Khalani Olama M’chikhulupiriro!
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Tito
MIPINGO Yachikristu yokhala pa chisumbu cha Krete wa ku Mediterranean idafunikira kusamaliridwa mwauzimu. Kodi ndani akadaithandiza? Eya, anali Tito wantchito mnzake wa mtumwi Paulo! Iye anali wolimba mtima, woyeneretsedwa kuphunzitsa, wachangu pa ntchito zabwino, ndi wolama m’chikhulupiriro.
Paulo anachezera Krete pakati pa kuikidwa kwake m’ndende koyamba ndi kwachiŵiri m’Roma. Iye anasiya Tito pachisumbupo kuti awongolere zinthu zina ndi kuika akulu mumpingo. Tito akaitanidwanso kukadzudzula aphunzitsi onyenga ndi kukhazikitsa chitsanzo chabwino. Zonsezi zavumbulidwa m’kalata ya Paulo yonka kwa Tito, yotumizidwa mwachiwonekere kuchokera ku Makedoniya pakati pa 61 ndi 64 C.E. Kugwiritsira ntchito uphungu wamtumwiyo kungathandize oyang’anira amakono ndi akhulupiriri anzawo kukhala olimba mtima, achangu, ndi olama mwauzimu.
Kodi Oyang’anira Amafunikira Kukhala Otani?
Kunali koyenerera kuika oyang’anira ndi kusamalira mavuto ena aakulu. (1:1-16) Kuti aikidwe monga woyang’anira, mwamuna adafunikira kukhala wopanda chirema, wokhazikitsa chitsanzo chabwino payekha ndi m’moyo wabanja lake, wochereza alendo, wolinganizika, ndi wodziletsa. Iye adafunikira kuphunzitsa chowonadi ndi kuchenjeza ndi kudzudzula okhala ndi malingaliro otsutsana naye. Panafunikira kulimba mtima popeza kuti amuna osaweruzika m’mipingo adafunikira kutsekedwa pakamwa. Izi zinali choncho makamaka kwa awo omamatira kumdulidwe, pakuti iwo anasanduliza mabanja onse. Chidzudzulo cholimba chikafunikira ngati mipingo idati ikhalebe yolama mwauzimu. Lerolino, oyang’anira Achikristu amafunikiranso kukhala olimba mtima kuti apereke chidzudzulo ndi kuchenjeza, ncholinga cha kumangirira mpingo.
Gwiritsirani Ntchito Chiphunzitso Cholamitsa
Tito adafunikira kugaŵira chiphunzitso cholamitsa mwauzimu. (2:1-15) Amuna okalamba adafunikira kukhala zitsanzo zabwino m’kudzisunga, m’kulemekezeka, kulama m’maganizo, m’chikhulupiriro, m’chikondi, ndi m’chipiriro. Akazi okalamba anayenera kukhala ndi “makhalidwe oyenera.” Monga ‘akuphunzitsa zabwino,’ iwo akathandiza akazi achichepere kuŵalingalira moyenera mathayo awo monga akazi okwatiwa ndi anakubala. Anyamata akayenera kukhala olama m’maganizo, ndipo akapolo anayenera kugonjera ambuye awo m’njira imene ikakometsera chiphunzitso cha Mulungu. Akristu onse adafunikira kudana nako kusapembedza ndi kukhala olama maganizo m’dongosolo iri lazinthu pamene akuyembekezera mawonekedwe aulemerero wa Mulungu ndi wa Yesu Kristu, ‘amene anadzipereka yekha mmalo mwa ife kuti akatiombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu ake enieni, achangu pa ntchito zabwino.’ Mwa kugwiritsira ntchito uphungu wolama woterowo, tiyeni nafenso ‘tikometsere chiphunzitso cha Mulungu.’
Uphungu wotsirizira wa Paulo umapititsa patsogolo kulama kwauzimu. (3:1-15) Nkofunikira kuŵagonjera moyenera olamulira ndi kukulitsa kufatsa. Akristu ali nchiyembekezo cha moyo wosatha, ndipo mawu a Paulo anayenera kugogomezeredwa kuti akawalimbikitse kusumikabe maganizo awo pa ntchito zokoma. Mafunso opusa ndi ndewu zokhudza Chilamulo zinafunikira kupeŵedwa, ndipo wopititsa patsogolo mpatuko anayenera kukanidwa atachenjezedwa kaŵiri. Pamene akulu akugwiritsira ntchito uphungu wotero lerolino, iwo ndi akhulupiriri anzawo adzakhala olama m’chikhulupiriro.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]
Asakhale Akapolo a Vinyo: Chinkana kuti akazi sayenera kuphunzitsa amuna mumpingo, alongo achikulire angalangize akazi achichepere mseri. Koma kuti akhale ogwira mtima pochita tero, akazi okalamba ayenera kutsatira mawu a Paulo akuti: “Akazi okalamba azikhala nawo makhalidwe oyenera, osasinjirira, asakhale akapolo a vinyo, akuphunzitsa zabwino.” (Tito 2:1-5, NW; 1 Timoteo 2:11-14) Chifukwa chodera nkhaŵa ziyambukiro zauchidakwa, oyang’anira, atumiki otumikira, ndi akazi okalamba ayenera kukhala achikatikati, osamwetsa vinyo. (1 Timoteo 3:2, 3, 8, 11) Akristu onse ayenera kupeŵa uchidakwa ndipo ayenera kupeŵa kumwa zakumwa zoledzeretsa pamene akuchita “ntchito yopatulika” yolengeza mbiri yabwino.—Aroma 15:16, NW; Miyambo 23:20, 21.