Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI SHARON GASKINS
PARADAISO padziko lapansi! Ndinadziyerekezera ndikuseŵera m’dambo, kuthamangitsa agulugufe, kuseŵera ndi ana a mkango. Zinamveka zosangalatsa kwambiri! Koma ndinali ndi zikaikiro. Kaŵirikaŵiri chiyembekezo changa chinathera m’kutaya mtima!
Kuyambira kale kwambiri, mpando wamagudumu ndiwo unakhala bwenzi langa lanthaŵi zonse. Kuyambira pamene ndinabadwa, matenda aubongo otchedwa cerebral palsy anandisoŵetsa chisangalalo chapaubwana. Ana ena ankaseŵera mosangalala pachipale chofeŵa ndi panjinga, koma ine ndinakhala ndekha, ndinalephera nkuyenda komwe. Chotero pamene Amayi anapita nane kwa ochiritsa ndi chikhulupiriro osiyanasiyana, tinayembekezera ndi mtima wonse kuwona chozizwitsa. Komabe, nthaŵi zonse tinabwerera kunyumba popanda thandizo. Zinandikhumudwitsa, koma zinali zopweteka chotani nanga kwa amayi!
Polakalaka chiyembekezo chenicheni, amayi anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kuchiyambi kwa 1964. Panthaŵiyo ndinali ndi zaka zakubadwa zisanu ndi chimodzi ndi theka.
Kunali kusangalatsa kuphunzira kuti panthaŵi ina padziko lapansili padali paradaiso wokongola. Momvetsa chisoni, munthu woyambayo, Adamu, anataya paradaiso ameneyo, koma ineyo ndinalakalaka kukhala ndi unansi wathithithi ndi Mulungu umene iyeyo adali nawo poyambapo. Kodi kukanakhala kotani kukhala ndi unansi ndi Mulungu? Kapena kukhala ndi moyo pamene Mwana wake weniweniyo anali padziko lapansi? Maloto angawo anandiperekanso ku Paradaiso wamtsogolo. Ngakhale pamsinkhu waung’ono umenewo, zinali zomvekera kwa ine kuti tinapeza chowonadi.
Amayi anayamba kutitenga monga banja kupita ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova. Misonkhano yawo inali yosiyana kwambiri ndi zimene tinawona m’matchalitchi! Anthuwo ndi malowo anakhudza kwambiri mtima wanga.
Amayi anali kuvutika popita nafe ku Nyumba Yaufumu. Kuwonjezera pa ine, panali ana ena atatu aang’ono, ndipo tinalibe galimoto. Akakhala ndi ndalama tinkakwera takisi. Ndimakumbukirabe mmene iwo anavutikira Sande lina. Sikunabwere takisi iliyonse. Ndiyeno mwadzidzidzi, panafika munthu wina ndi galimoto lake natitengako. Tinachedwa kufika kumsonkhanoko, koma tinafikabe. Tinayamika Yehova motani nanga!
Pasanapite nthaŵi yaitali, abale ndi alongo athu auzimu okondedwa amene anali ndi galimoto mwachikondi anayamba kusinthana kumatitenga. Chilimbikitso cha amayi chakuti sitiyenera kuphonya misonkhano kusiyapo ngati tadwala kwenikweni chinakhomereza m’maganizo mwanga kufunika kwa ‘kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Ahebri 10:24, 25) Atasonkhezeredwa ndi zimene anaphunzira, amayi anapatulira moyo wawo kwa Yehova ndipo anabatizidwa mu 1965.
Panthaŵiyo ndinali wamkulu wokhoza kumvetsera bwino lomwe pamisonkhano. Mumpingo wa Cypress Hills ku Brooklyn, New York, munali Azungu, anthu akuda, a Hispanic, ndi anthu ena akumalambirira pamodzi. Zinawoneka kukhala zabwino kuti anthu owopa Mulungu ayenera kukhala paubale weniweni woterowo.—Salmo 133:1.
Amayi anandiphunzitsa kukonzekera misonkhano. Zimenezi sizinandivute m’maganizo, koma zinali zovuta kwambiri kuzichita. Nthenda ya cerebral palsy imachititsa zinthu zosavuta kukhala zovuta kuzichita. Kunali kosatheka, ndipo nkosathekabe kuti ndilembe mzera wowongoka kuchonga yankho m’mabuku athu ofotokoza Baibulo. Komabe, mwakuyesayesa, kulemba mizera kwanga kunawongokera.
M’maganizo mwanga munali zinthu zambiri zoti ndinene. Koma polankhula, mawuwo anatuluka mwachibwibwi. Kupumula kunali kofunika kwambiri kotero kuti minofu yanga imasuke. Ndinafunikiranso kusumika maganizo pakutchula liwu lililonse momvekera bwino monga momwe ndikanathera. Zinali kundikwiyitsa ngati sindinanene bwino ndemanga yanga kapena nditadziŵa kuti anthuwo sanamvetsetse mawu angawo. Komabe, pamene iwo anandidziŵa, abale ndi alongo a mumpingomo anayamba kumva bwino mawu anga. Komabe, nthaŵi zina ndimasaukabe ndi vuto limeneli.
Miyezi Isanu ndi Umodzi Yokwiitsa
Pamsinkhu wazaka zisanu ndi zitatu, ndinali ndi chokumana nacho cha miyezi isanu ndi umodzi chimene chandiyambukira mpaka lerolino. Mosasamala kanthu za chithandizo chakulimbitsa thupi, kuphunzitsidwa kugwira ntchito, ndi kulankhula chimene ndinali nditapatsidwa kale, madokotala ananditumiza ku chipatala chophunzitsira opunduka kuchita ntchito zozoloŵereka ku West Haverstraw, New York. Ine ndi amayi tinakhumudwa kwambiri. Zaka zambiri kumbuyoko, pamene madokotala anapenda molakwa kuti ndinali wosokonekera maganizo, amayi anawauza kuti sakandipereka konse kuchipatala cha amisala. Chotero ngakhale kulekana kwakanthaŵi kochepa kunali kovuta kwa iwo. Komabe, anazindikira kuti ngati nditi ndidzakhale ndi moyo wopindulitsa popanda kudalira pa iwo kapena atate zinatanthauza kuti ndiyenera kukhala wokhoza kuchita ndekha zinthu monga momwe ndingathere.
Chipatalacho chinali chabwino, koma ndinamva kukhala wonyanyalidwa. Kuliralira ndi kukwiyakwiya kunasonyeza mmene ndinawonera malowo. Makolo anga sankatha kubwera kaŵirikaŵiri paulendo wa pa basi wamaola atatuwo, makamaka chifukwa chakuti Amayi anali ndi pakati pa mwana wawo wachisanu. Pamene anali kuchoka, ndinali kukwiya kwambiri kotero kuti dokotalayo ananena kuti sayenera kumabwera kaŵirikaŵiri. Ndinaloledwa kupita kunyumba kaŵiri kokha.
Akatswiriwo anandiphunzitsa kuyenda ndi ndodo zokhala ndi mtovu wolemera. Zinawoneka kukhala zolemera kwambiri. Komabe, kulemerako kunandichilikiza ndi kunditetezera kuti ndisagwe. Imeneyi inali njira yoyamba ya kuphunzira kuyenda ndekha osagwiritsira ntchito ndodo.
Kucheka chakudya, kumanga mabatani—ntchito iliyonse yofunikira kugwiritsira ntchito zala—inali yovuta ndipo yosatheka kwa ine. Koma ndinaphunzira pang’ono kudya ndekha ndi kuvala. Pambuyo pake zimenezi zinandithandiza muutumiki wanga kwa Mulungu.
Pamene ndinamaliza maphunzirowo, ndinabwereranso kunyumba. Amayi anandipatsa ntchito kuti ndizigwiritsira ntchito maluso anga atsopanowo. Zimenezo zinali zosautsa maganizo popeza kuti ngakhale kuti ndinafuna kuchita zinthuzo ndekha, kumaliza ntchitoyo kunali kokwiyitsa, kodya nthaŵi, ndi kotopetsa. Eya, kuvala kokha popita kumisonkhano kunali ntchito ya maola aŵiri!
Pamene tinasamukira kutsidya lina la khwalala lapafupi ndi Nyumba Yaufumu, ndinali kuyenda ndekha. Chimenecho chinali chilakiko chachikulu zedi!
Tsiku Losangalatsa Koposa m’Moyo Wanga
Amayi anatsimikizira kuti banja lathu linali kudya chakudya chauzimu chokwanira. Iwo anaphunzira nane ndipo anandiyembekezera kuŵerenga kope lililonse la magazini athu, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Panali misonkhano yofunikira kukonzekera ndi kufikako. Ngakhale kuti ndinasumika maganizo ndi mtima wanga pachidziŵitso chimenechi, malingaliro amphamvu akupatulira moyo wanga kwa Yehova ndi kusonyeza zimenezi mwa ubatizo wa m’madzi sanabwere m’maganizo. Amayi anandithandiza kuwona kuti mosasamala kanthu za kulemala kwanga, Mulungu anandiŵerengera kukhala ndi thayo langa lauzimu. Sindinayenera kuyembekezera kuloŵa m’dziko latsopano kudalira pa amayi anga.
Ndinamkonda Mulungu, koma mkhalidwewu unandichititsa kukhala wosiyana ndi ena—chinthu chopweteka kwambiri kwa wachichepere. Zinali zovuta kuvomereza kuperewedwa kwanga. Kaŵirikaŵiri ndinali kukwiya, ndipo ndinayenera kuletsa mkhalidwewu ndisanabatizidwe. (Agalatiya 5:19, 20) Ndipo bwanji ngati ndikalephera kukwaniritsa kudzipatulira kwanga kwa Yehova?
Mkulu wa mpingo analankhula nane pamene anapemphedwa ndi amayi anga. Iye anagwira mawu funso la mneneri Eliya kwa Aisrayeli lakuti: “Mukayikakayika kufikira liti?” (1 Mafumu 18:21) Kunena zowona, Yehova sanakondwere ndi kukayikakayika kwanga.
Ndinagalamuka mwauzimu ndi kupempherera mowona mtima chithandizo cha Yehova ndi kutsimikiza mtima kupatulira moyo wanga kwa iye. Mlongo wina wamumpingo anaphunzira nane. Iye anali wamng’ono kwa ine ndipo amayi ake anamwalira iye ali wamng’ono. Komabe, anadzipatulira kwa Mulungu ali wamng’ono.
Pamsinkhu wazaka 17, ndinapanga chosankha. Ndinafuna kutumikira Yehova monga momwe ndingathere. Pa August 9, 1974—pamene ndinabatizidwa—linali tsiku losangalatsa koposa m’moyo wanga.
Kusangalala Muutumiki
Kukhala ndi phande muutumiki kunapereka zopinga zonga mapiri. Vuto lalikulu kwambiri linali kumveketsa zimene ndimanena. Ndinali kuyesayesa kulankhula momvekera bwino monga momwe ndingathere. Komabe, ngati kunali koyenerera, mnzanga wa muutumiki wakumunda anali kubwereza mawu angawo kwa mwininyumbayo. Ena anaipidwa nazo, akumandiwona kukhala ndikuvutitsidwa ndi Mboni. Koma kulalikira kuli kuyenera kwanga ndi chikhumbo changa chamtima wonse.
Kuyenda kupita kukhomo ndi khomo ngakhale m’dadada umodzi wokha kumanditopetsa kotheratu. Nyumba zambiri za m’gawo lathu zili ndi makwerero, amene amachititsa kuti ineyo ndisazifikire. M’nthaŵi yachisanu, makwalala okhala ndi chipale chofeŵawo amachititsa ntchito yakunyumba ndi nyumba kukhala yosatheka konse kwa ine. (Machitidwe 20:20) Komabe, abale anga auzimu andithandiza kwambiri, ndipo Yehova wandidalitsa tsopano ndi mpando wamagudumu wainjini, umene umapangitsa utumiki wanga kukhala wopepukirapo.
M’kupita kwa nthaŵi, ndinayamba kulalikira mwakulemba makalata. Kulemba makalata ndi manja sikukanatheka chifukwa chakuti kalembedwe kanga sikaŵerengeka kwa anthu ambiri. Chotero taipi yamagetsi inakhala cholembera changa. Ndimalemba mochedwa kwambiri chifukwa chakusakhoza bwino kuyendetsa manja. Nthaŵi zambiri, ndimayamba ndaphonya lemba nkumenya lina. Kulemba tsamba limodzi lokha kunganditengere ola limodzi kapena kuposapo.
Mosasamala kanthu za kupanda mphamvu, nthaŵi ndi nthaŵi ndimatumikira monga mpainiya wothandiza, kuthera maola 60 kapena kuposapo muutumiki mwezi uliwonse. Zimenezi zimafunikira ndandanda yabwino, kuyesayesa kowonjezereka, ndi chichilikizo cha okhulupirira anzanga. Mzimu wawo waupainiya umandilimbikitsa. Amayi aperekanso chitsanzo chabwino mwakutumikira monga mpainiya wokhazikika kapena wothandiza ngakhale kuti anali ndi mavuto, kudwaladwala, ndipo anali ndi vuto lakulera ana asanu ndi aŵiri m’banja logaŵikana mwachipembedzo.
Kukhala Ndekha
Pamsinkhu wazaka 24, ndinalingalira zopita kwina kukakhala ndekha. Kusamukira kwanga ku chigawo cha Bensonhurst ku Brooklyn kunatsimikizira kukhala dalitso. Mpingo wa Marlboro unali ngati banja logwirizana kwambiri. Ha, zinali zolimbitsa chikhulupiriro chotani nanga kukhala nawo! Ngakhale kuti mumpingomo munali galimoto ziŵiri kapena zitatu zokha, abale anga auzimu anandipereka kumisonkhano yonse. Komabe sindinakhale kumeneko kwanthaŵi yaitali.
Nditadziwona kukhala wolephereratu, ndinabwerera kunyumba ndipo ndinachita tondovi kwa zaka zitatu. Mkwiyo wanga unabwerera. Ndiyeno kunabwera malingaliro ofuna kudzipha ndi kuyesayesa kudzipha kangapo. Nthaŵi zonse imfa inali kundiwopsa. Koma ndinadalira zolimba pa Mulungu ndi kulonjeza kusonyeza chiyamikiro kaamba ka mphatso yake ya moyo. Ndinalandira chitonthozo ndi uphungu kwa akulu. Zimenezi, limodzi ndi pemphero, phunziro laumwini, kuleza mtima kwa banja langa, ndi chithandizo cha akatswiri, zinawongolera kulingalira kwanga.
Kupyolera mu Nsanja ya Olonda, Yehova anapereka chidziŵitso chothandiza chachikondi chonena za kuchita tondovi. Inde, iye amasamalira anthu ake ndipo amamvetsetsa malingaliro athu. (1 Petro 5:6, 7) M’kupita kwanthaŵi kuchita tondoviko kunatha. Zaka khumi pambuyo pake, Yehova amandithandizabe kulaka kulefuka maganizo ndi kuchita tondovi. Nthaŵi zina malingaliro a kudziwona kukhala wopanda pake amandivutitsa kotheratu. Komabe, pemphero, phunziro la Baibulo, ndi banja langa lauzimu zakhala zinthu zothandiza zabwino kwambiri.
Pambuyo pa kufunafuna nyumba ina kosaphula kanthu, ndinagamula monyong’onyeka kukhala ndi banja langa kwa moyo wanga wonse. Ndiyeno Yehova anayankha mapemphero anga. Malo anapezeka kuchigawo cha Bedford-Stuyvesant ku Brooklyn. Pofika kumapeto kwa chilimwe cha 1984, ndinasamuka, ndipo ndakhala kumeneko mpaka tsopano.
Ziŵalo za mpingo wachikondi wa Lafayette zimandipereka mokoma mtima kumisonkhano. Ndimakumbukirabe Phunziro Labuku Lampingo loyamba kumeneko. Linachitidwira panyumba yosanja yachinayi—ndipo kunalibe chikepe! Ndinakwera ndi kutsika makwerero amenewo ndi chithandizo cha Yehova chokha. M’kupita kwanthaŵi panapezeka malo amene sanali ovuta kwa ine kufikako. Ndipo tsopano Yehova wandidalitsa ndi mwaŵi wokhala ndi Phunziro Labuku Lampingo m’nyumba mwanga.
Mpingo umenewu uli ndi mzimu wabwino kwambiri waupainiya. Pamene ndinafika, kunali apainiya pafupifupi 30, ndipo ena a iwo anandipatsa chisamaliro chapadera. Mkhalidwe wachanguwo unandisonkhezera kuchita upainiya wothandiza kaŵirikaŵiri.
Mu April 1989 mipingo ya Lafayette ndi Pratt inamanga Nyumba Yaufumu yatsopano pafupi ndi nyumba yanga. Zinachitika panthaŵi yoyenera, popeza kuti kuyenda kumavutanso chifukwa cha kukula kwa matenda anga. Pokhala ndi mpando wanga wamagudumu wainjiniwo limodzi ndi chithandizo cha abale ndi alongo auzimu, maulendo opita ndi kuchoka kumisonkhano amakhala osangalatsa. Ndimayamikira chotani nanga chithandizo chachikondi chimenecho!
Kuyamikira Chichilikizo cha Mulungu
Ngakhale kuti miyendo yanga imanjenjemera, mtima wanga ngwolimba. Kuphunzira kunachititsa moyo kukhala bwinopo, komabe Mulungu anandichilikiza. Nthaŵi zina, sindinadziŵe kuti ndikapeza motani chakudya changa chatsikulo, koma Yehova wandichilikiza ndipo wakhala Wogaŵira wokhulupirika. Ndithudi, mawu a Davide awa ngapamtima kwa ine: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.”—Salmo 37:23-25.
Nthaŵi zambiri Yehova anandikhozetsa kusunga kaimidwe Kamalemba mwakukana kulandira mwazi panthaŵi ya opareshoni. (Machitidwe 15:28, 29) Bambo anga anamwalira posachedwapa. Kutaikiridwa munthu wokondedwa chotero kunalidi kosautsa maganizo. Nyonga yochokera kwa Yehova yokha ndiyo yandithandiza kupyola zimenezi ndi ziyeso zina.
Umoyo wanga ungapitirize kunyonyotsoka, koma kukhulupirira kwanga Mulungu ndi unansi wanga ndi iye ndizo zondichilikiza. Ndine wachimwemwe chotani nanga kukhala pakati pa anthu ake ndi kukhala ndi chichilikizo chosalekeza cha Yehova!