimwaŵi wolemekezera Yehova Mulungu umene palibe munthu ayenera kuwunyalanyaza. Tingamlemekezenso Yehova Mulungu m’mapemphero athu, kumtamanda ndi kumuyamikira. (1 Mbiri 29:10-13) Kwenikweni, popeza kuti timadza kwa iye modzichepetsa ndi ulemu wakuya, kuyandikira kwathu kwa Mulungu m’pemphero kwenikweni nkumchitira ulemu.
20. (a) Kodi ndani omwe amalemekezedwa mofala ndi anthu akudziko, ndipo motani? (b) Kodi tingamulemekeze Yehova mwa kumvera lamulo liti?
20 Lerolino anthu ambiri, makamaka achichepere, amalemekeza anthu amene amaŵakhumbira mwakuŵatsanzira—mwakulankhula motsanzira iwo ndi kuchita mofanana nawo. Kaŵirikaŵiri anthu amene amaŵatsanzira ndingwazi m’dziko m’chigawo chamaseŵera kapena zosangulutsa. Mosiyana, monga Akristu, tiyenera kulemekeza Yehova Mulungu mwa kuyesayesa kumutsanzira. Mtumwi Paulo anatifulumiza kuti tiyenera kuchita tero, nalemba kuti: ‘Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.’ (Aefeso 5:1, 2) Inde, mwa kukalamira kutsanzira Yehova, timamulemekeza iye.
21. (a) Kodi nchiyani chomwe chidzatikonzekeretsa kupereka ulemerero ndi ulemu kwa Yehova? (b) Kodi ndimfupo zotani zimene Yehova amapatsa omulemekeza?
21 Zowonadi, pali njira zambiri zimene tiyenera kupereka ulemerero ndi ulemu kwa Mulungu. Tisaiŵale kuti kudya mokhazikika pa Mawu ake ndikukhala nthaŵi zonse ozoloŵerana naye bwino, tidzakhala okhoza kumlemekeza moposerapo. Kodi pali mfupo zotani za kuchitira tero? “Amene andilemekeza ine,” akutero Yehova, “ndidzawalemekeza.” (1 Samueli 2:30) Pomalizira pake Yehova adzalemekeza alambiri ake mwakuŵapatsa moyo wosatha wachimwemwe, kaya kumwamba monga olamulira anzake a Mwana wake, Yesu Kristu, kapena m’Paradaiso wa padziko lapansi.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi anthu amalemekeza yani mofala, ndipo kodi amanyalanyaza kulemekeza yani kaŵirikaŵiri?
◻ Kodi kulemekeza munthu wina kumatanthauzanji, ndipo kodi kungachitidwe m’njira ziti?
◻ Kodi ndizifukwa zina zazikulu zotani zimene Yehova Mulungu amayenerera ulemu?
◻ Kodi ndim’njira zina ziti mmene tingalemekezere Yehova?
◻ Kodi ndim’njira ziti mmene Yehova amafupira omulemekeza?