Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
“Musanditaye muukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.”—SALMO 71:9.
1. Kodi ndimotani mmene okalamba amachitiridwira m’zitaganya zambiri?
“KUFUFUZA kumasonyeza kuti pafupifupi anthu okalamba asanu ndi mmodzi mwa asanu ndi aŵiri (86%) ochitiridwa nkhanza amavutitsidwa ndi mabanja awo enieni,” inatero The Wall Street Journal. Magazini otchedwa Modern Maturity anati: “Kuchitiridwa nkhanza kwa okalamba kwakhala [chiwawa cha m’banja] chatsopano chovumbulidwa m’manyuzipepala a mu [United States].” Inde, anthu okalamba m’zitaganya zambiri achitiridwa nkhanza kwambiri ndi kunyalanyazidwa. Nthaŵi yathu ino mpamene anthu ambiri ali “odzikonda okha, . . . osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe.”—2 Timoteo 3:1-3.
2. Malinga nkunena kwa Malemba Achihebri, kodi ndimotani mmene Yehova amaonera okalamba?
2 Komabe, mmenemo sindimo mmene okalamba anafunikira kuchitiridwa mu Israyeli wakale. Chilamulo chinati: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuwope Mulungu wako; ine ndine Yehova.” Buku la miyambo yanzeru youziridwa limatilangiza kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” Limalamulira kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” Chilamulo cha Mose chinaphunzitsa kulemekeza ndi kusamalira okalamba onse. Mwachiwonekere, Yehova amakhumba kuti okalamba alemekezedwe.—Levitiko 19:32; Miyambo 1:8; 23:22.
Kusamalira Okalamba m’Nthaŵi za m’Baibulo
3. Kodi ndimotani mmene Yosefe anasonyezera chifundo kwa atate wake okalamba?
3 Ulemu unafunikira kusonyezedwa osati ndi mawu chabe komanso ndi ntchito zachifundo. Yosefe anasonyeza chifundo chachikulu kwa atate wake okalamba. Iye anafuna kuti Yakobo ayende ulendo wochokera ku Kanani kumka ku Igupto, mtunda wa makilomita oposa 300. Chotero Yosefe anatumizira Yakobo “abulu khumi osenza zinthu zabwino za m’Aigupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.” Pamene Yakobo anafika ku Goseni, Yosefe anapita kwa iye kukakumana naye “nagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake.” Yosefe anasonyeza chikondi chachikulu kwa atate wake. Nchitsanzo chosonkhezera mtima chotani nanga chimenechi cha kudera nkhaŵa okalamba!—Genesis 45:23; 46:5, 29.
4. Kodi nchifukwa ninji Rute ali chitsanzo chabwino chochitsatira?
4 Chitsanzo china chabwino kwambiri chotsatira m’kukhala okoma mtima kwa okalamba ndiye Rute. Ngakhale kuti anali Wakunja, anamamatirabe kwa apongozi ake amasiye, Achiyuda okalambawo, Naomi. Iye anasiya anthu a kwawo ndi kulolera mkhalidwe wa kusadzakwatiwanso. Pamene Naomi anamuumiriza kubwerera kwa anthu akwawo, Rute anayankha ndi mawu ena abwino koposa a m’Baibulo akuti: “Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.” (Rute 1:16, 17) Rute anasonyezanso mikhalidwe yabwino pamene anali wofunitsitsa kukwatiwa ndi Boazi wokalamba pansi pa kakonzedwe ka ukwati wa chokolo.—Rute, chaputala 2 mpaka 4.
5. Kodi ndimikhalidwe yotani imene Yesu anasonyeza pochita ndi anthu?
5 Yesu anapereka chitsanzo chofananacho m’kuchita kwake zinthu ndi anthu. Iye anali woleza mtima, wachifundo, wokoma mtima, ndi wodzetsa mpumulo. Anakonda munthu wosauka amene anali wopunduka, wosatha kuyenda, kwa zaka 38 namchiritsa. Anasonyeza chifundo kwa akazi amasiye. (Luka 7:11-15; Yohane 5:1-9) Ngakhale pamene anali kumva ululu wa imfa yake yopweteka pamtengo wozunzirapo, anatsimikizira kuti amake, mwinamwake a zaka za kuchiyambiyambi kwa 50, asamaliridwe. Yesu anali bwenzi labwino kwambiri kwa aliyense, kusiyapo kwa adani ake onyengawo. Motero, iye anali wokhoza kunena kuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”—Mateyu 9:36; 11:28, 29; Yohane 19:25-27.
Kodi Ndani Amene Amayenerera Kulingaliridwa?
6. (a) Kodi ndani amene ali oyenerera chisamaliro chapadera? (b) Kodi ndimafunso otani amene tingadzifunse?
6 Popeza kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ali zitsanzo zabwino zotero ponena za kusamalira, nkoyeneradi kuti Akristu odzipatulira atsanzire njira yawo. Tili ndi ena pakati pathu amene ali othodwa ndi olemetsedwa kwa zaka zambiri—abale ndi alongo okalamba amene afika m’zaka zawo zovuta. Ena angakhale makolo athu kapena agogo athu. Kodi timawaona mwachisawawa? Kodi timawachilikiza? Kapena kodi timayamikira mowona mtima chidziŵitso chawo chachikulu ndi luntha? Zowonadi, ena angayese kuleza mtima kwathu mwa makhalidwe ovuta ndi zizoloŵezi zimene zili zofala paukalamba. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi ine ndikakhala wosiyana nawo motani pansi pa mikhalidwe imeneyo?’
7. Kodi nchiyani chimene chimachitira fanizo la kufunika kwa kumvera chisoni anthu okalamba?
7 Ku Middle East kuli nkhani ina yokhudza mtima yonena za chifundo cha msungwana wina kwa anthu okalamba. Gogo wina anali kuthandiza kugwira ntchito m’khitchini ndipo mwatsoka anagwetsa mbale yadothi niphwanyika. Iye anaipidwa ndi kusachita zinthu kwake mwadongosolo; ndipo mwana wake wamkazi anakwiyitsidwa nazo kwambiri. Pamenepo mwana wake wamkaziyo anaitana kamwana kake kakakazi ndi kukatuma kusitolo kukagulira agogowo mbale ya mtengo. Kamsungwanako kanadza ndi mbale ziŵiri za mtengo. Amake anafunsa kuti: “Kodi waguliranji mbale ziŵiri?” Mdzukuluyo, mowopa, anayankha kuti: “Imodziyo nja agogo ndipo inayo njanu mukadzakalamba.” Inde, m’dziko lino tonsefe tikuyembekezera kukalamba. Kodi sitingayamikire kuchitiridwa moleza mtima ndi mokoma mtima?—Salmo 71:9.
8, 9. (a) Kodi ndimotani mmene tiyenera kuchitira ndi okalamba amene ali pakati pathu? (b) Kodi nchiyani chimene awo amene angokhala kumene Akristu ayenera kukumbukira?
8 Tisaiŵale konse kuti ambiri a abale ndi alongo athu okalamba ali ndi cholembedwa cha nthaŵi yaitali cha ntchito Yachikristu yochitidwa mokhulupirika. Iwo amayenereradi ulemu wathu ndi kuwalingalira, chithandizo chathu chokoma mtima ndi chilimbikitso. Munthu wanzeru molondola anati: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m’njira ya chilungamo.” Ndipo aimvi amenewo, amuna kapena akazi, ayenera kulemekezedwa. Ena a amuna ndi akazi okalamba ameneŵa akutumikirabe monga apainiya okhulupirika, ndipo amuna ambiri akupitirizabe kutumikira mokhulupirika monga akulu m’mipingo; ena amachita ntchito yabwino monga oyang’anira oyendayenda.—Miyambo 16:31.
9 Paulo analangiza Timoteo kuti: “Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale; akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Makamaka awo amene angofika kumene mumpingo Wachikristu kuchokera kudziko lopanda ulemu ayenera kulabadira mawu a Paulo, amene ali ozikidwa pachikondi. Achichepere, musatsanzire mkhalidwe wa maganizo woipa umene mumaona kusukulu. Musaipidwe ndi uphungu wokoma mtima wa Mboni zokalamba. (1 Akorinto 13:4-8; Ahebri 12:5, 6, 11) Komabe, pamene okalamba afunikira chithandizo chifukwa cha matenda kapena kusoŵa ndalama, kodi ndani amene ali ndi thayo lalikulu loŵathandiza?
Mbali ya Banja m’Kusamalira Okalamba
10, 11. (a) Malinga nkunena kwa Baibulo, kodi ndani amene ayenera kutsogolera m’kusamalira okalamba? (b) Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zonse kuli kovuta kusamalira okalamba?
10 Mumpingo woyambirira Wachikristu, munabuka mavuto ponena za kusamalira akazi amasiye. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza motani ponena za kusamalira zosoŵa zimenezi? “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”—1 Timoteo 5:3, 4, 8.
11 M’nthaŵi zosoŵa, ziŵalo zabanja zapafupi ziyenera kukhala zoyambirira kuthandiza okalamba.a Mwanjira imeneyi, ana achikulire angasonyeze chiyamikiro kaamba ka zaka zachikondi, ntchito, ndi chisamaliro zimene makolo awo anapereka. Zimenezitu nzovuta. Pamene anthu akukula, kaŵirikaŵiri amachita zinthu mochedwa, ndipo ena amakhaladi osakhoza kuchita zinthu. Ena angakhale okonda zawo zokha ndi ofuna zambiri, mwinamwake mosazindikira. Koma pamene tinali makanda, kodi nafenso sitinali okonda zathu zokha ndi ofuna zambiri? Ndipo kodi makolo athu sanali ofunitsitsa kutithandiza? Tsopano zinthu zasintha muukalamba wawo. Chotero, kodi nchiyani chimene chikufunika? Chifundo ndi kuleza mtima.—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:7, 8.
12. Kodi ndimikhalidwe yotani imene imafunika posamalira anthu okalamba—ndi ena onse mumpingo Wachikristu?
12 Mtumwi Paulo anapereka uphungu wopindulitsa pamene analemba kuti: “Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” Ngati kuli kwakuti tiyenera kusonyeza mtundu umenewu wa chifundo ndi chikondi mumpingo, kodi sitingasonyezenso kwambiri m’banja?—Akolose 3:12-14.
13. Kodi ndaninso, kupatulapo makolo okalamba kapena agogo, amene angafune chithandizo?
13 Nthaŵi zina mtundu umenewu wa chithandizo ungafunidwe osati kokha ndi makolo kapena agogo komanso ndi anansi ena okalamba. Okalamba ena amene alibe ana atumikira kwa zaka zambiri muutumiki waumishonale, utumiki woyendayenda, ndi m’ntchito zina za nthaŵi yonse. Iwo aika kwenikweni Ufumu pamalo oyamba m’moyo wawo wonse. (Mateyu 6:33) Pamenepo, kodi sikukakhala koyenera kuwasonyeza mzimu wosamalira? Ife ndithudi tili ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha njira imene Watch Tower Society imasamalirira ziŵalo zake zokalamba za pa Beteli. Pamalikulu a Beteli ku Brooklyn ndi panthambi zingapo za Sosaite, abale ndi alongo okalamba amasamaliridwa tsiku ndi tsiku ndi ziŵalo zophunzitsidwa za banjalo zogaŵiridwa ntchito imeneyi. Izo nzachimwemwe kusamalira okalamba ameneŵa monga ngati kuti ndimakolo awo kapena agogo awo enieni. Panthaŵi imodzimodziyo, amaphunzira zambiri kwa okalamba achidziŵitso ameneŵa.—Miyambo 22:17.
Mbali ya Mpingo Powasamalira
14. Kodi ndimakonzedwe otani amene anapangidwa kwa okalamba mumpingo Wachikristu woyambirira?
14 Maiko ambiri lerolino ali ndi madongosolo a ndalama zolandira paukalamba munthu utapuma pantchito ndiponso chisamaliro cha mankhwala choperekedwa ndi Boma kwa okalamba. Akristu akhoza kugwiritsira ntchito makonzedwe ameneŵa pamene ali oyenerera kuchita motero. Komabe, m’zaka za zana loyamba, kunalibe makonzedwe otero. Chifukwa chake, mpingo Wachikristu unalinganiza mchitidwe wa kuthandiza akazi amasiye osauka. Paulo analamulira kuti: “Asaŵerengedwe wamasiye [pa chithandizo cha mpingo] ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.” Motero, Paulo anasonyeza kuti mpingo nawonso uli ndimbali m’kuthandiza okalamba. Akazi amaganizo auzimu amene analibe ana okhulupirira anayenera chithandizo chotero.—1 Timoteo 5:9, 10.
15. Kodi nchifukwa ninji chithandizo chingafunike kuti papezeke thandizo la Boma?
15 Kumene kuli makonzedwe a Boma kaamba ka okalamba, kaŵirikaŵiri zimenezi zimaloŵetsamo ntchito yopeza zikalata imene ingaonekere kukhala yolefulitsa maganizo. M’zochitika zotero nkoyenera kwa oyang’anira mumpingo kulinganiza chithandizo choti chiperekedwe kotero kuti wokalambayo akhoze kufunsira, kukatenga, kapena ngakhale kuwonjezera chithandizo chotero. Nthaŵi zina kusintha m’mikhalidwe kungachititse kuwonjezereka kwa ndalama zopatsidwa utapuma pantchito. Komanso pali zinthu zina zopindulitsa zambiri zimene oyang’anira angalinganize kotero kuti okalamba asamaliridwe. Kodi nziti zimene zili zina za zimenezi?
16, 17. Kodi ndim’njira zosiyanasiyana ziti zimene tingasonyezeremo kuchereza kwa okalamba mumpingo?
16 Kuchereza alendo kuli mwambo umene unayambira kumbuyo m’nthaŵi za m’Baibulo. Kufikira lerolino m’maiko ambiri a ku Middle East, kuchereza alendo kumasonyezedwa kwa anthu osawadziŵa, mwa kuwapatsa kapu ya tii kapena kofi. Pamenepo, mposadabwitsa kuti Paulo analemba kuti: “Patsani zosoŵa oyera mtima; cherezani aulendo.” (Aroma 12:13) Liwu Lachigiriki la kuchereza alendo, phi·lo·xe·niʹa, kwenikweni limatanthauza “chikondi cha (kukonda, kapena kukomera mtima) alendo.” Ngati Mkristu ayenera kukhala wochereza alendo, kodi sikukakhala koyenera kwambiri kuchereza awo amene ali ogwirizana naye m’chikhulupiriro? Chiitano cha kudzadya nawo chakudya kaŵirikaŵiri chimapereka mpumulo woyamikirika m’zochitika za wokalamba zatsiku ndi tsiku. Ngati mukufuna kumva luntha ndi nzeru pamacheza anu, phatikizanipo okalamba.—Yerekezerani ndi Luka 14:12-14.
17 Pali njira zambiri zimene okalamba angathandizidwe nazo. Ngati tiumba kagulu koyenda ndi galimoto popita ku Nyumba Yaufumu kapena kumsonkhano, kodi pangakhale okalamba ena amene angafune kunyamulidwa? Musayembekezere kuti akupempheni. Apempheni kuwanyamula. Chithandizo china chabwino ndicho kukawagulira zinthu kusitolo. Kapena ngati ali okhoza, kodi tingamke nawo kokagula zinthu? Koma tsimikizirani kuti kumeneko kuli malo amene akhoza kukhala pansi ndi kupuma ngati zimenezo zingafunike. Mosakayikira kuleza mtima ndi kukoma mtima kudzafunika, koma chiyamikiro chowona mtima cha wokalamba chingakhale chofupa kwambiri.—2 Akorinto 1:11.
Chuma Chabwino Kwambiri cha Mpingo
18. Kodi nchifukwa ninji okalamba ali dalitso la mpingo?
18 Ndidalitso labwino kwambiri chotani nanga kuona anthu aimvi (ndiponso anthu adazi chifukwa cha ukalamba) mumpingo! Zimenezi zimatanthauza kuti pakati pa anthu achichepere aumoyo ndi anyonga, tili ndi kagulu ka anthu a luntha ndi achidziŵitso—chuma chenicheni kumpingo uliwonse. Chidziŵitso chawo chili ngati madzi otsitsimula amene ayenera kutungidwa m’chitsime. Zimenezi zili monga momwe lemba la Miyambo 18:4 limanenera: “Mawu a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.” Nkolimbikitsa chotani nanga kwa okalamba kudziona kuti amafunidwa ndi kuyamikiridwa!—Yerekezerani ndi Salmo 92:14.
19. Kodi ndimotani mmene ena achitira kudzimana kaamba ka makolo awo okalamba?
19 Ena okhala muutumiki wanthaŵi yonse alingalira zoleka mwaŵi wa gawo lawo kotero kuti abwerere kwawo kukasamalira makolo okalamba kapena odwala. Adzimana kaamba ka awo amene poyambapo anadzimana kaamba ka iwo. Mwamuna ndi mkazi wina, amene kale anali amishonale ndipo adakali muutumiki wanthaŵi yonse, anabwerera kwawo kukasamalira makolo awo okalamba. Achita zimenezi kwa zaka zoposa 20. Zaka zinayi zapitazo amake a mwamunayo anaikidwa kumalo osungira okalamba. Mwamunayo, tsopano amene ali m’ma 60, amakaona amake azaka 93 tsiku ndi tsiku. Iye akufotokoza kuti: “Kodi ndingawasiye motani? Iwo ndimayi wanga!” M’zochitika zina mipingo ndi anthu ena paokha apezeka ndi kudzipereka kuti asamalire okalamba kotero kuti ana awo akhalebe m’magawo awo. Chikondi chenicheni chimenecho nchoyenerera kuyamikiridwa kwambiri. Mkhalidwe uliwonse uyenera kusamaliridwa ndi mtima wonse chifukwa chakuti anthu okalamba sayenera kunyalanyazidwa. Sonyezani kuti mumakonda makolo anu okalamba.—Eksodo 20:12; Aefeso 6:2, 3.
20. Kodi ndichitsanzo chotani chimene Yehova watipatsa posamalira okalamba?
20 Ndithudi, abale ndi alongo athu okalamba ali korona wokongola m’banja kapena mumpingo. Yehova anati: “Ngakhale mpaka mudzakalamba ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.” Tisonyezetu kuleza mtima kumodzimodziko ndi chisamaliro kwa abale ndi alongo athu okalamba m’banja Lachikristu.—Yesaya 46:4; Miyambo 16:31.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1987, tsamba 13-18, kuti mupeze malingaliro atsatanetsatane onena za zimene ziŵalo za banja zingachite kuthandiza okalamba.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndizitsanzo za m’Baibulo zotani zimene tili nazo pankhani ya kusamalira okalamba?
◻ Kodi ndimotani mmene tiyenera kuchitira ndi okalamba?
◻ Kodi ndimotani mmene ziŵalo za banja zingasamalirire okalamba amene amawakonda?
◻ Kodi mpingo ungachitenji kuti uthandize okalamba?
◻ Kodi nchifukwa ninji okalamba ali dalitso kwa tonsefe?
[Chithunzi patsamba 23]
Rute anasonyeza kukoma mtima ndi ulemu kwa Naomi wokalamba
[Chithunzi patsamba 24]
Okalamba ali ziŵalo zamtengo wapatali za mpingo