Kodi Kuchiritsa kwa Chikhulupiriro Kumavomerezedwa ndi Mulungu?
“LERO taona zodabwitsa!” Inde, openyererawo anadabwa. Munthu wamanjenje anachiritsidwa pamaso pawo. Wochiritsayo anauza munthuyo kuti: “Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.” Ndipo munthuyo anachita zimenezo! Sanalinso wamanjenje. Nkosadabwitsa kuti amene analipo “analemekeza Mulungu”! (Luka 5:18-26) Kuchiritsa kumeneku, komwe kunachitidwa ndi Yesu Kristu pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, kunalidi kovomerezedwa ndi Mulungu.
Bwanji nanga za lerolino? Kodi kuchiritsa kozizwitsa kudakali kothekera kwa awo amene sangachiritsidwe ndi mankhwala? Yesu anachita zozizwitsa zakuchiritsa. Lerolino ochiritsa mwa chikhulupiriro amanena kuti amamtsanzira iye. Kodi tiyenera kuziwona motani zonena zawo?
Kuchiritsa kwa chikhulupiriro kwanenedwa kukhala “njira yochiza matenda mwakupemphera ndi kusonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu.” Encyclopædia Britannica ikutsimikizira kuti: “Mbiri ya kuchiritsa kwa chikhulupiriro m’Chikristu inayamba ndi mautumiki odabwitsa a Yesu mwiniyo ndi atumwi.” Inde, Yesu anachiritsa modabwitsa. Kodi ochiritsa mwa chikhulupiriro alerolino amachita zozizwitsa monga momwe iye anachitira?
Chikhulupiriro—Kodi Chiri Chiyeneretso?
Malinga nkunena kwa Black’s Bible Dictionary, Yesu “anagogomezera [chikhulupiriro] kukhala chiyeneretso cha zozizwitsa zake za kuchiritsa.” Koma kodi ndimo mmene zinaliri? Kodi Yesu anafuna kuti munthu wodwalayo akhale ndi chikhulupiriro asanachiritsidwe? Yankho ndilakuti ayi. Chikhulupiriro chinafunikira kwa wochiritsayo koma osati kwenikweni kwa wodwalayo. Nthaŵi ina ophunzira a Yesu analephera kuchiritsa mnyamata wakhunyu. Yesu anachiritsa mnyamatayo nawauza pambuyo pake ophunzirawo chifukwa chake analephera kumchiritsa. ‘Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching’ono.’—Mateyu 17:14-20.
Malinga ndi Mateyu 8:16, 17, Yesu ‘anachiritsa akudwala onse.’ Zowonadi, anthuŵa anali nacho chikhulupiriro pamlingo winawake mwa Yesu chimene chinawachititsa kumfikira. (Mateyu 8:13; 9:22, 29) M’zochitika zambiri anabwera kudzampempha asanawachiritse. Komabe, sanafunikire kulengeza chikhulupiriro chawo kuti chozizwitsa chichitidwe. Nthaŵi ina Yesu anachiritsa munthu wopuwala yemwe sanamdziŵe nkomwe Yesu. (Yohane 5:5-9, 13) Pa usiku umene anagwidwa, Yesu anabwezeretsa khutu loduka la mtumiki wa mkulu wansembe, ngakhale kuti munthuyu anali mmodzi wa gulu la adani a Yesu omwe anabwera kudzamgwira. (Luka 22:50, 51) Ndithudi, nthaŵi zina, Yesu anaukitsa ngakhale akufa!—Luka 8:54, 55; Yohane 11:43, 44.
Kodi Yesu anakhoza motani kuchita zozizwitsa zimenezo? Chifukwa chakuti anadalira pa mzimu woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Iyo ndiyo inali kuchiritsa, osati chikhulupiriro cha wodwalayo. Mutaŵerenga nkhani za m’Mauthenga Abwino, mudzawonanso kuti kuchiritsa kwa Yesu sikunali kwa dzoma lalikulu. Panalibe machitidwe odziwonetsera kwa anthu kapena ochititsa chidwi mopambanitsa. Ndiponso, mosasamala kanthu za nthendayo, Yesu sanalephere konse. Nthaŵi zonse anapambana, ndipo sanalipiritse.—Mateyu 15:30, 31.
Kodi Kuchiritsa Kwamakono Nkofanana ndi kwa Yesu?
Matenda ndivuto lowopsa, ndipo atatigwira, mwachibadwa timafunafuna chithandizo. Komabe, bwanji ngati timakhala kumalo kumene “adokotala amayesa anthu, makamaka osauka, kukhala zinthu mmalo mwa anthu”? Izi nzimene dokotala wina anawona m’dziko lina la ku Latin America. Ndipo bwanji ngati timakhala kumalo kumene, mofanana ndi m’dziko limodzimodzilo, ‘40 peresenti yokha ya adokotala ndiwo oyeneretsedwa kugwira ntchito yawo’?
Nkosadabwitsa kuti ambiri, posapeza njira ina, amakuwona kukhala kofunika kuyesa kuchiritsa kwa chikhulupiriro. Komabe, kuchiritsa kochitidwa ndi ochiritsa mwa chikhulupiriro kuli nkhani yokaikiritsa. Mwachitsanzo, chiŵerengero chongoyerekezera cha 70,000 chinapezekapo pa msonkhano ku São Paulo, Brazil, kumene ochiritsa aŵiri ‘anapondaponda mandala mazana ambiri otaidwa ndi khamu, akumalonjeza eni ake okhulupirirawo kuti adzabwezeretsa mphamvu zawo zakuwona bwino.’ Mmodzi wa ochiritsawo anavomereza mowona mtima pamene anafunsidwa nati: “Sindinganene kuti odwala onse amene timawapempherera adzachiritsidwa. Zimadalira pa chikhulupiriro chawo. Ngati munthuyo akhulupirira, adzachiritsidwa.” Ananena kuti kulephera kuchira kulikonse kwa munthu wodwalayo kuli chifukwa cha kupanda kwake chikhulupiriro. Komabe, monga momwe tawonera kale, kumbukirani kuti Yesu ananena kuti kulephera kuchira kuli chifukwa cha kupanda chikhulupiriro kwa wochiritsayo!
Wochiritsa wina analonjeza kuchiza kansa ndi manjenje. Kodi chinachitika nchiyani? Malinga ndi kunena kwa magazini a Veja, “mwachiwonekere, lonjezolo silinakwaniritsidwe.” Ndipo tamverani mmene munthuyo anachitira: “Mkati mwa pafupifupi maola aŵiri, [wochiritsa mwa chikhulupiriroyo] anasangulutsa khamulo ndi maulaliki, mapemphero, kufuula, kuimba—ngakhale nkhonya, ndi cholinga chothamangitsa ziŵanda zotsakamira m’matupi a okhulupirika. Pamapeto pake, anataya tayi yake ndi handikachifi kwa khamu losangalatsidwalo nayendetsa mbale ya zopereka kuti alandire ‘zopereka zodzifunira.’” Yesu ndi atumwi ake sanapemphe konse ndalama kaamba ka kuchiritsa kozizwitsa, ndipo sanachite modziwonetsera motero.
Pamenepo, nkowonekeratu kuti ochiritsa mwa chikhulupiriro amakono sakuchita zimene Yesu anachita. Ndipo nkovuta kuwona kuti Mulungu angavomereze zimene akuchita. Komabe, kodi amavomereza kuchiritsa kozizwitsa kulikonse lerolino? Kapena kodi pali njira ina imene chikhulupiriro chathu chingatithandizire pamene ifeyo kapena wokondedwa wathu adwala?