Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
“Thaŵa zilakolako zaunyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.”—2 TIMOTEO 2:22.
1. Kodi tili ndi chiyembekezo chotani mwa achichepere amene ali pakati pathu?
“MBONI ZA YEHOVA,” inatero Dagen (Tsiku) nyuzipepala ya Pentecost ya ku Sweden, “ndizo gulu limene limakhala ndi chiŵerengero chachikulu koposa cha ziŵalo zatsopano chaka chilichonse ndipo lili ndi khamu lalikulu koposa la achichepere.” Mwinamwake inu muli mmodzi wa khamu limeneli la achichepere audongo, owopa Mulungu. Mwinamwake munaleredwa m’njira Yachikristu kuyambira paubwana, kapena mwina munamva ndi kulabadira uthenga wa Ufumu pa inu nokha. Mulimonse mmene zingakhalire, tili okondwera kuti muli nafe pakati pathu. Ndipo chiyembekezo chathu nchakuti mudzapitirizabe kulondola njira yachilungamo, monga momwe anachitira achichepere Achikristu okhulupirika m’zaka za zana loyamba. Mawu a mtumwi Yohane angakhale akukulongosolani bwino lomwe kuti: “Muli amphamvu, ndi mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.”—1 Yohane 2:14.
2. Kodi nzotani zimene zingachititse kulondola njira yolungama kukhala kovuta mkati mwa “unamwali”?
2 Ambiri—inde ochulukadi—a achichepere Achikristu lerolino akuchilimika kukaniza zitsenderezo zadziko. Komabe, mungapeze kuti kusunga njira yotero sikuli kopepuka. Pamene muli mu “unamwali,” mungadzazidwe ndi malingaliro atsopano ndi otsendereza. (1 Akorinto 7:36) Panthaŵi imodzimodziyo, mungadzimve kukhala ndi mtolo wa mathayo owonjezereka kusukulu, panyumba, ndi mumpingo. Palinso chitsenderezo chochokera kwa Satana Mdyerekezi mwiniyo. Pokhala wofunitsitsa kusocheretsa ambiri monga momwe angathere, iye amaukira awo amene angawoneke kukhala osavuta—monga momwe anachitira m’munda wa Edene. Kalelo, analunjikitsa machenjera ake okopa, osati pa Adamu wokulirapoyo, ndi wachidziŵitso kwambiri, koma pa Hava wocheperapo ndi wopanda chidziŵitso kwambiri. (Genesis 3:1-5) Zaka mazana ambiri pambuyo pake, Satana anagwiritsira ntchito maluso ofananawo pampingo Wachikristu wanthete mu Korinto. Mtumwi Paulo anati: “Koma ndiwopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Hava ndikuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.”—2 Akorinto 11:3.
3, 4. Kodi ndizida zina zotani zimene Satana Mdyerekezi amagwiritsira ntchito kusocheretsa achichepere, ndipo ndi chotulukapo chothekera chotani?
3 Lerolino, makolo anu Achikristu mofananamo angakhale okuderani nkhaŵa. Osati kuti akuganiza kuti muli ndi chikhoterero choipa, koma adziŵa mwa zokumana nazo kuti makamaka achichepere ndiwo ali chandamale cha “machitachita amachenjera” a Satana. (Aefeso 6:11, NW, mawu amtsinde) Mmalo mowoneka yowopsa, misampha ya Satana imachititsidwa kuwoneka yokopa kwambiri, yolakalakika. Wailesi yakanema imasonyeza mwaluso kwambiri kukondetsa zinthu zakuthupi, chisembwere, chiwawa chokakala, ndi za mizimu monga zosangulutsa. Maganizo achichepere angadzazidwe ndi zinthu zimene sizili ‘zowona, zolemekezeka, zolungama, zoyera, ndi zokongola.’ (Afilipi 4:8) Chitsenderezo cha amsinkhu wanu ndicho chida china champhamvu cha Satana. Amsinkhu wanu angakutsenderezeni kwambiri kuti mugwirizane ndi njira yawo yamoyo, kavalidwe, ndi kapesedwe. (1 Petro 4:3, 4) Wolemba m’danga la nyuzipepala William Brown anati: “Ngati pali Mulungu wazinthu zakuthupi mmodzi yekha wa achichepere, ndiye Mulungu wa kulingana. . . . Kwa achichepere kukhala wosiyana nkoipirapo kuposa imfa.” Msungwana wina yemwe ndi Mboni mu Italiya anavomereza kuti: “Ndinali kuchita manyazi kuti anzanga akusukulu adziŵe kuti ndinali Mboni. Ndipo chifukwa ndinadziŵa kuti Yehova sanali wokondwera nane, ndinali wachisoni ndi wopsinjika maganizo.”
4 Musanyengedwe—Satana amafuna kukutsogolerani ku chiwonongeko. Achichepere ambiri m’dziko adzataya miyoyo yawo pachisautso chachikulu chifukwa chakuti akudzilola kusochezedwa. (Ezekieli 9:6) Njira yokha yopulumukira ndiyo kulondola cholungama.
Chenjerani ndi Mayanjano Oipa
5, 6. (a) Kodi mwamuna wachichepere Timoteo anayang’anizana ndi zitokoso zotani pamene anali kukhala mu Efeso? (b) Kodi Paulo anapereka uphungu wotani kwa Timoteo?
5 Imeneyo ndiyo inali mfundo yaikulu ya uphungu wa mtumwi Paulo kwa Timoteo wachichepere. Kwa zaka zoposa khumi, Timoteo anatsagana ndi mtumwi Paulo pamaulendo ake aumishonale. Panthaŵi ina pamene Timoteo anali kutumikira mumzinda wachikunja wa Efeso, Paulo anali m’ndende Yachiroma akuyembekezera kunyongedwa. Pamene nthaŵi ya imfa yake inayandikira, mosakaikira Paulo anali wodera nkhaŵa ponena za mmene Timoteo akachitira. Efeso unali mzinda wodziŵika chifukwa cha chuma chake, chisembwere, ndi zosangulutsa zoluluzika, ndipo Timoteo sakakhalanso ndi chichilikizo cha phungu wake wokondedwayo.
6 Chotero Paulo analembera ‘mwana wake wokondedwa’ zotsatirazi: “Koma m’nyumba yaikulu simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu. Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino. Koma thaŵa zilakolako zaunyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.”—2 Timoteo 1:2; 2:20-22.
7. (a) Kodi ‘zotengera zopanda ulemu’ zimene Paulo anachenjezerapo zinali chiyani? (b) Kodi achichepere lerolino angagwiritsire ntchito motani mawu a Paulo?
7 Chotero Paulo anachenjeza Timoteo kuti ngakhale pakati pa Akristu anzake pangakhale panali ‘zotengera zopanda ulemu’—anthu amene sanadzisungire mwaubwino. Tsono ngati kuyanjana ndi Akristu ena odzozedwa kukanakhala kovulaza kwa Timoteo, koposa chotani nanga kwa Mkristu wachichepere kuyanjana ndi anthu akudziko lerolino! (1 Akorinto 15:33) Izi sizitanthauza kunyalanyaza anzanu akusukulu. Koma muyenera kusamala kusagwirizana nawo kwambiri, ngakhale ngati kutero kungakuchititseni kumakhala nokha nthaŵi zina. Izi zingakhale zovuta kwambiri. Msungwana wina wa ku Brazil anati: “Kuli kovuta. Nthaŵi zonse ndimaitanidwa ndi anzanga akusukulu kupita ku mapwando ndi kumalo osayenera kupitako achichepere Achikristu. Iwo amati: ‘Wati chiyani! Sudzapita? Ukupenga eti!’”
8, 9. (a) Kodi mayanjano, ngakhale ndi anthu akunja owoneka kukhala abwino, angaike ngozi yotani kwa Mkristu? (b) Kodi ndikuti kumene mungapeze mabwenzi oyenera?
8 Achichepere ena akudziko angawoneke kukhala abwino kokha chifukwa chakuti samasuta fodya, samatukwana, kapena samachita chisembwere. Komabe, ngati iwo sakulondola chilungamo, maganizo awo akuthupi ndi makhalidwe zingakuyambukireni mosavuta. Ndiponso, kodi ndizinthu zingati zimene mungagwirizanepo ndi osakhulupirira? (2 Akorinto 6:14-16) Eya, makhalidwe abwino auzimu amene mumasamalira bwino ali chabe “zopusa” kwa iwo! (1 Akorinto 2:14) Kodi mungapitirize kukhala bwenzi lawo popanda kulolera molakwa pamakhalidwe anu abwino?
9 Chotero peŵani mayanjano oipa. Lekezerani mayanjano anu kwa Akristu amaganizo auzimu amene amakondadi Yehova. Chenjerani ngakhale ndi achichepere amumpingo amene ali otsutsa kapena osuliza. Pamene mukula mwauzimu, mwachiwonekere mudzasintha mabwenzi amene muwasankha. Akutero msungwana wina yemwe ndi Mboni: “Ndakhala ndikupanga mabwenzi atsopano m’mipingo yosiyana. Kwandichititsa kuzindikira mmene mabwenzi akudziko aliri osafunika.”
Kuthaŵa Zilakolako Zoipa
10, 11. (a) Kodi kumatanthauzanji “kuthaŵa zilakolako za nyamata”? (b) Kodi ndimotani mmene wina angalithaŵire “dama”?
10 Paulo analimbikitsanso Timoteo “kuthaŵa zilakolako zaunyamata.” Pamene muli wachichepere, chikhumbo chakukhala wotchuka, kupeza chisangalalo, kapena kukhutiritsa zilakolako zakugonana chingakhale champhamvu. Ngati sizilamuliridwa, zikhumbo zotero zingakutsogolereni ku tchimo. Chifukwa chake Paulo ananena za kuthaŵa zikhumbo zovulaza—kuthamanga monga ngati kuti moyo wanu unali pangozi.a
11 Mwachitsanzo, chilakolako chakugonana chachititsa achichepere Achikristu ambiri kuwonongeka mwauzimu. Chotero, pali chifukwa chabwino chimene Baibulo limatiuzira ‘kuthaŵa dama.’ (1 Akorinto 6:18) Ngati mnyamata ndi msungwana akutomerana, kupita kokacheza, angagwiritsire ntchito lamulo lamkhalidwe limeneli mwakupeŵa mikhalidwe yopereka chiyeso—monga ngati kukhala aŵiri ali okha m’chipinda kapena m’galimoto yoimikidwa. Kukhala ndi woperekeza limodzi nanu kungawoneke kukhala kwachikale, koma kungakhale chitetezo chenicheni. Ndipo ngakhale kuti machitidwe ena achikondi angakhale oyenerera, malire oyenerera ayenera kuikidwa kuti mupeŵe mkhalidwe wonyansa. (1 Atesalonika 4:7) Kuthaŵa dama kumaphatikizaponso kupeŵa akanema kapena maprogramu a TV amene angadzutse chilakolako choipa. (Yakobo 1:14, 15) Ngati malingaliro achisembwere abwera okha m’maganizo mwanu, sinthani nkhaniyo m’maganizo. Pitani kokawongola miyendo, ŵerengani, chitani ntchito ina yapanyumba. Makamaka pemphero lili chithandizo champhamvu pankhaniyi.—Salmo 62:8.b
12. Kodi mungaphunzire motani kuda choipa? Perekani chitsanzo.
12 Koposa zonse, muyenera kuphunzira kuda, kunyansidwa, ndi kuipidwa ndi choipa. (Salmo 97:10) Kodi mungade motani chimene poyamba chingakhale chotsitsimula kapena chokondweretsa? Mwakuganiza za zotulukapo zake! “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.” (Agalatiya 6:7, 8) Pamene muli pachiyeso chakuti mugonjere ku chilakolako, talingalirani za chotulukapo chowopsacho—mmene kudzampwetekera mtima Yehova Mulungu. (Yerekezerani ndi Salmo 78:41.) Ganizaninso, za kuthekera kwa mimba yosafunika kapena kutenga nthenda, monga AIDS. Talingalirani za kusweka mtima ndi kutaikiridwa ulemu wanu kumene mudzavutika nako. Pangakhalenso zotulukapo zanthaŵi yaitali. Mkazi wina Wachikristu akuvomereza kuti: “Mwamuna wanga ndi ine tinali kuchita chisembwere ndi anthu ena tisanakwatirane. Ngakhale kuti tsopano tonsefe ndife Akristu, moyo wathu wachisembwere wakalewo ukuchititsa kuvutana ndi nsanje muukwati wathu.” Ndiponso, zosayenera kunyalanyazidwa ndizo kutaikiridwa mathayo ateokratiki kapena kuthekera kwakuchotsedwa mumpingo Wachikristu! (1 Akorinto 5:9-13) Kodi chisangalalo chakanthaŵi chilichonse nchoyenerera kutaikiridwa konseko?
Kulondola Unansi Wathithithi ndi Yehova
13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji sikokwanira kungothaŵa choipa? (b) Kodi ndimotani mmene munthu ‘angalondolere kumdziŵa Yehova’?
13 Komabe, kungothaŵa choipa sikokwanira. Timoteo anachichizidwanso ‘kutsata chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere.’ Zimenezi zimasonyeza kufunika kwa kuchita mwamphamvu. Mofananamo mneneri Hoseya anapempha mtundu wa Israyeli wosakhulupirika kuti: “Tiyeni, tibwerere kumka kwa Yehova . . . tilondole kudziŵa Yehova.” (Hoseya 6:1-3) Kodi inuyo mukuchita kulondola kotero? Kumaphatikizapo zambiri kuposa kungopezeka pamisonkhano ndi kutsagana ndi makolo muutumiki wakumunda. Mkazi wina Wachikristu anavomereza kuti: “Makolo anga anandilerera m’chowonadi, ndipo ndinabatizidwa ndikali wachichepere. . . . Sindinaphonye msonkhano kaŵirikaŵiri ndipo sindinaphonye konse muutumiki, koma sindinakulitse konse unansi wathithithi ndi Yehova.”
14 Msungwana wachichepere wina akuvomereza kuti nayenso analephera kudziŵa Yehova monga Bwenzi ndi Atate, akumamlingalira kukhala Mzimu chabe. Iye anagwera m’chisembwere nabala mwana wapathengo ali ndi zaka 18. Musapange cholakwa chofananacho! ‘Londolani kudziŵa Yehova,’ monga momwe Hoseya analimbikitsira. Mwapemphero ndi kuyenda ndi Yehova tsiku lililonse, mungampange bwenzi lanu louza zamtseri zanu. (Yerekezerani ndi Mika 6:8; Yeremiya 3:4.) “Sakhala patali ndi yense wa ife” ngati timfunafuna. (Machitidwe 17:27) Chotero programu yokhazikika yaphunziro laumwini Labaibulo njofunika. Ndandanda imeneyo siifunikira kukhala yocholoŵana ndi yovuta. “Tsiku lililonse ndimaŵerenga Baibulo kwa mphindi monga 15,” akutero msungwana wina wachichepere wotchedwa Melody. Patulani nthaŵi yakuŵerenga kope lililonse la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Konzekerani misonkhano yampingo kuti mukhoze ‘kufulumiza [ena] kuchikondano ndi ntchito zabwino.’—Ahebri 10:24, 25.
Patsani Makolo Anu Mtima Wanu
15. (a) Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zina kuli kovuta kumvera makolo? (b) Kodi nchifukwa ninji kumvera nthaŵi zonse kumakhala ndi ubwino kwa wachichepere?
15 Makolo owopa Mulungu angakhale magwero achithandizo chenicheni ndi chichilikizo. Koma tawonani mbali imene muyenera kuchita: “Mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wanthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:1-3) Ndithudi, inu mukusinkhuka ndipo mwachiwonekere mufuna ufulu wowonjezereka. Mungakhalenso mukudziŵa mowonjezereka zolephera za makolo anu. “Makolo athu aumunthu,” anavomereza mtumwi Paulo, “anachita zimene anaganiza kukhala zabwino koposa.” (Ahebri 12:10, The Jerusalem Bible) Komabe, m’kupita kwanthaŵi, kumakhalabe kokupindulitsani kuwamvera. Makolo anu amakukondani ndipo amakudziŵani bwino kuposa wina aliyense. Ngakhale kuti sinthaŵi zonse pamene mungavomerezane nawo, iwo kaŵirikaŵiri amakhala akukufunirani zabwino koposa. Kodi nkutsutsiranji zoyesayesa zawo zofuna kukulerani “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW]”? (Aefeso 6:4) Ndithudi, chitsiru chokha nchimene ‘chimapeputsa mwambo wa atate wake.’ (Miyambo 15:5) Wachichepere wanzeru adzazindikira ulamuliro wa makolo ake ndi kusonyeza ulemu woyenerera.—Miyambo 1:8.
16. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kopanda nzeru kwa achichepere kubisa mavuto kwa makolo awo? (b) Kodi achichepere angachitenji kuti awongolere kulankhulana ndi makolo awo?
16 Zimenezo zikaphatikizapo kulankhula chowonadi kwa makolo anu, kuwauza ngati muli ndi mavuto, monga ngati kukhala ndi zikaikiro ponena za chowonadi kapena kugwera m’makhalidwe okaikirika. (Aefeso 4:25) Kubisira makolo anu mikhalidwe yovutitsa maganizo yotero kumangokulitsa mavuto. (Salmo 26:4) Zowona, makolo ena samayesayesa kwambiri kuchititsa kuti pakhale kulankhulana. “Amayi samakhala konse pansi kukambirana nane nkhani,” anadandaula msungwana wina wachichepere. “Ndimalephera kulimba mtima kuti ndinene zimene ndiganiza chifukwa chakuwopa kuti amayi adzandikalipira.” Ngati muli mumkhalidwe wofananawo, mwanzeru sankhani nthaŵi yoyenerera yoti muuze makolo anu mmene mumverera. “Mwananga, undipatse mtima wako,” ikulimbikitsa motero Miyambo 23:26. Yesani kukambitsirana nawo nkhaŵa zanu nthaŵi zonse, mavuto aakulu asanabuke.
Pitirizani Kulondola Chilungamo!
17, 18. Kodi nchiyani chingathandize wachichepere kupitiriza kulondola kwake chilungamo?
17 Chakumapeto kwa kalata yake yachiŵiri, Paulo analangiza Timoteo kuti: “Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo.” (2 Timoteo 3:14) Muyenera kuchita mofananamo. Musalole aliyense kapena chinthu chilichonse kukukopani kuchoka pakulondola chilungamo. Dziko la Satana —ndi zokopa zake zonse—nlodzala ndi kuipa. Posachedwapa ilo ndi onse amene ali mbali yake adzawonongedwa. (Salmo 92:7) Khalani otsimikiza mtima kuti simudzasesedwera limodzi ndi gulu la Satana.
18 Chotero, muyenera kupenda mosalekeza zonulirapo zanu, zikhumbo, ndi zikondwerero. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimasunga miyezo yapamwamba yakulankhula ndi makhalidwe pamene makolo anga ndi ziŵalo zampingo sizikundiwona? Kodi ndimasankha mabwenzi otani? Kodi amsinkhu wanga akudziko amandisankhira zovala ndi kapesedwe? Kodi nzonulirapo zotani zimene ndadziikira? Kodi mtima wanga wasumika pautumiki wanthaŵi zonse—kapena pantchito yodzisankhira m’dongosolo la zinthu la Satana likufali?’
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji wachichepere sayenera kuwopsezedwa ndi zofuna za Yehova? (b) Kodi achichepere angapindule ndi zogaŵira zotani?
19 Mwinamwake mumawona kufunika kwakupanga masinthidwe m’kuganiza kwanu. (2 Akorinto 13:11) Musawope. Kumbukirani kuti Yehova samayembekezera zoposa zimene mungathe kuchita. Mneneri Mika anafunsa kuti: “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” (Mika 6:8) Zimenezi sizidzakhala zovuta kwambiri ngati mugwiritsira ntchito zimene Yehova wagaŵira kuti zikuthandizeni. Yandikirani kwa makolo anu. Nthaŵi zonse yanjanani ndi mpingo Wachikristu. Makamaka, yesayesani kudziŵa akulu mumpingo. Iwo amasamala za ubwino wanu ndipo angakhale magwero achichilikizo ndi chitonthozo. (Yesaya 32:2) Koposa zonse, kulitsani unansi wathithithi ndi waubwenzi ndi Yehova Mulungu. Iye adzakupatsani nyonga ndi chikhumbo chakulondola cholungama!
20 Komabe, achichepere ena amawononga zoyesayesa zawo zakukula kwauzimu mwakumvetsera nyimbo zosayenera. Nkhani yotsatira idzapenda nkhaniyi mosamalitsa.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu Lachigiriki lakuti “kuthaŵa” lagwiritsidwanso ntchito pa Mateyu 2:13, pamene Mariya ndi Yosefe anauzidwa ‘kuthaŵira ku Igupto’ kuthaŵa chiŵembu chambanda cha Herode.—Yerekezerani ndi Mateyu 10:23.
b Mudzapeza malingaliro angapo othandiza kulamulira chikhumbo chakugonana m’mutu 26 wa buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji achichepere makamaka ndiwo ali pangozi ya “machenjero” a Satana?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuyanjana kwambiri ndi achichepere akudziko kuli kwangozi?
◻ Kodi ndimotani mmene mungathaŵire chisembwere?
◻ Kodi mungalondole motani unansi wathithithi ndi Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kulankhulana ndi makolo anu?
[Chithunzi patsamba 16]
Aŵiri otomerana amadziŵana mwanjira yanzeru pazochitika zonga maseŵera, zimene sizimawabisa kwa anthu ena