Kodi Mphatso ya Malilime Ndimbali ya Chikristu Chowona?
“PAMENE ndinamumva akupemphera m’malilime, ndinamva monga ngati kuti munali mphamvu zamagetsi mumlengalenga,” anatero Bill iye ndi ena asanu ndi mmodzi atasonkhana pamaso pa mlaliki pafupi ndi guwa latchalitchi. Kodi zokumana nazo zoterozo zimabwerezanso kugwira ntchito kwa mzimu woyera kwa m’zaka za zana loyamba? Kodi zimasonyeza chimene chiri chipembedzo cha Baibulo? Tingathe kupeza mayankho okhutiritsa mwa kupenda mosamalitsa Malemba.
Cholembedwa Chabaibulo chimavumbula kuti pamene mphatso yozizwitsa iriyonse ya mzimu inaperekedwa, panali pafupifupi mmodzi wa atumwi 12 kapena mtumwi Paulo. Choyamba cha zochitika zitatu zolembedwa za kulankhula m’malilime chinachitika pakati pa ophunzira a Yesu 120 osonkhana m’Yerusalemu pa Pentekoste wa 33 C.E. (Machitidwe 2:1-4) Zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, pamene kagulu ka Ataliyana osadulidwa kanali kumvetsera Petro akulalikira, iwo analandira mzimu nayamba “kulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu.” (Machitidwe 10:44-48) Ndipo zaka 19 pambuyo pa Pentekoste, pafupifupi mu 52 C.E., Paulo analankhula kukagulu mu Efeso naika manja ake pa ophunzira 12. Nawonso “analankhula ndi malilime, nanenera.”—Machitidwe 19:6.
Nchifukwa Ninji Mphatso ya Malilime?
Mwamsanga asanakwere kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Wonani kuti iye chotero anapereka chisonyezero cha mmenedi ntchito yochitira umboni yankhaninkhaniyo ikachitidwira—mwachithandizo cha mzimu woyera.
Dongosolo la kulankhulirana limene limatikhozetsa kutumiza mauthenga kuzungulira padziko lonse lapansi m’zinenero zambiri kunalibe kalelo. Mbiri yabwino inayenera kufalitsidwa kwakukulukulu mwamawu apakamwa, ndipo mwa izi mphatso yozizwitsa ya kulankhula m’malilime achilendo ikatsimikizira kukhala yothandiza kwambiri. Ndimo mmene zinaliri pamene Akristu a m’zaka za zana loyamba analalikira kwa Ayuda ndi otembenuka m’Yerusalemu pa Pentekoste wa 33 C.E. Aparti, Amedi, Aelami, Akrete, Aarabu, nzika za Mesopotamiya, Yudeya, Kapadokiya, Ponto, ndi m’chigawo cha Asiya, kudzanso alendo ochokera ku Roma, anamva “zazikulu za Mulungu” m’chinenero chawochawo namvetsetsa zimene zinanenedwa. Mwamsanga okwanira zikwi zitatu anakhulupirira.—Machitidwe 2:5-11, 41.
Mfundo imene imanyalanyazidwa kaŵirikaŵiri njakuti kulankhula m’malilime kunali imodzi ya ntchito za mzimu woyera zisanu ndi zinayi zimene mtumwi Paulo anatchula m’kalata yake kwa Akristu a ku Korinto. Ngakhale kuti Paulo analingalira kulankhula m’malilime kukhala mphatso yocheperapo, inali yopindulitsa kumpingo woyambirira powanditsa mbiri yabwino yonena za Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Inali imodzi ya “mphatso” zimene zinathandizira kukukula m’ziwerengero ndi kulimbikitsidwa kwa mpingo Wachikristu wakhandawo.—1 Akorinto 12:7-11; 14:24-26.
Ntchito zosiyanasiyana za mzimu woyera m’zaka za zana loyamba, kuphatikizapo kulankhula m’malilime, zinalinso umboni wowoneka wakuti Mulungu sanali kugwiritsiranso ntchito mpingo wa Israyeli wazaka 1,500 monga anthu ake apadera. Mosakaikira, chiyanjo chake tsopano chinali ndi mpingo Wachikristu watsopanowo, woyambidwa ndi Mwana wake wobadwa yekha.—Yerekezerani ndi Ahebri 2:2-4.
Zisonyezero za mzimu zimenezi zinali mirimo yaikulu poyambitsa mpingo Wachikristu watsopanowo ndi kuuthandiza kukula kuuchikulire. Paulo anafotokoza kuti pambuyo pa kukhala zitatumikira chifuno chake, mphatso zozizwitsa zimenezi zikatha: “Koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka.”—1 Akorinto 13:8.
Inde, Baibulo likumveketsa bwino kuti mphatso ya malilime ikatha. Koma liti kodi? Machitidwe 8:18 akuvumbula kuti mphatso za mzimu zinalandiridwa “mwa kuika manja a atumwi.” Pamenepa, mwachiwonekere, mtumwi wotsiriza atafa, kuperekedwa kwa mphatso za mzimu kukalekeka—kuphatikizapo kulankhula m’malilime. Chotero, pamene awo amene analandira mphatso zimenezi kwa atumwiwo nawonso anatha pankhope ya dziko lapansi, mphatso zozizwitsazo zikatha. Podzafika panthaŵiyo mpingo Wachikristu ukakhala ndi nthaŵi ya kukhazikitsidwa bwino lomwe ndipo ukakhala utafalikira m’maiko ambiri.
“Malilime Achilendo” ndi Kutanthauzira Kwawo
Kuyambiranso kwa kulankhula m’malilime kwa m’tsiku lathu “kwawonedwa ndi ena kukhala kusalamulirika kwa malingaliro a odziwonetsera otengeka maganizo, pamene kuli kwakuti ena amakuwona kukhala kofanana ndi chochitika chozizwitsa cha kulankhula m’malilime cha m’nthaŵi za Atumwi.” Pamisonkhano yamatchalitchi yamakono pamene kulankhula “m’malilime osadziwika” kumachitika, kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo kuchita phokoso konyanyuka mwa mawu osazindikirika. Mogwirizana ndi zimenezi, munthu wina anaulula kuti: “Ndimagwiritsira ntchito mphatso yanga yamalilime kwakukulukulu mtseri kaamba ka kusinkhasinkha kwanga. . . . Ndimachita manyazi pang’ono pamaso pa anthu ena.” Winanso anafotokoza kuti: “Ndimamva mawu anga, sindimawamvetsetsa, koma ndimamvabe lilime langa likusonkhezeredwa kulankhula.”
Kodi nchidziwitso chopindulitsadi chotani chimene chimaperekedwa mwamalilime osadziwika oterowo, ndipo kodi bwanji ponena za kumasulira kwake? Awo amene amanena kuti amamasulira kulankhula kumeneku apereka mafotokozedwe osiyanasiyana a maneno osazindikirika amodzimodziwo. Kodi nchifukwa ninji kusiyanako? Iwo amafotokoza mopeputsa kusiyanako mwa kunena kuti “Mulungu anapatsa munthu mmodzi mamasulidwe amodzi a mawu ndipo kwa munthu wina mamasulidwe ena.” Munthu wina anavomereza kuti: “Ndawona zochitika pamene mamasulidwe sanali olondola.” D. A. Hayes, m’bukhu lake lakuti The Gift of Tongues, anatchula chochitika chimene mwamuna wina anakana kumasulira mawu a mkazi wina amene analankhula m’lilime losadziwika chifukwa chakuti “chinenerocho chinali chonyansa koposa.” Nkosiyana chotani nanga ndi kulankhula m’malilime kumene kunalipo m’zaka za zana loyamba ndi kumene kwenikweni kunali kaamba ka kulimbikitsa mpingo!—1 Akorinto 14:4-6, 12, 18.
Lerolino ena amanena kuti amva mamasuliridwe odabwitsa, ndipo iwo angakhulupirire mowona mtima kuti Mulungu akugwiritsira ntchito mphatsoyi pamene iye “afuna kupereka uthenga wachindunji kwa anthu.” Koma kodi ndiuthenga wotani wochokera kwa Mulungu umene tifunikira lerolino umene Yesu Kristu ndi atumwi sanatipatse? Paulo, amene iyemwiniyo anali ndi mzimu woyera, anati: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
Chowonadi nchakuti, mpingo Wachikristu suulinso wakhanda, ndipo chotero mavumbulutso aumulungu kapena mphatso zodabwitsa za mzimuwo sizikufunikiranso kutsimikizira ntchito yake. Baibulo limachenjeza kuti: “Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene [“wosiyana ndi umene,” The New English Bible] tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.”—Agalatiya 1:8.
Kulankhula kozizwitsa m’malilime sikulinso kofunikira, ndipo palibe maziko Abaibulo okhulupiririra kuti ndiko mbali ya Chikristu chowona lerolino. Popeza kuti tsopano Baibulo nlachikwanekwane ndi lopezeka mofala, tiri ndi zimene tifunikira m’Mawu a Mulungu. Limatilola kupeza chidziwitso cholongosoka cha Yehova ndi Mwana wake chimene chimatsogolera ku moyo wamuyaya.—Yohane 17:3; Chivumbulutso 22:18, 19.
Ngakhale m’zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo anasonkhezereka kulembera mpingo m’Korinto kuwongolera lingaliro lawo la chifukwa chimene mphatso yamalilime inaperekedwera kwa Akristu oyambirira. Kukuwonekera kuti, ena anachititsidwa chidwi ndi mphatso ya malilime, ndipo anali kuchita ngati makanda, osakula msinkhu mwauzimu. Chigogomezero chopambanitsa chinali kuikidwa pa “malilime.” (1 Akorinto 14:1-39) Paulo anagogomezera kuti sanali Akristu onse a m’zaka za zana loyambawo amene analankhula m’malilime ozizwitsa. Sanali ofunikira kuti iwo apulumuke. Ngakhale kalelo pamene inalipo, mphatso ya malilime inali yachiwiri kukunenera kozizwitsa. Kulankhula m’malilime sikunali, ndipo sikuli, chofunika kuti Mkristu apeze moyo wamuyaya.—1 Akorinto 12:29, 30; 14:4, 5.
Mphamvu Yosonkhezera Malilime Osadziŵika Lerolino
Ena amakhulupirira kuti mphamvu yosonkhezera olankhula m’malilime amakono ndiyo atsogoleri a matchalitchi okhala ndi luso lachilendo amene amasonkhezera ziwalo za gulu lawo kupeza luso limeneli. M’zochitika zina kumachititsidwa ndi kunyanyuka maganizo ndi kusakhazikika. Cyril G. Williams, m’bukhu lakuti Tongues of the Spirit, akunena kuti kwafikira kukhala “m’zochitika zambiri chizindikiro cha kutsungula m’kagulu” ndipo kumapatsa munthuyo “usinkhu ndi ulamuliro pamaso pa kaguluko ndiponso m’maso mwa iwo eni.” Chifukwa chake, chisonkhezerocho, chingakhale chikhumbo cha kukhala wa kagulu kapamwamba ka olankhula lilime losadziwika.
Yemwe kale anali pulezidenti wa Yunivesite ya Loyola wotchedwa Donald P. Merrifield ananena kuti “malilime angakhale chokumana nacho cha kunyanyuka kosalamulirika, kapena, malinga ndi kunena kwa ena, koipa kwambiri.” Mkulu wachipembedzo wina Todd H. Fast anati: “Malilime ngochititsa mkangano. Mdyerekezi ali ndi njira zambiri zoyesera kutigwira.” Baibulo lenilenilo limachenjeza kuti Satana ndi ziwanda zake ali okhoza kusonkhezera anthu ndi kulamulira kalankhulidwe kawo. (Machitidwe 16:17, 18) Yesu anachita motsutsana ndi mzimu wauchiwanda umene unasonkhezera mwamuna wina kufuula ndi kugwa pansi. (Luka 4:33-35) Paulo anachenjeza kuti ‘Satana angadzisandulize iyemwini kukhala mngelo wa kuunika.’ (2 Akorinto 11:14) Lerolino awo amene akufunafuna mphatso ya malilime imene Mulungu samapatsanso anthu ake kwenikweni akudzipereka kuchinyengo cha Satana, amene, tikuchenjezedwa kuti, angagwiritsire ntchito “mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama.”—2 Atesalonika 2:9, 10.
Malilime—Ndi Chikristu Chowona
Akristu a m’zaka za zana loyamba amene analandira mphatso yolankhula m’malilime anaigwiritsira ntchito kufotokoza zinthu zazikulu za Mulungu. Chigogomezero chinaikidwa pa kufunika kwa kumasulira momvekera bwino uthenga woperekedwa m’malilime kotero kuti umvetsetsedwe ndi onse ndi kupangitsa kulimbikitsidwa kwa ambiri. (1 Akorinto 14:26-33) Paulo ananena kuti: “Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mawu omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.”—1 Akorinto 14:9.
Pamene kuli kwakuti mzimu wa Mulungu unapatsa Akristu oyambirira mphatso ya malilime, uwo suunawapangitse kulankhula mawu osazindikirika kapena mawu opanda tanthauzo osakhoza kumasuliridwa. Mogwirizana ndi uphungu wa Paulo, mzimu woyera unapereka kalankhulidwe kamene kanapangitsa mbiri yabwino ‘kufalitsidwa mofulumira m’chilengedwe chonse pansi pa thambo.’—Akolose 1:23.
Ponena za masiku otsiriza amenewa a dongosolo liripoli, Yesu Kristu analamulira kuti: “Ndipo Uthenga Wabwino [wa Ufumu wokhazikitsidwa] uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Monga momwe kunaliri m’zaka za zana loyamba, chilengedwe chonse chiyenera kumva uthenga Waufumu. Zimenezi nzotheka chifukwa chakuti tsopano Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, latembenuzidwira m’zinenero pafupifupi 2,000. Mzimu umodzimodziwo umene unasonkhezera Akristu oyambirira kulankhula molimba mtima ndi mopanda mantha tsopano ukuchirikiza ntchito yaikulu ndi yodabwitsa ya kulalikira imeneyi ya mpingo wamakono wa Mboni za Yehova. Mwamawu apakamwa ndi mogwiritsira ntchito maluso amakono osindikizira kupangitsa chowonadi Chamalemba kukhala chopezeka mwamasamba osindikizidwa, izo zikulankhula “chinenero choyera.” Uthenga umenewu ukulowa m’maiko oposa 200 ndi zisumbu za m’nyanja. Mboni za Yehova zikuima monga anthu amene amasonkhezeredwa ndi mzimu wa Mulungu kudziwitsa onse zinthu zodabwitsa za Mulungu.—Zefaniya 3:9; 2 Timoteo 1:13.
[Zithunzi patsamba 7]
Kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba m’Japan
Kuchitira Umboni kungalawa ndi ngalawa m’Colombia
Pansipa: Phunziro Labaibulo m’Guatemala
Pansi pothera: Kuchitira umboni kumidzi m’Netherlands