Kodi Mpambuyo Pake Pomwe Simumaganizira?
MASIKU atatu imfa yake isanafike, Yesu anali ndi tsiku lotanganidwa kwambiri m’Yerusalemu, tsiku lomwe linakhala lofunika koposa kwa Akristu okhala ndi moyo tsopano. Iye anaphunzitsa m’kachisi, akumagwetsa mafunso ambiri achinyengo omwe atsogoleri achipembedzo Achiyuda anayesa kunkola nawo. Pomalizira pake, analengeza chilengezo chopweteka kwa alembi ndi Afarisi chomwe chinawazindikiritsa kukhala onyenga ndi njoka zonka ku Gehena.—Mateyu, mitu 22, 23.
Pamene ankachoka pakachisi, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa iye: “Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.” Mosasangalatsidwa nazo, Yesu anati kwa iye: ‘Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.’ (Marko 13:1, 2) Kenaka Yesu anachoka kukachisi kwa nthaŵi yomalizira, natsikira m’Chigwa cha Kedroni, naoloka, nakwera matelezi a Phiri la Azitona.
Pamene anakhala akuwothera dzuŵa madzulo paphiripo, akumawona kachisi ali pa Phiri la Moriya kutsidya lina la chigwacho, Petro, Yakobo, Yohane, ndi Andreya anadza kwa iye mwamseri. Ankawavutitsa maganizo anali mawu amene anawanena onena za kugwetsedwa kwa kachisi. Iwo anafunsa kuti: ‘Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?’ (Mateyu 24:3; Marko 13:3, 4) Yankho lomwe anapereka ku funso lawo masana amenewo pa Phiri la Azitona nlofunika kwambiri kwa ife. Lingatithandize kusadikirira kwa nthaŵi yaitali mopambanitsa tisanayambe kulingalira za ‘mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.’
Funso lawo linali la mbali ziŵiri. Mbali yoyamba inali yonena za mapeto a kachisi ndi dongosolo Lachiyuda; inayo inakhudza za kukhalapo kwamtsogolo kwa Yesu monga Mfumu ndi mathedwe a dongosolo la zinthu liripoli. Mafunso aŵiri onsewa anakwaniritsidwa m’yankho la Yesu, monga momwe laperekedwera mu Mateyu 24 ndi 25, Marko 13, ndi Luka 21. (Onaninso Chibvumbulutso 6:1-8.) Ponena za mathedwe a dziko lino, kapena dongosolo la zinthu, Yesu analongosola zinthu zambiri zimene zitatengedwa pamodzi, zikakhala chizindikiro chachiungwe chozindikiritsa masiku otsiriza. Kodi chizindikiro chachiungwecho chikukwaniritsidwa? Kodi chimatiika m’masiku otsiriza onenedwa m’Baibulo? Kodi kukwaniritsidwa kwake kumatichenjeza kuti pangakhale pambuyo pake pomwe sitikuganizira?
Mbali imodzi ya chizindikiro chachiungwe cha Yesu ndi iyi: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Mu 1914, Nkhondo Yadziko ya I inayambika. Mboni za Yehova za m’zaka za makumi amenewo mofulumira zinakhala zogalamuka. Ndipo nchifukwa ninji? Mu December 1879, zaka 35 pasadakhale, magazini a Watch Tower mozikidwa pa kuŵerengera masiku kwa Baibulo anati, 1914 chikakhala chaka chosinthirapo zinthu m’mbiri ya anthu. Kodi nkhondo imeneyi, nkhondo yoyamba yochitikadi pa ukulu wa dziko lonse, imene potsirizira pake maiko 28 analoŵetsedwamo ndipo anthu 14 miliyoni anaphedwa, ikakhala kuyambika kwa zochitika zokwaniritsa chizindikiro chachiungwe cha Yesu cha mapeto? Kodi mbali zina za chizindikirocho zikatsatira?
Mu ‘chibvumbulutso cha Yesu Kristu,’ kukhetsedwa kwa mwazi kumodzimodziku kunanenedweratu. Panopa kavalo wofiira ndi wokwerapo wake ‘akuchotsa mtendere pa dziko.’ (Chibvumbulutso 1:1; 6:4) Zimenezo zinachitikadi kuyambira 1914 mpaka 1918. Ndipo Nkhondo Yadziko ya I inali chiyambi chokha. Mu 1939, Nkhondo Yadziko ya II inatsatira. Maiko 59 analoŵetsedwa mu mkangano umenewo, ndipo anthu okwanira 50 miliyoni anaphedwa. M’zaka 45 zotsatira Nkhondo Yadziko ya II, nkhondo zoposa 125 zamenyedwa, zikumapha anthu oposa 20 miliyoni.
Mbali ina ya chizindikirocho ndi iyi: “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Panali njala yofalikira m’nthaŵi ya Nkhondo Yadziko ya I ndi pambuyo pake. Lipoti lina likundandalitsa njala zazikulu zoposa 60 chiyambire 1914, zikumapha anthu mamiliyoni ambiri. Kuwonjezerapo, ngakhale tsopano ana 40,000 amafa tsiku lirilonse ndi kupereŵera kwa zakudya ndi matenda okhoza kuchinjirizidwa.
‘Kudzakhala zivomezi zazikulu.’ (Luka 21:11) Izo zinagwedeza dziko lapansi pambuyo pa kuyambika kwa Nkhondo Yadziko ya I. Mu 1915, chivomezi chinapha anthu 32,610 mu Italiya; mu 1920, china chinapha anthu 200,000 m’China; mu 1923, anthu 99,300 anafa m’Japani; mu 1935, anthu 25,000 anafa m’dziko lomwe tsopano likutchedwa Pakistan; mu 1939, anthu 32,700 anapululuka m’Turkey; mu 1970, anthu 66,800 anaphedwa m’Peru; mu 1976, anthu 240,000 (ena amati 800,000) anafa m’China; mu 1988, anthu okwanira 25,000 anafa mu Armenia. Ndithudi, pakhala zivomezi zazikulu chiyambire 1914!
“Miliri m’malo akuti akuti.” (Luka 21:11) Mu 1918 ndi 1919, anthu okwanira 1,000,000,000 ankadwala fuluwenza Yachispanya, ndipo oposa 20,000,000 anamwalira. Koma kumeneko kunali kuyambika kokha. M’maiko otukuka kumene, malungo, likodzo, khungu lochititsidwa ndi kulumidwa ndi ntchentche za m’mitsinje ina, kutseguka m’mimba koipitsitsa, ndi matenda ena zikupitirizabe kulemaza ndi kupha anthu mazana mamiliyoni ambiri. Kuwonjezerapo, matenda a mtima ndi kansa akupha anthu mamiliyoni ambiri. Matenda opatsirana mwakugonana akuwononga anthu. Wochititsa mantha m’mitima ya anthu lerolino ndi mliri wakupha wa AIDS, womwe ukuyerekezeredwa kuti ukuyambukira mnkhole watsopano mphindi iriyonse, popanda chiyembekezo cha kuuchiritsa.
‘Kuchuluka kwa kusayeruzika.’ (Mateyu 24:12) Kusayeruzika kwakula chiyambire 1914, ndipo lerolino kwafika poipitsitsa. Mbanda, zigololo zogwirira, kuba, nkhondo zazigaŵenga—izo zimakhala mitu yankhani pa manyuzipepala ndi nkhani zoulutsidwa pa wailesi ndi wailesi ya kanema. Chiwawa chopanda pake chikupitirizabe chosalamulirika. Mu United States, munthu wina anawombera zipolopolo zana limodzi ndi mfuti yamphamvu pakhamu la ana asukulu—5 anafa, 29 anavulazidwa. Mu Mangalande munthu wamisala anapha anthu 16 ndi mfuti yamphamvu ya AK-47. Mu Canada mwamuna amene ankada akazi anapita ku Yunivesite ya ku Montreal naphapo 14. Anthu oterowo ngofanana ndi mimbulu, mikango, zilombo zolusa, nyama zosalingalira obadwira kugwidwa ndi kuwonongedwa.—Yerekezerani ndi Ezekieli 22:27; Zefaniya 3:3; 2 Petro 2:12.
“Anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.” (Luka 21:26) Mwamsanga pambuyo pa kuphulika kwa bomba la atomu loyamba, wasayansi ya atomu, Harold C. Urey ananena motere za mtsogolo: “Tidzadya mantha, kugona mantha, kukhala m’mantha ndi kufa m’mantha.” Ku mantha a nkhondo ya nyukliya kwawonjezeredwa mantha a upandu, njala, kusakhazikika kwazachuma, kunyonyotsoka kwa makhalidwe, kusweka kwa mabanja, kuipitsa dziko lapansi. Kwenikweni, nthaŵi zovuta zofotokozedwa kwa ife tsiku lirilonse pa manyuzipepala ndi wailesi yakanema zimafalitsa mantha kulikonse.
Mtumwi Paulo analembanso za mikhalidwe imene ikakhalapo m’masiku otsiriza a dongosolo lazinthu liripoli. Kuŵerenga mawu ake kumafanana ndi kuŵerenga nyuzi zapatsikulo. Iye analemba kuti: ‘Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo mawonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.’—2 Timoteo 3:1-5.
Kodi Zinthu Zonse Zipitiriza ‘Monga Chiyambire Chilengedwe’?
Mtumwi Petro ananeneratu mbali ina ya masiku otsiriza iyi: ‘Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.’—2 Petro 3:3, 4.
Lerolino, pamene nkhani ya masiku otsiriza ibuka, anthu ambiri amakwaniritsa mawu aulosi a Petro mwakuseka ndikunena kuti: ‘Oo, zinthu zonsezo zinachitikapo kale. Ndi mbiri imene ikungodzibwereza yokha.’ Chotero iwo amanyalanyaza machenjezo ndikupitiriza ‘kuyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.’ Iwo amaiwala ‘dala’ kukwaniritsidwa kwa maulosi amene anazindikiritsa mowonekera bwino masiku otsiriza.—2 Petro 3:5.
Komabe, mbali zosiyanasiyana za chizindikiro chachiungwe chonenedweratu ndi Yesu sizinakwaniritsidwepo ndikalelonse zonse pamodzi m’nyengo ya nthaŵi yaifupi chotero kuukulu wotero wokhala ndi ziyambukiro zofika patali. (Mwachitsanzo, bwererani m’Mateyu 24:3-12; Marko 13:3-8; Luka 21:10, 11, 25, 26.) Ndipo tingakondenso kulunjikitsa chidwi chanu ku mbali inanso yonenedweratu ya masiku otsiriza, yofotokozedwa m’Chibvumbulutso.
Tiyeni titsegule Chibvumbulutso 11:18. Icho chikunena kuti pamene Ufumu wa Kristu uyamba kulamulira ndipo mitundu ikwiya ndi nthaŵi ya chiweruzo ifika, pamenepo Yehova ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ Kodi kuipitsa sikukuwononga malo okhala lerolino? Zowonadi, nthaŵi zonse anthu akhala akugwiritsira ntchito chuma chadziko lapansi kudzilemeretsa. Koma pochita tero, iwo sanakhoze konse kulisakaza kukhala pulaneti losakhalika. Tsopano, chifukwa cha luso lazopangapanga la sayansi lokulitsidwa chiyambire 1914, anthu alinayo mphamvu imeneyo, ndipo mwakuphanga chuma mwaumbombo, iwo akuwonongadi dziko lapansi, kuipitsa malo okhala ndikuika pangozi mphamvu ya dziko lapansi ya kuchilikiza moyo.
Chitaganya chaumbombo, chokondetsa zinthu zakuthupi chikuchita zimenezi tsopano pa liŵiro lalikulu kowopsa. Nawa ena a masoka otulukapo: mvula ya asidi, kutentha kwadziko lonse, ming’alu m’chiphimba thambo, vuto la zinyalala, zonyansa zapaizoni, mankhwala ambewu ndi tizilombo owopsa, zotaidwa za nyukliya, kutaikira kwa mafuta, zonyansa za m’chimbudzi zotaidwa mosasamala, kuikidwa paupandu kwa zamoyo, nyanja zopanda zamoyo, madzi a pansi panthaka oipitsidwa, nkhalango zowonongedwa, nthaka yoipitsidwa, kukokoloka kwa nthaka yapamwamba, ndi chifunga chowononga mitengo ndi mbewu limodzinso ndi thanzi la anthu.
Profesa Barry Commoner akuti: “Ndikhulupirira kuti ngati kuipitsidwa kwa dziko lapansi kudzapitiriza osaletsedwa, m’kupita kwa nthaŵi kudzawononga kukhoza kwa pulaneti lino kukhala malo oyenerera a anthu. . . . Vuto siliri pa umbuli wasayansi, koma umbombo wodzifunira.” Bukhu lakuti State of the World 1987 likunena motere patsamba 5: “Mlingo wa zochita za anthu wayamba kuwopseza kuthekera kwa kukhalidwa ndi anthu kwa dziko lapansi lenilenilo.” Mpambo waukulu wa nkhani za wailesi yakanema yosonyezedwa mu United States mu 1990 unali ndi mutu wakuti “Race to Save the Planet [Mpikisano Wakupulumutsa Pulaneti].”
Munthu sadzaleka konse kuipitsa; Mulungu yekha ndiye adzatero pamene adzawononga akuwononga dziko lapansi. Mulungu ndi Kazembe wake Wankhondo wakumwamba, Kristu Yesu, adzachita zimenezi mwakuweruza mitundu yokondetsa zinthu zakuthupi pankhondo yomalizira ya Armagedo.—Chibvumbulutso 16:14, 16; 19:11-21.
Pomalizira, onani mbali yapadera ya ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza iyi: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:14, NW) Mbiri yabwino imeneyi imanena kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira tsopano m’mwamba ndipo posachedwapa udzawononga dongosolo lazinthu loipa liripoli ndikubwezeretsa Paradaiso padziko lapansi. Uthenga wabwinowo unayamba walalikidwapo koma osati kukuta dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Komabe, chiyambire 1914, Mboni za Yehova zachita zimenezo, mosasamala kanthu za chizunzo chonenedweratu ndi Yesu—ziletso zaboma, chiwawa cha chipwirikiti, kuponyedwa m’ndende, kuzunzidwa, ndi imfa zambiri.
Mu 1919 panali Mboni za Yehova 4,000 zomwe zinkalalikira mbiri yabwino imeneyi. Chiŵerengero chawo chapitiriza kuwonjezeka, kotero kuti chaka chatha oposa 4,000,000 ankalalikira m’maiko 212, m’zinenero 200, kugaŵira mazana mamiliyoni ambiri a Mabaibulo, mabuku, ndi magazini, kuchititsa maphunziro Abaibulo mamiliyoni ambiri m’nyumba za anthu, ndi kuchita misonkhano m’mabwalo amaseŵera aakulu m’mbali zonse zadziko. Kulalikira uthenga wabwino kwakukulu kumeneku sikukanachitika konse 1914 isanafike. Kukwaniritsidwa kwake ku mlingo womwe wafikiridwa kunafunikira makina osindikizira aliŵiro amakono, zinthu zoyendera, makompyuta, makina a fax, ndiponso zinthu zotumizira ndi kulankhulirana zomwe ziripo mwapadera m’nthaŵi yathu.
Yerusalemu wa m’tsiku la Yeremiya anachenjezedwa za chiwonongeko chake chomadza; nzika zake zinangoseka, koma panali pambuyo pake pomwe sanaganizire. Lerolino, chenjezo lalikulu koposa la chiwonongeko cha Armagedo likuperekedwa, limodzi ndi umboni wochilikiza wochititsa mantha. (Chibvumbulutso 14:6, 7, 17-20) Anthu mamiliyoni ambiri akutseka makutu awo. Koma nthaŵi ikutha; mpambuyo pake pomwe sakuganizira. Kodi mpambuyo pake pomwe simumaganizira?
[Chithunzi patsamba 7]
M’tsiku la Yeremiya panali pambuyo pake pomwe sanaganizire