Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
‘Mundiwonetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’chowonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.’—SALMO 86:11.
1, 2. Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera Mboni za Yehova kukana kuthiridwa mwazi?
“MWINAMWAKE Mboni za Yehova nzolondola pokana kugwiritsira ntchito zinthu za mwazi, popeza nzowona kuti zoyambukiritsa matenda zambiri zikhoza kupatsiridwa mwakuthiridwa mwazi.”—Magazini azamankhwala a tsiku ndi tsiku Achifalansa a Le Quotidien du Médecin, December 15, 1987.
2 Anthu ena omwe anaiŵerenga ndemangayo angankhale analingalira kuti zinangokhala mwamwaŵi kuti Mboni za Yehova zimakana kuthiridwa mwazi kuyambira kalekale pamene kunali kusanadziŵidwe mofala mmene iko kungakhalire kwangozi, ngakhale kwakupha. Koma kaimidwe kamene Mboni za Yehova zakatenga ponena za mwazi sikamwamwaŵi, ndipo sindiko lamulo lopangidwa ndi gulu lampatuko lachilendo, kaimidwe kochititsidwa ndi mantha akuti mwazi ngwopanda chisungiko. Mmalomwake, Mboni zimakana mwazi chifukwa cha kutsimikiza mtima kwawo kofuna kuyenda momvera pamaso pa Mlangizi wawo Wamkulu—Mulungu.
3. (a) Kodi Davide anadzimva motani ponena za chidaliro chake pa Yehova? (b) Kodi nchotulukapo chotani chimene Davide anayembekezera chifukwa chokhulupirira Mulungu?
3 Mfumu Davide, yemwe anadzimvadi kukhala wodalira Mulungu, anali wotsimikiza mtima kulangizidwa ndi iye ndi ‘kuyenda m’chowonadi chake.’ (Salmo 86:11) Panthaŵi inayake Davide analangizidwa kuti ngati anapeŵa kukhala waliŵongo lamwazi pamaso pa Mulungu, ‘moyo wake ukamangika m’phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova.’ (1 Samueli 25:21, 22, 25, 29) Monga momwe anthu anakutira zinthu zamtengo wapatali kuzitetezera ndi kuzisunga, momwemonso moyo wa Davide ukatetezeredwa ndi kusungidwa ndi Mulungu. Pokhala analandira uphungu wanzeruwo, Davide sanafune kudzipulumutsa yekha mwa zoyesayesa zaumwini koma anadalira pa Uyo amene anali magwero a moyo wake: ‘Mudzandidziŵitsa njira ya moyo: Pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; M’dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.’—Salmo 16:11.
4. Kodi nchifukwa ninji Davide anafuna kulangizidwa ndi Yehova?
4 Ndi kaimidwe kamaganizo kameneko, Davide sanalingalire kuti akadzisankhira kuti ndi malamulo aumulungu ati omwe anali ogwira ntchito kapena ofunikira kuwamvera. Kaimidwe kake kamaganizo kanali kakuti: ‘Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, Munditsogolere pa njira [yachilungamo, NW]’ ‘Mundiwonetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’chowonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu. Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse.’ (Salmo 27:11; 86:11, 12) Nthaŵi zina kuyenda m’chowonadi pamaso pa Mulungu kungawoneke kukhala kovutitsa kapena kungatanthauze kudzimana kwakukulu, koma Davide anafuna kulangizidwa m’njira yolondola ndi kuyendamo.
Kulangizidwa Ponena za Mwazi
5. Kodi Davide ayenera kuti anadziŵanji ponena za lingaliro la Mulungu pa mwazi?
5 Tiyenera kudziŵa kuti kuyambira unyamata wake mpaka kukula, Davide anaphunzitsidwa lingaliro la Mulungu la mwazi, lingaliro limene silinali chinsinsi chachipembedzo. Pamene Chilamulo chinaŵerengedwa kwa anthu, Davide ayenera kuti anamva izi: ‘Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi.’—Levitiko 17:11, 12; Deuteronomo 4:10; 31:11.
6. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu anafunikira kupitirizabe kumalangizidwa ponena za mwazi?
6 Malinga ngati Mulungu anagwiritsira ntchito Israyeli monga anthu a mpingo wake, awo ofuna kumkondweretsa anafunikira kulangizidwa ponena za mwazi. Mibadwo ndi mibadwo ya anyamata ndi asungwana Achiisrayeli analangizidwa motero. Koma kodi chilangizo choterocho chikapitirizabe pambuyo pakuti Mulungu analandira mpingo Wachikristu, wopangidwa ndi “Israyeli wa Mulungu”? (Agalatiya 6:16) Inde, ndithudi. Lingaliro la Mulungu la mwazi silinasinthe. (Malaki 3:6) Lingaliro lake lofotokozedwa ponena za kusagwiritsira ntchito mwazi molakwa linalipo pangano la Chilamulo lisanakhazikitsidwe, ndipo linapitirizabe pambuyo pakuti Chilamulocho chinachotsedwapo.—Genesis 9:3, 4; Acts 15:28, 29.
7. Kodi nchifukwa ninji kulangizidwa ndi Mulungu ponena za mwazi kuli kofunika kwambiri kwa ife?
7 Kulemekezedwa kwa mwazi kuli mfundo yaikulu ya Chikristu. ‘Kodi kumeneko sindiko kunena mopambanitsa?’ ena angafunse motero. Komabe, kodi nchiyani chingakhale mfundo yaikulu ya Chikristu ngati sindiyo nsembe ya Yesu? Ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi wa [Yesu], chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.’ (Aefeso 1:7) The Inspired Letters, lotembenuzidwa ndi Frank C. Laubach, limamasulira vesilo motere: “Mwazi wa Kristu wolipiridwa kaamba ka ife ndipo tsopano ndife Ake.”
8. Kodi ndimotani mmene ‘khamu lalikulu’ limadalira pa mwazi kaamba ka moyo?
8 Onse amene amayembekezera kupulumuka ‘chisautso chachikulu’ choyandikiracho ndi kusangalala ndi madalitso a Mulungu pa dziko lapansi laparadaiso amadalira pamwazi wokhetsedwa wa Yesu. Chibvumbulutso 7:9-14 chimawalongosola ndi kunena mosonyeza zimene iwo achita kale kuti: ‘Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ Onani kanenedweka panopa. Sikakunena kuti awa opulumutsidwa kupyola m’chisautso chachikulu ‘analandira Yesu’ kapena ‘kusonyeza chikhulupiriro mwa iye,’ chinkana kuti ndithudi zimenezo ndi mbali zofunika kwambiri. Iko kamapyolapo ndi kunena kuti iwo ‘anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa [Yesu].’ Ichi nchifukwa chakuti mwazi wake uli ndi mtengo wakuwombola.
9. Kodi nchifukwa ninji kumvera Yehova ponena za mwazi kuli kowopsa motero?
9 Kuuzindikira mtengo umenewu kumathandiza Mboni za Yehova kukhala zotsimikiza mtima kusagwiritsira ntchito mwazi molakwa, ngakhale ngati sing’anga wa m’chipatala mowona mtima anganene kuti kuthiridwa mwazi nkofunika. Iye angakhulupirire kuti mapindu othekera a kuthiridwa mwazi akupambana maupandu operekedwa ndi mwazi weniweniwo. Koma Mkristu sanganyalanyaze upandu woopsa koposa, upandu wakutaikiridwa chivomerezo cha Mulungu mwakuvomereza kugwiritsira ntchito mwazi molakwa. Paulo panthaŵi ina analankhula za amene “anachita tchimo mwadala pambuyo polandira chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi.” Kodi nchifukwa ninji tchimo lirilonse la mtundu umenewo linali lowopsa kwambiri? Chifukwa chakuti munthu woteroyo “wapondereza Mwana wa Mulungu ndipo . . . wayesa mtengo wa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nawo kukhala wopanda pake.”—Ahebri 9:16-24; 10:26-29, NW.
Athandizeni Ena Kukhala Olangizidwa
10. Kodi nchifukwa chotani chimene chimatikhalitsa otsimikiza mtima kupeŵa mwazi?
10 Ife amene timazindikira nsembe ya Yesu yadipo timasamala kusachita tchimo, kukana mtengo wa mwazi wake wopulumutsa moyo. Pokhala tinalingalira nkhaniyo kotheratu, timazindikira kuti chiyamikiro chathu kwa Mulungu kaamba ka moyo mwa icho chokha chiyenera kutisonkhezera kukana kulolera molakwa kulikonse kwa malamulo ake olungama, amene ndife achidaliro kuti anaperekedwa kaamba ka maubwino athu—maubwino anthu okhalitsa. (Deuteronomo 6:24; Miyambo 14:27; Mlaliki 8:12) Komabe, bwanji ponena za ana athu?
11-13. Kodi ndilingaliro lolakwika lotani ponena za ana awo ndi mwazi limene makolo ena Achikristu ali nalo, ndipo chifukwa ninji?
11 Pamene kuli kwakuti ana athu ndimakanda kapena ngaang’ono kwambiri osakhoza kumvetsetsa, Yehova Mulungu angawawone kukhala oyera ndi olandirika pa maziko a kudzipereka kwathu. (1 Akorinto 7:14) Chotero nzowona kuti ana aang’ono m’banja Lachikristu angakhale asanamvetsetse ndi kupanga chosankha ponena za kumvera lamulo la Mulungu la mwazi. Komabe, kodi timachita zomwe tingathe kuwalangiza m’nkhani yofunika koposa imeneyi? Makolo Achikristu afunikira kulingalira chimenechi mosamalitsa kwambiri, popeza kuti makolo ena akuwoneka kukhala ndi maganizo olakwika ponena za ana awo ndi mwazi. Ena akuwoneka kukhala akulingalira kuti alibe ulamuliro kwenikweni wakuti kaya ana awo aang’ono ayenera kuthiridwa mwazi. Kodi nchifukwa ninji pali lingaliro lolakwika limeneli?
12 Maiko ambiri ali ndi malamulo kapena mabungwe a boma otetezera ana onyalanyazidwa ndi ochitiridwa nkhanza. Ana a Mboni za Yehova sakunyalanyazidwa kapena kuchitiridwa nkhanza pamene makolo awo asankha kuti mwana wawo wokondedwa asapatsidwe mwazi, panthaŵi imodzimodzi akumapempha kugwiritsira ntchito njira ina yochiritsira imene mankhwala amakono angapereke. Ngakhale m’lingaliro la zamankhwala, kumeneku sindiko kunyalanyaza kapena kuchitira nkhanza, polingalira ngozi zoperekedwa ndi kuchiritsa kwa kuthiridwa mwazi. Kuli kachitidwe kolondola kupenda maupandu oloŵetsedwamo kenaka nkusankha njira yochiritsira.a Komabe, ena ogwira ntchito zamankhwala atembenukira ku malamulo aboma pofuna ulamuliro wa kukakamiza kuthira mwazi kosafunidwa.
13 Makolo ena, podziŵa kuti kungakhale kosavuta kwa ogwira ntchito zamankhwala kupeza chichirikizo cha khoti kuti amthire mwazi mwana, angalingalire kuti iwo alibe mphamvu pankhaniyo, kuti palibe chimene makolowo angachite kapena chimene afunikira kuchita. Ndilingaliro lolakwika chotani nanga limenelo!—Miyambo 22:3.
14. Kodi ndimotani mmene Davide ndi Timoteo analangizidwira m’nthaŵi ya uchichepere wawo?
14 Tawona kuti Davide analangizidwa m’njira ya Mulungu kuchokera kuuchichepere wake mpaka kukula. Chimenecho chinamkonzekeretsa kuwona moyo kukhala mphatso yochokera kwa Mulungu ndi kudziŵa kuti mwazi umaimira moyo. (Yerekezerani ndi 2 Samueli 23:14-17.) Timoteo analangizidwa m’malingaliro a Mulungu ‘kuyambira ukhanda wake.’ (2 Timoteo 3:14, 15) Kodi simukuvomereza kuti ngakhale pamene Davide ndi Timoteo anali asanafike pausinkhu wauchikulire woikidwa ndi lamulo wa lerolino, iwo anali okhoza kulongosola malingaliro awoawo bwino lomwe pa nkhani zoloŵetsamo chifuniro cha Mulungu? Mofananamo, akali kutali ndikufika pausinkhu, Akristu achichepere lerolino ayenera kulangizidwa m’njira ya Mulungu.
15, 16. (a) Kodi ndilingaliro lotani limene lakula m’malo ena ponena za zoyenerera za ana aang’ono? (b) Kodi nchiyani chimene chinachititsa kuti wachichepere wina apatsidwe mwazi?
15 M’maiko ena otchedwa achichepere ofikapo amapatsidwa zoyenerera zofanana ndi za akulu. Kudalira pa usinkhu kapena kulingalira kofikapo, kapena zonse ziŵiri, wachichepere angalingaliridwe kukhala wofikapo kudzipangira zosankha pa njira yakuchiritsa. Ngakhale kumene ichi sichiri lamulo, oweruza kapena nduna za boma zingalingalire mosamalitsa zikhumbo za wachichepere wokhoza kulongosola momvekera bwino chosankha chake cholimba ponena za mwazi. Mosiyana, pamene wachichepere satha kufotokoza zikhulupiriro zake momvekera bwino ndi mwauchikulire, khoti lingalingalire kuti liyenera kusankha chimene chikuwoneka kukhala chabwino koposa, monga momwe zingakhalire kwa khanda.
16 Mnyamata wina ankaphunzira Baibulo, mwa apa ndi apo kwa zaka zambiri koma sanabatizidwe. Mosasamala kanthu kuti panangotsala milungu isanu ndi iŵiri yokha kuti apeze “kuyenerera kwa kudzisankira chithandizo chamankhwala,” chipatala chomsamalira kaamba ka kansa chinafuna chichirikizo cha khoti kuti amthire mwazi motsutsana ndi zikhumbo zake ndi za makolo ake. Woweruza wachikumbumtima chabwino anamfunsa mafunso ofunika ponena za zikhulupiriro zake pa mwazi, onga ngati maina a mabuku asanu oyambirira a Baibulo. Mnyamatayo sanathe kuwatchula nalepheranso kupereka umboni wokhutiritsa wakuti anamvetsetsa chifukwa chimene anakanira mwazi. Mwachisoni, woweruzayo analamula kuthiridwa mwazi, nathirira ndemanga kuti: “Kukana kuthiridwa mwazi kwake sikozikidwa pa kumvetsetsa kwauchikulire zikhulupiriro zake zachipembedzo.”
17. Kodi ndikaimidwe kotani kamene msungwana wina wazaka 14 anakatenga ponena za kupatsidwa mwazi, ndipo ndi chotulukapo chotani?
17 Zinthu zingachitike mosiyana kwa mwana amene analangizidwa bwino lomwe m’njira za Mulungu ndi kuyenda mokangalika m’chowonadi Chake. Mkristu wocheperapo wina anali ndi kansa ya mtundu wosawanda yofananayo. Msungwanayo ndi makolo ake anamvetsetsa ndi kuvomereza kuchiritsidwa kolinganizidwa kotchedwa chemotherapy ndi katswiri wina pa chipatala chotchuka. Chikhalirechobe, nkhaniyo inaperekedwa ku khoti. Woweruza analemba kuti: “D.P. anapereka umboni wakuti adzakana kuthiridwa mwazi mwanjira iriyonse imene akatha. Iye analingalira kuthiridwa mwazi kukhala kulakwira thupi lake ndipo anakulinganiza ndi kugwiriridwa chigololo. Iye anapempha Khoti kulemekeza chosankha chake ndi kumlola kupitiriza [kukhala m’chipatala] popanda kuthiridwa mwazi kolamulidwa ndi Khoti.” Chilangizo Chachikristu chimene analandira chinamthandiza panthaŵi yovuta imeneyi.—Onani bokosi.
18. (a) Kodi ndikaimidwe kolimba kotani kamene msungwana wodwala anakatenga ponena za kulandira mwazi? (b) Kodi woweruza anagamulanji ponena za chithandizo chake chakuchiritsa?
18 Msungwana wa zaka 12 ankachiritsidwa nthenda ya leukemia. Bungwe losamalira ana linapereka nkhaniyo ku khoti kotero kuti mwazi ukakamizidwe pa iye. Woweruza anagamula kuti: “L. wauza khoti lino momvekera bwino ndiponso motsimikiza kuti, ngati ayesa kumthira mwazi, iye akalimbana mokana kuthiridwa mwaziko ndi nyonga yake yonse imene angakhale nayo. Iye wanena, ndipo ndikumkhulupirira, kuti adzakuŵa ndi kupalapata ndikuti adzasolola chiŵiya chothirira mwazicho kuchichotsa pamkono pake ndipo akayesayesa kutaira mwazi wokhala m’thumbamo pakama pake. Ineyo ndikukana kupanga lamulo lirilonse limene likaika mwanayu m’tsoka loterolo . . . Kwa wodwalayu, chithandizo cholingaliridwa ndi chipatala chimachita ndi nthendayi kokha m’lingaliro la zakuthupi. Chikulephera kuchita ndi zofunika zake zamalingaliro ndi zikhulupiriro zake zachipembedzo.”
Makolo—Langizani Bwino
19. Kodi ndithayo lapadera lotani limene makolo ayenera kulikwaniritsa kwa ana awo?
19 Zokumana nazo zoterozo zimapereka uthenga wamphamvu kwa makolo okhumba kuti onse m’banja lawo akhale ndi moyo mogwirizana ndi lamulo la Mulungu la mwazi. Chifukwa china chimene Abrahamu analiri bwenzi la Mulungu chinali chakuti Iye anadziŵa kuti khololo ‘likalamulira ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti akasunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo.’ (Genesis 18:19) Kodi zimenezi siziyenera kukhala choncho kwa makolo Achikristu lerolino? Ngati ndinu kholo, kodi mumalangiza ana anu okondedwa kuyenda m’njira ya Yehova kotero kuti akhale ‘okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakufunsa chiyembekezo chiri mwa [iwo], komatu ndi chifatso ndi mantha’?—1 Petro 3:15.
20. Kodi nchiyani choyamba chimene timafuna kuti ana athu adziŵe ndi kukhulupirira ponena za mwazi? (Danieli 1:3-14)
20 Chinkana kuti kukakhala kwabwino kuti ana athu adziŵitsidwe ponena za ngozi za matenda ndi maupandu ena a kuthiridwa mwazi, kulangiza ana athu m’lamulo langwiro la Mulungu pa mwazi sikumatanthauza kwakukulukulu kuyesa kuwapangitsa kuwopa mwazi. Mwachitsanzo, ngati woweruza anafunsa msungwana chifukwa chimene sanafunire kupatsidwa mwazi ndipo yankho lake kwakukulukulu linali lakuti analingalira kuti mwazi ngwaupandu kapena ngwoopsa, kodi nchiyani chingakhale chotulukapo? Woweruzayo angagamule kuti iye anangochita mwachibwana ndi kuchita mantha kwenikweni, monga momwe akawopera kutumbulidwa kochotsa appendix kwakuti akalira ndi kukana opareshoniyo imene ngakhale makolo ake anaiwona kukhala yabwino koposa kwa iye. Ndiponso, tawona poyambirirapo kuti chifukwa chachikulu chimene Akristu amakanira kuthiridwa mwazi sichakuti mwazi ngwoipitsidwa koma kuti ngwamtengo wapatali kwa Mulungu wathu ndi Mpatsi wa Moyo. Ana athu ayenera kudziŵa zimenezo, limodzinso ndikuti maupandu azamankhwala othekera a mwazi amawonjezera kuwopsa kwa kaimidwe kathu kachipembedzo.
21. (a) Kodi makolo ayenera kudziŵanji ponena za ana awo ndi lingaliro Labaibulo ponena za mwazi? (b) Kodi ndimotani mmene makolo angathandizire ana awo m’nkhani ya mwazi?
21 Ngati muli ndi ana, kodi ndinu otsimikiza kuti iwo amavomereza ndipo akhoza kufotokoza kaimidwe kozikidwa pa Baibulo pa kuthiridwa mwazi? Kodi iwo amakhulupiriradi kaimidwe kameneka kukhala chifuniro cha Mulungu? Kodi ngokhutiritsidwa kuti kulakwira lamulo la Mulungu nkowopsa kwakuti kukaika pachiswe chiyembekezo cha Mkristu cha moyo wosatha? Makolo anzeru adzakambitsirana nkhanizi ndi ana awo, kaya akhale aang’ono kwambiri kapena otsala pang’ono kukhala achikulire. Makolo angalinganize magawo akuyesera mmene wachichepere aliyense akayang’anizirana ndi mafunso omwe angafunsidwe ndi woweruza kapena mkulu wachipatala. Chonulirapo sichakuti wachichepere aloŵeze ndikukhoza kubwereza pamtima mfundo zosankhidwa kapena mayankho. Nkofunika kwambiri kuti adziŵe chimene iwo amakhulupirira, ndi chifukwa chake. Ndithudi, pa mlandu wa ku khoti, makolo kapena ena angapereke chidziŵitso chonena za maupandu a mwazi ndi kukhalapo kwa njira zina zochiritsira. Koma chimene woweruza kapena nduna mwachiwonekere akafuna kudziŵa mwakulankhula ndi ana nchakuti kaya iwo amamvetsetsa mwauchikulire mkhalidwe wawo ndi zosankha zokhalapo ndiponso kaya iwo ali ndi miyezo yawoyawo ndi zikhulupiriro zolimba.—Yerekezerani ndi 2 Mafumu 5:1-4.
22. Kodi nchiyani chimene chingakhale chotulukapo chosatha cha kukhala kwathu olangizidwa ndi Mulungu ponena za mwazi?
22 Tonsefe tifunikira kumvetsetsa ndikumamatira motsimikiza ku lingaliro la Mulungu la mwazi. Chibvumbulutso 1:5 chimalongosola Kristu kukhala amene ‘anatikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake.’ Kokha mwakuvomereza mtengo wa mwazi wa Yesu ndipamene tingapeze chikhululukiro chokwanira ndi chosatha cha machimo athu. Aroma 5:9 momvekera bwino amanena kuti: ‘Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa iyeyo.’ Pamenepo, nkwanzeru motani nanga, kwa ife ndi ana athu kumalangizidwa ndi Yehova pankhaniyi ndi kukhala otsimikiza mtima kuyenda m’njira yake kosatha!
[Mawu a M’munsi]
a Onani brosha yakuti How Can Blood Save Your Life?, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, pamasamba 21-2, 28-31.
Mfundo Zazikulu za Malangizo
◻ Kodi tiyenera kukhala ndi lingaliro lotani ponena za kulangizidwa ndi Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji kumvera lamulo la Mulungu la mwazi nkofunika kwambiri?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti achichepere akhale okhoza kufotokoza momvekera bwino ndi molimba zikhulupiriro zawo ponena za mwazi?
◻ Kodi ndimotani mmene makolo Achikristu angathandizire ana awo kukhala olangizidwa bwino m’lamulo la Yehova la mwazi?
[Bokosi patsamba 17]
KHOTI LINAKONDWERETSEDWA
Kodi chigamulo cha khoti chinanenanji ponena za D.P., wotchulidwa m’ndime 17?
“Khoti linakondweretsedwa koposa ndi luntha, kulimba mtima, ulemu, ndi kulankhula mwamphamvu kwa wachichepere wa zaka 14-1/2 ameneyu. Iye ayenera kukhala anachita mantha kuti anapezedwa ndi mtundu wa kansa imene imapha . . . Komabe, iye anali wachichepere wofikapo yemwe anabwera ku Khoti kudzapereka umboni. Iye anawoneka kuti analingalira mosamalitsa pa chothetsa nzeru chovuta chimene anayang’anizana nacho. Iye anapita ku magawo onse opereka uphungu, anavomereza kuchiritsa kokonzekeredwa, anakulitsa lingaliro la mmene monga munthu akayang’anizirana ndi chitokoso chamankhwala chimenechi, ndipo anabwera ku Khoti ndi pempho logwira mtima: talemekezani chosankha changa . . .
“Kuwonjezera pa uchikulire wake, D.P. walongosola mokwanira maziko a chosankha chake kuti Khoti lichilemekeze. Iye akavulazidwa mwauzimu, mwamaganizo, mwamakhalidwe, ndi mwamalingaliro ngati apatsidwa chithandizo choloŵetsamo kuthiridwa mwazi. Khoti lidzalemekeza chosankha chake cha makonzedwe a kumthandiza.”
[Chithunzi patsamba 16]
Woweruza kapena mkulu wa m’chipatala angafune kudziŵa zimene wachichepere Wachikristu amakhulupiriradi, ndi chifukwa chake