‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
‘Mulankhule Trufena, ndi Trufosa [akazi, “NW”] amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye.’—AROMA 16:12.
1. Kodi uminisitala wapadziko lapansi wa Yesu unatsimikizira motani kukhala dalitso kwa akazi?
UMINISITALA wapadziko lapansi wa Yesu unalidi dalitso kwa akazi Achiyuda. Ntchito imene anaiyamba inabweretsa chitonthozo, chiyembekezo, ndi ulemu watsopano kwa akazi a mafuko onse. Iye sanalabadire miyambo Yachiyuda imene ‘inapeputsa mawu a Mulungu.’ (Mateyu 15:6) Yambiri ya miyambo imeneyo inalakwira zoyenera zenizeni za akazi zopatsidwa ndi Mulungu.
Mkhalidwe wa Yesu Kulinga kwa Akazi
2. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti lingaliro la Yesu la akazi linali kusintha kwakukulu kwa panthaŵiyo?
2 Ha, panali kusiyana kotani nanga pakati pa mkhalidwe wa Yesu kulinga kwa akazi ndi uja wa atsogoleri achipembedzo Achiyuda! Kugwira mawu Encyclopaedia Judaica, omalizirawo analingalira akazi kukhala “aumbombo, otchera khutu ku zinsinsi, aulesi, ndiponso ansanje.” Kukambitsirana ndi mkazi kunali kunyazitsidwa, ndipo “chinali chamanyazi kwa katswiri kulankhula ndi mkazi m’khwalala.” (Jerusalem in the Time of Jesus, lolembedwa ndi Joachim Jeremias; yerekezerani ndi Yohane 4:27.) Zambiri zinganenedwe ponena za mkhalidwe wonyoza wa atsogoleri Achiyuda kulinga kwa akazi. Koma zomwe ziri pamwambazo zidzasonyeza mokwanira mmene lingaliro la Yesu la akazi linaliridi kusintha kwakukulu panthaŵiyo.
3. Kodi nzochitika zotani za m’nthaŵi ya uminisitala wa Yesu zimene zikusonyeza kuti iye anali wofunitsitsa kuphunzitsa akazi chowonadi chauzimu chozama?
3 Yesu amapereka chitsanzo changwiro cha mmene amuna angakhalire ndi unansi waubwenzi komabe woyera ndi akazi. Iye sanangolankhula nawo komanso anawaphunzitsa chowonadi chauzimu chozama. Kwenikweni, munthu woyambirira weniweni amene anamuululira poyera kuti ndiye Mesiya anali mkazi, ndipotu anali mkazi Wachisamariya. (Yohane 4:7, 25, 26) Kuwonjezerapo, chochitika chokhudza Malita ndi Mariya chimasonyeza bwino lomwe kuti mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda, Yesu sanalingalire kuti mkazi analibe kuyenera kwakusiya ntchito yake yophika kuti akawonjezere chidziŵitso chake chauzimu. Panthaŵi imeneyo, Mariya “anasankha dera lokoma,” mwakuika zinthu zauzimu patsogolo. (Luka 10:38-42) Koma miyezi yoŵerengeka pambuyo pake, apo nkuti mchimwene wawo anamwalira, anali Malita, osati Mariya, amene anasonyeza kufunitsitsa kokulira kwakukumana ndi Ambuye. Timakondweretsedwa chotani nanga ngakhale lerolino pamene tiŵerenga za kukambitsirana kwauzimu kwakuya pakati pa Yesu ndi Malita ponena za chiyembekezo cha kuuka! (Yohane 11:20-27) Ha, umenewo unali mwaŵi wotani nanga kwa Malita!
Akazi Amene Anatumikira Yesu
4, 5. Pambali pa atumwi, kodi ndani anatsata Yesu mu uminisitala wake wa ku Galileya, ndipo kodi iwo anamtumikira motani?
4 Yesu anavomerezanso kutumikiridwa ndi akazi pamene ankayendayenda m’dziko. Mu Uthenga wake Wabwino, Marko akutchula “akazi . . . amene anamtsata Iye [Yesu], pamene anali m’Galileya, namtumikira.” (Marko 15:40, 41) Kodi akazi ameneŵa anali yani, ndipo kodi anamtumikira motani Yesu? Sitikuwadziŵa maina awo onse, koma Luka akupereka maina ochepa ndikulongosola njira imene anatumikirira Yesu.
5 Luka akulemba kuti: ‘Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza [mbiri yabwino ya, NW] ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi aŵiriwo, ndi akazi ena amene anachiritsidwa mizimu yoipa ndi nthenda zawo, ndiwo, Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziŵanda zisanu ndi ziŵiri zinatuluka mwa iye, ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chawo.’ (Luka 8:1-3) Yesu anali wofunitsitsa kuti akazi ameneŵa amtsate ndikugwiritsira ntchito chuma chawo kutumikira zosoŵa zake zakuthupi ndi za atumwi ake.
6. (a) Kodi ndani amene anatsagana ndi Yesu paulendo wake womalizira womka ku Yerusalemu? (b) Kodi ndani anali pambali pa Yesu mpaka imfa yake, ndipo kodi ena a iwo anafupidwa motani? (c) Malinga ndi kawonedwe kazinthu ka miyambo Yachiyuda, kodi nchiyani chimene chiri chapadera ponena za cholembedwa cha pa Yohane 20:11-18?
6 Pamene Yesu anaphedwa, ‘anali pomwepo akazi ambiri, akuyang’anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira iye; mwa iwo amene munali Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake wa Yakobo, ndi wa Yose.’ (Mateyu 27:55, 56) Chotero, akazi ambiri okhulupirika anali pambali pa Yesu panthaŵi ya imfa yake. Chofunikanso nchakuti akazi anali mboni zoyambirira za kuuka kwake. (Mateyu 28:1-10) Chimenechi mwa icho chokha chinali chothetsa nzeru ku mwambo Wachiyuda, popeza kuti m’Chiyuda akazi ankalingaliridwa kukhala osayenerera kukhala mboni za lamulo. Polingalira zimenezi, ŵerengani Yohane 20:11-18, ndipo yesani kulingalira za malingaliro amphamvu amene Mariya wa Magadala anali nawo pamene Ambuye woukitsidwayo anawonekera kwa iye, kumuitana ndi dzina, ndikumgwiritsira ntchito monga mboni yake kudziŵitsa ophunzira ake kuti iye alidi wamoyo!
Akazi Achikristu Okhulupirika Pambuyo pa Pentekoste
7, 8. (a) Kodi timadziŵa motani kuti akazi analipo pamene mzimu unatsanulidwa pa Pentekoste? (b) Kodi akazi Achikristu anakhala motani ndi phande m’kufutukuka koyambirira kwa Chikristu?
7 Pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Yesu, akazi opembedza anali pamodzi ndi atumwi okhulupirika m’chipinda chosanja ku Yerusalemu. (Machitidwe 1:12-14) Chenicheni chakuti padali akazi pakati pa awo amene anatsanuliridwa mzimu woyera pa Pentekoste nchodziŵikiratu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pamene Petro analongosola zomwe zinachitika, iye anagwira mawu Yoweli 2:28-30, amene amatchula mwachindunji ‘ana . . . aakazi’ ndi “adzakazi,” kapena “akapolo [aakazi, NW].” (Machitidwe 2:1, 4, 14-18) Chotero akazi Achikristu obadwa ndi mzimu, odzozedwa anali mbali ya mpingo Wachikristu kuyambira pachiyambi penipeni.
8 Akazi anachita mbali yaikulu, chinkana kuti osati yowonekera, m’kufalitsa Chikristu. Mariya, amake wa Marko ndi azakhali a Barnaba, anapereka nyumba yawo yaikulu kuti idzigwiritsiridwa ntchito ndi mpingo wa ku Yerusalemu. (Machitidwe 12:12) Ndipo anali ofunitsitsa kuchita zimenezi panthaŵi imene panali kuulika kwatsopano kwa chizunzo cha Akristu. (Machitidwe 12:1-5) Ana aakazi anayi a mlengezi Filipo anali ndi mwaŵi wakukhala aneneri aakazi Achikristu.—Machitidwe 21:9; 1 Akorinto 12:4, 10.
Mkhalidwe wa Paulo Kulinga kwa Akazi
9. Kodi ndiuphungu wotani umene Paulo anapereka ponena za akazi Achikristu m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, ndipo kodi ndilamulo lamakhalidwe abwino laumulungu lotani limene iye analimbikitsa akazi kulilemekeza?
9 Nthaŵi zina mtumwi Paulo amapatsidwa mlandu wa kuwada ndi kusawakhulupirira akazi. Zowonadi, anali Paulo amene anaumirira kuti akazi asunge malo awo oyenerera mu mpingo Wachikristu. M’zochitika za nthaŵi zonse, iwo sanayenera kuphunzitsa pamisonkhano yampingo. (1 Akorinto 14:33-35) Ngati mkazi Wachikristu analankhula pamsonkhano, chifukwa chakuti panalibe mwamuna Wachikristu kapena chifukwa chakuti ananenera mwa chitsogozo cha mzimu woyera, iye anafunikira kuvala chophimba kumutu. Chophimba chimenechi chinali “chizindikiro cha ulamuliro,” umboni wowonekera wakuti mkaziyo amazindikira kakonzedwe ka Mulungu ka umutu.—1 Akorinto 11:3-6, 10, NW.
10. Kodi ndi mlandu wanji umene anthu ena amampatsa Paulo, koma kodi nchiyani chimene chikutsimikizira kuti chinenezo chimenechi nchabodza?
10 Mwachiwonekere Paulo anachipeza kukhala choyenera kukumbutsa Akristu oyambirira za malamulo amakhalidwe abwino ateokratiki ameneŵa kotero kuti ‘zonse zichitike koyenera’ pamisonkhano yampingo. (1 Akorinto 14:40) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Paulo anali wokana akazi, monga momwe ena amanenera? Ayi, sizimatero. Kodi sanali Paulo amene anatumiza moni kwa akazi Achikristu asanu ndi anayi m’mutu womalizira wa kalata yake ya kwa Aroma? Kodi iye sanasonyeze chiyamikiro chakuya kwa Febe, Priska (Priskila), Trufena, ndi Trufosa, akumatcha aŵiri omalizirawa kukhala ‘akazi amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye’? (Aroma 16:1-4, 6, 12, 13, 15) Ndipo anali Paulo amene mouziridwa analemba kuti: ‘Nonse amene munabatizidwa mwa Kristu mudavala Kristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.’ (Agalatiya 3:27, 28) Mwachiwonekere Paulo anakonda ndipo anayamikira alongo ake Achikristu, kuphatikizapo Lidiya, yemwe anasonyeza kuchereza kwabwino m’nthaŵi ya chiyeso.—Machitidwe 16:12-15, 40; Afilipi 4:2, 3.
Akazi Ogwiritsa Ntchito Lerolino
11, 12. (a) Kodi ndimotani mmene Salmo 68:11 likukwaniritsidwira m’njira yeniyeni lerolino? (b) Kodi alongo athu ambiri amadzipeza mu mkhalidwe wotani, ndipo nchifukwa ninji amafunikira chikondi ndi mapemphero athu?
11 Mkati mwa mpingo Wachikristu lerolino, muli akazi ambiri Achikristu amene ‘agwiritsa ntchito mwa Ambuye.’ Kwenikweni, ziŵerengero zimasonyeza kuti ‘akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu,’ lopanga mbali yaikulu ya khamu la Mboni zimene Yehova akugwiritsira ntchito m’nthaŵi ino yamapeto. (Salmo 68:11) Akazi Achikristu ogwiritsa ntchito ameneŵa adzipezera dzina labwino popeza kuti iwo amalimbikira kukwaniritsa mathayo awo monga akazi okwatiwa, amayi, okonza nyumba, opezera chakudya banja lawo, ndiponso aminisitala Achikristu.
12 Chiŵerengero cha alongo abwino ameneŵa ali ndi amuna osakhulupirira. Iwo amayenera kulaka mkhalidwewu kwa maola 24 patsiku. Ena akhala akulimbikira kwa zaka zambiri kuti akhale akazi abwino pamene akufikiritsa ziyeneretso za atumiki okhulupirika a Yehova. Sizinakhale zokhweka, koma iwo apirira, nthaŵi zonse akumayembekezera kuti amuna awo ‘akakodwe opanda mawu’ kupyolera mwa mayendedwe awo abwino Achikristu. Ndipo zimakhala zokondweretsa chotani nanga ku banja lonse pamene amuna oterowo avomereza! (1 Petro 3:1, 2) Pakali pano, alongo okhulupirika ameneŵa amafunikiradi chikondi chaubale ndi mapemphero a ziŵalo zina za mpingo. Monga momwedi ‘mzimu wofatsa ndi wachete’ umene amayesayesa kusonyeza uli ‘wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu,’ momwemonso umphumphu wawo wochilimika ngwamtengo wake pamaso pathu.—1 Petro 3:3-6.
13. Kodi nchifukwa ninji tingawatche alongo athu achipainiya kuti ndiwo ‘akazi amene akugwiritsa ntchito mwa Ambuye,’ ndipo kodi ayenera kulingaliridwa motani m’mipingo yawo yosiyanasiyana?
13 Alongo amene akutumikira monga apainiya anganenedwedi kukhala ‘akugwiritsa ntchito mwa Ambuye.’ Ambiri a iwo ali ndi nyumba, mwamuna, ndi ana ofunika kuwasamalira, kuwonjezera pa ntchito yawo yolalikira. Ena amagwira ntchito yaganyu kuti apeze zosoŵa zawo zakuthupi. Zonsezi zimafunikira kulinganiza kwabwino, kutsimikiza mtima, kupirira, ndi kugwira ntchito zolimba. Akazi Achikristu ameneŵa ayenera kukhala okhoza kuchiwona chikondi ndi chichilikizo cha awo amene mikhalidwe yawo simawalola kupereka maola aupainiya ku ntchito yochitira umboni.
14. (a) Kodi nchitsanzo chabwino chotani chakupirira chimene chatchulidwa? (b) Kodi ndiakazi Achikristu ena ati amene afunikira chiyamikiro, ndipo kodi nchifukwa ninji? Tchulani zitsanzo zina zakumaloko.
14 Akazi ena Achikristu asonyeza kulimba mtima kodabwitsa muutumiki waupainiya. Mu Canada, Grace Lounsbury analawa upainiya wake koyamba mu 1914. Iye anayenera kuchoka pa ndandanda ya apainiya mu 1918 chifukwa cha kudwala, koma pofika mu 1924 iye anabwereranso muutumiki wanthaŵi zonse. Panthaŵi imene tikulemba nkhaniyi, iye adakali pa ndandanda ya apainiya, mosasamala kanthu za msinkhu wake wa zaka 104! Alongo ambiri achimishonale amene anaphunzitsidwa m’makalasi oyambirira a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower m’ma 1940 adakatumikirabe mokhulupirika, kaya m’munda wawo waumishonale kapena monga ziŵalo za banja la Beteli ku Brooklyn kapena imodzi ya nthambi za Watch Tower Society. Akazi Achikristu onseŵa, ndipo ndithudi alongo onse amene amagwira ntchito muutumiki wa pa Beteli, amasonyeza mzimu wakudzimana ndipo ali zitsanzo zabwino. Kodi timawadziŵitsa kuti iwo amayamikiridwa?
Akazi a Oyang’anira Oyendayenda
15, 16. Kodi ndigulu liti la akazi Achikristu limene makamaka lifunikira chiyamikiro chathu chakuya, ndipo nchifukwa ninji?
15 Akazi a oyang’anira oyendayenda amapanga gulu lina la akazi Achikristu amene amafunikira chiyamikiro chakuya ndi chilimbikitso. Alongo okondedwa ameneŵa ngokonzekera kutsatira amuna awo pamene akupita ku mpingo ndi mpingo, kapena dera ndi dera, kuti akamangirire abale awo mwauzimu. Ambiri a iwo asiya zisangalatso za nyumba; iwo amagona pakama wosiyana mlungu uliwonse, ndipo osati kama wabwino nthaŵi zonse. Koma amakhala achimwemwe kulandira zirizonse zimene abale awo amapereka. Iwo ali zitsanzo zabwino kwa alongo awo auzimu.
16 Akazi Achikristu ameneŵa amaperekanso chilikizo lamtengo wake kwa amuna awo, mofanana ndi akazi opembedza amene anatsagana ndi Yesu ‘kumtsata iye . . . namtumikira.’ (Marko 15:41) Iwo sali okhoza kuthera nthaŵi yaikulu ali ndi amuna awo, omwe nthaŵi zonse amakhala ‘akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Ena a iwo, monga Rosa Szumiga m’Falansa, yemwe anayamba utumiki wanthaŵi zonse mu 1948, akhala akulonga masutikesi a amuna awo ndi kuyenda nawo kwa zaka 30 kapena 40. Iwo ngofunitsitsa kudzimana kaamba ka Yehova ndi abale ndi alongo awo. Iwo afunikira chiyamikiro, chikondi, ndi mapemphero athu.
Akazi a Akulu
17, 18. (a) Kodi ndimikhalidwe yotani imene imafunikira kwa akazi a abale omwe aikidwa m’malo autumiki? (b) Kodi ndi kudzimana kotani kumene akazi a akulu amavomereza kukupanga kaamba ka Yehova ndi abale awo, ndipo kodi akazi ena angaŵathandize motani amuna awo?
17 Pondandalitsa ziyeneretso za abale amene angaikidwe monga akulu ndi atumiki otumikira, mtumwi Paulo anatchulanso akazi, akumalemba kuti: ‘Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadyerekeza, odzisunga, okhulupirika m’zonse.’ (1 Timoteo 3:11) Zowonadi, uphungu wachisawawa umenewu umagwira ntchito kwa akazi onse Achikristu. Koma polingalira mawu apatsogolo ndi apambuyo a lembalo, mwachiwonekere uyenera kutsatiridwa monga chitsanzo ndi akazi a abale amene aikidwa mmalo a utumiki.
18 Mwachimwemwe, mmenemu ndi mmene zimakhalira ndi akazi a oyang’anira Achikristu zikwi zambiri. Iwo ali odzisunga m’zizoloŵezi ndi kavalidwe kawo, olama maganizo pa kakhalidwe Kachikristu, osamalitsa ndi zimene amanena, ndipo amakalamira mowona mtima kukhala okhulupirika m’zonse. Iwo amavomerezanso kudzimana, kuvomereza kuti amuna awo athere nthaŵi yaikulu yomwe akanakhala nawo ku zochita za mpingo. Akazi Achikristu okhulupirika ameneŵa amayenera chikondi chathu chakuya ndi chilimbikitso. Mwinamwake abale owonjezereka angafikire mathayo m’mipingo yathu yambiri ngati akazi awo angavomereze modzichepetsa kupanga kudzimana koteroko kaamba ka ubwino wa onse.
“Akazi Okalamba” Okhulupirika
19. Kodi nchifukwa ninji “akazi okalamba” okhulupirika ambiri amayamikiridwa kwakukulu m’mipingo yawo, ndipo kodi malingaliro athu ayenera kukhala otani kulinga kwa iwo?
19 Kupendanso kwathu kwa akazi otchulidwa m’Baibulo kwatitheketsa kuwona kuti msinkhu sumaletsa akazi okhulupirika kutumikira Yehova. Mfundo imeneyi inachitiridwa fanizo m’nkhani ya Sara, Elizabeti, ndi Ana. Lerolino, pali akazi okalamba ambiri Achikristu amene ali zitsanzo zabwino za kukhulupirika ndi kupirira. Kuwonjezerapo, iwo angachilikize mwanzeru akulu mwakuthandiza alongo achichepere. Pokhala ozoloŵera kwa nthaŵi yaitali, iwo angapereke uphungu wanzeru kwa akazi achichepere, monga momwedi Malemba amawalamulira kutero. (Tito 2:3-5) Zingachitike kuti nthaŵi zina mkazi wokalamba weniweniyo ndiye akufunikira uphungu. Ngati nditero, mkulu wochita zimenezoyo ayenera ‘kumdandaulira monga mayi.’ Akulu ayenera ‘kuchitira ulemu amasiye’ ndipo, ngati lingafunikire, kulinganiza thandizo lakuthupi kaamba ka iwo. (1 Timoteo 5:1-3, 5, 9, 10) Alongo athu okalamba ayeneradi kudzimva kuti ngofunidwa ndipo oyamikiridwa.
Olamulira ndi Kristu
20. Kodi ndimwaŵi wapamwamba wotani umene waperekedwa kwa akazi Achikristu ambiri, ndipo kodi nchifukwa ninji nkhosa zina ziyenera kukhala zachimwemwe ponena za chimenechi?
20 Nchowonekeratu kuchokera ku Malemba kuti “Mulungu alibe tsankhu” ponena za fuko kapena kuti kaya ndi mkazi kapena mwamuna. (Aroma 2:10, 11; Agalatiya 3:28) Ndipo izi nzowonanso m’njira imene Yehova amasankhira awo amene akagwirizana ndi Mwana wake m’boma la Ufumu. (Yohane 6:44) Khamu lalikulu liyenera kukhala loyamikira chotani nanga kuti akazi okhulupirika, monga ngati Mariya, amake wa Yesu, Mariya wa Magadala, Priskila, Trufena, Trufosa, ndi khamu la akazi ena m’mpingo Wachikristu woyambirira, tsopano ali ndi phande mu ulamuliro wa Ufumu, kulemeretsa boma limenelo ndi malingaliro awo achifundo ndi kuzoloŵera kwa akazi! Ha, ndi chiyang’aniro chachikondi ndi nzeru chotani nanga cha Yehova!—Aroma 11:33-36.
21. Kodi malingaliro athu lerolino ngotani kulinga kwa ‘akazi amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye’?
21 Ife lerolino tingakhale ndi malingaliro onga a mtumwi Paulo pamene analankhula mwachikondi ndiponso moyamikira za “akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu [mbiri yabwino, NW].” (Afilipi 4:3) Mboni zonse za Yehova, amuna ndi akazi, zimachiwona kukhala chosangalatsa ndi mwaŵi kugwira ntchito pamodzi ndi ‘khamu lalikulu la akazi akulalikira mbiri yabwino,’ inde, ‘akazi amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye.’—Salmo 68:11; Aroma 16:12.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi Yesu anasonyeza motani kuti analibe malingaliro atsankho a atsogoleri achipembedzo Achiyuda motsutsana ndi akazi?
◻ Kodi akazi owopa Mulungu anamtumikira motani Yesu, ndipo kodi ndimwaŵi waukulu wotani umene ena a iwo analandira?
◻ Kodi ndiuphungu wotani umene Paulo anapereka ponena za akazi m’misonkhano yampingo?
◻ Kodi ndimagulu a alongo ati amene ayenera chikondi chathu chapadera ndi chichilikizo, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi tiyenera kulingalira motani za onse amene lerolino ali ‘akazi amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye’?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Akazi anatumikira Yesu ndi atumwi ake
[Zithunzi patsamba 18]
Akazi odzimana a oyang’anira oyendayenda ndi a akulu ena amathandizira kwakukulu ntchito ya Mulungu