Ŵetani Gulu la Nkhosa la Mulungu Mofunitsitsa
“Ŵetani gulu [la nkhosa] la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma [mofunitsitsa, NW].”—1 PETRO 5:2.
1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera akulu Achikristu ‘kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu mofunitsitsa’?
YEHOVA amaŵeta anthu ake mofunitsitsa. (Salmo 23:1-4) “Mbusa wabwino,” Yesu Kristu, mofunitsitsa anapereka moyo wake wangwiro kaamba ka anthu onga nkhosa. (Yohane 10:11-15) Motero, mtumwi Petro anafulumiza akulu Achikristu ‘kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu mofunitsitsa.’—1 Petro 5:2.
2. Kodi ndimafunso otani amene ayenera kulingaliridwa ponena za ntchito zakuŵeta za akulu Achikristu?
2 Kufunitsitsa kuli chizindikiro cha atumiki a Mulungu. (Salmo 110:3) Koma kuti aikidwe monga woyang’anira kapena mbusa wamng’ono, pamafunikira zoposa kufunitsitsa kwa mwamuna Wachikristu. Kodi ndani amene amayeneretsedwa kukhala abusa oterowo? Kodi kuŵeta kwawo kumaloŵetsamo chiyani? Kodi ndimotani mmene kungachitidwire bwino koposa?
Kutsogoza Banja
3. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti njira imene mwamuna Wachikristu amasamalira banja lake imayambukira kuyeneretsedwa kwake monga mbusa mumpingo?
3 Mwamuna asanaikidwe pa “udindo wa woyang’anira,” ayenera kufitsa ziyeneretso Zamalemba. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Choyamba, mtumwi Paulo anati woyang’anira ayenera kukhala “mwamuna wotsogoza banja lake la iye yekha mumkhalidwe wabwino, wokhala ndi ana ogonjera limodzi ndi kulingalira konse.” Pali chifukwa chabwino cha zimenezi, pakuti Paulo anati: “Ngati ndithudi mwamuna aliyense sadziŵa kutsogoza banja lake la iye yekha, kodi iye adzasamalira bwanji mpingo wa Mulungu?” (1 Timoteo 3:4, 5, NW) Poika amuna akulu m’mipingo ya pachisumbu cha Krete, Tito anauzidwa kufuna “munthu aliyense wopanda chinenezo, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala ndi ana okhulupirira amene sananenezedwe kuipa kapena kusalamulirika.” (Tito 1:6, NW) Inde, njira imene mwamuna Wachikristu amasamalira banja lake iyenera kulingaliridwa pofuna kudziŵa ngati iye akuyeneretsedwa kusenza thayo lolemerapolo la kuŵeta mpingo.
4. Kuwonjezera pakukhala ndi phunziro Labaibulo lokhazikika ndi pemphero, kodi ndimotani mmene makolo Achikristu amasonyezera chikondi kumabanja awo?
4 Amuna amene amatsogoza mabanja awo mumkhalidwe wabwino amachita zoposa kungopemphera ndi kuphunzira Baibulo limodzi ndi mabanja awo mokhazikika. Iwo amakhala okonzekera nthaŵi zonse kuthandiza okondedwa awo. Kwa awo amene amakhala makolo, zimenezi zimayamba patsiku limene mwana wabadwa. Makolo Achikristu amadziŵa kuti pamene amamatira kwambiri panjira yaumulungu ya kachitidwe ka zinthu, mpamenenso mwanayo adzalondola mwamsanga m’ndandanda yawo ya zochita Zachikristu m’moyo wa tsiku ndi tsiku. Kutsogoza kwabwino kwa atate Wachikristu m’mikhalidwe imeneyi, kumasonyeza kuyenerera kwake monga mkulu.—Aefeso 5:15, 16; Afilipi 3:16.
5. Kodi ndimotani mmene atate Wachikristu angalelere ana ake “m’chilangizo ndi kutsogoza maganizo kwa Yehova”?
5 Potsogoza banja lake, atate Wachikristu wa chikumbumtima chabwino amalabadira uphungu wa Paulo wakuti: “Musakwiyitse ana anu, komatu pitirizani kuwalera m’chilangizo ndi kutsogoza maganizo kwa Yehova.” (Aefeso 6:4, NW) Phunziro Labaibulo labanja lokhazikika, lophatikizapo mkazi ndi ana omwe, limapereka mipata yabwino yoperekera chilangizo chachikondi. Motero ana amalandira “chilangizo,” kapena chiphunzitso chowawongolera. “Kutsogoza maganizo” kumene kumachitika kumathandiza mwana aliyense kufika pakudziŵa mmene Yehova amawonera zinthu. (Deuteronomo 4:9; 6:6, 7; Miyambo 3:11; 22:6) Ali mumkhalidwe womasuka wa kusonkhana pamodzi kwauzimu kumeneku, atate wosamala amamvetsera mosamalitsa pamene ana ake akulankhula. Mafunso otsogolera ku yankho ndi okoma mtima amafunsidwa kutheketsa anawo kukamba mowona mtima zakukhosi ponena za nkhaŵa ndi maganizo awo. Atate sayenera kulingalira kuti amadziŵa zonse za m’maganizo osakhwima a ana awo. Indedi, “wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi,” pamatero pa Miyambo 18:13. Lerolino, makolo ambiri amapeza kuti mikhalidwe imene ana awo amayang’anizana nayo imasiyana kwambiri ndi imene iwo anakumana nayo pamene anali achichepere. Chifukwa chake, atate adzayesayesa kudziŵa bwino mkhalidwewo ndi zoloŵetsedwamo za vutolo asananene mmene ayenera kuchitira nalo.—Yerekezerani ndi Yakobo 1:19.
6. Kodi nchifukwa ninji atate Wachikristu ayenera kufufuza Mawu a Mulungu pothandiza banja lake?
6 Kodi chimachitika nchiyani pamene mavuto, nkhaŵa, ndi maganizo a ana anu adziŵika? Atate amene amatsogoza mumkhalidwe wabwino amasanthula Malemba, amene ‘apindulitsa pachiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’ Amaphunzitsa ana ake mmene angagwiritsirire ntchito zitsogozo zouziridwa za m’Baibulo. Mwanjira imeneyi, achichepere m’zaka amenewo amakhala ‘okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Timoteo 3:16, 17; Salmo 78:1-4.
7. Kodi nchitsanzo chotani chimene atate Achikristu ayenera kupereka ponena za pemphero?
7 Achichepere aumulungu amayang’anizana ndi nthaŵi zovuta kwa anzawo akusukulu akudziko. Chotero kodi ndimotani mmene atate Achikristu angachotsere mantha kwa ana awo? Imodzi ya njirazo ndiyo kupemphera nawo nthaŵi zonse ndi kuwapempherera. Pamene achichepereŵa ayang’anizana ndi mikhalidwe yopereka chiyeso, mwachiwonekere adzatsanzira chidaliro cha makolo awo pa Mulungu. Mtsikana wina wa zaka 13, atafunsidwa asanabatizidwe kusonyeza kudzipatulira kwake kwa Mulungu, anati anali kunyodoledwa ndi kuchitiridwa nkhanza ndi anzake apasukulu. Pamene anachirikiza chikhulupiriro chake chozikidwa pa Baibulo cha kupatulika kwa mwazi, atsikana ena anamkantha ndi kumlavulira. (Machitidwe 15:28, 29) Kodi iye anabwezera? Iyayi. “Ndinapitirizabe kupemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wabata,” iye anatero. “Ndinakumbukiranso zimene makolo anga anandiuza paphunziro lathu labanja ponena za kufunika kwa kudziletsa pamene tiyang’anizana ndi choipa.”—2 Timoteo 2:24.
8. Kodi ndimotani mmene mkulu wopanda ana angatsogolere banja lake mumkhalidwe wabwino?
8 Mkulu amene alibe ana nayenso angapereke zogaŵira zokwanira zauzimu ndi zakuthupi kwa awo okhala m’banja lake. Zimenezi zimaphatikizapo mnzake wamuukwati ndipo mwinamwake achibale ena Achikristu okhala m’nyumba yake. (1 Timoteo 5:8) Motero kutsogoza banja mumkhalidwe wabwino kuli chimodzi cha ziyeneretso zimene mwamuna woikidwa kusenza thayo monga mkulu mumpingo ayenera kuzifitsa. Pamenepo, kodi ndimotani mmene akulu oikidwa ayenera kuwonera mwaŵi wawo wa mathayo mumpingo?
Tsogozani ‘Mowona Mtimadi’
9. Kodi ndimkhalidwe wamaganizo wotani umene akulu Achikristu ayenera kukhala nawo kulinga kumagawo awo autumiki?
9 M’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu, mtumwi Paulo anatumikira monga mdindo m’nyumba ya Mulungu, mpingo Wachikristu pansi pa umutu wa Kristu. (Aefeso 3:2, 7; 4:15) Nayenso Paulo, anafulumiza okhulupirira anzake m’Roma kuti: “Pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chopatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; kapena yakutumikira, tidzipereke kuutumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugwira achite ndi mtima wowona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.”—Aroma 12:6-8.
10. Posamalira gulu la nkhosa za Mulungu, kodi nchitsanzo chotani chimene Paulo anapereka kwa akulu a m’tsiku lathu?
10 Paulo anakumbutsa Atesalonika kuti: “Tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu muloŵe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.” (1 Atesalonika 1:1; 2:11, 12) Chilimbikitsocho chinaperekedwa mwanjira yachifundo, kotero kuti Paulo analemba kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Mogwirizana ndi chitsanzo chautate cha Paulo, akulu okhulupirika ali ndi chisamaliro chozama kaamba ka onse mumpingo.
11. Kodi ndimotani mmene akulu oikidwa angasonyezere changu?
11 Chifundo, limodzi ndi changu, ziyenera kuwoneka m’kuyang’anira kwachikondi kumene abusa Achikristu okhulupirika amakuchita. Kachitidwe kawo ka zinthu kamasonyeza zambiri. Petro akulangiza akulu kuŵeta nkhosa za Mulungu “osati mokangamiza” kapena “[ku]tsata phindu lonyansa.” (1 Petro 5:2) Pamfundo imeneyi, sikolala William Barclay anapereka chenjezo, akumalemba kuti: “Pali njira yolandirira udindo ndi yochitira utumiki monga ngati kuti inali ntchito yochititsa chisoni ndi yosasangalatsa, monga ngati kuti inali yotopetsa, monga ngati inali yothodwetsa yosakhumbika. Nkotheka kwa munthu kupemphedwa kuchita chinthu china, ndi kuti iye achite, koma iye nkuchichita mwanjira yosakondweretsa kotero kuti ntchito yonseyo ingowonongeka. . . . Koma [Petro] akunena kuti Mkristu aliyense ayenera kukhala wachangu ndi chinthenthe kuchita utumiki woterowo monga mmene angakhozere, ngakhale kuti akudziŵa bwino lomwe mmene saliri kanthu pochita zimenezo.”
Abusa Ofunitsitsa
12. Kodi akulu Achikristu angasonyeze motani changu?
12 “Ŵetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, . . . mofunitsitsa,” akufulumizanso motero Petro. Woyang’anira Wachikristu amene amasamala nkhosa amatero mofunitsitsa, mwachifuniro chake, pansi pa chitsogozo cha Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Kutumikira mofunitsitsa kumatanthauzanso kuti mbusa Wachikristu ayenera kugonjera kuulamuliro wa Yehova, ‘mbusa ndi woyang’anira wa miyoyo yathu.’ (1 Petro 2:25) Mbusa Wachikristu wamng’ono mofunitsitsa amasonyeza ulemu kumakonzedwe ateokratiki. Iye amatero pamene atsogolera awo ofunafuna uphungu m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ngakhale kuti chidziŵitso cha nthaŵi yaitali chimathandiza mkulu kukhala ndi nkhokwe ya uphungu wozikidwa pa Baibulo, zimenezi sizitanthauza kuti iye pomwepo akhoza kukhala ndi yankho la m’Malemba pavuto lirilonse. Ngakhale ngati akudziŵa yankho la funso, iye ndi wofunsayo, angakuwone kukhala kwanzeru kufufuza Watch Tower Publications Index kapena maindekisi ena. Motero iye amaphunzitsa mwanjira ziŵiri: Amasonyeza mmene munthu angapezere chidziŵitso chothandiza ndi kusonyeza ulemu kwa Yehova modzichepetsa mwakutsogolera maganizo a winayo ku zimene gulu la Mulungu lafalitsa.
13. Kodi ndinjira zotani zimene akulu angatsatire kuti apereke uphungu wolama?
13 Kodi mkulu angachitenji ngati palibe chimene chinafalitsidwa m’mabuku a Sosaite pavuto lakutilakuti limene liripo? Mosakayikira, iye adzapempherera chidziŵitso ndipo adzafunafuna malamulo amkhalidwe ena a Baibulo amene angagwirenso ntchito pankhaniyo. Iye angakupezenso kukhala kopindulitsa kupereka lingaliro lakuti munthu wofuna chithandizoyo alingalire chitsanzo cha Yesu. Mkuluyo angafunse kuti: “Kukanakhala kuti Yesu, Mphunzitsi Wamkuluyo, ndiye anali mumkhalidwe wanu, kodi muganiza kuti akanachitanji?” (1 Akorinto 2:16) Kulingalira koteroko kungathandize wofunsayo kupanga chosankha chanzeru. Koma kukakhala kopanda nzeru chotani nanga kwa mkulu kungopereka malingaliro ake chabe monga ngati kuti ndiuphungu wa m’Malemba! Mmalomwake, akulu angakambitsirane mavuto aakulu wina ndi mnzake. Iwo angaperekedi nkhani zofunika kwambiri pakukumana kwa bungwe la akulu kuti akambitsirane. (Miyambo 11:14) Zosankha zochitika pemenepo zidzakhozetsa onse kunena mogwirizana.—1 Akorinto 1:10.
Kufatsa Nkofunika
14, 15. Kodi chofunika nchiyani kwa akulu pamene akuwongolera Mkristu amene ‘agwidwa nako kulakwa’?
14 Mkulu Wachikristu ayenera kusonyeza chifatso pophunzitsa ena, makamaka powapatsa uphungu. “Abale,” akulangiza motero Paulo, “ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mumzimu wa chifatso.” (Agalatiya 6:1) Mokondweretsa, liwu Lachigiriki panopa lotembenuzidwa ‘kubweza’ limasonya ku liwu lazakuchiritsa logwiritsiridwa ntchito kulongosola kukonza bwino fupa kuti munthuyo asapunduke kwa moyo wake wonse. Wolemba dikishonale W. E. Vine akugwirizanitsa zimenezi ndi kubwezeretsa “kochitidwa ndi awo amene ali auzimu, kwa munthu wotengedwa ndi tchimo, wokhala ngati chiŵalo choguluka cha thupi lauzimu.” Matembenuzidwe ena amati, “kubwezeretsa m’malo oyenera; kuika m’njira yoyenera.”
15 Kuti munthu awongolere kuganiza kwake sikuli kopepuka, ndipo kungakhale kovuta kwambiri kuika malingaliro a munthu wochimwa m’njira yoyenera. Koma chithandizo chopatsidwa mumzimu wachifatso mwachiwonekere chingalandiridwe ndi chiyamikiro. Chifukwa chake, akulu Achikristu ayenera kulabadira uphungu wa Paulo wakuti: ‘Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.’ (Akolose 3:12) Kodi akulu ayenera kuchitanji pamene munthu wofuna kuwongoleredwa ali ndi mkhalidwe woipa wamaganizo? Ayenera ‘kutsata . . . chifatso.’—1 Timoteo 6:11.
Kuŵeta Mochenjera
16, 17. Kodi akulu ayenera kuchenjera ndi ngozi zotani popereka uphungu kwa ena?
16 Uphungu wa Paulo pa Agalatiya 6:1 uli nzambiri. Iye akufulumiza amuna oyeneretsedwa mwauzimu kuti: “Mubweze [wochimwayo] mumzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.” Nzotsatirapo zowopsa chotani nanga zimene zingakhalepo ngati uphungu umenewu sutsatiridwa! Posonkhezeredwa ndi malipoti onena za mtsogoleri wachipembedzo wa tchalitchi cha Angilikani akuti anachita chigololo ndi avirigo aŵiri, magazini a The Times a ku London anati umenewu “ndimkhalidwe wosayembekezereka: wakuti wopereka uphungu, mwamuna wosonyeza utate kapena ubale agonja kuchiyeso nachimwa ndi munthu amene iye akumpatsa uphungu.” Ndiyeno wolemba m’danga anasonya ku zonena za Dr. Peter Rutter kuti “zochitika zolima munthu pamsana pakati pa ofuna chithandizo ndi owathandiza awo achimuna—madokotala, maloya, ansembe ndi akulu antchito—zinakhala, m’chitaganya chathu chololera chisembwere, mliri wosavomerezeka, wopweteka ndi wonyazitsa.”
17 Sitiyenera kulingalira kuti anthu a Yehova sakhoza kugonjetsedwa ndi ziyeso zimenezi. Mkulu wina wolemekezeka amene anatumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri anagwera m’chisembwere chifukwa chakuti anapanga ulendo wokaŵeta kwa mlongo wina wokwatiwa pamene mlongoyo anali yekha. Ngakhale kuti mbaleyo analapa, anatayikiridwa ndi mathayo ake onse. (1 Akorinto 10:12) Pamenepo, kodi ndimotani mmene akulu oikidwa angapangire maulendo okaŵeta mwanjira imene singawagwetsere m’chiyeso? Kodi angalinganize motani kukhala ndi mlingo wa mkhalidwe wa mtseri, kaamba ka pemphero, ndi mpata wakuti asanthule m’Mawu a Mulungu ndi mabuku Achikristu?
18. (a) Kodi kugwiritsira ntchito lamulo laumutu kungathandize motani akulu kupeŵa mikhalidwe yochititsa kulolera molakwa? (b) Kodi ndimakonzedwe otani amene angapangidwe popanga ulendo wokaŵeta kwa mlongo?
18 Mfundo ina imene akulu ayenera kuilingalira ndiyo lamulo laumutu. (1 Akorinto 11:3) Ngati wachichepere akufuna chitsogozo, yesani kuphatikizamo makolo ake m’kukambitsiranako pamene kuli koyenera. Pamene mlongo wokwatiwa apempha chithandizo chauzimu, kodi mungalinganize kuti mwamuna wake akakhalepo pakuwonanako? Koma bwanji ngati zimenezi ziri zosatheka kapena ngati mwamunayo ali wosakhulupirira amene wakhala akuchitira nkhanza mlongoyo mwanjira yakutiyakuti? Pamenepo pangani makonzedwe ofanana ndi amene mukanachita paulendo wokaŵeta kwa mlongo wosakwatiwa. Kukakhala kwanzeru kuti abale aŵiri oyeneretsedwa mwauzimu akachezere mlongoyo. Ngati zimenezi siziri zoyenera, mwinamwake mungasankhe nthaŵi yoyenera yakuti abale aŵiri akakambitsirane naye pa Nyumba Yaufumu, makamaka m’chipinda cholola mkhalidwe wamtseri. Pokhala ndi abale ena ndi alongo alimo m’holomo, ngakhale kuti sakuwona ndi kumva zimene akukambitsirana, mwachiwonekere adzapeŵa chokhumudwitsa chilichonse.—Afilipi 1:9, 10.
19. Kodi kuŵeta nkhosa za Mulungu mofunitsitsa kumadzetsa zotulukapo zabwino zotani, ndipo nkwayani kumene timasonyeza chiyamikiro chathu pokhala ndi abusa ofunitsitsa?
19 Kuŵeta nkhosa za Mulungu mofunitsitsa kumadzetsa zotulukapo zabwino—gulu la nkhosa lolimba lauzimu, ndi lotsogozedwa bwino. Mofanana ndi mtumwi Paulo, akulu Achikristu a m’tsiku lathu amasamala kwambiri za okhulupirira anzawo. (2 Akorinto 11:28) M’nthaŵi zino zovuta, thayo lakuŵeta anthu a Mulungu nlolemera kwambiri. Chifukwa chake, tili oyamikira kwenikweni ntchito yabwino imene abale athu otumikira monga akulu akuichita. (1 Timoteo 5:17) Potidalitsa ndi “mphatso mwa amuna” amene amaŵeta mofunitsitsa, tikupereka chitamando kwa Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro,” Mbusa wathu wachikondi wakumwamba, Yehova—Aefeso 4:8, NW; Yakobo 1:17.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene mwamuna angatsogozere banja lake mumkhalidwe wabwino?
◻ Kodi uyang’aniro wa akulu Achikristu uyenera kusonyeza mikhalidwe yotani?
◻ Kodi ndimotani mmene akulu angasonyezere kudzichepetsa ndi kufatsa popereka uphungu?
◻ Kodi nchiyani chimathandiza kuchititsa kulungamitsa kwauzimu kukhala kogwira mtima?
◻ Kodi ndimotani mmene akulu angapeŵere mikhalidwe yochititsa kulolera molakwa poŵeta gulu la nkhosa?
[Chithunzi patsamba 18]
Mkulu Wachikristu ayenera kutsogoza banja lake mukhalidwe wabwino
[Chithunzi patsamba 21]
Ubusa Wachikristu uyenera kuchitidwa ndi chifatso ndi kulingalira kolama